Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 16:23 - Buku Lopatulika

23 Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Koma Yesu adacheuka namdzudzula. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Ufuna kundilakwitsa. Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Yesu anatembenuka nati kwa Petro, “Choka pamaso panga Satana! Iwe ndi chokhumudwitsa kwa Ine; iwe suganizira zinthu za Mulungu koma zinthu za anthu.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 16:23
19 Mawu Ofanana  

Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:


Koma Davide anati, Ndili ndi chiyani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa mu Israele lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israele lero?


Pamenepo Satana anaukira Israele, nasonkhezera Davide awerenge Israele.


Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israele, khwekhwe ndi msampha wa okhala mu Yerusalemu.


Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ai.


Tsoka lili ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! Pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka lili ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye.


Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, namdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.


Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.


Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi?


Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa panjira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.


Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako.


chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.


Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa