Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo zinampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa ku chiphompho chakuya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo zinampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa ku chiphompho chakuya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Kenaka mizimuyo idapempha Yesu kuti asailamule kuti ikaloŵe ku chiphompho chao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Ndipo ziwandazo zimamupempha mobwerezabwereza kuti asazitumize ku dzenje la mdima.

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:31
14 Mawu Ofanana  

Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.


Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau aakulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze.


Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya m'phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola.


kapena, Adzatsikira ndani ku chiphompho chakuya? Ndiko, kukweza Khristu kwa akufa,


Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao chilombo chokwera kutuluka m'chiphompho chakuya chidzachita nazo nkhondo, ndipo chidzazigonjetsa, ndi kupha izo.


Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.


Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure:


Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake mu Chihebri Abadoni, ndi mu Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa