Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:28 - Buku Lopatulika

28 Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau aakulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau akulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Pamene iye adaona Yesu, adafuula nadzigwetsa ku mapazi ake, ndipo adanena mokweza mau kuti, “Kodi ndakuputani chiyani Inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wopambanazonse? Ndakupembani, musandizunze.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Iye ataona Yesu, anakuwa nagwa pa mapazi ake akufuwula kwambiri kuti, “Mukufuna chiyani ndi ine, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Ndikupemphani Inu, musandizunze ine!”

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:28
14 Mawu Ofanana  

Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.


Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike?


Ndipo atatuluka pamtunda Iye, anakomana naye mwamuna wa kumzinda, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanavale chovala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda.


Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu.


Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira.


Pakuti ngati Mulungu sanalekerere angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika kumaenje a mdima, asungike akaweruzidwe;


iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.


Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa