Lero ndikufuna ndikukumbutse kuti Mulungu amakupatsa mphamvu zokumana ndi vuto lililonse lovuta. Nthawi zambiri timaganiza kuti mavuto akabwera sitikonzeka kulimbana nawo, koma ukunama, Mulungu nthawi zonse amatikonzekeretsa. Mawu ake amati Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha, koma wa mphamvu, chikondi ndi kudziletsa. Choncho limbika mtima, Mulungu ali nawe, akulimbana nkhondo zako zonse.
Gwiritsa ntchito zipangizo zimene Mulungu anakupatsa kudzera m'mawu ake ndi mzimu wake woyera. Khala wolimba mtima, pita patsogolo molimba mtima komanso modzidalira. “Limbikani mtima, mukhale amphamvu, nonsenu inu akuyembekezera Yehova.” (Masalimo 31:24) Choncho limbika mtima, Mulungu sanama.
Mulungu ndiye mphamvu yako, ndiye wokulanditsa wako, ndiye mthandizi wako, ndiye chishango chako, ndiye pothawirapo pako, khulupirira Atate wako wakumwamba, zonse zidzakhala bwino. “Mulungu ndiye amene amandipatsa mphamvu; Mulungu ndiye amene anwongola njira yanga.” (2 Samueli 22:33)
Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. “Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.
“Ngati anthu odalira zapansipano adana nanu, kumbukirani kuti adadana ndi Ine asanadane nanu. Mukadakhala a mkhalidwe wao, akadakukondani chifukwa cha kukhala anzao. Koma amadana nanu, chifukwa Ine ndidakusankhani pakati pa iwo, motero sindinu anzao. Iwo amadula nthambi iliyonse mwa Ine imene siibala zipatso. Ndipo nthambi iliyonse yobala zipatso, amaitengulira kuti ibale zipatso zambiri koposa kale. Kumbukirani mau aja amene ndidakuuzani kuti, ‘Wantchito saposa mbuye wake.’ Ngati Ine adandisautsa, inunso adzakusautsani. Ngati adamvera mau anga, adzamvera mau anunso.
Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo. Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu. Anthu akakuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, chifukwa ndiye kuti Mzimu wa ulemerero, Mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu.
Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.” Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda. Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.
Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai.
Adaŵalimbitsa mtima ophunzira aja, naŵauzitsa kuti asataye chikhulupiriro chao. Adaŵauza kuti, “Kuti tiloŵe mu Ufumu wa Mulungu tiyenera kupirira masautso ambiri.”
Paja Iye adakupatsani mwai, osati wakungokhulupirira Khristu ai, komanso wakumva zoŵaŵa chifukwa cha Iye.
Kumbukirani masiku akale aja mutangolandira kuŵala chatsopano. Pa nthaŵi imene ija mudaalimbana ndi mazunzo ambiri. Mwina ankakunyozani ndi kukuchitani chipongwe, anthu akuwonerera. Mwinanso munkamva nawo zoŵaŵa amene ankasautsidwa motero. Munkasaukira limodzi ndi amene adaaponyedwa m'ndende, ndipo mudalola mokondwa kuti alande chuma chanu, mutadziŵa kuti muli ndi chuma choposa ndi chosatha. Tsono musataye kulimba mtima kwanu, pakuti kumabweretsa mphotho yaikulu. Pafunikadi kupirira, kuti muchite zimene Mulungu akufuna, kuti motero mukalandire zimene adalonjeza.
“Ndinu odala anthu akamadana nanu, akamakusalani ndi kukuchitani chipongwe, ndipo akamaipitsa dzina lanu chifukwa cha Ine Mwana wa Munthu. Nthaŵi imeneyo sangalalani ndi kuvina ndi chimwemwe, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi zomwenso makolo ao ankaŵachita aneneri kale.
Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha? Ngakhale bambo wanga ndi mai wanga andisiye ndekha, Inu Chauta mudzandisamala. Mundiwonetse njira zanu zachifundo, Inu Chauta, munditsogolere m'njira yosalala, chifukwa ndili ndi adani ambiri. Musandipereke m'manja mwa adani angawo. Mboni zonama zandiwukira, ndipo zimandiwopseza. Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta m'dziko la amoyo. Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta. Pamene adani ndi amaliwongo anga andiputa kuti andiphe, adzaphunthwa ndipo adzagwa. Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda. Anthu muchenjere nawo, pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu, ndipo adzakukwapulani m'nyumba zao zamapemphero. Adzapita nanu kwa nduna ndi mafumu chifukwa cha Ine, mwakuti mudzandichitira umboni pamaso pao, ndi pa anthu a mitundu ina.
Koma ngakhale mumve zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima,
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.
Pakuti monga tikumva zoŵaŵa kwambiri pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatilimbitsa mtima kwambiri. Ngati tikuzunzika, nkuti inu mupeze chokulimbitsani mtima ndiponso chipulumutso. Ngati ife atilimbitsa mtima, nkuti inunso mulimbitsidwe mtima ndi kulandira mphamvu za kupirira pamene mulikumva zoŵaŵa zomwezo zimene ifenso timamva. Chikhulupiriro chathu pa inu ncholimba. Tikudziŵa kuti monga mulikumva zoŵaŵa pamodzi nafe, momwemonso mudzapeza chokulimbitsani mtima pamodzi nafe.
Musachite nazo mantha zoŵaŵa zimene mukukakumana nazo. Ndithu enanu Satana adzakuponyetsani m'ndende kuti akuyeseni, ndipo mudzazunzika pa masiku khumi. Khalani okhulupirika mpaka kufa, ndipo ndidzakupatsani moyo ngati mphotho yanu.
Iwo adachoka kubwaloko ali okondwa kuti Mulungu waŵaŵerengera ngati oyenera kunyozeka chifukwa cha dzina la Yesu.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,
Kodi pali chiyani choti nkukuyamikirani ngati mupirira pamene akumenyani chifukwa choti mwachimwa? Koma mukapirira zoŵaŵa mutachita zabwino, apo mwachita chinthu chovomerezedwa ndi Mulungu. Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angagwedezeke chifukwa cha mazunzoŵa. Mukudziŵa nokha kuti Mulungu ndiye adalola kuti zimenezi zitigwere. Pajatu pamene tinali pamodzi nanu, tidaakuuziranitu kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziŵa, zimenezi zidachitikadi.
Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena.
Iye adasankha kuzunzikira nawo limodzi ana a Mulungu, koposa kukondwerera zosangalatsa za uchimo kanthaŵi pang'ono. Adaaona kuti kuzunzika chifukwa cha Wodzozedwa wa Mulungu kunali chuma chachikulu koposa chuma chonse cha ku Ejipito, pakuti maso ake anali ndithu pa mphotho yakutsogolo.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Masiku anga ali m'manja mwanu. Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza. Yang'aneni mtumiki wanune mwa kukoma mtima kwanu, pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Chauta sadzaŵataya anthu ake, sadzaŵasiya okha osankhidwa ake. Chilungamo chidzaŵabwereranso kwa anthu ake, ndipo onse oongoka mtima adzachitsata.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Koma kunyoza kwao sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziŵa kuti sadzandichititsa manyazi.
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku. Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira. Usachite manyazi tsono kuchitira umboni Ambuye athu. Usachitenso manyazi chifukwa cha ine amene ndili m'ndende chifukwa cha iye, koma umve nao zoŵaŵa chifukwa cha Uthenga Wabwino, ndi chithandizo cha mphamvu za Mulungu.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu. Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu. Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa. Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Koma pa zonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu pakupirira kwambiri m'masautso, m'zoŵaŵa ndiponso m'nkhaŵa. Tidakwapulidwa, tidaponyedwa m'ndende, ndipo anthu adatiwukira mwachipolowe. Tidagwira ntchito kwambiri, mwina osagona tulo, osaona chakudya.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.” Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
“Koma zisanachitike zonsezi, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzapita nanu ku milandu ku nyumba zamapemphero, nadzakuponyani m'ndende. Adzakuperekani kwa mafumu ndi kwa akulu ena a Boma chifukwa chotsatira Ine. Umenewu udzakhala mpata wanu wondichitira umboni.
Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni. Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.
Ngakhale agwe sadzapweteka, popeza kuti Chauta amamgwira dzanja. Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya. Nthaŵi zonse munthu wolungama amapatsa mosaumira, ndipo amakongoza mwaufulu, ana ake amakhala madalitso.
Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu. Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani. Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena. Paja munthu amene amangomva chabe mau, osachita zimene wamvazo, ali ngati munthu woyang'anira nkhope yake yachibadwa m'galasi. Tsono amati akadzipenya, amachokapo, posachedwa nkuiŵalako m'mene akuwonekera. Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse. Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga. Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi. Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika. Koma kulimbika kumeneku kuzigwira ntchito yake kotheratu, kuti mukhale angwiro, opanda chilema ndi osapereŵera pa kanthu kalikonse.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Nchifukwa chake ife timakunyadirani, m'mipingo yonse ya Mulungu, chifukwa cha kulimbika kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso ndi mazunzo onse amene adakugwerani. Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Cholinga chake nchakuti inu mupezeke oyenera kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu umene mukuusaukira tsopano.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndikukupemphani tsono kuti musataye mtima chifukwa chakuti ndikukusaukirani. Kwenikweni muyenera kunyadira chifukwa cha kusauka kwangaku.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi champhamvu, kotero kuti maziko a ndende adagwedezeka. Nthaŵi yomweyo zitseko zonse zidatsekuka, maunyolo a mkaidi aliyense nkumasuka.
Mupemphere kwa Ine pa tsiku lamavuto. Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro. Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira. Ambuye amene ali Woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphothoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso.
Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga! Fuula ndi chimwemwe, iwe dziko lapansi! Yambani nyimbo, inu mapiri! Chauta watonthoza mtima anthu ake, ndi kuŵamvera chifundo anthu ake ovutika.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Sindichita mantha ngakhale adani anga ndi osaŵerengeka, ngakhale andizinge ndi kundithira nkhondo.
Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.
“Ndikukuuzani inu, abwenzi anga, kuti musamaopa anthu. Iwo angathe kupha thupi lokha, koma pambuyo pake alibenso china choti angachitepo. Choncho inunso khalani okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene simukuyembekeza.” Pamenepo Petro adati, “Ambuye, kodi fanizoli mukuphera ife tokha, kapena mukuuza onse?” Yesu adati, “Tsono kapitao wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake? Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi. Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse. “Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’ Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, amuna ndi akazi, ndiponso kumadya, kumamwa ndi kuledzera. Tsono mbuye wake adzangoti mbwe mwadzidzidzi, pa tsiku limene iye sakumuyembekeza. Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu osakhulupirika. “Wantchito amene akudziŵa zimene mbuye wake amafuna, koma osakonzekera kuzichita, adzamkwapula kwambiri. Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.” “Ndidabwera kudzaponya moto pa dziko lapansi, ndipo ndikadakonda utayaka kale. Koma ndikuchenjezeni: amene muyenera kumuwopa ndi Mulungu. Iye atalanda moyo wa munthu, ali nazonso mphamvu za kumponya m'Gehena. Ndithu ndi ameneyo amene muzimuwopa.
Munthu woyesa kusunga moyo wake, adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzausunga.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Muuze onse a mtima wamantha kuti, “Limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.”
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”
Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani? Chauta ali pa mbali yanga kuti andithandize. Odana nane ndidzaŵayang'ana monyoza nditaŵapambana.
Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.
Pamene anthuwo ankamuponya miyala, Stefano adayamba kupemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” Mulungu adati, ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo ku dziko lina kumene eniake adzaziyesa akapolo, nadzazizunza pa zaka mazana anai.’ Ndipo adagwada pansi nafuula kwakukulu kuti, “Ambuye, musaŵaŵerengere tchimoli.” Atanena mau ameneŵa, adafa.
Tsono ndimakondwera pamene ndili wofooka, pamene anthu andinyoza, namandizunza, ndiponso pamene ndimva zoŵaŵa ndi kusautsidwa chifukwa cha Khristu. Pakuti pamene ndili wofooka, mpamene ndili ndi mphamvu.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye. Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima. Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu, chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake.
“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.
Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.
“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, ndidzampatsa mwai wodya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku Paradizo la Mulungu Kumwamba.”
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.
Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Atamandike Chauta, thanthwe langa londitchinjiriza, amene amaphunzitsa manja anga ndi zala zanga kumenya nkhondo. Inu amene mumapambanitsa mafumu pankhondo, amene mumalanditsa Davide mtumiki wanu. Landitseni kwa adani ankhalwe, mundipulumutse m'manja mwa akunja, amene amalankhula zabodza, ndipo amalumbira zonama. Ana athu aamuna pachinyamata pao akhale amphamvu ngati mitengo, ana athu aakazi akhale okongola ngati nsanamira zozokotedwa zapangodya, zoti zikometse nyumba yaufumu. Nkhokwe zathu zikhale zodzaza, zisunge zokolola za mtundu uliwonse. Nkhosa zathu zibale ana zikwizikwi m'mabusa athu. Ng'ombe zathu zikhale ndi maŵele, zisapoloze kapena kulephera kubereka. M'miseu mwathu musakhale kulira chifukwa cha mavuto. Ngodala anthu olandira madalitso ameneŵa. Ngodala anthu amene Mulungu wao ndi Chauta. Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga.
Onse amene Atate andipatsa, adzabwera kwa Ine. Ndipo munthu aliyense wodza kwa Ine, sindidzamkana konse.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.
“Mverani, inu amene mukudziŵa chilungamo, inu amene mukusunga malamulo anga mumtima mwanu. Musachite mantha anthu akamakudzudzulani, musataye mtima akamakulalatirani. Anthu otereŵa adzatha ngati nsalu yodyewa ndi njenjete, adzatha ngati thonje lodyewa ndi mbozi. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, kuwombola kwanga kudzakhala kwa nthaŵi zonse.”
Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.” Usaope, iwe Yakobe, wofooka ngati nyongolotsi, usachite mantha, iwe Israele, wooneka ngati mtembo, chifukwa Ineyo ndidzakuthandiza. Mpulumutsi wako ndine, Woyera uja wa Israele.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.
Ndiponso ndikufuna kuti mudziŵe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa, Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika ku dzanja lake lamanja m'dziko la Kumwamba.
Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Ndiye tsono Ambuye, onani zimene akutiwopsezazi, ndipo mutithandize atumiki anufe, kuti tilankhule mau anu molimba mtima ndithu. Tsono adaŵagwira, ndipo poti kunali kutada kale, adaŵaika m'ndende kufikira m'maŵa. Tambalitsani dzanja lanu kuti anthu achire, ndipo pachitike zizindikiro ndi zozizwitsa m'dzina la Mtumiki wanu wopatulika.” Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Ndidzatsogolera anthu akhungu m'miseu imene sadaidziŵe, ndidzaŵaperekeza pa njira zimene sadadzerepo konse. Ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwao kuti ukhale kuŵala, ndipo ndidzasalaza malo osasalala. Zimenezi ndidzazichitadi ndipo sindidzazilekera padera.
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
“Sipadzafikanso dzuŵa loti likuŵalire masana, kapena mwezi wokuŵalira usiku. Koma Ine Chauta ndiye ndidzakuŵalire mpaka muyaya. Ine Mulungu wako ndiye ndidzakhale ulemerero wako. Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuŵalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Chokuunikira ngati dzuŵa sichidzaloŵanso, ndipo chokuunikira ngati mwezi sichidzazimiriranso, chifukwa ndi Chauta amene adzakhala kuŵala kwako mpaka muyaya. Choncho masiku ako olira adzatha.
Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Paja ndi Mulungu amene adaati, “Kuŵala kuunike kuchokera mu mdima.” Mulungu yemweyo ndiye adatiwunikiranso m'mitima mwathu, kuti anthu adziŵe ulemerero wa Mulungu umene ukuŵala pa nkhope ya Khristu.
Chomwecho inunso mukuvutika tsopano, koma ndidzakuwonaninso. Pamenepo mtima wanu udzakondwa, ndipo palibe munthu amene adzakulandani chimwemwe chanucho.
Koma ngati mumva zoŵaŵa chifukwa chakuti ndinu akhristu, musachite manyazi, koma mulemekeze Mulungu chifukwa cha dzinalo.
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse. Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Tsono abale, khalani olimbika, ndipo mugwiritse miyambo imene tidakuphunzitsani ndi mau apakamwa kapena am'makalata. Mulungu Atate athu adatikonda, ndipo mwa kukoma mtima kwake adatipatsa kulimba mtima kosatha ndi chiyembekezo chokoma. Iye pamodzi ndi Yesu Khristu Ambuye athu athuzitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse.
Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.]
Tsono ananu, khalani mwa Iye, kuti tikakhale olimba mtima Iye akadzaoneka, ndipo tisadzachite manyazi Iye akadzabweranso.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Koma ine ndikupempha Chauta, ndipo Iye adzandithandiza. Madzulo, m'maŵa ndi masana ndikudandaula ndi kulira, ndipo Iye adzamva mau anga.
Zoonadi, ndinu thanthwe langa ndi linga langa. Tsogolereni ndi kundiwongolera chifukwa Inu ndinu Chauta. Onjoleni mu ukonde umene anditchera, pakuti Inu ndinu pothaŵira panga. Ndikupereka moyo wanga m'manja mwanu. Inu Chauta wokhulupirika, mwandiwombola.
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.