Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:15 - Buku Lopatulika

15 Koma ena mwa iwo anati, Ndi Belezebulu mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma ena mwa iwo anati, Ndi Belezebulu mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Koma ena mwa iwo adati, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipazi nzochokera kwa Belezebulu, mkulu wa mizimu yoipayo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Koma ena mwa iwo anati, “Iye akutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mfumu ya ziwanda.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:15
11 Mawu Ofanana  

Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?


Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamchiritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya.


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda.


Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumva Iye bwanji?


Khamu la anthu linayankha, Muli ndi chiwanda: afuna ndani kukuphani Inu?


Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?


Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa