Mulungu wapatsa mphatso ana ake, ndipo Mzimu Woyera amagawa mphatso zimenezi monga mmene Iye akufunira. Monga mmene lemba la 1 Akorinto 12:11 limatiuza, "Mzimu yemweyo amagwira ntchito mwa onse, akugaŵira aliyense payekha monga mmene Iye akufunira."
Mphatso zauzimu ndi zipangizo zapadera zimene Mulungu amapatsa ana ake kuti amange mpingo wake ndi anthu ake, malinga ndi zosowa za kuwonetsa mphamvu yake. Tiyenera kugwiritsa ntchito mphatso zimenezi kuti tidalitsane wina ndi mnzake ndipo motero timange mpingo wamphamvu wolemekeza Mulungu.
Mphatso imene Mzimu Woyera waika mwa iwe ndi chizindikiro cha chikondi cha Atate wakumwamba. Choncho, usayibise kapena kuilola kuti itaike, uyisamalire ngati chuma chamtengo wapatali ndipo uthokoze Mulungu nthawi zonse kuti uzitha kuyigwiritsa ntchito potumikira ena, podziwa kuti si ya phindu lako, koma ya phindu la iwo akuzungulira iwe.
Mulungu wakutuma kuti ukhale yankho la mapemphero awo. Kumbukira nthawi zonse kuti mphatso sizichoka, kutanthauza kuti Ambuye sadzachotsa chimene wakupatsa. Choncho, khalani woyang'anira bwino wa chimene Mulungu wakupatsa ndipo usaiwale kumupatsa ulemerero nthawi zonse, chifukwa ndiwe chotengera m'manja mwake.
Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu.
Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike;
Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.
Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro;
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;
kotero kuti sichikusowani inu chaufulu chilichonse; pakulindira inu vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Khristu;
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro; kapena yakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako; kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.
Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi. Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu. Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye. Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira, koma kwa iwo osakhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira. Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka? Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse; zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu. Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira. Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire. Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu. Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire. Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa. Koma ngati kanthu kuvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo. Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzimmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe; ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri; pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima. Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena. Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna ao a iwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo. Kodi mau a Mulungu anatuluka kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha? Ngati wina ayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye. Koma ngati wina akhale wosadziwa, akhale wosadziwa. Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime. Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo.
Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;
Chikondi sichitha nthawi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.
Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime.
Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;
Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.
monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu; akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.
Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;
Kodi ali onse atumwi? Ali aneneri onse kodi? Ali aphunzitsi onse? Ali onse ochita zozizwa? Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera. Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malilime? Kodi onse amasulira mau?
Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.
Momwemo inunso, popeza muli ofunitsitsa mphatso za Mzimu, funani kuti mukachuluke kukumangirira kwa Mpingo.
Chifukwa chake ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe mwa kuika kwa manja anga.
Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira.
Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo. Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,
m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu. Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa.
Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo.
Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.
umene anandikhalitsa mtumiki wake monga mwa mphatso ya chisomo cha Mulungu, chimene anandipatsa ine, monga mwa machitidwe a mphamvu yake.
Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhale ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu; kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.
Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito, mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;
pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.
pakuti kale lonse chinenero sichinadze ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.
Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.
Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse.
Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano; adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzachira.
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
Musazime Mzimuyo; Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. Musanyoze manenero; Yesani zonse; sungani chokomacho,
Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira, koma kwa iwo osakhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira.
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.
Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?
Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m'chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu.
Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;