Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 3:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo njoka inali yochenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo njoka inali yakuchenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Njoka inali yochenjera kupambana zamoyo zonse zimene Chauta adazilenga. Njokayo idafunsa mkazi uja kuti, “Kodi nzoona kuti Mulungu adakuletsani kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse m'munda muno?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 3:1
14 Mawu Ofanana  

Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa.


Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate.


nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala.


nati kwa Iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.


Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.


Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.


Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.


Ndipo njokayo inalavula m'kamwa mwake, madzi ngati mtsinje, potsata mkazi, kuti mkaziyo akakokoleredwe nao.


Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.


Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa