Mulungu ndiye analenga zonsezi. Dziko, thambo, zonse zomwe zili mmenemu, ndi zake. Iye ndiye anazipanga. Monga mmene Baibulo limanenera pa Ekisodo 20:11, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zomwe zili mmenemu m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo anapumula pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. N’chifukwa chake tsiku la Sabata ndi lopatulika. Zonse zimene Mulungu analenga zinali zangwiro, ndipo tiyenera kumutamanda chifukwa cha zodabwitsa zimene anachita.
Tiyeni tiope Mulungu ndi kumupatsa ulemu, chifukwa nthawi ya chiweruzo chake yafika. Tiyeni tilambire iye amene analenga kumwamba, dziko, nyanja, ndi akasupe a madzi. Tiyeni timupatse Mulungu ulemu wonse. Ukakhala pa gombe, ukayang’ana mitengo, kapena mapiri, kumbukira kuti Mlengi wako ndiye anazipanga zokongola ndi zangwiro. Usaleke kupatsa Mulungu ulemu.
Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziŵeto zake, koma munthu woipa mtima chifundo chake nchankhwidzi.
Zitatha izo Mulungu adati, “Tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam'nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoŵeta, ndi zokwaŵa zonse za pa dziko lapansi.”
Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Bulu wa mdani wako akagwa ndi katundu, usabzole ndi kumsiya, koma umthandize kuti adzuke.
Kulungama kwanu kumaonekera ngati mapiri aatali, kuweruza kwanu nkozama ngati nyanja yakuya, Inu Chauta, mumasamalira anthu ndi nyama zomwe.
Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako.
Mimbulu ndi anaankhosa zidzadyera pamodzi. Mkango udzadya udzu monga ng'ombe. Fumbi ndiye lidzakhale chakudya cha njoka. Pa phiri langa loyera la Ziyoni sipadzakhala chinthu chopweteka kapena choononga,” akuterotu Chauta.
Pita kwa nyerere, mlesi iwe. Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru. Ilibe ndi mfumu yomwe, ilibe kapitao kapena wolamulira. Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe, ndipo imatuta chakudyacho m'masika.
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
Nthaŵi imeneyo ndidzachita chipangano ndi nyama zakuthengo, mbalame zamumlengalenga, ndi zokwaŵa pansi, kuti ziyanjane ndi anthu anga. Tsono ndidzathyola uta, lupanga, ndi zida zina zonse zankhondo, ndipo ndidzazichotsa m'dzikomo, kuti iwo apeze moyo wamtendere.
Nanga Ine, kodi sindiyenera kuumvera chisoni mzinda waukulu wa Ninive? M'mene mujatu muli anthu opitirira zikwi 120, amene sadziŵa kusiyanitsa kuti zabwino nziti, zoipa nziti, mulinso ziŵeto zochuluka.”
Ngati mupeza chisa cha mbalame mu mtengo kapena pansi, make ali pa mazira, kapena ali ndi tiana take, musaitenge mbalameyo pamodzi ndi tiana take. Tianato mungathe kutenga, koma makeyo mloleni apite, kuti mukakhale ndi moyo wabwino ndi wautali.
“Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu.
Tsono Chauta adamtenga munthuyo, namukhazika m'munda wa Edeni uja kuti azilima ndi kumausamala.
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi, mwanawang'ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi, mwana wamng'ono nkumaziŵeta zonsezo.
Kodi khwangwala amampatsa chakudya chake ndani, pamene maunda ake akulirira kwa Mulungu, namadzandira chifukwa chosoŵa chakudya?”
Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.
Nyama iliyonse yofa yokha, musadye. Alendo okha amene mumakhala nawo, alekeni adye, kapena mungogulitsa nyamayo kwa alendo ena. Pajatu inu ndinu opatulika a Chauta, Mulungu wanu. Musaphike mwanawankhosa kapena mwanawambuzi mu mkaka wa make.
“Popeza kuti nyama iliyonse yam'nkhalango ndi yanga, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku mapiri ochuluka. Mbalame zonse zamumlengalenga, zamoyo zonse zoyenda ku thengo ndi zanga.
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Mudampatsa ulamuliro pa ntchito za manja anu. Mudamgonjetsera zolengedwa zonse, nkhosa, ng'ombe ndi nyama zakuthengo, mbalame zamumlengalenga, nsomba zam'nyanja, ndi zonse zoyenda pansi pa nyanja.
Make akakhala ng'ombe kapena nkhosa, musaphe makeyo pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzi.
Kenaka adaŵafunsa kuti, “Ndani mwa inu, bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime pa tsiku la Sabata, sangaitulutse pa Sabata pomwepo?”
Nyama zakuthengo zidzandilemekeza, nkhandwe ndi nthiŵatiŵa zidzanditamanda, chifukwa ndidzayendetsa madzi m'chipululu ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiŵapatse madzi anthu anga osankhidwa.
Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino.
Paja timaŵerenga m'Malamulowo kuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe pamene ikupuntha tirigu.” Kodi pamene adanena zimenezi, Mulungu adangosamala za ng'ombe zokha?
“Sindikudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu, popeza kuti mumapereka nsembe zanu zopsereza kwa Ine nthaŵi zonse. Ndithudi, sindilandira ng'ombe kapena mbuzi iliyonse ya m'makola anu.
Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake.
Akadzidzi adzamangako zisa zao, nkuikirako mazira, ndi kuswa ana ao namaŵasamala. Adembo adzasonkhana kumeneko aŵiriaŵiri.
Yesu adaŵayankha kuti, “Ndani mwa inu atakhala ndi nkhosa imodzi, nkhosayo nkugwa m'dzenje pa tsiku la Sabata, angapande kuigwira nkuitulutsa? Nanji munthu, amene amaposa nkhosa kutalitali! Ndiye kutitu Malamulo amalola kuchita zabwino pa tsiku la Sabata.”
Ng'ombe yaikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi, ndipo ana ao adzagona pamodzi. Mkango udzadya udzu ngati ng'ombe.
anaankhosa adzakupatsa chovala, ndi ubweya wao, ndipo pogulitsa mbuzi udzapeza chogulira munda.
“Kodi iwe ungathe kuufunira chakudya mkango? Kodi ungathe kuipatsa chakudya misona yake ija,
“Munthu akasiya dzenje lapululu, kapena akakumba dzenje, koma osaphimbira, tsono ng'ombe kapena bulu nkugweramo, ayenera kulipira chifukwa cha choŵetacho. Alipire ndalama kwa mwini choŵetacho, koma nyamayo atenge ikhale yake.
Ndidzaziŵetera ku mabusa abwino, ndipo zizidzadya msipu wonenepetsa ku mapiri okwera a Israele. Kumeneko zidzapumula ku mabusa abwino amsipu. Zidzapezadi mabusa abwino ku mapiri a Israele.
Chauta adatenga dothi naumba nyama zonse ndi mbalame zonse, nabwera nazo kwa Adamu kuti azitche maina. Mwakuti maina amene Adamu adazitcha, maina ake ndi omwewo.
“Ndikadakhala ndi njala sindikadakuuzani, pakuti dziko lonse ndi zonse zam'menemo, ndi zanga.
Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali.
Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”
Ndidzakutaya ku chipululu, iweyo pamodzi ndi nsomba za m'mitsinje yako. Udzagwera ku thengo popanda wina wokutola kuti aike maliro ako. Ndidzakusandutsa chakudya cha zilombo ndi mbalame.’
Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena choononga pa phiri lopatulika la Mulungu. Ndipo anthu a pa dziko lonse lapansi adzakhala odzaza ndi nzeru ya kudziŵa Chauta, monga nyanja imadzazira ndi madzi.
Chikondi chanu chosasinthika ndi chamtengowapatali. Nchifukwa chake anthu anu amathaŵira m'munsi mwa mapiko anu.
amenenso amatiphunzitsa kupambana nyama zam'dziko ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zouluka.’
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Ngakhale timba amapeza malo okhalapo, nayenso namzeze amamanga chisa chake m'mene amagonekamo ana ake, pafupi ndi maguwa anu, Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
Tsono Mulungu adakumbukira Nowa pamodzi ndi nyama zonse zakuthengo ndi zoŵeta zimene zinali naye m'chombomo. Adalamula mphepo kuti iwombe pa dziko lapansi, pomwepo madzi adayamba kutsika.
Mngelo wa Chauta adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako chotere katatu? Ndabwera kudzakutsekera njira, chifukwa ulendo wakowu ukundiipira. Bulu wako anandiwona, ndipo anasiya njira katatu konse atandiwona. Akadapanda kusiya njira atandiwona, ndithu ndikadakuphera pomwepo, koma buluyo ndikadamleka kuti akhale moyo.”
Ndipo udzatengenso nyama za mtundu uliwonse, yaimuna ndi yaikazi, kuti zisungidwe ndi moyo. Ana aamuna a Mulungu adaona kuti ana aakazi a anthu anali okongola, nayamba kukwatira amene ankaŵakonda. Mbalame za mtundu uliwonse ndi nyama zazikulu ndi zokwaŵa zomwe, zidzaloŵe m'chombo kuti zisungidwe ndi moyo.
Bulu wa Mwisraele mnzanu akagona mu mseu, muutseni. Muchitenso chimodzimodzi ndi ng'ombe yake, musailekerere. Mthandizeni mnzanu kuti adzutse choŵetacho.
Mundipatsenso ana oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwayo adzangokhala ndi mai wake masiku asanu ndi aŵiri, ndipo mudzampereka kwa Ine pa tsiku lachisanu ndi chitatu.
Amaphimba zakumwamba ndi mitambo, amapatsa nthaka mvula, amameretsa udzu pa magomo. Amapereka chakudya kwa nyama ndi kwa ana a khungubwi pamene akulira chakudya.
“Auzeni Aisraele kuti nyama zimene angathe kudya pakati pa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi izi: “Zonse za miyendo inai, zouluka, nzonyansa kwa inu. Komabe pakati pa zouluka zonse za miyendo inai, mungathe kudya zokhazo zimene zili ndi miyendo yolumphira pa dothi. Pa zimenezo mungathe kudya izi: dzombe la mitundu yonse, atsokonombwe a mitundu yonse, nkhululu za mitundu yonse, ndi ziwala za mitundu yonse. Koma zamapiko zina zonse zokhala ndi miyendo inai nzonyansa kwa inu. “Tsono zimenezi mukazikhudza, zidzakuipitsani, ndipo aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Aliyense akanyamula chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo, achape zovala zake, komabe akhala woipitsidwa mpaka madzulo. Nyama iliyonse yokhala ndi ziboda zogaŵikana, koma mapazi ake osagaŵikana, kapenanso yosabzikula, njonyansa imeneyo kwa inu, ndipo aliyense woikhudza, adzakhala woipitsidwa. Pakati pa nyama zonse za miyendo inai, nyama zonse zokhala ndi zikhadabo ku mapazi, nzonyansa kwa inu, ndipo aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Ndipo munthu amene anyamula nyamazi zitafa, achape zovala zake, komabe akhala woipitsidwa mpaka madzulo. Zimenezi nzonyansa kwa inu. “Tsono zokwaŵa zonse zimene zili zonyansa kwa inu ndi izi: likongwe, mbeŵa, ng'azi za mitundu yonse, ‘Nyama zonse zokhala ndi ziboda zogaŵikana, ndi zobzikula, angathe kudya zimenezo.
Mukaona ng'ombe kapena nkhosa ya Mwisraele mnzanu ikusokera, musailekerere. Itengeni, mukampatse mwiniwake.
Pali zinthu zinai zing'onozing'ono pa dziko lapansi, koma ndi zochenjera kwambiri: Nyerere zili ngati anthu opanda nyonga, komabe zimakonzeratu chakudya chake m'chilimwe.
Tsono tenga magulu asanu ndi aŵiri a nyama, ziŵiriziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zimene amaperekera nsembe, ndipo utengenso nyama ziŵiriziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zosaperekera nsembe. Tsono adakwererakwerera ndithu mpaka kubzola nsonga za mapiriwo mamita asanu ndi aŵiri. Zamoyo zonse zokhala pa dziko lapansi zidafa, monga mbalame, zoŵeta, nyama zakuthengo, mtindiri wa tizilombo tosiyanasiyana, ndi anthu onse. Zamoyo zonse za pa dziko lapansi zidafa. Chauta adaononga zamoyo zonse za pa dziko: anthu, nyama, zokwaŵa ndi mbalame. Nowa yekha adapulumuka pamodzi ndi onse amene anali naye m'chombomo. Madziwo adakhala osaphwa konse pa dziko lapansi masiku 150. Utengekonso mbalame ziŵiriziŵiri za mtundu uliwonse, magulu asanu ndi aŵiri. Uchite zimenezi pofuna kuti nyama ndi mbalame za mitundu yonse zisungidwe ndi moyo, ndipo kuti zidzaswanenso pa dziko lapansi.
muzidzapereka kwa Chauta chilichonse choyamba kubadwa. Zoŵeta zanu zamphongo zoyamba kubadwa nza Chauta zimenezo.
Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata la Chauta, Mulungu wako. Pa tsiku limenelo, usagwire ntchito iliyonse iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, wantchito wako wamwamuna, mdzakazi wako, ng'ombe yako, bulu wako, kaya choŵeta chako chilichonse, ngakhale mlendo wokhala m'mudzi mwako. Motero atumiki ako aamuna ndi aakazi azipumanso monga iwe wemwe.
ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m'nsalu namgoneka m'chodyera cha zoŵeta, chifukwa adaasoŵa malo m'nyumba ya alendo.
ndimadzifunsa kuti, “Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?” Ndiyetu mudamlenga mochepera pang'ono kwa Mulungu amene, mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu. Mudampatsa ulamuliro pa ntchito za manja anu. Mudamgonjetsera zolengedwa zonse, nkhosa, ng'ombe ndi nyama zakuthengo, mbalame zamumlengalenga, nsomba zam'nyanja, ndi zonse zoyenda pansi pa nyanja.
Tsopano mungathe kudya nyama zonse, monga ndidakulolani kudya ndiwo zamasamba. Ndakupatsani zonsezi kuti zikhale chakudya chanu. Koma pali chinthu chimodzi chokha chimene simuyenera kudya, ndicho nyama imene ikali ndi magazi. Ndaletsa poti magaziwo ndiwo moyo wake.
Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu, amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala.
“Kodi ndiwe amene umapatsa mphamvu kavalo? Nanga ndiwe amene umaveka chenjerere m'khosi mwake? Kodi ungathe kuŵerenga miyezi imene zimakhala ndi bele? Kodi nthaŵi imene nyamazi zimaswa iwe umaidziŵa? Kodi ndiwe amene umamlumphitsa ngati dzombe? Kavalo akamadzuma, mpweya wake ndi waukali ndiponso woopsa. Kavaloyo amalumphalumpha m'chigwa, ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse. Sachita mantha, sachita nkhaŵa, ndipo sabwerera m'mbuyo akaona lupanga. Zida zankhondo za wokwerapo wake zimachita kwichikwichi m'phodo, ndipo mkondo ndi nthungo zimanyezemira pa dzuŵa. Akavalowo amanjenjemera ndi ukali nathamangira kutsogolo, ndipo akangomva lipenga sangathe kuima. Lipenga likalira amati, ‘Twee!’ Amamva fungo la nkhondo ali patali. Amamva kufuula kwa atsogoleri ankhondo.
“Muzitsata malamulo anga. Musalole kuti ng'ombe zanu zikwerane ndi zoŵeta za mtundu wina. Musafese mbeu za mitundu iŵiri m'munda mwanu, ndipo musavale chovala chopangidwa ndi nsalu za mitundu iŵiri.
Pali zinthu zitatu zimene zimayenda chinyachinya. Pali zinthu zinai zimene zimayenda monyadira: Sindidaphunzire nzeru, ndipo Woyera uja sindimdziŵa. Mkango umene uli ndi mphamvu kupambana nyama zonse, ndipo suthaŵa kanthu kalikonse. Tambala woyenda chinyachinya, ndi tonde, ndiponso mfumu yoyenda pakati pa anthu ake.
Kodi ndani angatsimikize kuti mzimu wa munthu ndiwo umakwera kumwamba, koma mpweya wa nyama umatsikira kunsi kwa nthaka?
Ndipo Mulungu adati, “Padziko pakhale mitundu yonse ya zamoyo potsata mitundu yake: zoŵeta, zokwaŵa, ndi nyama zakuthengo, potsata mitundu yake.” Ndipo zidachitikadi.
“Pajatu moyo wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi mwake. Nchifukwa chake ndaŵauza Aisraele kuti, ‘Musadye magazi a cholengedwa chilichonse, pakuti moyo wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi mwakemo. Aliyense wodya magazi adzachotsedwa.
“Koma pali ena amene amangochita zoŵakomera. Kwa iwo nchimodzimodzi kupereka ng'ombe yamphongo ngati nsembe kapena kupha munthu, kupha mwanawankhosa kuti aperekere nsembe kapena kupha galu, kupereka chopereka cha chakudya kapena kupereka magazi a nkhumba, kupereka lubani ku nsembe yachikumbutso kapena kupembedza fano. Anthu ameneŵa mtima wao umakondwera nazo zonyansa zao.
“Koma ufunse kwa nyama zakuthengo, zidzakuphunzitsa. Ufunse mbalame zamumlengalenga, zidzakuuza.
Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka. Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.
Chauta akunena kuti, “Ndikulenga thambo lam'mwamba latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zakale sadzazikumbukiranso, zidzaiŵalika kotheratu.
“Nthiŵatiŵa ikukupiza mapiko ake monyadira, koma nthenga zake ndi mapiko ake sizikuithandiza kuuluka monga amachitira kakoŵa. Nthiŵatiŵa imafotsera mazira ake pansi, kuti afundidwe m'nthaka. Koma imaiŵala kuti mapazi ake omwe angathe kuphwanya mazirawo, ndipo kuti nyama zakuthengo nkuŵapondereza. Nthiŵatiŵa imachita ana ake nkhalwe ngati si ake. Zakuti idaavutika poŵabereka imaiŵalako. Paja Mulungu adaimana nzeru, kotero kuti simvetsa kanthu kalikonse. Komabe nthiŵatiŵayo ikadzambatuka nkuyamba kuthaŵa, imamsiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake.
Mzimu wa Chauta udaŵapumitsa, monga m'mene ng'ombe zimapumulira ku dambo.” Motero Inu Chauta mudatsogolera anthu anu, kuti dzina lanu lilemekezeke.