Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


MAVESI A MAKOLO “ABADI”

MAVESI A MAKOLO “ABADI”

Monga bambo, ndinu munthu wofunika kwambiri pa moyo wa mwana wanu. Ndinu mtsogoleri panyumba panu, wotsogolera ana anu ndi kuwaphunzitsa makhalidwe abwino ndi Mawu a Mulungu. Ndinu chitsanzo kwa anthu amene akuzungulirani. Choncho, zochita zanu n’zofunika kwambiri chifukwa ana anu amatsanzira zitsanzo zanu.

Baibulo limati: “Atate wa wolungama adzasangalala kwambiri; ndipo iye wakubala wanzeru adzakondwera naye.” (Miyambo 23:24). Mulungu wakuyikani kukhala mutu wa banja lanu kuti muzisamalira ndi kutsogolera banja lanu. Mukapempha thandizo kwa Mulungu, Iye adzakuphunzitsani mmene mungachitire zimenezi.

Monga momwe bambo amachitira chifundo ana awo, momwemonso Ambuye amachitira chifundo anthu amene amamuopa. (Masalmo 103:13).




Eksodo 20:12

“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-3

Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:20

Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:8-9

Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa. Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluŵa pamutu pako, zili ngati mkanda wa m'khosi mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:20-22

Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako. Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako. Pamene ukuyenda, zidzakulozera njira. Pamene ukukhala chogona, zidzakulonda. Pamene ukudzuka, zidzakulangiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:16

“Uzilemekeza atate ako ndi amai ako, monga momwe Chauta, Mulungu wako, adakulamulira, kuti pakutero masiku a moyo wako achuluke ndipo kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:3

Aliyense mwa inu aziwopa mai wake ndi bambo wake. Muzisunga masiku anga a Sabata, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:22

Umvere atate ako amene adakubala, ndipo usamanyoza amai ako atakalamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:24-25

Bambo wa mwana waulemu adzakondwa kwambiri. Wobala mwana wanzeru adzasangalala naye. Atate ako ndi amai ako asangalale, mai amene adakubala iwe akondwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:17

Aliyense amene amaseka bambo ndi kumanyozera kumvera mai, makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso, ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:4

Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:15

“Munthu aliyense amene amenya bambo wake kapena mai wake, aphedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 27:16

“Atembereredwe aliyense wosalemekeza atate ndi amai ake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:1

Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:6

Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba, ulemerero wa ana ndi atate ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:19

lemekeza atate ako ndi amai ako, ndiponso konda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:20

Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:10

Paja Mose adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:17

“Munthu aliyense wotemberera bambo wake kapena mai wake, aphedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:4

Koma ngati mai wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wao pa banja lao moopa Mulungu, kuti pakutero abwezere makolo ao zimene adalandira kwa iwo. Pakuti zimenezi Mulungu amakondwera nazo akamaziwona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3-5

Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake. Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:4

Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:51

Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankaŵamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:9

Tinali nawo azibambo athu apansipano amene ankatilanga, ndipo tinkaŵalemekeza. Kwenikweni tsono tikadayenera kugonjera Mulungu, Atate a mizimu, kuti tikhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:8

Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:26

Amene amachita ndeu ndi atate ake ndi kupirikitsa amai ake, ameneyo ndi mwana wochititsa manyazi ndiponso wonyozetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:20

Wina akatemberera bambo wake kapena mai wake, moyo wake udzatha ngati nyale yozima mu mdima wandiweyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:10

“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:15

Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru, koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:1

Mwana wanzeru amamvera malangizo a atate ake, koma wonyoza samvetsera akamamdzudzula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:1-4

Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake. Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino. Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako. Zoonadi, ndimo m'mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:1-2

Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:6-7

Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:1-4

Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu. Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera pa njira za moyo wolungama. Ukamayenda, mapazi ako sazidzaombana. Ukamathamanga, sudzakhumudwa ai. Uŵasamale zedi, pakuti moyo wako wagona pamenepo. Usayende m'njira za anthu oipa, usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa. Njira zao uzipewe, usapitemo konse. Uzilambalale, ndi kungozipitirira. Iwo ajatu sangagone, mpaka atachita ndithu choipa. Tulo sangatiwone, mpaka atakhumudwitsapo munthu. Paja kuchita zoipa ndiye chakudya chao, kuchita ndeu ndiye chakumwa chao. Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu. Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani. Ine ndikukupatsani malamulo abwino, musasiye zimene ndikukuphunzitsani. Mwana wanga, mvetsetsa mau anga. Tchera khutu ku zimene ndikunena. Zisachoke m'mutu mwakomu, uzisunge bwino mumtima mwako. Paja zimampatsa moyo amene wazipeza, zimachiritsa thupi lake lonse. Mtima wako uziwulonda bwino, pakuti m'menemo ndimo muli magwero a moyo. Ulekeretu kulankhula zokhotakhota, usiyiretu kukamba zopotoka. Maso ako aziyang'ana kutsogolo molunjika, uzipenya kutsogolo osacheukacheuka. Uzisamala m'mene mukupita mapazi ako, ndipo njira zako zonse zidzakhala zosapeneketsa. Usapatukire kumanja kapena kumanzere, usayende pamene pali choipa chilichonse. Pamene ndinali mwana m'nyumba mwa atate anga, m'menemo ndili kamwana kapamtima ka amai anga, atatewo adandiphunzitsa ndi mau akuti, “Ugwiritse mumtima mwako zimene ndikukuuzazi, usunge malamulo anga, kuti ukhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:5

Chitsiru chimanyoza malangizo a bambo wake, koma wochenjera amamvera chidzudzulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:13

Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 18:19

Ndamsankha iyeyu kuti alamule ana ake ndi mabanja ake akutsogolo kuti azidzamvera mau anga, pochita zabwino ndi zolungama. Choncho ndidzachita zonse zimene ndidamlonjeza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:18

Uzimlanga mwana wako chikhulupiriro chikadalipo, ukapanda kutero, wamuwononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:17

Uzimlanga mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere mu mtima, adzakondweretsa mtima wako m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 19:26-27

Pamene Yesu adaona amai ake ndi wophunzira uja amene Iye ankamukonda kwambiri, akuimirira pafupi, adauza amai ake kuti, “Mai, nayu mwana wanu.” Adauzanso wophunzirayo kuti, “Naŵa amai ako.” Ndipo kuyambira pamenepo wophunzirayo adaŵatenga amaiwo kumakaŵasamala kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Munthu wokonda mwambo amakonda kudziŵa zinthu, koma wodana ndi chidzudzulo ngwopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:2

Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:26

Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:5-6

Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai. Komatu anthu ambirimbiri a mibadwo yosaŵerengeka amene amandikonda, namatsata malamulo anga, ndimaŵakonda ndi chikondi chosasinthika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:13-14

Usamaleka kumpatsa mwambo mwana, ukamkwapula ndi tsatsa sadzafa. Ngati umkwapula ndi tsatsa, udzapulumutsa moyo wake ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:10-11

Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera pa njira za moyo wolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:21

Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, kuti angataye mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:12

Ana athu aamuna pachinyamata pao akhale amphamvu ngati mitengo, ana athu aakazi akhale okongola ngati nsanamira zozokotedwa zapangodya, zoti zikometse nyumba yaufumu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:7

Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru ndiye zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:1-5

Mwana wanga, uvomere mau anga, ndi kusunga bwino malamulo anga. Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako, kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa. Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza. Nzeruyo idzakupulumutsa ku mayendedwe oipa, idzakuteteza kwa amtherakuŵiri, amene amasiya njira zolungama, namayenda m'njira zamdima. Iwoŵa amakondwa pochita zoipa, amasangalala ndi ntchito zosalungama. Anthu ameneŵa njira zao nzokhotakhota, makhalidwe ao ngonyenga. Udzapulumuka kwa mkazi wadama, kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika, amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta, kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake. Pakuti nyumba yake imatsenderekera ku imfa, njira zake zimamufikitsa kwa anthu akufa. Opita kwa iye, palibe ndi mmodzi yemwe wobwerako, sazipezanso njira zopita ku moyo. Uzitchera khutu ku nzeru, uziikapo mtima pa kumvetsa zinthu. Ndiye iwe, uzitsata njira za anthu abwino, uziyenda m'njira za anthu ochita chilungamo. Paja anthu olungama ndiwo adzakhale m'dziko, anthu okhulupirika ndiwo adzakhazikike m'menemo. Koma anthu oipa Mulungu adzaŵachotsa pa dziko, anthu onyenga adzaŵatulutsa m'dzikomo. Ndikutitu upemphe mtima wozindikira zinthu, ndi kupemba kuti ukhale womvetsa zinthu. Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva, ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika. Ukatero, udzamvetsa za kuwopa Chauta, udzapeza nzeru za kudziŵa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:1-2

Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe. Mungodzivuta nkulaŵirira m'mamaŵa ndi kukagona mochedwa, kugwira ntchito movutikira kuti mupeze chakudya. Paja Chauta amapatsa okondedwa ake zosoŵa zao iwowo ali m'tulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:9

Mukhale tcheru, ndipo musadzaiŵale zonse zimene mudaziwona. Zimenezo zisachoke m'mitima mwanu pa moyo wanu wonse. Muzizifotokoza kwa ana anu ndi kwa zidzukulu zanu zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:1

Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo, koma mau ozaza amakolezera ukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:4

Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:24

Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti samkonda, koma amene amakonda mwana wake, sazengereza kumlanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:3

Wokonda nzeru amasangalatsa atate ake, koma amene amayenda ndi akazi adama amamwaza chuma chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:2

nthaŵi zonse pamene muli moyo, inu ndi zidzukulu zanu. Muzikaopa Chauta, Mulungu wanu, ndipo muzikamvera malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsaniŵa, kuti pakutero mukakhale moyo nthaŵi yaitali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:13

Ndidzakusangalatsani ku Yerusalemu monga momwe mai amasangalatsira mwana wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:13

Mwana wopusa ndi tsoka kwa atate ake, mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula ya mvumbi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:1-2

Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira. Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye. Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse. Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi. Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera. Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.” Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite. Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:7

Munthu abwino amakhala mwachilungamo, ndipo Mulungu amadalitsa ana amene amatsata njira yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:15

Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:4-7

Sitidzabisira ana ao, koma tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo ntchito zotamandika za Chauta, tidzaŵasimbira mphamvu zake ndi zodabwitsa zimene wakhala akuchita. Kaŵirikaŵiri ankamuukira m'chipululu, ankamumvetsa chisoni. Kaŵirikaŵiri ankamuyesa, ankamputa Woyera wa Israele. Sadakumbukire mphamvu zake kapena tsiku limene adaŵaombola kwa adani ao, pamene Iye adachita zizindikiro zamphamvu ku Ejipito, ndiponso zozizwitsa zake ku dera la ku Zowani. Paja Mulungu adasandutsa madzi a mitsinje yao kuti akhale magazi, kotero kuti Aejipito sadathe kumwa madziwo. Adaŵatumira nthenje za ntchentche zimene zidaŵazunza, ndiponso achule amene adasakaza dziko lao. Adalola kuti kapuchi adye mbeu zao ndiponso kuti dzombe lidye zonse za m'minda mwao. Adaononga mphesa zao ndi matalala ndiponso mitengo yao yankhuyu ndi chisanu. Adalola kuti ng'ombe zao zife ndi matalala ndi kuti nkhosa zao zife ndi zing'aning'ani. Adagwetsa moto wa ukali wake pa iwo: adaŵapsera mtima naŵakwiyira nkuŵagwetsera mavuto. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo oononga. Adapereka mau odzichitira umboni kwa Yakobe, adakhazikitsa malamulo ake mu Israele. Adalamula makolo athu kuti aziŵaphunzitsa ana ao malamulowo. Adalola kukwiya, osadziletsa, sadaŵapulumutse ku imfa, koma adapereka moyo wao ku miliri. Adapha ana achisamba onse a Aejipito, ana oyamba a mphamvu zao, m'zithando za zidzukulu za Hamu. Tsono Mulungu adaŵatulutsa anthu ake ngati nkhosa, naŵatsogolera m'chipululu ngati zoŵeta. Adaŵatsogolera bwino lomwe kotero kuti sanalikuwopa, koma nyanja idamiza adani ao. Adaŵafikitsa ku dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene adaŵagonjetsera ndi dzanja lake lamphamvu. Adapirikitsa mitundu ina ya anthu, kuŵachotsa m'njira. Adagaŵagaŵa dziko la anthuwo kuti likhale la anthu ake, adakhazikitsa mafuko a Israele m'midzi ya anthuwo. Komabe Aisraele adamuputa ndi kumuukira Mulungu Wopambanazonse, sadasunge malamulo ake, koma iwo adakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo ao. Adapotoka ngati uta wosakhulupirika. Iwo adakwiyitsa Mulungu ndi akachisi ao opembedzerako mafano ku mapiri. Adamupsetsa mtima chifukwa cha mafano ao osemawo. Pamene Mulungu adamva zimenezi, adakwiya kwambiri, ndipo adakana Aisraele kotheratu. Motero mbadwo wakutsogolo wa ana amene sanabadwebe, udzaŵadziŵa, ndipo nawonso udzafotokozera ana ake. Adasiya malo ake a Silo kumene ankakhala, adasiya hema limene ankakhalamo pakati pa anthu, ndipo adalola adani athu kuti alande Bokosi la Chipangano chake, limene linali chizindikiro cha mphamvu zake ndi ulemerero wake. Chifukwa adakwiyira anthu ake, adalola kuti anthu akewo aphedwe pa nkhondo. Nkhondo yoyaka ngati moto idaononga anyamata ao, ndipo atsikana ao adasoŵa oŵaimbira nyimbo zaukwati. Ansembe ao omwe adaphedwa ndi lupanga, ndipo akazi ao amasiye sadaŵalole kulira maliro. Pomaliza Ambuye adachita ngati kudzuka kutulo, ngati munthu wamphamvu wofuula chifukwa choledzera. Tsono Mulungu adaŵapirikitsa adani ake, naŵachititsa manyazi anthaŵizonse. Adakana banja la Yosefe, sadasankhule fuko la Efuremu. Koma adasankhula fuko la Yuda, ndiponso phiri la Ziyoni limene amalikonda. Adamanga malo ake opatulika ngati malo ake akumwamba, okhazikika ngati dziko lapansi mpaka muyaya. Anawo aike chikhulupiriro chao pa Mulungu, ndipo asaiŵale ntchito za Mulungu, koma asunge malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:20

Malamulo ukuŵadziŵa: Usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, lemekeza atate ako ndi amai ako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 9:27

Mulungu amkuze Yafeti. Zidzukulu zake zidzagaŵane madalitso ndi zidzukulu za Semu. Kanani adzakhale kapolo wa Yafetiyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 11:19

Muŵaphunzitse kwa ana anu. Muziphunzitsa mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:33

Koma amene amamvera ine adzakhala pabwino, adzakhala mosatekeseka, osaopa choipa chilichonse”.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5

Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:7

Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:20-25

Nthaŵi zakutsogoloko, ana anu adzakufunsani kuti, “Kodi chifukwa chiyani Chauta, Mulungu wathu, adakulamulani kuti muzimvera malamulo ndi malangizo ndi zina zonse zoyenera kuzitsatazi?” Tsono inu mudzaŵauze kuti, “Ife tidaali akapolo a mfumu ya dziko la Ejipito, koma Mulungu adatipulumutsa ndi mphamvu zake zazikulu. Ife tidapenya ndi maso athu Chauta akuchita zodabwitsa ndi zoopsa kuti alange Aejipito, mfumu yao ndi banja lao lonse. Mulunguyo adatitulutsa ife ku Ejipito, natifikitsa kuno ndi kutipatsa dziko lino, monga momwe adalonjezera kwa makolo athu. Pamenepo Mulungu wathu adatilamula kuti tizimvera malamulo onseŵa, ndiponso kuti tizimuwopa. Tikamatero, Iyeyo adzasunga mtundu wathu, ndipo adzautukula monga momwe akuchitiramu tsopano. Tikamasunga mokhulupirika zonse zimene Chauta Mulungu wathu watilamula, Iyeyo adzakondwera nafe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:5

Mwana womakolola nthaŵi yachilimwe ndiye wanzeru, koma womangogona nthaŵi yokolola amachititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:29

Wovutitsa a m'nyumba mwake adzaloŵa m'mavuto, chitsiru chidzasanduka kapolo wa munthu wanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:4-5

Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:1-2

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake. Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse. Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:31

Imvi zili ngati chisoti chaufumu chopatsa ulemerero, munthu amazipata akakhala ndi moyo wautali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:18

Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:17

Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino, koma munthu wankhwidzi amadzipweteka yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:1

Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 113:9

Amapatsa banja mkazi wosabala, namsandutsa mai wosangalala wa ana. Tamandani Chauta!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3

Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:1

Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:6-7

Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:15

Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana, koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:25

Mwana wopusa amamvetsa chisoni atate ake, ndipo amapweteka mtima wa amai ake amene adambala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:8

Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:23

Paja malamulowo ali ngati nyale, maphunzitsowo ali ngati kuŵala, madzudzulo a mwambo aja ndiwo mkhalidwe weniweni pa moyo wa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:5

Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:7

Kumbukirani zakale, lingalirani zamakedzana ndithu, funsani atate anu, akuuzani zimene zidachitika. Funsani akuluakulu, akufotokozerani zakalezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:7-8

Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu. Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:14

Udziŵe kuti nzeru ndi yoteronso mumtima mwako. Ukaipeza, zinthu zidzakuyendera bwino m'tsogolo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:7

Tsono muzipereka kwa onse zimene zikukhalira iwowo: msonkho kwa okhometsa msonkho, zolipira kwa oyenera kuŵalipira. Muzilemekeza oyenera kuŵalemekeza, ndi kuchitira ulemu oyenera kuŵachitira ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:6

“Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukammiza m'nyanja pozama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:17

Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:22

Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake choloŵa, koma chuma cha munthu woipa amachilandira ndi anthu abwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 28:1

Pamenepo Isaki adaitana Yakobe namdalitsa, ndipo adamlamula kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 13:11

Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:15-16

Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru, nanenso mtima wanga udzasangalala. Mtima wanga udzakondwa ndikadzakumva ukulankhula zolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:2

Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:4-6

Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’ Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni, ndazipereka kwa Mulungu,” ameneyo sasoŵanso kulemekeza atate ake.’ Pakutero, chifukwa cha mwambo wanuwo, mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:10

Mwana wanga, anthu oipa akafuna kukukopa, usamaŵamvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 133:1

Ati kukoma ndi kukondweretsa ati, anthu akakhala amodzi mwaubale!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-13

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:8

Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:28-29

Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala. Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati, “Inde alipo akazi ambiri olemerera kwabasi, koma kuyerekeza ndi iwe, onsewo nchabe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 21:7

Ndipo adati, “Akadadziŵa ndani kuti Sara nkuyamwitsa mwana? Komabe ndamubalira mwana wamwamuna Abrahamu pamene ali nkhalamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:7

Amene amatsata malamulo ndiye mwana wanzeru, koma amene amayenda ndi anthu adyera, amachititsa atate ake manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:11

Pali ena amene amatemberera atate ao, ndipo sadalitsa amai ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:3

Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 111:10

Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Wotsata malamulo ake amakhala ndi nzeru zenizeni. Chauta ndi wotamandika mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:9

Ngodala anthu odzetsa mtendere, pakuti Mulungu adzaŵatcha ana ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:25

Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:16

Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13-14

Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi. Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:2-3

Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:3-4

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:7

Tsono muzilandirana monga momwe Khristu adakulandirirani inu, kuti Mulungu alemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:32

Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:5

Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 27:34-35

Esau atamva zimenezi, adalira kwambiri ndi mtima woŵaŵa, ndipo adati, “Bambo, pepani inenso mundidalitseko.” Koma Isaki adayankha kuti, “Mng'ono wako anabwera, ndipo wandinyenga. Iyeyo ndiye amene watenga madalitso ako onse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:3-4

Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu. Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba. Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:4

Mibadwo ndi mibadwo idzatamanda ntchito zanu, idzalalika ntchito zanu zamphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:25-26

Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake. Amaganiza zakutsogolo mosangalala. Amalankhula mwanzeru, ndipo amaphunzitsa anthu ndi mau okoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:13

Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:37-39

Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:11

Bwerani ana anga, mundimvere, ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:40

Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 18:19-20

Tandimverani tsono, ndikulangizeni, ndipo Mulungu adzakhala nanu. Inu muyenera kuima m'malo mwa anthu pamaso pa Mulungu ndi kubwera ndi makangano ao kwa Iye. Motero adabwera ndi Zipora, mkazi wa Mose, amene Moseyo anali atamsiya. Muyenera kuŵaphunzitsa mau ndi malamulo a Mulungu, ndi kuŵafotokozera m'mene azikhalira ndi m'mene azichitira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:15

“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:32-33

“Ndipo tsopano, ana anga, tamverani, ngodala anthu amene amasunga malangizo anga. Muzimva malangizo, kuti muzikhala anzeru, musamanyozere mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:19-21

Mwana wanga, tamvera, ndipo ukhale wanzeru, mtima wako uuyendetse m'njira yabwino. Ngati ndiwe munthu wadyera, udziletse kuti usachite khwinthi. Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera, kapena pakati pa anthu odya nyama mwadyera. Paja chidakwa ndi munthu wadyera adzasanduka amphaŵi, ndipo munthu waulesi adzasanduka mvalansanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 48:9

Yosefe adayankha kuti “Ameneŵa ndi ana anga amene Mulungu adandipatsa ku Ejipito kuno.” Apo Yakobe adati, “Chonde abwere kuno anawo kuti ndiŵadalitse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:17-18

Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga, ndipo ndikulalikabe ntchito zanu zodabwitsa. Choncho Inu Mulungu, musandisiye ndekha ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbu, mpaka nditalalika mphamvu zanu kwa mibadwo yonse yakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 38:19

Amoyo, amoyo okha, ndiwo amakutamandani, monga m'mene ndikuchitira ine tsopanomu. Atate amauza ana ao za kukhulupirika kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:13

Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:19

Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31-32

Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse. Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:12-13

Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate. Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:50

Amaŵachitira chifundo anthu a mibadwo ndi mibadwo amene amamlemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:1-2

Pitirizani kukondana monga abale. Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo. Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa. Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake. Tiyeni tsono tipite kwa Iye kunja kwa misasa kuti tikanyozekere naye limodzi. Paja ife tilibe mzinda wokhazikika pansi pano, tikufunafuna wina umene ulikudza. Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera. Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu. Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe. Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo. Ndikukupemphani makamaka kuti mupemphere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga. Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:14

Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:17-18

Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:30-31

Zidzukulu zam'tsogolo zidzatumikira Ambuye. Anthu adzauza mbadwo umene ukudzawo za Iye. Adzalalika za chipulumutso chake kwa anthu amene mpaka tsopano sanabadwe, ponena kuti Chauta ndiye adapulumutsa anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Wamphamvuzonse! Atate Woyera ndikubwera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wanga Yesu Khristu, lero ndikufuna kukuyamikani chifukwa cha makolo anga. Ndikupemphani kuti mundiphunzitse tsiku lililonse kuwalemekeza ndi kuwateteza kotero kuti ndibwezere pang'ono pa zonse zomwe achita chifukwa cha ine ndipo koposa zonse ndilandire cholowa chawo cha chikhulupiriro ndi chikondi cha mawu anu. Inu mukuti m'mawu anu: "Lemekeza atate wako ndi amayi wako, monga momwe Yehova Mulungu wako anakulangizira, kuti masiku ako atalikirane, ndi kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Yehova Mulungu wako akuupatsa." Atate Woyera, Inu ndinu chitsanzo chabwino kwambiri cha kumvera Makolo ndipo ndithudi chifuniro chanu ndicho kuti tikhale ngati Inu, ana okhala ndi mtima womvera ndi wolangika, omwe amayamikira malamulo ndi mawu anu, akuyamika chiphunzitso chilichonse ndi malangizo a makolo. Ikani mwa iwo chilakolako chofuna kufunafuna kukhalapo kwanu ndi kusinkhasinkha mawu anu, kuti miyoyo yawo isinthe ndi kutsogozedwa ndi Inu. Ambuye, ndikukuyamikani chifukwa cha makolo anga omwe akhala anthu ofunikira kwambiri pa moyo wanga, ndikupemphani kuti mundiphunzitse kugonjera ndi kumvera chifukwa izi n'zokondweretsa ndi zolungama pamaso panu. M'dzina la Yesu, ndikukupatsani ulemerero ndi ulemu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa