Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 6:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Kodi Khristu nkuvomerezana ndi Satana? Kodi mkhristu ndi mkunja angagaŵanenso chiyani pamodzi?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Pali mgwirizano wanji pakati pa Khristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupirira angayanjane bwanji ndi munthu wosakhulupirira?

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 6:15
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.


Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akulu otsala a nyumba za makolo a Israele, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi mfumu ya Persiya watilamulira.


Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.


ndipo makamaka anaonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi;


Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.


koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupirira?


Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.


chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m'mzindawo, ndiwo anthu otama zopanda pake, anazinga nyumba, nagogodagogoda pachitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Tulutsa mwamunayo adalowa m'nyumba mwako kuti timdziwe.


Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pake, okhala mu Gibea, kuti tiwaphe, ndi kuchotsera Israele choipachi. Koma Benjamini sanafune kumvera mau a abale ao, ana a Israele.


Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa