Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


104 Mau a m'Baibulo Okhudza Kulamulira Mkwiyo

104 Mau a m'Baibulo Okhudza Kulamulira Mkwiyo

Ndikakhala ndi mtendere wa Mulungu mumtima mwanga, palibe malo a maganizo oipa. Ukali uli ndi mphamvu yowononga kulankhulana, kusokoneza ubale, komanso kusokoneza chimwemwe ndi thanzi la anthu ambiri.

N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri anthufe timapeza zifukwa zotsimikizira ukali wathu m’malo motenga udindo. Komabe, tingathe kuugonjetsa ukaliwu motsatira mfundo za m’Baibulo, poona Mulungu pakati pa mayesero, kupemphera nthawi zonse, ndi kudzipereka kwa Iye.

Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tione mayesero osiyanasiyana ngati chifukwa chachikulu cha chimwemwe, podziwa kuti mayesero a chikhulupiriro chathu amabala chipiriro. Ndipo chipirirocho chizigwira ntchito yake yonse mwa ife, kuti tikule bwino m’zonse, osasowa kanthu kalili konse (Yakobo 1:2-4).




Aefeso 4:26-27

Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31

Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:23

Zimene anthu abwino amazilakalaka zimathera mwabwino, koma zimene oipa amayembekezera zimathera ku mkwiyo wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:9

Usamafulumira kukwiya, pakuti mkwiyo umakhalira zitsiru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31-32

Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse. Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:32

Munthu wosapsa mtima msanga amapambana wankhondo, amene amadzigwira mtima amapambana msilikali wogonjetsa mzinda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:8

Lewa kupsa mtima ndi kukwiya. Usachite zimenezi, pakuti sudzapindula nazo kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:19-20

Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso. Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:1

Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo, koma mau ozaza amakolezera ukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 11:10

Choncho muchotseretu zokusautsani mu mtima mwanu, mupewe zokupwetekani m'thupi mwanu. Pajatu unyamata ndi ubwana, zonse nzopandapake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:29

Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:11

Wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:18

Munthu wopsa mtima msanga amautsa mkangano, koma munthu woleza mtima amabweretsa mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:23-24

Uzikana matsutsano opusa ndi opanda nzeru, paja ukudziŵa kuti zotere zimautsa mikangano. Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:11

Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:19

Munthu wa ukali woopsa adzalandira chilango chomuyenerera, pakuti ukamlekerera wotereyu, zidzaipa koposa kale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:3

Nchaulemu kwa munthu kumalewa mikangano, koma aliyense wopusa amakonda kulongolola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:27

Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziŵa zinthu, munthu wodekha mtima ndiye womvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:23

Amene amagwira pakamwa ndi kusamala zokamba zake, sapeza mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:24-25

Usachite naye chibwenzi munthu wopsa mtima msanga, ndipo usamayenda naye munthu waukali, kuwopa kuti ungadzaphunzireko mayendedwe ake, ndi kukodwa mu msampha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:26

Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:28

Munthu wosadzimanga mtima ali ngati mzinda umene adani authyola nkuusiya wopanda malinga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:22

Munthu wamangaŵa amautsa mikangano, munthu wokalipakalipa amabweretsa zolakwa zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:22

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:44

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:14-15

“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:21-22

Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 11:25

Ndipo pamene mukuti mupemphere, muziyamba mwakhululukira mnzanu ngati muli naye nkanthu. Mukatero, Atate anunso amene ali Kumwamba adzakukhululukirani machimo anu.” [

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:27-28

“Koma inu amene mukumva mau anga, ndikukuuzani kuti, Muzikonda adani anu, muziŵachitira zabwino amene amadana nanu. Muziŵafunira madalitso amene amakutembererani, muziŵapempherera amene amakuvutitsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:31

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:17-19

Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:10

Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:4-5

Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 10:3-5

Ndi zoona kuti ndife anthu, koma sitimenya nkhondo motsata za anthu chabe. Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga, ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:32

Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:1-2

Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira. Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye. Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse. Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi. Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera. Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.” Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite. Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:8

Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-13

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:15

Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:15

Onetsetsani kuti wina aliyense mnzake akamchita choipa, asabwezere choipacho. Koma nthaŵi zonse muziyesetsa kuchitira zabwino anzanu ndi anthu ena onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:8

Ndikufuna kuti paliponse amuna popemphera azikweza manja ao kwa Mulungu momchitira ulemu, mopanda mkwiyo kapena kukangana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:24-25

Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto. Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:2

Uŵauze kuti asamakamba zoipa za wina aliyense, apewe kukangana, akhale ofatsa, ndipo nthaŵi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:30

Paja tikumdziŵa kale amene adati, “Kulipsira nkwanga, ndidzakhaulitsa ndine.” Adatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:14

Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:17-18

Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso. Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:1

Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:23

Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sadabwezere chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:9

Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:8

Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:9

Munthu akamati ali m'kuŵala, komabe nkumadana ndi mnzake, akali mu mdima ameneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:11

Munthu wodana ndi mnzake, ali mu mdima, ndipo akuyenda mu mdima. Sadziŵa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa m'maso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:15

Aliyense wodana ndi mnzake, ndi wopha anthu. Ndipo mukudziŵa kuti aliyense wopha anthu, alibe moyo wosatha mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:7-8

Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu. Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:20

Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:16

Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:14

Chiyambi cha mkangano chili ngati kukhamulira madzi, ndiye uzichokapo ndeu isanabuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:12

Chidani chimautsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 4:4

Opani Mulungu, ndipo musachimwe. Mukhale phee ndipo muganize zimenezi mu mtima pamene mukugona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:8-9

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga, ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu. Akatikalipira, mkwiyo wake sudzakhala woyaka mpakampaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 141:3

Muike mlonda pakamwa panga, Inu Chauta. Mulonde pa khomo la milomo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:3-4

Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke. “Tsiku limenelo, amene ali pa denga, asadzatsike kukatenga katundu wake m'nyumba. Chimodzimodzinso amene ali ku munda, asadzabwerere ku nyumba. Kumbukirani za mkazi wa Loti. Aliyense woyesa kudzisungira moyo wake, adzautaya, koma woutaya adzausunga. Kunena zoona, usiku umenewo, padzakhala anthu aŵiri pa bedi limodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Azimai aŵiri adzakhala akusinja pamodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya, Anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.” Apo ophunzira ake adamufunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti, Ambuye?” Yesu adati, “Kumene kwafera chinthu, nkumeneko kumasonkhana miphamba.” Akakuchimwira kasanunkaŵiri pa tsiku, nabwera kasanunkaŵiri kudzanena kuti, ‘Pepani,’ umkhululukire ndithu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:19

Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:18-19

Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho. Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:5

Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:7

Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:15

Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:15

Kupirira ndiye kumagonjetsa wolamula, ndipo kufeŵa m'kamwa kumafatsitsa mtima wouma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:16

Kukwiya kwa munthu wopusa kumadziŵika msanga, koma munthu wanzeru salabadako za chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:18

Wofulumira kulankhula, zonena zake zimalasa ngati mpeni, koma mau a munthu wanzeru amachiza anzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:24

Mau okometsera ali ngati chisa cha uchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:8-9

Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:5-6

Anthu omvera khalidwe loipalo, amaika mtima pa zilakolako zathupi. Koma anthu omvera Mzimu Woyera, amaika mtima pa zimene Mzimu Woyerayo afuna. Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:7

Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:12

Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:5

Motero nonse mukhale ndi mtima womwe uja umene adaali nawonso Khristu Yesu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:1

Pitirizani kukondana monga abale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:13-14

Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa. Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi wodzikonda, musamanyada ndi kutsutsana ndi choona pakunena mabodza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:15

“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:36-37

Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo.” “Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:12

Lamulo langa ndi lakuti muzikondana monga momwe Ine ndakukonderani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:5

Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:14

Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:15

Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:14

Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:11

Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:12

Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:23-24

Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika. Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:9

Abale musamanenerana zoipa pakati panu, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Onani, woweruza waima pa khomo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:11

Alewe zoipa, azichita zabwino. Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuupeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5-6

Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.” Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:18

Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:4

Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:2

Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga wamuyaya, wamphamvu ndi wamkulu, Inu nokha ndinu woyenera ulemerero ndi ulemu wonse! Atate Woyera, ndikubwerera kwa Inu chifukwa ndikudziwa kuti ndikufunika mphamvu yanu yobwezeretsa ndi kumasula. Ndikupempha kuti Mzimu Woyera wanu undipatse mphamvu ndi kudziletsa kuti ndipewe makambirano opanda pake omwe amangondipangitsa kutaya mtima chifukwa cha mkwiyo, zomwe zimapangitsa kuti pakhale mikangano yambiri m'moyo wanga ndi m'banja langa. Ndikudziwa kuti kudzera m'mawu anga ndi zochita zanga zoyipa ndawalasa anthu omwe ali pafupi nane ndipo pamapeto pake chomwe ndimachita ndikumva ndili ndi liwongo ndipo nthawi yomweyo ndikufesa mkwiyo, kupsa mtima ndi ululu. Ndithandizeni kuti ndisagonjedwe ndi maganizo ndi malingaliro anga, chifukwa, ndithudi, mawu anu amati: "Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, kapena kupatsa Mdyerekezi malo." Ambuye, ndipatseni nzeru kuti ndizitsatira mawu anu ndipo kuti kukhalapo kwanu tsiku lililonse kulamulire moyo wanga. Ndikutsutsa mkwiyo, kupsa mtima ndi ukali. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa