Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


MAVESI OKHUDZA NKHANI ZA KUGONANA

MAVESI OKHUDZA NKHANI ZA KUGONANA

Nkhani ya kugonana nthawi zambiri imakhala yovuta kuyankhula, yokutidwa ndi manyazi ndi kukana. Koma monga Akhristu, tiyenera kudzifunsa kuti, “Kodi cholinga cha Mulungu ndi chotani pankhani ya kugonana?” Baibulo silikhala chete pankhaniyi, koma limatipatsa malangizo ofunikira.

Ahebri 13:4 amati, “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” Ukwati ndi chinthu cholemekezeka, ndipo tonsefe tiyenera kuulemekeza.

Thawa chigololo. Danyani ndi kupewa zodetsa zonse. Mulungu amadana ndi kugonana kunja kwa ukwati. Ngakhale kuti maganizo a anthu pa nkhani ya kugonana amasiyana, tiyenera kudziwa kuti Mulungu ndiye amene analenga zonse zokongola, ndipo sitiyenera kuchita manyazi ndi chilichonse chimene iye analenga.

Popeza Mulungu ndiye analenga kugonana, njira yokhayo yololeka yokhutiritsira chilakolako cha kugonana ndi mkati mwa pangano la ukwati. Ukwati ndiwo chizindikiro cha pangano limeneli, ndipo ndi zimene Mulungu amafuna. Mulungu analenga kugonana kuti chizikhala mkati mwa ukwati, osati kunja kwake.

Aukwati okhulupirika sadzadwala matenda opatsirana pogonana chifukwa chogonana kwambiri. Koma ngati mmodzi wa iwo atathyola pangano la ukwati n’kupita kukagonana ndi wina, akhoza kudwala matenda opatsirana pogonana ndi mavuto ena chifukwa cha tchimo limenelo.




Mateyu 5:28

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:32

Amene amachita chigololo ndi wopanda nzeru, amangodziwononga yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:18

Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5

Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:27-28

Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi. Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:1-2

Tsopano ndiyankhe zimene mudandifunsa m'kalata yanu. Nkwabwino kuti munthu asakwatire, Kwa anthu am'banja lamulo langa, limenetu kwenikweni ndi lochokera kwa Ambuye, ndi ili: Mkazi asalekane ndi mwamuna wake. Koma ngati amuleka, akhale wosakwatiwanso, kapena ayanjane nayenso mwamuna wakeyo. Chimodzimodzinso mwamuna asasudzule mkazi wake. Kwa ena mau anga, osati a Ambuye ai, ndi aŵa: Ngati mkhristu ali ndi mkazi wachikunja, ndipo mkaziyo avomera kukhala naye, mwamunayo asathetse ukwatiwo. Momwemonso ngati mkhristu wamkazi ali ndi mwamuna wachikunja, ndipo mwamunayo avomera kukhala naye, mkaziyo asathetse ukwatiwo. Pakuti mwamuna wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mkazi wakeyo. Nayenso mkazi wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mwamuna wakeyo. Pakadapanda apo, bwenzi ana anu atakhala akunja, koma monga zilirimu, ndi ana a Mulungu. Koma ngati wakunja uja afuna kuleka mkhristu, amuleke. Zikatero, ndiye kuti mkhristu wamwamunayo kapena wamkaziyo ali ndi ufulu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale ndi moyo wamtendere. Kodi iwe, mkazi wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzampulumutsa mwamuna wako? Kapenanso iwe, mwamuna wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzapulumutsa mkazi wako? Aliyense atsate moyo umene Ambuye adamkonzera, moyo umene Mulungu adamuitanira. Ndizo zimene ndimaŵalamula anthu onse amumpingo. Ngati wina Mulungu adamuitana ali woumbalidwa, asavutike nkubisa kuumbala kwakeko. Chimodzimodzi ngati wina adamuitana ali wosaumbalidwa, asaumbalidwe. Kuumbala si kanthu ai, kusaumbala si kanthunso. Kanthu nkutsata malamulo a Mulungu. koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:2

koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:5

Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:3

Mwamuna azipereka kwa mkazi wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mkazi wake, momwemonso mkazi azipereka kwa mwamuna wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mwamuna wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:18-19

Uzikhutira ndi mkazi wako, uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako. Iye uja ngwokongola ngati mbaŵala, ndi wa maonekedwe osiririka ngati mbalale. Uzikhutitsidwa ndi maŵere ake nthaŵi zonse, uzikokeka ndi chikondi chake pa moyo wako wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 2:24

Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aŵiriwo amakhala thupi limodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:4

Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 4:1

Adamu adakhala ndi mkazi wake Heva ndipo mkaziyo adatenga pathupi. Tsono adabala mwana wamwamuna, ndipo adati, “Ndalandira mwana wamwamuna mwa chithandizo cha Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Kaini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 9:1

Mulungu adadalitsa Nowa ndi ana ake omwe, nati “Mubale ana ambiri ndi kuchulukana, kuti mudzaze dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 19:5

Adaitana Loti namufunsa kuti, “Kodi anthu abwera kwanu usiku uno aja ali kuti? Atulutse, abwere kuno kuti tigone nawo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:14

“Usachite chigololo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:6-7

“Munthu wina aliyense mwa inu asagone ndi wachibale wake. Ine ndine Chauta. Usachititse manyazi bambo wako pakugona ndi mai wako. Ameneyo ndi mai wako, usamchititse manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:20

Usagone ndi mkazi wa mnzako ndi kudziipitsa naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:22

Usagone ndi mwamuna ngati mkazi. Chimenecho ndi chinthu chonyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:23

Ndipo usagone ndi nyama ndi kudziipitsa nayo, ngakhalenso mkazi aliyense asadzipereke kwa nyama kuti agone nayo, pakuti chimenecho ndi chisokonezo choopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:10

“Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo onsewo aphedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:13

Munthu akagona ndi munthu wamwamuna mnzake ngati mkazi, onsewo achita chinthu chonyansa, ndipo ayenera kuphedwa. Magazi ao akhale pa iwowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:15-16

Mwamuna akagona ndi nyama, ayenera kuphedwa, ndipo nyamayo muiphenso. Mkazi akagona ndi nyama, aphedwe pamodzi ndi nyamayo. Aphedwe ndipo magazi ao akhale pa mkaziyo ndi nyamayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:18

“Usachite chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:13-21

Mwina munthu angathe kukwatira mtsikana, namakhala naye ndithu, pambuyo pake nkunena kuti mkaziyo sakumfuna. Tsono ayamba kumnenera zabodza zochititsa manyazi ndi kuipitsa mbiri yake ponena kuti, “Mkazi ameneyu sadaoneke ngati namwali wosadziŵa mwamuna pa nthaŵi yomukwatira.” Zitatero, makolo a mkaziyo atenge zizindikiro zotsimikizira akuluakulu abwalo am'mudzimo kuti mwana waoyo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ndithu. Pamenepo bambo wake wa mtsikanayo aŵauze abwalowo kuti, “Ndidalola mwana wanga wamkazi kuti akwatiwe ndi munthu uyu, koma tsopano akuti sakumufuna. Wamnamizira momchititsa manyazi kuti ati sadali namwali wosadziŵa mwamuna pomkwatira. Koma pano tili ndi umboni wotsimikizira kuti mwana wangayu adaali namwali wangwiro ndithu. Onani, zizindikiro zake ndi izi.” Apo adzaonetse chovala cha mkaziyo kwa akuluakuluwo. Tsono akuluakulu am'mudzimo amtenge mwamunayo ndi kumkwapula. Pambuyo pake amlipitsenso masekeli asiliva makumi khumi, ndipo azipereke kwa bambo wa mtsikanayo. Alipe ndithu chifukwa choti adanyozetsa mnamwali Wachiisraele amene sadamdziŵeko mwamuna. Komanso adzakhalabe mkazi wake ndithu, ndipo pa moyo wake wonse sadzathanso kumsudzula. Koma ngati mwiniwake kwao nkutali, kapena simumdziŵa, itengeni mupite nayo kwanu, muisunge komweko. Koma mwiniwake akabwera kudzaifunafuna, mumpatse. Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo umboni wakuti mtsikanayo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ukusoŵa, pamenepo apite naye pakhomo pa bambo wake. Pomwepo amuna amumzindamo amuphe pakumponya miyala. Mtsikanayo wachita chinthu chochititsa manyazi pakati pa mtundu wathu wa Israele pochita zadama m'nyumba ya bambo wake. Motero mudzachotsa choipa pakati pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:22

Munthu akagwidwa akuchita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, aphedwe onsewo, mwamuna ndi mkazi yemwe. Choncho mudzachotsa choipa pakati pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:23-24

Tiyese kuti mwagwira munthu mumzinda momwemo akuchita chigololo ndi mnamwali wofunsidwa mbeta, amene sadamdziŵeko mwamuna. Muŵatenge onsewo, mupite nawo kunja kwa mzinda, ndipo muŵaphe poŵaponya miyala. Mtsikanayo aphedwe chifukwa ngakhale anali m'mudzi, sadakuwe kuti anthu adzamthandize. Mwamunayo aphedwe chifukwa wachimwa ndi mtsikana wofunsidwa mbeta ndi mnzake. Motero mudzachotsa choipa pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:28-29

Mwina munthu agwidwa akugwirira mnamwali wosafunsidwa mbeta, amene sadamdziweko mwamuna, nachita naye chigololo momkakamiza. Munthuyo alipe bambo wake wa mtsikanayo mtengo wofunsira mbeta, ndiye kuti masekeli asiliva makumi asanu, ndipo amtenge kuti akhale mkazi wake chifukwa choti adamkakamiza kuchita naye chigololo. Tsono pa moyo wake wonse sangathenso kumsudzula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 16:1

Samisoni adapita ku Gaza ndipo kumeneko adaonako mkazi wadama naloŵa m'nyumba yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 11:2-4

Zidangochitika kuti tsiku lina chakumadzulo, Davide adadzuka pabedi pake, namayenda pamwamba pa denga la nyumba yake yaufumu. Ali padengapo, adaona mkazi wina akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwabasi. tsono ngati mfumu ikapse mtima, nikakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mudapita kufupi ndi mzinda kuti mukamenye nkhondo? Kodi simunkadziŵa kuti adzakulasani kuchokera m'kati mwa linga? Kodi Abimeleki mwana wa Gideoni adamupha ndani? Kodi adamupha si mkazi, pomkunkhunizira mwalawamphero kuchokera pa linga, kotero kuti adafera ku Tebezi? Chifukwa chiyani mudakafika pafupi ndi khoma?’ Pamenepo iweyo ukanene kuti, ‘Wankhondo wanu, Uriya Muhiti uja, nayenso adaphedwa.’ ” Wamthenga uja adapita, nakafika kwa Davide, nakamuuza zonse zimene Yowabu adamuuza kuti akanene. Adauza Davide kuti, “Adani athu adaatipambana, ndipo adaatuluka kukalimbana nafe ku thengo. Koma ife tidaŵabweza mpaka ku khomo lakuchipata. Tsono anthu oponya mivi ankalasa ankhondo anu kuchokera m'linga. Ndipo ankhondo ena mwa ankhondo a inu mfumu adaphedwa. Wankhondo wanu uja, Uriya Muhiti, nayenso adaphedwa.” Apo Davide adauza wamthenga uja kuti, “Kamuuze Yowabu kuti, ‘Zimenezi usavutike nazo, poti wakufa sadziŵika. Ulimbike polimbana ndi mzindawo, ndi kuugonjetsa.’ Choncho ukamlimbitse mtima Yowabuyo.” Pamene mkazi wa Uriya adamva kuti mwamuna wake Uriya adaphedwa, adalira, kulira mwamuna wake. Mkaziyo atatha kulira malirowo, Davide adatuma munthu nakamtenga, nkubwera naye kunyumba kwa mfumu, ndipo Davide adamukwatira. Mkaziyo adambalira mwana wamwamuna. Koma zimene adachita Davidezi zidaipira Chauta. Pomwepo Davide adatuma munthu kuti akafunsitse za mkaziyo. Ndipo munthuyo adamuuza kuti, “Mkazi ujatu ndi Bateseba, mwana wa Eliyamu, mwamuna wake ndi Uriya Muhiti.” Apo Davide adatuma amithenga kuti akamtenge mkaziyo. Iwo adabwera naye kwa Davide, ndipo Davideyo adagona naye. Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo atangomaliza kusamba. Pambuyo pake mkazi uja adabwerera kunyumba kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 13:11-14

Koma atafika nacho chakudyacho pafupi ndi Aminoni kuti adye, Aminoni adamgwira Tamara, namuuza kuti, “Bwera ugone nane, iwe Tamara.” Koma Tamarayo adayankha kuti, “Iyai, mlongo wanga, usandikakamize. Zimenezi sizidachitikepo nkale lonse ku Israele. Usachite zauchitsiru zotere. Kodi ine sindidzachita manyazi poyenda pakati pa anthu? Ndipo iwe udzakhala mmodzi mwa zitsiru pakati pa Aisraele. Nchifukwa chake tsono, chonde, ndapota nawe, ulankhule ndi amfumu, poti iwowo sadzandikaniza kuti ndikwatiwe nawe.” Koma Aminoni sadamve zimene ankanena Tamarazo. Ndipo popeza kuti anali ndi mphamvu zoposa Tamara, Aminoniyo adamkakamiza Tamarayo nagona naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:15-19

Iwe, uzimwera m'chitsime chakochako, ndiye kuti khala wokhulupirika kwa mkazi wako. Kodi ana ako azingoti mbwee ponseponse ngati madzi ongoyenda m'miseu? Anawo akhale a iwe wekha, osatinso uŵagaŵane ndi alendo. Uzikhutira ndi mkazi wako, uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako. Iye uja ngwokongola ngati mbaŵala, ndi wa maonekedwe osiririka ngati mbalale. Uzikhutitsidwa ndi maŵere ake nthaŵi zonse, uzikokeka ndi chikondi chake pa moyo wako wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:24-29

Zimenezi zidzakupulumutsa kwa mkazi woipa, zidzakuthandiza kuti usamvere mau osalala a mkazi wachiwerewere. Mumtima mwako usamakhumbira kukongola kwake, usakopeke nawo maso ake. Paja mkazi wachiwerewere ungathe kumgula ndi buledi, koma wadama wokwatiwa amakulanda ndi moyo wako womwe. Kodi munthu angathe kufukata moto, zovala zake osapsa? Kodi munthu angathe kuponda makala amoto, mapazi ake osapserera? Ndizo zimamchitikira wokaloŵerera mkazi wamwini. Aliyense wokhudza mkazi wotero adzalangidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 7:21-23

Amamkopa mnyamatayo ndi mau onyengerera, amamkakamiza ndi mau ake oshashalika. Pamenepo mnyamatayo amatsatira mkaziyo monga momwe ng'ombe imapitira kokaphedwa, kapena monga momwe mbaŵala imakodwera mu msampha, mpaka muvi kuilasa m'mimba mwake. Amakhala ngati mbalame yothamangira m'khwekhwe, osadziŵako kuti aferapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 9:17-18

“Madzi akuba ndiwo amatsekemera, buledi wodya mobisa ndiye amakoma.” Koma mwamunayo sadziŵa kuti kumeneko kuli imfa, kuti alendo ake aloŵa kale m'manda ozama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:14

Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lakuya. Amene Chauta amamkwiyira adzagwamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 9:9

Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi amene umamkonda, pa masiku onse a moyo wako wopandapakewu umene Mulungu wakupatsa pansi pano. Ndi zokhazo zimene ungaziyembekeze pa moyo wako ndiponso pa ntchito zako zolemetsa zimene umazigwira pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 1:2-4

Undimpsompsone ndi milomo yako, chifukwa chikondi chako nchoposa vinyo kukoma kwake. Mafuta ako odzola ngonunkhira bwino, dzina lako likundikumbutsa za mafuta otsanyukako. Nchifukwa chaketu, atsikana sangaleke kukukonda. Tenge, ndizikutsata, tiye tifulumire. Iwe mfumu yanga, kandiloŵetse m'chipinda mwako. Tizisangalala kwambiri ndi kukondwa limodzi. Chikondi chako tichitamande kupambana vinyo. Akazi onse amakukondera kaone!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 2:6-7

Ha, ndidakakonda ineyo nditatsamira dzanja lake lamanzere, iyeyo nkundikumbatira ndi dzanja lamanja! Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, pali mphoyo ndi nswala zakuthengo, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Mkazi

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 4:10-12

Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, chikondi chako nchosangalatsa. Chikondi chako nchosangalatsa kupambana vinyo, mafuta ako ndi onunkhira bwino kupambana zonunkhira zabwino zonse. Iwe mkazi wanga, milomo yako ili uchi mvee! Kunsi kwa lilime lako kuli ngati uchi ndi mkaka. Fungo la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni. Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, uli ngati munda wopiringidza, ngati munda wopiringidza, ngati kasupe wochingidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 7:6-9

Ndiwe wokongola zedi, ndiponso wosangalatsa, iwe wokondedwawe, namwali wokondweretsawe. Msinkhu wako uli ngati mtengo wa mgwalangwa, maŵere ako ali ngati masango a zipatso zake. Ndidati, ndikwera mu mtengo wa mgwalangwawu, ndikathyole zipatso zake. Maŵere ako akhale ngati masango a mphesa, fungo la mpweya wako likhale lonunkhira bwino ngati la maapulosi. Ukamandimpsompsona, ine kukhosi see, ngati ndikumwa vinyo wokoma kwambiri. Mkazi Tsono vinyo ameneyu amthirire wokondedwa wanga, ayenderere pa milomo yake ndi m'mano mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:3-5

Senderani kuno, inu anthu ochita zoipa, pakuti muli ngati zidzukulu zam'chigololo, zochokera m'zadama. Kodi inu mukuseŵera ndi yani? Kodi mukunena yani? Mukunyoza yani? Kodi ochimwa sindinu? Onyenga sindinu? Mumapembedza mafano pa mitengo ya thundu, patsinde pa mtengo wogudira uliwonse. Mumapereka ana anu ngati nsembe m'zigwa, m'ming'alu yam'mathanthwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:26

Udachita zigololo ndi Aejipito adama oyandikana nawe, ndipo udandikwiyitsa chifukwa udachulukitsa zigololo zako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 23:37-39

Adachita chigololo, ndipo adapha anthu. Adachita chigololo popembedza mafano ao, ndipo ana anga amene adandibalira, adaŵapereka kwa mafanowo ngati chakudya chao. Adachitanso izi: adaipitsa malo anga ondipembedzera, ndipo adanyoza masiku anga a Sabata. Adangoti atapereka ana ao nsembe kwa mafano ao, nthaŵi yomweyo nkuloŵa m'Nyumba yanga yoyera naiipitsa. Ndithu zimenezi nzimene adachita m'Nyumba mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:18

Kubadwa kwa Yesu Khristu kudaatere: amai ake Maria adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe; koma asanaloŵane, Maria adaapezeka kuti ali ndi pathupi mwa mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:27-28

“Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usachite chigololo.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:19

Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:4-6

Yesu adaŵayankha kuti, “Kodi simunaŵerenge kuti Mulungu amene adalenga anthu pa chiyambi, adalenga wina wamwamuna, wina wamkazi? Ndipo kuti Iye yemweyo adati, ‘Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ake ndi amai ake, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.’ Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:21-23

Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana, zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa. Zoipa zonsezi zimachokera m'kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:6-9

Komatu pachiyambi paja, pamene Mulungu adalenga zonse, adaŵalenga anthu, wina wamwamuna wina wamkazi. Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ndi amai, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi. Choncho tsopano salinso aŵiri, koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumikiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 20:34-35

Yesu adaŵayankha kuti, “Anthu okhala pansi pano amakwatira ndi kukwatiwa. Koma amene amaŵayesa oyenera kukakhala ndi moyo kutsogoloko, anthu atauka kwa akufa, sadzakwatiranso kapena kukwatiwa ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:24-27

Nchifukwa chake Mulungu adaŵasiya kuti azingochita zonyansa zimene mitima yao inkalakalaka, mpaka kunyazitsa matupi ao. Adasiya zoona za Mulungu namatsata zabodza. Adayamba kupembedza ndi kutumikira zolengedwa m'malo mwa kupembedza ndi kutumikira Mlengi mwini, amene ali woyenera kumlemekeza mpaka muyaya. Amen. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adaŵasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe adaleka machitidwe achibadwa pa zachikwati, namatsata machitidwe ena otsutsana ndi achibadwawo. Chimodzimodzinso amuna, adaleka machitidwe achibadwa osirira akazi, nkumakhumbana amuna okhaokha. Ankachitana zamanyazi, motero adadziitanira chilango choyenera molingana ndi zochita zao zopotokazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:12-13

Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake. Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:13-14

Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:1

Mbiri yawanda ponseponse yonena kuti pakati panu pali dama. Ndipo damalo ndi la mtundu wakuti ndi anthu akunja omwe sachita. Ndamva ndithu kuti munthu wina akukhala ndi mkazi wa bambo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:13

Chakudya, kwake nkuloŵa m'mimba, ndipo mimba, kwake nkulandira chakudya. Koma Mulungu adzaononga ziŵiri zonsezo. Thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:18-20

Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe. Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:3-5

Mwamuna azipereka kwa mkazi wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mkazi wake, momwemonso mkazi azipereka kwa mwamuna wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mwamuna wake. Amene akulira, akhale monga ngati sakulira, amene akukondwa, akhale monga ngati sakukondwa, amene akugula zinthu, akhale monga ngati sali nazo zinthuzo. Ndipo amene akugwiritsa ntchito zinthu zapansipano, zisaŵagwire mtima zinthuzo. Pakuti dziko lino lapansi, monga liliri tsopanomu, likupita. Ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhaŵa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye. Koma munthu wokwatira amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mkazi wake. Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake. Ndikunenatu zimenezi kufuna kuti ndikuthandizeni, osati kuti ndikuletseni ufulu wanu ai. Makamaka ndifuna kuti muzichita zonse moyenera, ndipo kuti muzidzipereka kwathunthu potumikira Ambuye. Koma ngati wina akuganiza kuti akumlakwira namwali wake amene adamtomera, ndipo ngati namwaliyo unamwali wake ukupitirira, tsono munthuyo nkuganiza kuti ayenera kumkwatira, angathe kuchita zimenezo, si kuchimwa ai. Komabe ngati wina, mwaufulu wake, popanda womukakamiza, watsimikiza kwenikweni kuti samkwatira namwali adamtomerayo, nayenso wachita bwino. Ndiye kuti, munthu wokwatira namwali amene adamtomera, akuchita bwino, koma woleka osamkwatira, akuchita bwino koposa. Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati, nthaŵi yonse pamene mwamuna wake ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi mwamuna amene iye afuna, malinga ukwatiwo ukhale wachikhristu. Mkazi thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mwamuna wake yemwe. Momwemonso mwamuna thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mkazi wake yemwe. Koma m'mene ndikuganizira ine, adzakhala wokondwa koposa ngati akhala wosakwatiwanso. Ndipo ndikuyesa inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu. Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:9

Koma ngati sangathe kudziletsa, aloŵe m'banja, pakuti nkwabwino kuloŵa m'banja kupambana kupsa ndi moto wa zilakolako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:36-38

Koma ngati wina akuganiza kuti akumlakwira namwali wake amene adamtomera, ndipo ngati namwaliyo unamwali wake ukupitirira, tsono munthuyo nkuganiza kuti ayenera kumkwatira, angathe kuchita zimenezo, si kuchimwa ai. Komabe ngati wina, mwaufulu wake, popanda womukakamiza, watsimikiza kwenikweni kuti samkwatira namwali adamtomerayo, nayenso wachita bwino. Ndiye kuti, munthu wokwatira namwali amene adamtomera, akuchita bwino, koma woleka osamkwatira, akuchita bwino koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:14-15

Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima? Kodi Khristu nkuvomerezana ndi Satana? Kodi mkhristu ndi mkunja angagaŵanenso chiyani pamodzi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:19

Mitima yao idaludzulala ndipo adangodzipereka ku zonyansa, kuti azichita zoipa zilizonse mosadziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:3

Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:31-33

Paja mau a Mulungu akuti, “Nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amai ake, nkukaphatikizana ndi mkazi wake, kuti aŵiriwo asanduke thupi limodzi.” Mau ameneŵa akutiwululira chinsinsi chozama, ndipo ndikuti chinsinsicho nchokhudza Khristu ndi Mpingo. Komabe akunenanso za inu, kuti mwamuna aliyense azikonda mkazi wake monga momwe amadzikondera iye mwini, ndiponso kuti mkazi aliyense azilemekeza mwamuna wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:3-5

Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama. Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa. Musamangotsata zilakolako zonyansa, monga amachitira akunja, amene sadziŵa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:7

Paja Mulungu sadatiitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:22

Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:4-5

kuti choncho athe kuphunzitsa azimai achitsikana kukonda amuna ao ndi ana ao. Aŵaphunzitse kukhala a maganizo anzeru, opanda dama, osamala bwino zapabanja, ndi omvera amuna ao. Pamenepo anthu sanganyoze mau a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:14-15

Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola. Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:11

Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:7

Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:3

Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:2

Ambiri adzatsata mkhalidwe wodzilekerera ndipo anthu adzanyoza njira ya choona chifukwa cha iwowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:10

Makamaka adzalanga anthu amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi namanyoza ulamuliro. Aphunzitsi onyenga ndi odzikuza, osasamala munthu, saopa kuchita chipongwe aulemerero a Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:14

Maso ao ndi adama, osafuna kuleka kuchimwa. Amanyengerera anthu a mtima wosakhazikika. Ali ndi mtima wozoloŵera kuumirira chuma. Anthu otembereredwa!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:16

Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:7

Mukumbukirenso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu ake m'menemonso ankangochita dama, namachitanso zonyansa zotsutsana ndi umunthu. Mulungu adaaŵaika ngati chitsanzo pakuŵalanga ndi moto wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:14

Koma pali zinthu zingapo zoti ndikudzudzulireni. Kwanuko muli ndi anthu ena otsata chiphunzitso cha Balamu mneneri wonama uja. Iye uja adaaphunzitsa mfumu Balaki kukopa Aisraele kuti azidya za nsembe zoperekedwa kwa mafano, ndi kumachita chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:20-22

Komatu pokudzudzulirani palipo: ndi apa pakuti mumamlekerera mkazi uja Yezebele, amene amadzitcha mneneri. Iye uja amanyenga atumiki anga nkumaŵaphunzitsa kuti azichita dama ndi kumadya zansembe zoperekedwa kwa mafano. Ndidampatsa nthaŵi kuti atembenuke mtima, koma safuna kutembenuka ndi kuleka kusakhulupirika kwake. Tsono ndidzamgwetsa m'matenda, ndipo ochita naye dama lakelo, ndidzaŵagwetsa m'masautso aakulu, akapanda kutembenuka mtima ndi kuleka zoipa zonse zimene ankachita naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 9:21

Anthuwo sadatembenukenso kuti aleke kupha anzao, ufiti, dama ndi kuba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:4

Ndi ameneŵa amene ankadzisunga angwiro osadziipitsa ndi akazi. Ndi ameneŵa amene amatsata Mwanawankhosa uja kulikonse kumene akupita. Ndiwo amene adaomboledwa pakati pa anthu ena onse, kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 17:1-2

Pambuyo pake mmodzi mwa angelo asanu ndi aŵiri aja, amene anali ndi mikhate isanu ndi iŵiri ija, adadzalankhula nane. Adati, “Tiye kuno ndikakuwonetse m'mene akukaweruzidwira mkazi wadama wotchuka uja, amene akukhala pambali pa madzi ambiri. Ikufaniziranso mafumu asanu ndi aŵiri. Mwa iwo, asanu adagwa, imodzi ikulamulirabe, imodzi inayo siinafikebe. Koma ikadzafika, idzayenera kungokhala kanthaŵi. Tsono chilombo chija chimene kale chidaali chamoyo, koma tsopano si chamoyonso, chikufanizira mfumu yachisanu ndi chitatu ichocho, komabe ndi imodzi mwa mafumu asanu ndi aŵiri aja, ndipo ikupita kukaonongedwa. “Nyanga khumi zimene unaona, zikufanizira mafumu khumi amene asanayambebe kulamulira. Koma adzalandira mphamvu zolamulira ngati mafumu pa ora limodzi, pamodzi ndi chilombo chija. Mafumu khumi ameneŵa, cholinga chao ndi chimodzi, ndipo amapereka mphamvu zao ndi ulamuliro wao m'manja mwa chilombo chija. Iwoŵa adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa uja. Koma Mwanawankhosayo adzaŵagonjetsa, pakuti ndi Mbuye wa ambuye onse, ndi Mfumu ya mafumu onse. Ndipo anthu ake oitanidwa, osankhidwa ndi okhulupirika, nawonso adzapambana pamodzi naye.” Mngelo uja adandiwuzanso kuti, “Madzi unaona aja amene mkazi wadama uja wakhalapo, akufanizira mitundu ya anthu, makamu a anthu, mafuko a anthu ndiponso anthu a zilankhulo zosiyanasiyana. Tsono nyanga khumi unaona zija, pamodzi ndi chilombo chija, zidzadana naye mkazi wadamayo. Zidzamlanda zake zonse ndi kumsiya maliseche. Zidzadyako mnofu wake, kenaka nkumuponya pa moto kuti apserere. Zidzaterodi, pakuti Mulungu adazipatsa mtima wofuna kuchita zimene Iye adazikonzeratu. Zimenezi nzakuti zidzagwirizana pakupereka mphamvu zake zolamulira kwa chilombo chija, mpaka zitachitika zonse zimene Mulungu adanena. “Mkazi unaona uja akufanizira mzinda waukulu uja wolamulira mafumu onse a pa dziko lapansi.” Mafumu a pa dziko lapansi ankachita naye chigololo, ndipo anthu okhala pa dziko lapansi ankaledzera naye vinyo wa dama lakelo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 17:5

Pamphumi pake padaalembedwa dzina lachinsinsi lakuti, “Babiloni wotchuka uja, manthu wa achiwerewere onse, ndi a zonyansa zonse za dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 18:3

Pakuti adamwetsa anthu a mitundu yonse vinyo wa zilakolako zadama. Mafumu a pa dziko lonse lapansi adachita naye chigololo, ndipo anthu amalonda a pa dziko lonse lapansi ankalemererapo pa zolakalaka zake zodziwunjikira chuma.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 18:9

Mafumu a pa dziko lapansi amene ankachita naye chigololo ndi kudzisangalatsa naye, adzalira ndi kumva naye chisoni kwambiri, poona utsi uli phaphapha, mzindawo ulikupsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:8

Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:15

Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:10-12

Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali. Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasoŵa phindu. Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13-14

Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:27-28

Mkazi wadama ali ngati dzenje lakuya, mkazi wachiwerewere ali ngati chitsime chophaphatiza. Amabisalira ngati mbala yachifwamba, ndipo chifukwa cha iyeyo amuna ambiri amasanduka osakhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:23

Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:10

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:17

Aliyense atsate moyo umene Ambuye adamkonzera, moyo umene Mulungu adamuitanira. Ndizo zimene ndimaŵalamula anthu onse amumpingo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:5-6

Anthu omvera khalidwe loipalo, amaika mtima pa zilakolako zathupi. Koma anthu omvera Mzimu Woyera, amaika mtima pa zimene Mzimu Woyerayo afuna. Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:8

Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:4

Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:25-28

Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo. Adachita zimenezi kuti aupatule ukhale wakewake, atauyeretsa pakuutsuka ndi madzi ndiponso ndi mau ake. Adafuna kuti akauimike pamaso pake uli waulemerero, wopanda banga kapena makwinya, kapena kanthu kena kalikonse kouipitsa, koma uli woyera ndi wangwiro kotheratu. Momwemonso amuna azikonda akazi ao, monga momwe eniakewo amakondera matupi ao. Amene amakonda mkazi wake, ndiye kuti amadzikonda iye yemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, Wamuyaya, Wapamwambamwamba! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, woyenera ulemerero ndi kulambira konse. Atate Woyera, zikomo chifukwa choti mudalenga kugonana pakati pa mwamuna ndi mkazi kuti abereke ana mkati mwa ukwati. Ndikukupemphani kuti mundithandize kukhala ndi moyo wogonana wathanzi, m'thupi ndi mzimu. Atate Woyera, ndiloleni ine ndi mnzananga tikhale ndi moyo wachimwemwe muukwati wathu, ngati tingakane kugonana, zikhale ndi mgwirizano, ndipo tithandizeni kumvetsa kuti sikuti ndi za kugonana kokha, koma za chikondi, ulemu ndi kumvetsa. Ndikukupemphani kuti Mzimu Wanu Woyera undipatse mphamvu kuti ndisunge bedi langa la ukwati kukhala loyera ndi kusangalala nalo, chifukwa Mawu Anu amati: "Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndi bedi likhale lopanda banga; koma adama ndi achigololo Mulungu adzawaweruza." Tikumbutseni kuti chifuniro chanu ndi chakuti kugonana kukhale ulendo umene tonsefe tikufika paukalamba, tikudziona ndi kusangalalana ngakhale patatha zaka zambiri, popanda munthu wachitatu. Ambuye, ganizo langa ndi malingaliro anga zilamuliridwe ndi Mzimu Wanu Woyera. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa