Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 5:17 - Buku Lopatulika

17 Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a chipatuko cha Asaduki, nadukidwa,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a chipatuko cha Asaduki, nadukidwa,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Pamenepo mkulu wa ansembe onse pamodzi ndi anzake aja, ndiye kuti a m'chipani cha Asaduki, onsewo adadukidwa nazo. Tsono adagamula zochitapo kanthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Koma mkulu wa ansembe pamodzi ndi onse omuthandiza, amene anali a gulu la Asaduki, anachita nsanje.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 5:17
24 Mawu Ofanana  

Pakuti mkwiyo umapha wopusa, ndi nsanje imakantha wopanda pake.


Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; koma nsanje ivunditsa mafupa.


Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka; koma ndani angalakike ndi nsanje?


Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pakuti anadziwa kuti anampereka Iye mwanjiru.


Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?


Koma ansembe aakulu anapangana kuti akaphe Lazaronso;


Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.


Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.


Koma anauka ena a mpatuko wa Afarisi okhulupirira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge chilamulo cha Mose.


Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m'mzinda; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu.


Anadzindandalitsa mafumu a dziko, ndipo oweruza anasonkhanidwa pamodzi, kutsutsana ndi Ambuye, ndi Khristu wake.


ndi Anasi mkulu wa ansembe, ndi Kayafa, ndi Yohane, ndi Aleksandro, ndi onse amene anali a fuko la mkulu wa ansembe.


Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.


Ndipo makolo aakuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye,


njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.


Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?


Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa