Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

110 Mau a m'Baibulo Okhudza Temberero

Mulungu, mwa nzeru zake zazikulu, amatiuza kudzera m’Malemba Opatulika kuti temberero limabwera chifukwa cha uchimo ndi kusamvera chifuniro chake choyera. Kuyambira pachiyambi cha anthu, pamene Adamu ndi Eva sanamvere Mulungu m’munda wa Edeni, temberero linalowa m’dziko.

Temberero ndi chiwonetsero cha chilungamo cha Mulungu, chomwe chimabwera chifukwa chosamvera Mulungu ndi kutsata njira zathu. M’buku la Genesis, Mulungu atati munthu wachimwa, anati: “Nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; ndi zowawa udzadya zipatso zake masiku onse a moyo wako.” (Genesis 3:17). Temberero limeneli silinagwire ntchito kwa Adamu ndi Eva okha, koma kwa anthu onse, kuyambira pamenepo, masautso, ululu ndi mavuto zinakhalapo m’miyoyo ya anthu.

Komabe, ngakhale kuti temberero linalowa m’dziko, Mulungu, m’chikondi chake chachikulu ndi chifundo, amatipatsa yankho kudzera mwa Yesu Khristu, amene anatenga temberero la uchimo pa mtanda, motero tingamasulidwe ku katundu ameneyu, monga mwalembedwera m’buku la Agalatiya: “Khristu anatiwombola ku temberero la chilamulo, pokhala temberero m’malo mwathu.” (Agalatiya 3:13). Yesu anakhala temberero m’malo mwathu, natenga chilango chimene tinali kuyenera kulandira.

Choncho, poyang’ana Yesu Khristu ndi kumulandira ngati Mpulumutsi wathu, tingamasulidwe ku temberero ndi kulowa m’moyo watsopano woyanjana ndi Mulungu. Baibulo limatiphunzitsa kuti mwa Khristu ndife cholengedwa chatsopano: “Chotero ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, iye ndiye cholengedwa chatsopano; zakale zapita; taonani, zatsopano zapangidwa.” (2 Akorinto 5:17).


Agalatiya 3:13

Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.”

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:29

M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:15

Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa:

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:8

Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:16-19

Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu.

Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu.

Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe.

Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:7

“Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Mulunguyo sadzamleka aliyense wotchula pachabe dzina lakelo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 23:10

Dziko lino ladzaza ndi anthu achigololo. Chifukwa cha temberero la Chauta m'dziko mwagwa chilala, mabusa akuchipululu auma. Amene amangothamangira zoipa, amalimbikira kuchita zosalungama.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:5

Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 3:10

Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 11:26-28

Lero ndikukupatsani zinthu ziŵiri kuti musankhepo, madalitso kapena matemberero.

Madalitso kwa inu, mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndikukupatsani leroŵa.

Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 48:10

“Ndi wotembereredwa amene amagwira ntchito ya Chauta mwaulesi. Ndi wotembereredwa amene amaletsa lupanga lake kutema ndi kupha anthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 17:5

Chauta akunena kuti, “Tsoka kwa munthu wodalira munthu mnzake, amene amagonera pa munthu mnzake kuti amthandize, pamene mtima wake wafulatira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:14

Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 26:14-16

“Koma mukapanda kundimvera ndi kutsata malamulo anga onseŵa,

mukamanyoza malamulo anga, ndipo mtima wanu ukamadana ndi zimene ndikulamulani, mpaka kusamvera malamulo anga onse ndi kuswa chipangano changa,

ndidzakuchitani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi, chifuwa chachikulu choondetsa ndiponso malungo oononga maso ndi ofooketsa moyo. Mudzabzala mbeu zanu, koma osakololapo kanthu, chifukwa choti adani anu adzazidya.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 109:17

Ankakonda kutemberera, choncho matemberero amgwere. Sadakonde kudalitsa anthu ena, choncho madalitso akhale kutali ndi iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 27:15-26

“Atembereredwe aliyense wopanga fano losema kapena loumba, namalipembedza mobisa. Chauta amanyansidwa nacho chinthu chopanga mmisiricho.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

“Atembereredwe aliyense wosalemekeza atate ndi amai ake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

“Atembereredwe aliyense wosuntha malire a mnansi wake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

“Atembereredwe aliyense wosokeza munthu wakhungu.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

“Atembereredwe aliyense woweruza mopotoza milandu ya alendo, ya ana amasiye, ndi ya akazi amasiye.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

Pa tsiku limene muzaoloke mtsinje wa Yordani ndi kuloŵa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani, mudzaimiritse miyala yaitali, ndipo mudzaikulungize.

“Atembereredwe aliyense wogona ndi mkazi wa bambo wake, chifukwa wavula mkazi wa bambo wake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

“Atembereredwe aliyense wogona ndi nyama.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

“Atembereredwe aliyense wogona ndi mlongo wake, kapena mlongo wake wa mimba ina.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

“Atembereredwe aliyense wogona ndi mpongozi wake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

“Atembereredwe aliyense wopha mnzake mwachinsinsi.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

“Atembereredwe onse olandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

“Atembereredwe aliyense wosavomereza ndi wosatsata malamulo amene tatchulaŵa.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 3:17

Kenaka Mulungu adauza Adamu kuti, “Iwe unamvera mkazi wako, wadya zipatso zija zimene ndidaakuuza kuti usadye. Nthaka idzatembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi. Udzayenera kugwira ntchito yathukuta nthaŵi ya moyo wako wonse, kuti upeze chakudya chokwanira.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 6:28

Muziŵafunira madalitso amene amakutembererani, muziŵapempherera amene amakuvutitsani.

Mutu    |  Mabaibulo
Malaki 3:9

Ndinu otembereredwa nonsenu, mtundu wanu wonse, chifukwa choti mumandibera.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 3:14

Pamenepo Chauta adauza njokayo kuti, “Chifukwa chakuti wachita zimenezi, ndiwe wotembereredwa pakati pa nyama zonse za pansi pano, zoŵeta ndi zakuthengo zomwe. Kuyambira tsopano mpaka muyaya udzakwaŵa ndi kumimba kwako, ndipo chakudya chako chidzakhala fumbi.

Mutu    |  Mabaibulo
Numeri 23:8

Koma ine ndingathe bwanji kumtemberera amene Mulungu sadamtemberere? Ndingathe bwanji kumufunira zoipa amene Chauta sadamfunire zoipa?

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 30:19

Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo,

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 3:1

Pambuyo pake Yobe adalankhula, nayamba kutemberera tsiku lake lobadwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:33

Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 5:3-4

Tsono adandiwuza kuti, “Pamenepo palembedwa temberero limene lidzagwera dziko lonse lapansi. Aliyense wakuba adzachotsedwa m'dziko potsata zimene zalembedwa mbali iyi, ndipo aliyense wolumbira zabodza nayenso adzachotsedwa potsata zimene zalembedwa mbali inai.

Chauta Wamphamvuzonse wanena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza m'nyumba ya munthu wakuba ndi m'nyumba ya munthu wolumbira zabodza potchula dzina langa. Lidzakhala m'nyumbamo mpaka kuiwonongeratu, mitengo yake ndi miyala yake yomwe.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 22:14

Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lakuya. Amene Chauta amamkwiyira adzagwamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 26:2

Monga imachitira mpheta yokhalira kuuluka, monga amachitira namzeze kumangoti zwezwezwe, ndimonso limachitira temberero lopanda chifukwa, silitha.

Mutu    |  Mabaibulo
Malaki 2:2

Mukapanda kundimvera, mukapanda kulemekeza dzina langa, ndidzakutembererani. Zabwino zimene mumazilandira nazonso ndidzazitemberera. Ndithu, ndazitemberera kale chifukwa simudamvere ndi mtima wonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 25:41

“Pambuyo pake Mfumuyo idzauzanso a ku dzanja lake lamanzere aja kuti, ‘Chokani apa, inu otembereredwa. Pitani ku moto wosatha, umene Mulungu adakonzera Satana ndi angelo ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 24:6

Nchifukwa chake Mulungu watemberera dziko lapansi, anthu am'dzikomo akuzunzika chifukwa cha machimo ao. Iwo amalizika, ndipo atsala ndi oŵerengeka okha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 11:3

Uŵauze kuti mau a Chauta, Mulungu wa Israele, ndi aŵa: Atembereredwe munthu amene sasunga mau a chipangano,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 15:23

Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Malaki 4:6

Iyeyo adzayanjanitsa atate ndi ana ao, ana ndi atate ao, kuwopa kuti ndingadzabwere kudzatemberera dziko lanu kuti liwonongeke.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:20-22

Mukamachita zoipa ndi kumkana Mulungu, Iye adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndiponso zokuvutani pa ntchito zanu zonse, mpaka mutaonongeka ndi kufa nonsenu pa kamphindi kochepa.

Adzakutumizirani matenda otsatanatsatana, mpaka mutatha nonse kuti psiti m'dziko limene muli kukakhalamolo.

Chauta adzakukanthani ndi nthenda zopatsana, zotupatupa ndi zamalungo. Adzakutumiziraninso kutentha koopsa ndi chilala ndiponso chinsikwi ndi chinoni zoononga mbeu zanu. Masoka amenewo adzakhala pa inu mpaka kukufetsani.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 6:8

Koma ngati ibereka minga ndi nthula, ndi yachabe ndipo ili pafupi kutembereredwa. Mathero ake nkutenthedwa m'moto.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:16

Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:17

Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 109:17-18

Ankakonda kutemberera, choncho matemberero amgwere. Sadakonde kudalitsa anthu ena, choncho madalitso akhale kutali ndi iye.

Kutemberera anzake kunali ngati chovala chake, motero matemberero amgwere ngati mvula. Akhale ngati mafuta oloŵa m'mafupa mwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 21:22-23

Munthu akaphedwa chifukwa cha mlandu, ndipo mtembo wake ndi wopachikidwa pa mtengo,

mtembowo usagonere pamtengopo. Uikidwe tsiku lomwelo, chifukwa kuti mtembo ugonerere pamtengo ndi chinthu chobweretsa matemberero a Mulungu. Kwirirani mtembowo, kuwopa kuti mungaipitse dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 28:27

Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 7:26

Musadzaloŵe nazo m'nyumba mwanu zimenezi, kuti tsoka limene lili pa iwowo lingadzakhale pa inu. Mudzadane ndi mafanowo ndi kuŵanyoza, chifukwa Chauta adaŵatemberera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 65:20

Ana sadzafanso ali akhanda, ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zao zonse. Amene adzafe ali a zaka zana limodzi zokha adzaoneka ngati anyamata. Kufa zisanakwane zaka zana limodzi kudzasonyeza kutembereredwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:28

Mafumu anu adaipitsa malo anga opatulika. Nchifukwa chake ndidalola kuti banja la Yakobe liwonongedwe, ndidalola kuti Aisraele anyozedwe.”

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 3:17-19

Kenaka Mulungu adauza Adamu kuti, “Iwe unamvera mkazi wako, wadya zipatso zija zimene ndidaakuuza kuti usadye. Nthaka idzatembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi. Udzayenera kugwira ntchito yathukuta nthaŵi ya moyo wako wonse, kuti upeze chakudya chokwanira.

M'nthakamo mudzamera zitsamba za minga ndi za nthula, ndipo iwe udzadya zomera zakuthengo.

Udzayenera kukhetsa thukuta kuti upeze chakudya, mpaka udzabwerera kunthaka komwe udachokera. Udachokera ku dothi, udzabwereranso kudothi komweko.”

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 4:11-12

Tsopano watembereredwa, sudzailimanso nthaka yomwe yamwa magazi a mng'ono wako, amene waŵakhetsa ndi manja ako.

Ukamalima mbeu, nthakayo sidzakubalira, ndipo udzakhala womangoyendayenda, wosoŵa pokhala penipeni pa dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 24:24

Amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wosalakwa,” anthu adzamtemberera, ndipo mitundu ya anthu idzaipidwa naye.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 29:19-20

Chonde muchenjere kuti pasakhale wina pano lero, womva mau ameneŵa, komabe namanena mumtima mwake kuti zinthu zidzamuyenderabe bwino, ngakhale akhale wokanika chotani nkumachita zake. Zimenezi zidzangoputira nonsenu chiwonongeko, abwino ndi oipa omwe.

Mose adaitana Aisraele onse aja, naŵauza kuti: Paja mudadziwonera nokha zimene Chauta adachita mfumu ya ku Ejipito ndi nduna zake ndi dziko lake lonse.

Munthu wotere Chauta sadzamkhululukira. Ndithu Chauta adzamkwiyira ndi nsanje yoyaka. Matemberero olembedwa m'buku muno adzamgwera ndipo Chauta adzamuwonongeratu ndipo adzaiŵalika pa dziko.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:22

Anthu amene Chauta adaŵadalitsa, adzalandira dziko kuti likhale lao, koma amene Chauta adaŵatemberera adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 34:5

Chauta akuti, “Lupanga langa lakhutiratu kumwamba. Si ili likutsika kudzalanga Aedomu, anthu amene ndatsimikiza kuti ndiŵaononga.”

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 18:20

Munthu wochimwa ndiye amene adzafe, osati wina. Mwana sadzafera machimo a bambo wake, ndipo bambo sadzafera machimo a mwana wake. Munthu wabwino adzakolola zipatso za ubwino wake. Munthu woipa adzakolola zipatso za kuipa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 23:5

Koma Chauta, Mulungu wanu, sadamumvere Balamuyo. Matembererowo adaŵasandutsa madalitso pa inu, popeza kuti adakukondani inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 1:8-9

Koma aliyense, kaya ndife kaya ndi mngelo wochokera Kumwamba, akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi uja tidakulalikiraniwu, ameneyo akhale wotembereredwa.

Ndikubwereza kunena zimene tidaanenanso kale, kuti munthu aliyense akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi Uthenga Wabwino umene mudalandira uja, iyeyo akhale wotembereredwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Oweruza 5:23

“Mngelo wa Chauta akuti, ‘Utemberere Merozi, utemberere koopsa nzika zake, chifukwa chakuti sizidabwere kudzathandiza Chauta, pakulimbana ndi adani ake amphamvu.’

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 9:25

ndipo adati, “Atembereredwe Kanani! Adzakhala kapolo weniweni wa abale ake.” Popitiriza mau adati,

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 30:7

Koma Chauta, Mulungu wanu, adzagwetsa matemberero onse aja pa adani anu amene adakuzunzani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:21

Inu mumadzudzula onyada, amene ali otembereredwa, amene amasiya malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:44

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 3:14

M'kamwa mwao m'modzaza ndi matemberero, mumatuluka mau oŵaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 12:3

Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti munthu amene Mzimu wa Mulungu amamtsogolera, sanganene kuti, “Yesu atembereredwe.” Ndiponso, munthu amene Mzimu Woyera samtsogolera, sanganene kuti, “Yesu ndi Ambuye.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:45

Masoka onseŵa adzakugwerani. Adzakhala pa inu mpaka mutaonongeka, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudatsate malamulo ndi malangizo onse amene Iye adakupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Petro 2:14

Maso ao ndi adama, osafuna kuleka kuchimwa. Amanyengerera anthu a mtima wosakhazikika. Ali ndi mtima wozoloŵera kuumirira chuma. Anthu otembereredwa!

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 11:10-11

Abwereranso ku machimo a makolo ao amene adakana kundimvera. Akutsata milungu ina ndi kumaipembedza. A ku Israele ndi a ku Yuda aphwanya chipangano chimene ndidapangana ndi makolo ao.

Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti ndidzaŵagwetsa m'mavuto amene sangathe kuŵalewa. Ngakhale alire kwa Ine, sindidzamvera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:53

Ndimapsa mtima kwambiri chifukwa cha anthu oipa amene amaphwanya malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 65:15

Anthu anga osankhidwa adzatchula dzina lanu potemberera, ndipo Ine Chauta ndidzakuphani. Koma amene amandimvera ndidzaŵapatsa dzina lina latsopano.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:58-59

Muzimvera mau onse a malamulo aŵa a m'buku muno, ndipo dzina ili lodabwitsa ndi lochititsa mantha la Chauta, Mulungu wanu, muzilitamanda.

Mukapanda kutero, inuyo ndi zidzukulu zanu, Chauta adzakugwetserani masautso apadera, mavuto aakulu okhalitsa ndiponso nthenda zoopsa zosamva mankhwala.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 13:19

Mwandichotsa ulemu pamaso pa anthu anga, chifukwa chofuna kulandira manja angapo a barele ndiponso zidutswa chabe za buledi. Mukupha anthu osayenera kufa, ndipo mukupulumutsa anthu osayenera kukhala moyo, pomanamiza anthu angaŵa amene amamva zabodza zanuzo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 17:7-8

“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo.

Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 27:15

“Atembereredwe aliyense wopanga fano losema kapena loumba, namalipembedza mobisa. Chauta amanyansidwa nacho chinthu chopanga mmisiricho.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 109:28

Iwo atemberere, koma Inu mundidalitse. Ondiputa muŵachititse manyazi, koma ine mtumiki wanu ndisangalale.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 2:24

Tsono Elisayo adatembenuka, ndipo ataŵaona anyamatawo, adaŵatemberera m'dzina la Chauta. Pompo padatuluka zimbalangondo ziŵiri zazikazi kuchokera kuthengo, nkuphapo anyamata 42.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 16:22

Ngati munthu sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Maranatha! Ambuye athu, bwerani!

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 6:23

Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:21-23

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.

Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’

Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 42:18

“Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunenanso kuti, ‘Monga momwe anthu okhala ku Yerusalemu ndidaŵakwiyira mwaukali, momwemonso ndidzakukwiyirani inuyo mukadzapita ku Ejipito. Mudzasanduka chinthu chonyansa ndi chochititsa mantha, chomachiseka ndi chonyozeka. Malo ano simudzaŵaonanso.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:1-3

Chauta akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira Ine! Amachita zodzikonzera okha osati zokonza Ine. Amachita chipangano chaochao, chosatsata chifuniro changa, ndipo amanka nachimwirachimwira.

Amauza oona zobisika kuti, ‘Musaonenso.’ Amauza aneneri kuti, ‘Musatiloserenso zoona. Mutiwuze zotikomera, mutilosere zam'mutu chabe.

Chokani apa, osakhala pa njira. Sitifuna kumvanso za Woyera uja wa Israele.’ ”

Nchifukwa chake Woyera uja wa Israele akunena kuti, “Inu mumanyozera zimene ndimakuuzani, mumakhulupirira zopsinja anzanu ndipo mumadalira mabodza.

Nchifukwa chake tchimo lanuli lidzakhala ngati mng'ankha pa chipupa chachitali choŵinuka, chimene kugwa kwake nkwadzidzidzi.

Zidzakhala ngati kuphwanyika kwa mbiya, imene ili yotekedzekeratu, popanda ndi phale lomwe lopalira moto, kapena lotungira madzi m'chitsime.”

Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.

Mudati, “Tidzathamanga pa akavalo.” Chabwino, mudzathaŵe! Mudatinso, “Tidzakwera pa magareta aliŵiro.” Chabwino, koma okuthamangitsani adzakhalanso aliŵiro.

Anthu chikwi chimodzi mwa inu adzathaŵa poona mdani mmodzi. Asilikali asanu okha adzakwanira kukuthamangitsani. Otsalira mwa inu adzakhala ngati mtengo wa mbendera wapaphiri, ngati chizindikiro chapagomo.

Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!

Ndithudi, inu anthu a ku Ziyoni, okhala ku Yerusalemu, simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu, ndipo akadzangomva, pompo adzakuyankhani.

Amapita ku Ejipito kukapempha chithandizo, Ine osandifunsa. Amathaŵira kwa Farao kuti aŵatchinjirize, amakafuna malo opulumukirako ku Ejipito.

Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona.

Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”

Pamenepo mudzatenga mafano anu, ena okutidwa ndi siliva, ena okutidwa ndi golide, ndipo mudzaŵataya ngati zinyalala, ndikunena kuti, “Zichoke zonsezi!”

Mukamadzabzala mbeu zanu, Chauta adzakugwetserani mvula kuti zimere, ndipo mudzakolola zambiri. Tsiku limenelo ng'ombe zanu zidzapeza mabusa aakulu.

Ng'ombe ndi abulu zokuthandizani kulima zidzadya chakudya chamchere chopapasa ndi fosholo ndi chifoloko.

Pa tsiku limene nsanja zankhondo za adani anu zidzagwe, anthu ake naphedwa, pa phiri lililonse lalikulu ndi pa gomo lililonse lalitali, padzayenda mitsinje ya madzi.

Mwezi udzaŵala ngati dzuŵa, ndipo dzuŵa lidzaŵala kwambiri ngati kasanunkaŵiri kuŵala kwa pa tsiku limodzi. Zimenezi zidzachitika pamene Chauta adzamange ndi kupoletsa zilonda zimene Iye yemwe adachititsa pakuŵalanga anthu ake.

Onani, ulemerero wa Chauta ukuwonekera kuchokera kutali. Akuwonetsa mkwiyo m'kati mwa moto ndi m'kati mwa chiwutsi chatolotolo. Akulankhula mwaukali, ndipo mau ake akutentha ngati moto woononga.

Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, wa madzi oyesa m'khosi. Akusefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza. Ngati akavalo, akuŵaika m'kamwa chitsulo choti chiŵasokeretse.

Koma inu anthu a Mulungu, mudzakondwa ndi kuimba monga m'mene mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika. Mudzasangalala ngati anthu opita naimba toliro ku phiri la Chauta, thanthwe la Israele.

Koma kutchinjiriza kwa Farao kudzakuchititsani manyazi, ndipo malo opulumukirako a ku Ejipitowo mudzachita nawo manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 14:8

Ndiye kuti ndidzalimbana naye munthu ameneyo. Ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo, ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anga. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 11:28

Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 5:3

Ine ndidaona chitsiru chitamera mizu, koma mwadzidzidzi nyumba yake ndidaitemberera.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 27:25

Anthu onse aja adati, “Imfayo mlandu wake ugwere ife ndi ana athu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:63-64

Monga momwe kudakomera Chauta kukudalitsani ndi kukuchulukitsani kuti mukhale ambiri, momwemo kudzamkomeranso kuti akuwonongeni kotheratu. Adzakuchotsani m'dziko limene mukuliloŵa kukakhalamolo.

Ndipo Chauta adzakumwazani pakati pa mitundu yonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko mpaka ku malekezero ake enanso. Kumeneko muzidzapembedza milungu yamitengo ndi yamiyala, imene inu ndi makolo anu simudaidziŵe nkale lonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 2:1-3

Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu, amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa. Akadzuka m'maŵa amakazichitadi, pakuti mphamvu zake ali nazo.

Nyamukani, chokani, ano simalo opumulirapo. Zonyansa zanu zaŵaipitsa, zadzetsapo chiwonongeko choopsa.

Munthu wina atamapita uku ndi uku akulalika zabodza kuti, ‘Ndithudi mudzakhala ndi vinyo ndi zakumwa zamphamvu zambiri,’ mlaliki wotere ndi amene anthu aŵa angamkonde.

“Koma inu banja lonse la Yakobe, ndidzakusonkhanitsani. Onse otsala a ku Israele ndidzaŵasonkhanitsa pamodzi ngati nkhosa m'khola, ngati gulu la zoŵeta pa busa lake. Malowo adzakhala thithithi ndi chinamtindi cha anthu.”

Woŵapulumutsa adzaŵatsogolera, ndipo onse adzathyola pa chipata nathaŵa. Idzayambira ndi mfumu yao kudutsa, Chauta adzakhala patsogolo pao.

Akasirira minda, amailanda. Akakhumbira nyumba, amazilanda. Amavutitsa munthu ndi banja lake, naŵatengera zonse zimene ali nazo.

Nchifukwa chake zimene akunena Chauta ndi izi: “Imvani, ndidzakufitsirani tsoka chifukwa cha zoipa zonsezi. Ndidzakuvekani goli m'khosi mwanu, limene simungathe kulivula. Apo simudzayendanso monyada, chifukwa nthaŵi imeneyo idzakhala yoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 22:28

“Musanyoze Mulungu, ndipo musatemberere mtsogoleri wa anthu anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:23-24

Mvula sidzakugwerani ndipo nthaka yanu idzauma kuti gwa ngati chitsulo.

M'malo mwa mvula, Chauta adzakugwetserani fumbi ndi mchenga, mpaka mutaonongeka nonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 35:11-15

Tsono Ine Ambuye Mulungu ndikuti, Pali Ine ndemwe, ndidzakuchitani zomwe mudaŵachita anthu anga poŵaonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu. Mudzandidziŵadi pakati panupo, ndikadzakulangani.

Mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndidamva mau anu onse onyoza mapiri a ku Israele. Mudanena kuti, ‘Mapiri a ku Israele asiyidwa, ndipo atipatsa kuti tiŵaononge.’

Ndidamva zondinyoza zimene mudanena monyada. Ndidadzimvera ndekha zonse!

Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzakusandutsani bwinja kotheratu, kotero kuti dziko lonse lapansi lidzakondwa nako kugwa kwanu.

Monga momwe inu mudakondwera ndi kugwa kwa Israele, Ine ndidzakuchitaninso zomwezo. Iwe phiri la Seiri, ndi dziko lonse la Edomu, udzasanduka bwinja. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 48:27

Kodi suja Israele adaali chinthu chonyozeka kwa iwe? Kodi adapezeka pakati pa mbala, kuti nthaŵi zonse polankhula za iye uzimpukusira mutu momunyoza?”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:41-42

Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi ndithu, koma sadzakhala anu, chifukwa adzatengedwa ukapolo.

Mitengo yanu yonse ndi dzinthu dzanu dzam'munda zidzatha ndi tizilombo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:1

Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 50:13

Udzakhala wopanda anthu chifukwa cha mkwiyo wa Chauta, udzakhala chipululu chokhachokha. Onse odutsa ku Babiloni azidzachita nyansi, nkumangotsonya chifukwa cha mabala a mzindawo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 11:21

Zoonadi, anthu oipa chilango sichidzamuphonya, koma anthu a Mulungu adzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 10:1-3

Tsoka kwa amene amapanga malamulo opanda chilungamo, ndi kwa alembi amene amalemba zongovutitsa anzao.

Ine ndidakantha mafumu a anthu opembedza mafano, amene mafano ao ndi aakulu kupambana a ku Yerusalemu ndi a ku Samariya.

Ndiye ndingalephere kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake omwe, monga momwe ndidachitira Samariya ndi mafano ake?”

Ambuye atamaliza ntchito yao yolanga onse pa phiri la Ziyoni ndiponso ku Yerusalemu, adzalanganso mfumu ya ku Asiriya, chifukwa cha kudzitama kwake ndi kunyada kwake.

Pakuti mfumuyo ikuti, “Ndachita zimenezi ndi mphamvu zanga ndiponso ndi nzeru zanga, pakuti kumvetsa nkwanga. Ndachotsa malire a mitundu ya anthu, ndipo ndafunkha chuma chao. Ndaŵatsitsa amene anali pa mipando yaufumu.

Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu, monga momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame. Monga momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, ndimo m'mene Ine ndidasonkhanitsira dziko lonse lapansi. Ndipo panalibe mbalame ndi imodzi yomwe yoti mapiko phephere-phephere, kapena yoti kukamwa yasa kapena yolira kuti psepsepse.”

Koma Chauta akuti: “Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Kodi sowo ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti mkwapulo ukuzunguza munthu, kapena ndodo yanyamula munthu!”

Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzatumiza matenda oondetsa kwa ankhondo amphamvu a mfumu ya ku Asiriya. Ndipo mfumuyo kunyada kwake kudzapsa ndi moto wosazimika.

Mulungu, Kuŵala kwa Israele, adzakhala ngati moto. Mulungu, Woyera Uja wa Israele, adzakhala ngati malaŵi a moto. Motowo udzaŵatentha ndi kuŵapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.

Adzaononga nkhalango yaikulu ndi nthaka yachonde. Zidzaonongeka m'kati ndi kunja kwake, ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuwonda.

Mitengo yotsalira yam'nkhalangomo idzakhala yochepa kwambiri, yoti ndi mwana yemwe nkuiŵerenga.

Pakutero amapotoza malamulo poweruza amphaŵi mosalungama. Amaŵalanda zoŵayenerera anthu anga osauka, amafunkha za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye!

Tsiku limenelo otsalira a ku Israele, opulumuka a m'banja la Yakobe, sadzadaliranso anthu amene adaŵakantha, koma ndithu adzadalira Chauta, Woyera Uja wa Israele.

Otsalira adzabwerera, otsalira a m'banja la Yakobe, adzabwereradi kwa Mulungu wamphamvu.

Iwe Israele, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wakunyanja, otsalira oŵerengeka okha ndiwo adzabwerere. Chiwonongeko chalamulidwa, chidzaonetsa chilungamo chosefukira.

Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzaononga ndithu dziko lonse monga momwe adalamulira.

Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, akunena kuti, “Inu anthu anga okhala ku Ziyoni, musaŵaope Aasiriya pamene akukanthani ndi ndodo, nakumenyani ndi zibonga zao, monga m'mene Aejipito ankachitira.

Patsala pang'onong'ono kuti uthe mkwiyo wanga pa inu, koma ndidzaŵakwiyira iwonso mpaka kuŵaononga.

Ine, Chauta Wamphamvuzonse, ndidzaŵakwapula monga momwe ndidakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu. Ndi ndodo yanga ndidzaŵalanga, monga momwe ndidalangira Aejipito panyanja paja.

Tsiku limenelo ndidzakusanjulani katundu wa Aasiriya pa mapewa anu, ndi goli lao m'khosi mwanu, golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa.”

Adani aja akudza afika ku Aiyati. Apyola ku Migironi, aikiza katundu wao ku Mikimasi.

Adzera pa mpata uja, nagona ku Geba usiku. Anthu a ku Rama akunjenjemera, a ku Gibea, mzinda wa Saulo, athaŵa.

Kodi mudzatani pa tsiku lachilango pofika namondwe wochokera kutali? Kodi mudzathaŵira kwa yani kuti akuthandizeni? Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 3:11

Koma tsoka kwa anthu oipa! Zinthu zidzaŵaipira. Zimene akhala akuchitira anzao zomwezo zidzaŵabwerera.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 23:21

Mumvere iyeyo, ndipo mumvetse zimene akunena. Musamchite zaupandu, chifukwa sadzakhululukira tchimo lotere. Iye akuchita zimenezi m'dzina langa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 1:9

Chilango chao nchakuti adzaonongedwa kwamuyaya, sadzaona konse nkhope ya Ambuye kapena ulemerero wa mphamvu zake,

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 18:30

“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 44:8

Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga pochita zoipa ndi manja anu ndiponso pomafukizira lubani milungu ina m'dziko la Ejipito m'mene mukukhala? Mudziwononga nokha, ndipo musanduka chinthu chomachiseka ndi chonyozeka m'maso mwa anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:38-39

Mudzabzala zambiri, koma mudzakolola pang'ono chabe, chifukwa dzombe lidzadya zolima zanuzo.

Minda yamphesa mudzalimadi, mpaka kuisamala bwino, koma mphesa zake simudzathyola kapena kumwako vinyo wake, chifukwa tizilombo ndito tidzadye mphesazo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 14:22-23

Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzauthira nkhondo mzinda wa Babiloni. Ndidzathetseratu dzina lake ndi onse otsaliramo. Sipadzapulumuka ana ndi zidzukulu zomwe. Ndatero Ine Chauta.

Mzindawo ndidzausandutsa dambo lamatope ndi malo okhalamo akanungu. Ndidzausesa ndi tsache lofafaniza zonse zotsala. Ndatero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 18:21

Nchifukwa chake mulange ana ao ndi njala. Muŵaononge ndi nkhondo. Akazi ao akhale amasiye, opanda ana. Amuna ao afe ndi mliri, anyamata ao afe ndi lupanga ku nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 4:6

Anthu anga akuwonongeka chifukwa Ine sandidziŵa. Ndidzakukanani kuti musanditumikire ngati ansembe, chifukwa choti mwakana kuphunzitsa za Ine. Mwaiŵala malamulo a Mulungu wanu, tsono Inenso Mulungu wanu ndidzaiŵala ana anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 22:3

Mumzindamo simudzapezekanso kanthu kalikonse kotembereredwa ndi Mulungu. Mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja udzakhala m'menemo, ndipo atumiki ake adzampembedza.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 48:42

Mowabu adzaonongeka, sadzakhalanso mtundu wa anthu, pakuti adadzikuza poukira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Nahumu 1:14

Za inu a ku Ninive Chauta walamula kuti, “Simudzakhala ndi adzukulu otchedwa dzina lanu. Ndidzaononga mafano osema ndi oumba m'nyumba ya milungu yanu. Ndidzakukumbirani manda, chifukwa ndinu opandapake.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 106:36-39

Adatumikira mafano ao amene adasanduka msampha kwa iwo.

Adapereka nsembe ana ao aamuna ndi aakazi kwa mizimu yoipa.

Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo.

Adadzidetsa ndi ntchito zao, nakhala osakhulupirika pa zochita zao ngati mkazi wachigololo.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 16:9

Anthu adapserera nako kutentha koopsako, ndipo adayamba kunyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi. Komabe iwo sadatembenuke mtima kuti azitamanda Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 2:17

Zimenezi zakuwonekerani chifukwa mudasiya Chauta, Mulungu wanu, pamene Iye adakuikani pa njira yabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 25:7

Nchifukwa chake Ine ndidzakukanthani ndi dzanja langa ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha mitundu ina ya anthu. Ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu, ndipo ndidzakufafanizani pa dziko lapansi. Ndidzakuwonongeranitu, ndipo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 29:27

Motero Chauta adakwiyira anthu ake, ndipo adaŵagwetsera masoka onse olembedwa m'buku muno.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 1:21-22

Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.”

Ngakhale zidaayenda motero, Yobe sadachimwe kapena kunena kuti, “Mulungu walakwa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 1:1-2

Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu,

koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Mulungu wolungama ndi wowona, wangwiro m'njira zanu zonse, wodzala ndi nzeru ndi luntha, palibe chomwe mungalakwitse, ndinu chilungamo, umphumphu ndi zonse zomwe tifunikira kuti tikhale oyera, tiphunzitseni Ambuye kutsata malamulo anu ndi kukhala olimba m'mawu ndi malamulo anu, kuti tisakhale osamvera chifuniro chanu, koma kuti tikakhale ndi madalitso opitilira, chifukwa aliyense wochoka m'mawu mwanu ndi kusamvera malamulo anu amakhala m'temberero, ndikufuna kuti mutenge malingaliro anga, ndi zonse zomwe ndili kuti zitsogozedwe ndi chikondi chanu, ndilengeni mwa ine Ambuye mtima woyera ndi kundikonzeranso mzimu wolungama mkati mwanga, mundimasule ku temberero lililonse ndi mphamvu ya magazi anu Yesu, kuti pasakhale chilichonse chomwe chingamandipangitse kukhala wotembereredwa chifukwa ndawomboledwa ndi magazi a Khristu ndipo iye anatenga pa mtanda wake mphulupulu yanga yonse ndi kupanduka kwanga chifukwa chake ndidzilengeza kuti ndine womasuka kwathunthu ndipo ndikutumikira Mulungu wanga, popeza anandikonda poyamba ndipo anapereka moyo wake m'malo mwanga ndidzamukonda ndi kumulambira nthawi yonse ya moyo wanga, m'dzina la Yesu, Ameni.