Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 4:4 - Buku Lopatulika

4 Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 4:4
26 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu.


Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.


Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova.


Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu;


si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.


Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.


Ndipo anati, Chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu.


Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako.


Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.


Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.


Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni.


Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.


Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.


Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu;


Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m'kamwa mwa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa