Mulungu wandipatsa lonjezo pa vuto lililonse. Alipo nthawi zonse pa moyo wanga, ndipo chifukwa cha chikondi Chake, wandipatsa malonjezo okongola, kuti ndikhulupirire kuti ali nane nthawi zonse, ndikupumula mwa Iye.
Palibe lonjezo la Mulungu lomwe silinakwaniritsidwe. Zonse zakwaniritsidwa. Lonjezo lililonse lomwe ndingapemphe m'dzina la Khristu, latsimikizika ndipo Mulungu adzalikwaniritsa pa ine, kuti Iye alemekezedwe.
Malonjezo nthawi zonse amakhala ndi mbali ziwiri: choyenera kuchita ndi zotsatira zake, zomwe zimatengera kuchita choyenera kuchitacho. Lonjezo la Mulungu ndi mawu ochokera kwa Iye omwe ali ndi mphamvu yokwaniritsidwa, bola ngati nditachita zomwe ayenera kuchita.
Ndikakhala nthawi ndikuphunzira Malemba, ndimapeza malonjezo ambiri ochokera kwa Mulungu. Chitsanzo chabwino ndi lonjezo la chipulumutso lomwe lili mu Pangano Latsopano. Mulungu akunena kudzera mwa Paulo kuti, “Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndiye Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumutsidwa” (Aroma 10:9).
Pa lonjezo la chipulumutso lomwe ndalitchula, zimatengera ine ngati ndidzakhulupirira ndi kuvomereza kuti Yesu ndi Ambuye. Ndikakhulupirira ndi kuvomereza, lonjezolo limayamba kugwira ntchito ndi kukwaniritsidwa. Koma zimatengera ine. Mulungu akufuna kupulumutsa aliyense, koma si onse omwe amatsegula mphamvu ya lonjezolo.
Ekisodo 20:12 imati: “Lemekeza atate wako ndi amayi ako, kuti masiku ako akhale ochuluka m’dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa.” Ili ndi lonjezo la Mulungu lomwe lidzakwaniritsidwa pokhapokha ndikalemekeza atate ndi amayi anga. Choncho, kuti ndione lonjezoli likukwaniritsidwa pa moyo wanga, ndiyenera choyamba kuchita zomwe ayenera kuchita, ndipo zotsatira za lonjezolo zidzabwera.
Mulungu akudalitseni.
Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika. Mudzatichitiranso chifundo. Mudzapondereza pansi zolakwa zathu, mudzataya machimo athu onse pansi pa nyanja.
“Mufunefune Chauta pamene angathe kupezeka, mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi. Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”
“Adzabzala mwamtendere, mpesa udzabala zipatso zake, ndipo nthaka idzabereka kwambiri. Mvula idzagwa kuchokera kumwamba. Madalitso onseŵa ndidzaŵapatsa otsala mwa anthuŵa.
Pamene amphaŵi ndi osauka akufunafuna madzi, koma osaŵapeza, ndipo kum'mero kwao kwangoti gwa ndi ludzu, Ine Chauta ndidzayankha pemphero lao, Ine Mulungu wa Israele sindidzaŵasiya. Ndidzayendetsa mitsinje pakati pa zitunda zouma, ndipo akasupe adzatumphuka m'zigwa. Ndidzasandutsa chipululu kukhala chidziŵe cha madzi, ndi dziko louma kukhala akasupe.
Pamenepo Chauta, Mulungu wanu, adzakukhazikaninso pabwino ndi kukuchitirani chifundo. Adzakusokolotsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu, kumene adakumwaziraniko, ndipo adzakusandutsaninso olemera.
mau achisangalalo ndi achimwemwe, mau achikondwerero a mkwati wamwamuna ndi wamkazi. M'Nyumba ya Mulungunso mudzamveka nyimbo ya anthu odzapereka nsembe zothokozera Mulungu. Nyimbo yake azidzati, “ ‘Tamandani Chauta Wamphamvuzonse, popeza kuti ndi wabwino ndipo chikondi chake nchamuyaya!’ Ndithudi, ndidzaŵabwezeranso pabwino monga momwe adaaliri,” akutero Chauta.
Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.
Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe.
Inu Chauta, chiritseni ndipo ndidzachiradi. Pulumutseni ndipo ndidzapulumukadi. Ndinu amene ndimakutamandani.
Adati, “Mukamandimvera Ine Chauta, Mulungu wanu, kumachita zolungama, kumasamala malamulo anga ndi kumamvera zimene ndikukulamulani, sindidzakulangani ndi nthenda zilizonse zimene ndidalanga nazo Aejipito. Ine ndine Chauta amene ndimakuchiritsani.”
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
“ ‘Tsono zimene Ine Ambuye Chauta ndikunena ndi izi: Tsopano a m'fuko la Yakobe ndidzaŵakhazikanso pabwino. Aisraelenso onse ndidzaŵachitira chifundo. Dzina langa loyera ndidzaliteteza.
Chauta akuti, “Ndidzachiza matenda ao a kusakhulupirika. Ndidzaŵakonda kwambiri, pakuti ndaleka kuŵakwiyira.
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.
Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala, dziko louma lidzakondwa ndi kuchita maluŵa. Amene Chauta adaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu. Dzikolo lidzakhala ndi maluŵa ochuluka ongodzimerera okha. Lidzasangalala ndi kufuula ndi chimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero wonga wa mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake adzakhala okongola ngati a ku Karimele ndi Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Chauta ndi ukulu wa Mulungu wathu.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga! Fuula ndi chimwemwe, iwe dziko lapansi! Yambani nyimbo, inu mapiri! Chauta watonthoza mtima anthu ake, ndi kuŵamvera chifundo anthu ake ovutika.
Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
Nthaŵi ikubwera yoti ndidzaŵabwezere anthu anga, Israele ndi Yuda, ku dziko limene ndidapatsa makolo ao, ndipo lidzakhaladi lao.”
Chauta akunena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzasonkhanitsa opuwala, ndidzakusa amene adachotsedwa kwao, ndiponso amene ndidaŵalanga. Opundukawo ndidzaŵasandutsa anthu anga otsala, amene adachotsedwa kwao ndidzaŵasandutsa mtundu wamphamvu. Ine Chauta ndidzakhala mfumu yao pa phiri la Ziyoni, kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya.
Ndidzachita chotheka kuti ndiŵachitire zabwino ndi kuŵabwezeranso ku dziko lao. Ndidzaŵamanga osati kuŵapasula. Ndidzaŵakhazikitsa, osati kuŵazula ai.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Akuti: Unditame mopemba, ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziŵa.
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi imene ndidakukomera mtima, ndidakuyankha, ndipo tsiku la chipulumutso ndidakuthandiza. Ndidakusunga ndipo ndidakusandutsa kuti ukhale chipangano kwa anthu, kuti ndilibwezere dziko mwakale ndi kuligaŵagaŵa dziko loonongekali.
Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro, mau a Chauta ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
Pamenepo wokhala pampando wachifumu uja adati, “Tsopano ndisandutsa zonse kuti zikhale zatsopano.” Adanenanso kuti, “Lemba zimenezi, pakuti mau ameneŵa ndi oona ndi oyenera kuŵakhulupirira.”
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Chauta akunena kuti, “Ndikulenga thambo lam'mwamba latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zakale sadzazikumbukiranso, zidzaiŵalika kotheratu.
“Ndinu odala, inu amene mukumva njala tsopano, chifukwa mudzakhuta. “Ndinu odala, inu amene mukulira tsopano, chifukwa mudzakondwa.
Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira.
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Mudzanditsitsimutsanso Inu amene mwandiwonetsa mavuto ambiri oŵaŵa, mudzanditulutsanso m'dzenje lozama la pansi pa nthaka.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Chauta akunena kuti, “Monga momwe ndidaŵaonongera anthuŵa, momwemonso ndidzaŵapatsa mtendere umene ndidzaŵalonjeza.
Fuulani mokondwera inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Chauta waŵatonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha. M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.
Chauta akunena kuti, “Tonthola, usadzenso misozi. Ndithu udzalandira mphotho ya ntchito zako, akutero Chauta. Ndipo anthu adzabwerako ku dziko la adani.
Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza.
Motero ndidzakubwezerani zonse zimene zidaonongedwa ndi dzombe, mandowa, mphutsi ndi ziwala. Limenelitu ndiye gulu lankhondo lija limene ndidatuma kudzakukanthani.
Bwererani ku linga lanu lolimba, inu akapolo amene tsopano muli ndi chikhulupiriro. Lero ndi tsiku limene ndikulengeza kuti ndidzakubwezerani zabwino moŵirikiza.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Inu Mulungu, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka.
Ndidzatsitsimutsa anthu ofooka, ndipo anthu anjala ndidzaŵadyetsa chakudya nadzakhuta.”
Anthu akunena kuti, “Tiyeni, tibwerere kwa Chauta. Watikadzula, komabe adzatichiritsa. Watikantha, komabe adzamanga mabala athu.
Anthu anu adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthaŵi yaitali. Adzamanganso pa maziko akalekale. Apo mudzatchedwa anthu okonza makoma, omanganso nyumba zamabwinja, kuti anthu azikhalamo.”
Koma inuyo, ndidzachiza matenda anu, ndidzapoletsa mabala anu, chifukwa anthu ena amati ndinu otayika, amati, ‘Ndi anthu a ku Ziyoni aŵa, opanda oŵasamala,’ ” akuterotu Chauta.
Popeza kuti mudalandira manyazi, manyozo ndi zotukwana moŵirikiza, tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu moŵirikizanso. Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.”
ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.
“Ndidaona m'mene ankachitira, komabe ndidzaŵachiritsa. Ndidzaŵatsogolera ndi kuŵatonthoza. Anthu olira nao adzandiyamika ndi milomo yao.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu.
“Komabe m'tsogolo mwake ndidzaupatsanso moyo ndi kuuchiritsa. Anthu ake ndidzaŵachiritsa ndi kuŵapatsa zabwino zochuluka ndi mtendere weniweni.
Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.
Ndiye amene amakupatsa zabwino nthaŵi zonse za moyo wako, choncho umakhalabe wa mphamvu zatsopano ngati mphungu.
“Nthaŵi imeneyo itafika, masiku amene ndidzakwezanso anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu,
Unene kuti zimene Ine Ambuye Chauta ndikuŵauza mafupawo ndi izi: Ndidzauzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo.
Ndidzakusamaliraninso inu anthu a ku Israele, motero mudzapezanso bwino. Mudzakondwanso poimba ting'oma tolira, ndipo mudzapita nawo limodzi anthu ovina mwachimwemwe.
“Iwe dziko, usachite mantha. Kondwa ndipo usangalale, pakuti Chauta mwini wake adachita zazikulu.
Adzabwerera kwao akulira, koma Ine ndidzaŵaperekeza ndi mtima wachifundo. Ndidzaŵatsogolera ku mitsinje yodzaza ndi madzi. Sadzaphunthwa, njira yao idzakhala yosalala kwambiri. Ine ndine bambo wake wa Israele, Efuremu ndi mwana wanga wachisamba.
Ndachotsa zolakwa zako ngati mtambo ndiponso machimo ako ngati nkhungu. Bwerera kwa Ine poti ndakuwombola.”
Inu Chauta mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere mwakale. Mutipatsenso masiku onga amakedzana aja.
“Inu anthu anga, mudzachoka ku Babiloni mokondwa, adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere. Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo. Nayonso mitengo yonse yam'thengo idzakuwomberani m'manja.
Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.”
Mwezi udzaŵala ngati dzuŵa, ndipo dzuŵa lidzaŵala kwambiri ngati kasanunkaŵiri kuŵala kwa pa tsiku limodzi. Zimenezi zidzachitika pamene Chauta adzamange ndi kupoletsa zilonda zimene Iye yemwe adachititsa pakuŵalanga anthu ake.
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
“Ndidzaŵabwezeranso pabwino anthu anga Aisraele. Adzamanganso mizinda yamabwinja ndi kumakhalamo. Adzalima minda ya mphesa ndipo adzamwa vinyo wake. Adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina, mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo.
Anamwali adzavina mokondwa, achinyamata ndi okalamba omwe adzasangalala. Kulira kwao kuja ndidzakusandutsa chimwemwe. Ndidzaŵasangalatsa, ndidzaŵakondwetsa, nkuchotsa chisoni chao.
Ndidzatonthoza mtima Ziyoni, ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake. Ngakhale dziko lake ndi chipululu, ndidzalisandutsa ngati Edeni. Ngakhale dziko lake ndi thengo, ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta. Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala, adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza.
Mudzanditsitsimutsanso Inu amene mwandiwonetsa mavuto ambiri oŵaŵa, mudzanditulutsanso m'dzenje lozama la pansi pa nthaka. Inu mudzaonjezera ulemu wanga ndipo mudzandisangalatsanso.
“Banja la Yuda ndidzalilimbitsa, banja la Yosefe ndidzalipambanitsa. Anthuwo ndidzaŵabwezanso kwao chifukwa choti ndaŵamvera chifundo. Tsono adzakhala ngati kuti sindidaŵataye, pakuti Ine ndine Chauta, Mulungu wao, ndipo ndidzayankha zopempha zao.
“Bwererani kwa Ine, inu anthu anga osakhulupirika. Ndidzakuchiritsani kuti mukhale okhulupirika.” Inu mukuti, “Tikubwera kwa Inu, poti ndinu Chauta, Mulungu wathu.