Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:29 - Buku Lopatulika

29 Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Adaatero chifukwa Yesu anali atalamula mzimu woipawo kuti utuluke mwa munthuyo. (Ndiye kuti kaŵirikaŵiri ukamugwira, anthu ankamumanga manja ndi maunyolo, nkumumanganso miyendo ndi zitsulo kuti amugwiritse bwino. Koma iyeyo ankazingomwetsula zomangirazo, ndipo mzimuwo unkamupirikitsira ku thengo.)

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Pakuti Yesu analamula mzimu woyipawo kuti utuluke mwa munthuyo. Kawirikawiri umamugwira iye, ndipo ngakhale anali womangidwa ndi unyolo dzanja ndi mwendo ndi kuti ankamuyangʼanira, koma amadula maunyolo akewo ndipo ziwanda zimamutengera kumalo a yekha.

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:29
9 Mawu Ofanana  

Pakuti ananena kwa iye, Tuluka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu.


Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau aakulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze.


Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye.


ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, suchoka pa iye, koma umsautsa koopsa.


Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa