Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Tsono Yesu adamufunsa munthuyo kuti, “Dzina lako ndani?” Iye adayankha kuti, “Dzina langa ndine Chigulu,” chifukwa mizimu yoipa yochuluka inali itamuloŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Yesu anamufunsa kuti, “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti, “Legiyo,” chifukwa ziwanda zambiri zinalowa mwa iye.

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:30
7 Mawu Ofanana  

Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike?


Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri.


Ndipo anamfunsa, Dzina lako ndani? Ndipo ananena kwa Iye, Dzina langa ndine Legio; chifukwa tili ambiri.


ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye,


Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa