Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 18:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adafuula mokweza mau ndi kunena kuti, “Wagwa, wagwa Babiloni wotchuka uja! Wasanduka malo okhalamo mizimu yoipa, malo othaŵiramo mizimu yonse yonyansa, malo othaŵiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodedwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti: “ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’ Wasandulika mokhalamo ziwanda ndi kofikako mizimu yonse yoyipa ndi mbalame zonse zonyansa ndi zodetsedwa.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 18:2
26 Mawu Ofanana  

Ndidzayesapo pokhala nungu, ndi maiwe a madzi; ndipo ndidzasesapo ndi tsache la chionongeko, ati Yehova wa makamu.


Chifukwa chake muwanenere iwo mau onse awa, ndi kuti kwa iwo, Yehova adzabangula kumwamba, nadzatchula mau ake mokhalamo mwake moyera; adzabangulitsira khola lake; adzafuula, monga iwo akuponda mphesa, adzafuulira onse okhala m'dziko lapansi.


Ndipo Babiloni adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, chizizwitso, chotsonyetsa, wopanda okhalamo.


Babiloni wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zake vunguti, kapena angachire.


Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.


Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pake; nyama zonse za mitundumitundu; ndi vuwo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zake; adzaimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala chipasuko; pakuti anagadamula ntchito yake ya mkungudza.


ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m'ng'anjo; ndi mau ake ngati mkokomo wa madzi ambiri.


nafuula ndi mau aakulu, monga ngati mkango ubangula; ndipo pamene anafuula mabingu asanu ndi awiri analankhula mau ao.


Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala lamzinda waukulu, umene utchedwa, ponena zachizimu, Sodomu ndi Ejipito, pameneponso Ambuye wao anapachikidwa.


Ndipo mngelo wina anatuluka mu Kachisi, wofuula ndi mau aakulu kwa Iye wakukhala pamtambo, Tumiza chisenga chako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zachetsa.


Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake.


Ndipo ndinaona motuluka m'kamwa mwa chinjoka, ndi m'kamwa mwa chilombo, ndi m'kamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati achule;


Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndi mizinda ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake.


Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mzinda waukulu, wakuchita ufumu pa mafumu a dziko.


ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.


chifukwa chakuopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mzinda waukuluwo, Babiloni, mzinda wolimba! Pakuti mu ora limodzi chafika chiweruziro chanu.


Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala ngati mphero yaikulu, naiponya m'nyanja, nanena, Chotero Babiloni, mzinda waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.


Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu wakulalikira ndi mau aakulu, Ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikiro zake?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa