1 Samueli 16:14 - Buku Lopatulika14 Koma mzimu wa Yehova unamchokera Saulo, ndi mzimu woipa wochokera kwa Yehova unamvuta iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Koma mzimu wa Yehova unamchokera Saulo, ndi mzimu woipa wochokera kwa Yehova unamvuta iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Nthaŵi imeneyo mzimu wa Chauta udaamchokera Saulo ndipo mzimu wina woipa, wotumidwa ndi Chauta, udayamba kumzunza. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Nthawi imeneyo Mzimu wa Yehova unamuchokera Sauli, ndipo mzimu woyipa wochokera kwa Yehova unayamba kumuzunza. Onani mutuwo |
Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.