Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 12:27 - Buku Lopatulika

27 Koma inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Koma inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Tsopano inu ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense wa inu ndi chiwalo cha thupilo.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 12:27
14 Mawu Ofanana  

chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina.


kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala mu Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:


Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi.


Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.


Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.


Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Khristu? Chifukwa chake ndidzatenga ziwalo za Khristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi wachiwerewere? Msatero iai.


amene ali thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse m'zonse.


kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;


Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.


pakuti tili ziwalo za thupi lake.


Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.


Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;


kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa