Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:15 - Buku Lopatulika

15 kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Tsono anthu ankatulutsira odwala ao m'miseu yamumzinda, nkumaŵagoneka pa mabedi ndi pa mphasa, kuti Petro podutsapo, chithunzithunzi chake chokha ena mwa iwo chiŵafike.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Chifukwa cha zimenezi, anthu anabweretsa odwala mʼmisewu ya mu mzinda nawagoneka pa mabedi ndi pa mphasa kuti chithunzi chokha cha Petro chikhudze ena mwa iwo iye akamadutsa.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:15
8 Mawu Ofanana  

mphindi yakupha ndi mphindi yakuchiza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga;


ndipo anampempha Iye, kuti akhudze mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.


pakuti analikunena mwa iye yekha, Ngati ndingakhudze chofunda chake chokha ndidzachira.


nathamangira dziko lonselo nayamba kunyamula anthu odwala pa mphasa zao, kufika nao kumene anamva kuti analiko Iye.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate.


Ndipo patachitika ichi, enanso a m'chisumbu, okhala nazo nthenda, anadza, nachiritsidwa;


Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa