Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Yohane 2:13 - Buku Lopatulika

13 Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamgonjetsa woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamlaka woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Inu atate, ndikukulemberani, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Inu achinyamata, ndikukulemberani, chifukwa mwampambana Woipa uja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Inu abambo, ndikukulemberani popeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi. Inu anyamata, ndikukulemberani popeza kuti munagonjetsa woyipayo.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 2:13
36 Mawu Ofanana  

Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana.


Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.


Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.


Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yao; kukongola kwa nkhalamba ndi imvi.


Ndipo kudzachitika m'tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya;


Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.


Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha, ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.


Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.


Ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo;


Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.


Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye.


Mukadazindikira Ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira Iye, ndipo mwamuona Iye.


Yesu ananena naye, Kodi ndili ndi inu nthawi yaikulu yotere, ndipo sunandizindikire, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?


Ndipo izi adzachita, chifukwa sanadziwe Atate, kapena Ine.


Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.


kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu munandituma Ine.


Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.


Chifukwa chake ananena ndi Iye, Ali kuti Atate wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukadadziwanso Atate wanga.


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale;


Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa;


Chimene chinaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiona m'maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mau a moyo,


Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama;


Ndikulemberani, tiana, popeza machimo adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lake.


Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamgonjetsa woipayo.


osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.


Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munaipambana; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi;


Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


Ndipo iwo anampambana iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonde moyo wao kungakhale kufikira imfa.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa