Ndikuganiza kuti Yesu anali ndi anzake ambiri, ndipo anatipatsa chitsanzo chabwino cha ubwenzi. Mnzako ndi munthu wofunika kwambiri pa moyo wako. Baibulo limatiuza kuti awiri aposa mmodzi, chifukwa akamagwa mnzake amamuthandiza kudzuka. Ndi dalitso komanso mwayi kukhala ndi mnzake wabwino komanso wowona.
Mnzako ali ngati m'bale wako nthawi ya mavuto. Mnzako amakulangiza, amasangalala ndi zinthu zako zabwino, ndipo amakhala nawe nthawi ya chisoni. Mnzako nthawi zonse amafuna kuti zinthu zikuyendere bwino, ndipo amakutsogolera kwa Mulungu.
Ubwenzi umapezeka pa nthawi zosiyanasiyana pa moyo wathu. Anzake amakhala ngati banja lathu, choncho n'kofunika kudziwa kuti uli ndi mnzake amene ubwenzi wake ndi weniweni. Palibe chikondi choposa kupereka moyo wako chifukwa cha anzanu. (Yohane 15:13)
Ndaima pakhomo pano, ndipo ndikugogoda. Wina akamva mau anga, nkutsekula chitseko, ndiloŵa, ndipo Ine ndi iye tidyera limodzi.
Choncho Chauta ankalankhula ndi Mose pamasompamaso, monga momwe munthu amalankhulira ndi bwenzi lake. Tsono pambuyo pake Mose ankabwerera kumahema komweko. Koma mnyamata wina, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, amene anali mtumiki wa Mose, sankachoka kuchihemako.
Sindikutchulaninso antchito ai, pakuti wantchito sadziŵa zimene mbuye wake akuchita. Koma ndikukutchulani abwenzi, chifukwa zonse zimene ndidamva kwa Atate anga, ndidakudziŵitsani.
Koma iwe Israele mtumiki wanga, iweyo Yakobe amene ndakusankhula, ndiwe mdzukulu wa Abrahamu bwenzi langa.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye.
Motero zidachitikadi zimene Malembo adaanena, kuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, nchifukwa chake Mulungu adamuwona kuti ngwolungama;” mwakuti ankatchedwa bwenzi la Mulungu.
Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.
Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kulankhula zabwino, adzakhala bwenzi la mfumu.
Kodi Inu, Mulungu wathu, suja mudapirikitsa nzika za dziko lino pamene ankafika Aisraele, anthu anu, ndi kulipereka kwa zidzukulu za Abrahamu, bwenzi lanu mpaka muyaya?
Lamulo langa ndi lakuti muzikondana monga momwe Ine ndakukonderani. Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
“Iwe Yobe, uziyanjana ndi Mulungu kuti ukhale pa mtendere, ukatero udzaona zabwino. Uzimvera malangizo amene Iyeyo amaphunzitsa, uziikapo mtima pa mau ake. Ubwerere kwa Mphambe modzichepetsa, uchotse zosalungama zonse zimene zimachitika m'nyumba mwako. Golide wako yense umuyese wachabechabe, ndithu, chuma chamtengowapatali uchiwone ngati dothi, Koma Mphambe ndiye akhale ngati golide wako, akhale ngati siliva wako wamtengowapatali.
Mkwati wamkazi mwini wake ndi mkwati wamwamuna. Koma bwenzi la mkwati wamwamuna limaimirira pafupi, nkumamvetsera. Limakondwa kwakukulu likamva mau a mkwati wamwamunayo. Momwemonso ine ndakondwa kwakukulu.
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Chauta amapalana chibwenzi ndi anthu omvera Iye, ndipo amaŵadziŵitsa chipangano chake.
Pakuti aliyense wochita zimene Atate anga akumwamba akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.”
Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi. Iwo adzaperekedwa kuti akaphedwe ku nkhondo, motero adzasanduka chakudya cha nkhandwe. Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu. Onse olumbirira Iye, adzamtamanda, koma pakamwa pa anthu abodza padzatsekedwa. Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo.
Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera. Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse.
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.
“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni.
Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe.
Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa. Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.
Ndipo Chauta adanena mwa Iye yekha kuti, “Abrahamuyu sindingamubisire chomwe ndikuti ndichite. Zidzukulu zake zidzakhala mtundu waukulu wamphamvu. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa chifukwa cha iye. Ndamsankha iyeyu kuti alamule ana ake ndi mabanja ake akutsogolo kuti azidzamvera mau anga, pochita zabwino ndi zolungama. Choncho ndidzachita zonse zimene ndidamlonjeza.”
Chauta akunena kuti, “Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake, munthu wamphamvu asanyadire mphamvu zake, ndipo munthu wolemera asanyadire chuma chake. Koma ngati wina afuna kunyadira, anyadire ichi chakuti amamvetsa za Ine, ndipo amandidziŵa. Amadziŵa kuti Ine ndine Chauta wokonda chifundo, chilungamo, ndi ungwiro pa dziko lapansi. Ndithudi, pazimenezi ndipo pali mtima wanga.”
Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
“Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.”
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene ndikulamulani. Sindikutchulaninso antchito ai, pakuti wantchito sadziŵa zimene mbuye wake akuchita. Koma ndikukutchulani abwenzi, chifukwa zonse zimene ndidamva kwa Atate anga, ndidakudziŵitsani.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano.
Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho. Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike.
Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu.
Popeza kuti timakhulupirira Iyeyu, tingathe kulimba mtima kuyandikira kwa Mulungu mosakayika konse.
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda. Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa. Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.
Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.
Chimene tidachiwona ndi kuchimva, tikukulalikirani, kuti inunso mukhale a mtima umodzi ndi ife. Kuyanjana kwathu tikuyanjana ndi Atate, ndiponso ndi Mwana wao, Yesu Khristu.
Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu. Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene.