Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:16 - Buku Lopatulika

16 Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yoŵaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Anthu ochuluka ochokera ku mizinda yayingʼono ozungulira Yerusalemu amasonkhananso atatenga odwala awo ndi iwo amene amasautsidwa ndi mizimu yoyipa ndipo onsewo amachiritsidwa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:16
16 Mawu Ofanana  

Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse;


Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, Iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapo Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene anachokera kumidzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi Iye yakuwachiritsa.


ndipo ovutidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa,


Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate.


m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.


kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo.


Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a chipatuko cha Asaduki, nadukidwa,


kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu mmodziyo;


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa