Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 13:4 - Buku Lopatulika

4 pakuti anapachikidwa mu ufooko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tili ofooka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi Iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 pakuti anapachikidwa m'ufooko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tili ofooka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi Iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Anali wofooka pamene adapachikidwa pa mtanda, komabe tsopano ali moyo mwa mphamvu ya Mulungu. Ifenso ndife ofooka mwa Iye, koma tidzakhala amoyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, pogwira ntchito yathu pakati panu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Pofuna kutsimikizira, anapachikidwa ali wofowoka koma ali ndi moyo mwamphamvu ya Mulungu. Chomwechonso, ife ndife ofowoka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, potumikira pakati panu.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 13:4
26 Mawu Ofanana  

Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.


Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.


Ndipo pa chikhulupiriro cha m'dzina lake dzina lakelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo chikhulupiriro chili mwa Iye chinampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.


amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Khristu Ambuye wathu;


Pakuti, chifukwa cha ichi Khristu adafera, nakhalanso ndi moyo, kuti Iye akakhale Ambuye wa akufa ndi wa amoyo.


Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.


Chifukwa kuti chopusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zao; ndipo chofooka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yao.


lifesedwa m'mnyozo, liukitsidwa mu ulemerero; lifesedwa m'chifooko, liukitsidwa mumphamvu;


Ndipo ine ndinakhala nanu mofooka ndi m'mantha, ndi monthunthumira mwambiri.


koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yake.


Pakuti, makalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.


Chifukwa chake ndisangalala m'mafooko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, chifukwa cha Khristu; pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.


Pakuti tikondwera, pamene ife tifooka ndi inu muli amphamvu; ichinso tipempherera, ndicho ungwiro wanu.


kuti ndimzindikire Iye, ndi mphamvu ya kuuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake;


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa