Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 15:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mai wina wachikanani, wa ku madera amenewo, adadza kwa Yesu. Adafuula kuti, “Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi ngwogwidwa koopsa ndi mzimu woipa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 15:22
19 Mawu Ofanana  

Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.


Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.


Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.


si kwa mitundu yambiri ya anthu a chinenedwe chosamveka ndi chovuta, amene sungathe kudziwitsa chinenedwe chao. Zedi ndikakutumiza kwa iwowa adzamvera iwe.


Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.


Koma Iye sanamyankhe mau amodzi. Ndipo ophunzira ake anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu.


Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi.


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.


ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire chifundo.


Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.


ndipo ovutidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa