Ngakhale imfa si mdani wathu otsatira Yesu Khristu, imapweteka kwambiri kwa ife omwe tatsala ndi kwa okondedwa athu amene atimwalira. Baibulo limanena za mitundu iwiri ya imfa: imfa ya uchimo ndi imfa ya thupi. Timafa ku uchimo pamene tilandira Ambuye Yesu ngati Mpulumutsi wathu. Imfa ya thupi ndi pamene tichoka m’dziko lino. Imfa ya thupi imabweretsa chisoni chachikulu, koma tili ndi chiyembekezo mwa Mulungu kuti okondedwa athu afika kumwamba ndipo ali bwino. Choncho, musalole chisoni kukulamulirani. Kondwerani chifukwa wokondedwa wanu wapeza chipulumutso.
Mzimu Woyera ndiye Mtonthozi wanu panthawi yachisoni. Lolani kuti athetse ululu wanu ndi kukudzazani ndi mtendere ndi chilimbikitso. Palibe chomwe chingatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, ngakhale imfa, ndipo Mawu ake amatsimikizira izi (Aroma 8:38-39). Ndimasangalala podziwa kuti ngakhale titamwalira, tidzakhala ndi chipambano chifukwa tidzakhala ndi Atate wathu wakumwamba, titamaliza mpikisano wathu.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Njoka inali yochenjera kupambana zamoyo zonse zimene Chauta adazilenga. Njokayo idafunsa mkazi uja kuti, “Kodi nzoona kuti Mulungu adakuletsani kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse m'munda muno?”
Tsiku lina pamene angelo a Mulungu ankabwera kudzadziwonetsa pamaso pa Chauta, nayenso Satana adafika nawo limodzi. Pamenepo Chauta adafunsa Satanayo kuti, “Nanganso iwe Satana, kutereku ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira dzikoli.”
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Zitatha izi, Mzimu Woyera adatsogolera Yesu kupita ku chipululu kuti Satana akamuyese. Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ” Pamenepo Satana adamsiya, angelo nkubwera kumadzamutumikira Yesuyo.
Munthu amene amachimwa, ndi wa Satana, pakuti Satana ndi wochimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu adaoneka ndi cholinga chakuti aononge zochita za Satana.
Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni.
Inu ndinu ana a Satana. Iye ndiye tate wanu, ndipo mukufuna kumachita zimene tate wanuyo amalakalaka. Iye uja chikhalire ngwopha anthu. Sadakhazikike m'zoona, chifukwa mwa iye mulibe zoona. Kunena bodza ndiye khalidwe lake, pakuti ngwabodza, nkukhalanso chimake cha mabodza onse.
Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye. Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.
Ndipo Mulungu amene amapatsa mtendere, posachedwa adzatswanya Satana pansi pa mapazi anu. Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni.
Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.
Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.]
Koma Petro adamufunsa kuti, “Iwe Ananiya, chifukwa chiyani walola mtima wako kugwidwa ndi Satana mpaka kumanamiza Mzimu Woyera pakupatula ndalama zina za munda wako? Mulungu wa makolo athu adaukitsa Yesu kwa akufa, Iye amene inu mudaamupha pakumpachika pa mtanda. Ameneyo Mulungu adamkweza ku dzanja lake lamanja kuti akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi. Adachita zimenezi kuti apatse Aisraele mwai wotembenuka mtima kuti machimo ao akhululukidwe. Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera Iye.” Pamene abwalo aja adamva zimenezi, adakwiya kwambiri nafuna kuŵapha. Koma wina mwa iwo, Mfarisi dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa Malamulo, amene anthu onse ankamlemekeza, adaimirira. Adalamula kuti anthu aja abaapita panja. Tsono adauza abwalowo kuti, “Inu Aisraele, chenjerani ndi zimene mukufuna kuŵachita anthuŵa. Pajatu si kale pamene munthu wina dzina lake Teudasi adaabwera nkuyesa kudzimveketsa, ndipo anthu ngati mazana anai adamtsata. Iye uja adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana natheratu. Pambuyo pake, pa nthaŵi ya kalembera, padabweranso wina dzina lake Yudasi, wa ku Galileya, nakopa anthu ambiri kuti amtsate. Iyenso adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana. Nchifukwa chake pa nkhani imeneyi ndikukuuzani kuti, muŵaleke anthuŵa, ndipo muŵalole azipita. Ngati zimene iwo akuganiza ndiponso zimene akuchitazi nzochokera kwa anthu, zidzakanika zokha. Koma ngati nzochokera kwa Mulungu, inu simungathe kuŵaletsa ai. Mwina mungapezeke kuti mukulimbana ndi Mulungu.” Usanaugulitse, sunali wako kodi? Ndipo utaugulitsa, suja ndalama zake zinali m'manja mwako? Nanga udalola bwanji zoterezi mumtima mwako? Pamenepatu sudanamize anthu, koma wanamiza Mulungu.”
Yesu, ali wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, adabwerako ku mtsinje wa Yordani kuja. Mzimu Woyerayo ankamutsogolera m'chipululu Paja Malembo akuti, “ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni.’ Ndiponso, “ ‘Iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ” Koma Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Usaŵayese Ambuye, Mulungu wako.’ ” Tsono Satana atatha kumuyesa mwa zonsezi, adalekana naye, kudikira nthaŵi ina. Yesu adabwereranso ku Galileya ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mbiri yake idawanda kuzungulira dziko lonselo. Ankaphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, ndipo anthu onse ankamutamanda. Nthaŵi ina Yesu adafika ku Nazarete kumene adaaleredwa. Ndipo pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapemphero, monga adaazoloŵera, naimirira kuti aŵerenge mau. Adampatsa buku la mneneri Yesaya. Tsono Iye adafutukula bukulo, napeza pamene padalembedwa kuti, “Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa, ndi kukalalika za nthaŵi imene Ambuye adzapulumutsa anthu ao.” masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala.
Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Ndikukutuma kuti anthu ameneŵa uŵatsekule maso, kuti atembenuke kuchoka mu mdima wa machimo nkuloŵa m'kuŵala, ndiponso kuchoka m'mphamvu ya Satana nkutsata Mulungu. Ndifuna kuti akhulupirire Ine, kuti machimo ao akhululukidwe, ndipo alandire nao madalitso pamodzi ndi anthu amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale akeake.’
Zimenezitu si zododometsa ai, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu.
Chinjoka chachikulu chija chidagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakale ija yotchedwa “Mdyerekezi” ndiponso “Satana”, wonyenga anthu a pa dziko lonse lapansi. Chidagwetsedwa pa dziko lapansi pamodzi ndi angelo ake onse.
Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu.
Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye pa phiri lalitali kwambiri, ndipo adamuwonetsa maufumu onse a pansi pano ndi ulemerero wake. Tsono adamuuza kuti, “Zonsezi ndidzakupatsani mukagwada pansi ndi kundipembedza.”
Mdani wodzafesa namsongole uja ndi Satana. Kudula kuja nkutha kwake kwa dziko lino lapansi, ndipo odula aja ndi angelo.
Tsono adamuuza kuti, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wonsewu, chifukwa zidapatsidwa kwa ine, ndipo ndimazipatsa aliyense amene ndifuna.
Tsopano ndiyo nthaŵi yoti anthu a dziko lino lapansi aweruzidwe. Tsopano Satana, mfumu ya anthu ochimwa a dziko lino lapansi, adzaponyedwa kunja.
Sindilankhula nanunso zambiri tsopano ai, pakuti Satana, mfumu ya anthu ochimwa a dziko lapansi, alikudza. Iyeyo alibe mphamvu pa Ine,
Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe adasanduka munthu wonga iwowo. Adachita zimenezi kuti ndi imfa yake aononge Satana amene anali ndi mphamvu yodzetsa imfa.
Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana.
Motero mwa Khristu Mulungu adaŵalanda zida maufumu ndi maulamuliro onse, ndipo pamaso pa onse, adaŵayendetsa ngati akaidi pa mdipiti wokondwerera kupambana kwake.
“Simoni, Simoni, chenjera! Mulungu walola Satana kuti akupeteni nonse ngati tirigu. Koma Ine ndakupempherera, kuti usaleke kundikhulupirira. Ndipo iweyo utatembenuka mtima, ukaŵalimbitse abale akoŵa.”
Akuti: Ndikudziŵako kumene inuyo mumakhala, ndiye kuti kumene kuli mpando wachifumu wa Satana. Inu ndinu okhulupirika kwa Ine, simudataye chikhulupiriro chanu, ngakhale pa nthaŵi ya Antipa, mboni yanga, munthu wanga wokhulupirika. Paja iye uja adamuphera kwanu komwe, kumene amakhala Satana.
Koma Yesu adacheuka namdzudzula. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Ufuna kundilakwitsa. Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.”
Choncho kondwerani inu, Dziko la Kumwamba, ndi onse okhalamo. Koma muli ndi tsoka, inu dziko lapansi ndi nyanja, pakuti Satana adatsikira kwa inu, ali wokalipa kwambiri, chifukwa wadziŵa kuti yangomutsalira nthaŵi pang'ono.”
Yesuyo adakhala kumeneko masiku makumi anai, Satana akumuyesa. Komweko kunalinso nyama zakuthengo, ndipo angelo ankamutumikira.
Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya.
Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita.
Asakhale munthu wolandiridwa mu mpingo chatsopano, kuwopa kuti angadzitukumule nkulangidwa monga momwe Satana adalangidwira.
Tikudziŵa kuti ndife ake a Mulungu, ndipo kuti onse odalira zapansipano ali m'manja mwa Woipa uja.
Musachite nazo mantha zoŵaŵa zimene mukukakumana nazo. Ndithu enanu Satana adzakuponyetsani m'ndende kuti akuyeseni, ndipo mudzazunzika pa masiku khumi. Khalani okhulupirika mpaka kufa, ndipo ndidzakupatsani moyo ngati mphotho yanu.
Chauta adauza Satana kuti, “Chabwino, zonse zimene Yobe ali nazo ndaziika m'manja mwako. Koma iye yekhayo usamkhudze.” Pamenepo Satanayo adachoka, kumsiya Chauta.
Tsono m'masomphenya Chauta adandiwonetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, ataima pamaso pa mngelo wake, ku dzanja lake lamanja kutaima Satana woti amuimbe mlandu. Tsiku limenelo, nonsenu mudzaitanizana kuti mukakondwerere ufulu wanu, aliyense atakhala pa mtengo wake wa mphesa ndi wa mkuyu,’ akutero Chauta Wamphamvuzonse.” Mngelo wa Chauta uja adauza Satanayo kuti, “Chauta akudzudzule, iwe Satana! Chauta amene adasankhula Yerusalemu akudzudzule ndithu iwe! Kodi uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?”
“Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba, iwe Nthanda, mwana wa Mbandakucha? Wagwetsedwa pansi bwanji, iwe amene unkagonjetsa mitundu ya anthu? Mumtima mwako unkati, ‘Ndidzakwera mpaka kumwamba. Ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu. Ndidzakhala pampandopo pa phiri la kumpoto kumene imasonkhanako milungu yonse. Ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanafana naye Wopambanazonse.’ Koma watsitsidwa m'manda, pansi penipeni pa dzenje.
“Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo ya maliro, kulira mfumu ya ku Tiro. Uiwuze mau angaŵa akuti, Udaali chitsanzo cha ungwiro weniweni. Udaali wanzeru ndiponso wokongola kwabasi. Unkakhala ngati ku Edeni, ku munda wa Mulungu, ndipo unkadzikongoletsa ndi miyala yamtengowapatali ya mitundu yonse: karineliyoni, topazi, jasipere, kirisoliti, berili, onikisi, safiro, rubi ndi emeradi. Zoikamo miyalayo zinali zagolide. Adakupangira zonsezi pa tsiku limene udalengedwa. Ndidakuikira mngelo woopsa kuti azikulonda. Unkakhala pa phiri langa lopatulika, ndipo unkayenda pakati pa miyala yamoto. Makhalidwe ako anali angwiro kuyambira tsiku limene udalengedwa mpaka nthaŵi imene udayamba kuchita zoipa. Potanganidwa ndi zamalonda, udaachulukitsa zandeu ndi kumangochimwa. Nchifukwa chake ndidakuchotsa ku phiri langa lopatulika. Mngelo amene ankakulonda adakupirikitsa kuchokera ku miyala yamotoyo. Unkanyada chifukwa cha kukongola kwako, udaipitsa nzeru zako chifukwa chofuna kukhala wotchuka. Motero ndidakugwetsa pansi kuti ukhale chenjezo kwa mafumu ena.
koma m'kati mwanga ndimaona lamulo lina lolimbana ndi lamulo limene mtima wanga wavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa kapolo wa lamulo la uchimo lokhala m'kati mwanga.
Adachipembedza chinjoka chija chifukwa chidaapatsa ulamuliro wake kwa chilombo chija. Nachonso chilombo chija adachipembedza nkumanena kuti, “Ndani angafanane ndi chilombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”
“Pambuyo pake Mfumuyo idzauzanso a ku dzanja lake lamanzere aja kuti, ‘Chokani apa, inu otembereredwa. Pitani ku moto wosatha, umene Mulungu adakonzera Satana ndi angelo ake.
Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma Satana amabwera, nkuchotsa mau aja m'mitima mwao, kuwopa kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.
Koma Afarisi atamva zimenezi adati, “Iyai, mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa sizichokeratu kwina, koma kwa Belezebulu, mkulu wa mizimu yoipayo.” Yesu adaadziŵa zimenezi, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo anthu a m'mudzi uliwonse kapena a m'banja lililonse akayamba kuukirana, mudzi wotere kapena banja lotere silingalimbe ai. Ngati a mu ufumu wa Satana atulutsana okhaokha, ndiye kuti agaŵikana. Nanga Satanayo ufumu wake ungalimbe bwanji?
Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma nthaŵi yomweyo Satana amabwera, nkuchotsa mau aja amene adafesedwa m'mitima mwao.
Pamenepo nzeru zao zidzabweramo, ndipo adzapulumuka mu msampha wa Satana, amene adaaŵagwira kuti azichita zofuna zake.
Ukadachita zabwino, ndikadakondwera nawe. Koma chifukwa choti wachita zoipa, tchimo lakukhalirira pa khomo ngati chilombo cholusa. Likulakalaka kuti likugwire, koma iweyo uligonjetse tchimolo.”
Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana. Simungathe kumwera m'chikho cha Ambuye nkumweranso m'chikho cha Satana. Simungathe kudyera pa tebulo la Ambuye nkudyeranso pa tebulo la Satana.
Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo. Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola. Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.
Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Tsono ngati a mu ufumu wa Satana ayamba kuukirana, Satanayo ufumu wake ungalimbe bwanji? Paja inu mukuti Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu.
Alipo ena a mpingo wa Satana, amene sali Ayuda, koma amanama kuti ndi Ayuda. Iwoŵa ndidzaŵabweretsa kwa inu kuti adzadzigwetse kumapazi kwanu. Pamenepo adzadziŵa kuti ndimakukondani.
Mbiri yake idabuka m'dziko lonse la Siriya, kotero kuti anthu ankabwera kwa Iye ndi odwala onse ovutika ndi nthenda ndi zoŵaŵa zosiyanasiyana, ogwidwa ndi mizimu yoipa, akhunyu ndi opunduka, Iye nkumaŵachiritsa.
Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka.
Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu oipa. Tchinjirizeni kwa anthu ankhanza. Makala amoto aŵagwere, aponyedwe m'maenje ozama, asatulukemonso. Musalole kuti woononga mbiri ya mnzake akhazikike m'dziko. Choipa chimlondole munthu wankhanza mpaka kumuwononga. Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa. Zoonadi, anthu ochita zabwino adzatamanda dzina lanu. Anthu amenewo adzakhala pamaso panu. Iwo amalingalira mumtima mwao kuti achite zoipa, amautsa nkhondo nthaŵi zonse. Amanola lilime lao kuti likhale ngati la njoka, m'kamwa mwao muli ululu wa mamba. Inu Chauta, tetezeni kwa anthu oipa, tchinjirizeni kwa anthu andeu, amene amaganiza zofuna kundigwetsa. Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika, atchera ukonde wa zingwe, anditchera misampha m'mbali mwa njira.
Musalole kuti mtima wanga upendekere ku zoipa, ndisadzipereke ku ntchito zoipa pamodzi ndi anthu ochita zoipa, ndisadye nawo maphwando ao.
“Palibe munthu amene angathe kuloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkufunkha chuma chake, atapanda kuyamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Atatero ndiye angafunkhe zam'nyumbamo.
Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.
munthuyo mumpereke kwa Satana, kuti thupi lake liwonongedwe, ndipo pakutero mzimu wake udzapulumutsidwe pa tsiku la Ambuye.
Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha.
Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.
“Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mudzamanga pansi pano, chidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo chilichonse chimene mudzamasula pansi pano, chidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.
Bwanji anthu akunja akufuna kuchita chiwembu? Chifukwa chiyani anthu ameneŵa akulingalira zopandapake? Nchifukwa chake tsono khalani anzeru, inu mafumu. Chenjerani inu amene muli olamula dziko lapansi. Tumikirani Chauta mwamantha ndi monjenjemera. Mumgonjere molapa, kuwopa kuti angakukwiyireni, ndipo inu mungaonongeke, chifukwa ukali wake umayaka msanga. Ngodala onse amene amathaŵira kwa Iye. Mafumu ao akuchita upo, olamula ao akhala pamodzi kuti apangane zoipa, zoukira Chauta ndi mfumu yake yodzozedwa. Akuti, “Tiyeni timasule maunyolo aoŵa, tichokeretu mu ulamuliro wao.”
Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho.
Inu Mulungu, musakhalenso chete. Musangoti phee, musangoti duu, Inu Mulungu. amene adaŵaononga ku Endori, ndi kuŵasandutsa ndoŵe m'nthaka. Akalonga ao muŵachite zomwe mudachita Orebu ndi Zeebu, ndipo ana a mafumu ao onse, muŵachite zomwe mudachita Zeba ndi Zalimuna, amene adati, “Tiyeni tilande dziko la Mulungu likhale lathu.” Inu Mulungu wanga, muŵasandutse ngati fumbi louluka ndi kamvulumvulu, akhale ngati mankhusu ouluka ndi mphepo. Monga momwe moto umatenthera nkhalango, monga momwe malaŵi amayakira pa mapiri, momwemonso Inu muŵapirikitse ndi mkuntho, ndipo muŵaopseze ndi kamvulumvulu wanu. Inu Chauta, muŵachititse manyazi, kuti azifunafuna dzina lanu. Achitedi manyazi ndi mantha mpaka muyaya, ndipo afe imfa yonyozeka. Adziŵe kuti Inu nokha, amene dzina lanu ndinu Chauta, ndinu Wopambanazonse wolamulira dziko lonse lapansi. Onani, adani anu akuchita chiwawa. Amene adana nanu akukuukirani. Akuchitira anthu anu upo wonyenga. Akuŵapangira zoipa anthu anu amene mumaŵateteza.
Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.
Pakuti Mulungu sadaŵalekerere angelo amene adachimwa aja, koma adaŵaponya m'ng'anjo yamoto, m'maenje amdima momwe ali omangidwa kudikira chiweruzo.
Mukumbukire angelo amene sadakhutire ndi ulamuliro wao, koma adasiya malo amene Mulungu adaaŵapatsa. Mulungu adaŵamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuŵasunga m'malo amdima mpaka tsiku lalikulu lija pamene adzaŵaweruza.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani? Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere? Ndani angaŵaimbe mlandu anthu amene Mulungu adaŵasankha? Mulungu mwiniwake amaŵaona kuti ngolungama pamaso pake. Tsono palibe amene angaŵaweruze kuti ngopalamula. Khristu Yesu amene adafa, kaya tinene kuti amene adauka kwa akufa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndiye amene akutinenera kwa Mulunguyo. Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.” Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda. Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.
Inu mumakhulupirira kuti Mulungu ndi mmodzi yekha. Ai chabwino, mumakhoza, komatu ndi mizimu yoipa yomwe imakhulupirira zimenezi, imachitanso kunjenjemera.
pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.
Chenjerani kuti wina aliyense angakusokonezeni ndi mau olongosola nzeru zapatali. Ameneŵa ndi mau onyenga chabe. Paja nzeru zimenezi zimangochokera ku miyambo ya anthu, ndi ku maganizo ao okhudza zapansipano, osati kwa Khristu ai.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Mose atakula adakana kutchedwa mdzukulu wa Farao, mfumu ya ku Ejipito. Iye adasankha kuzunzikira nawo limodzi ana a Mulungu, koposa kukondwerera zosangalatsa za uchimo kanthaŵi pang'ono.
Inu Mulungu, pulumutseni, pakuti madzi ayesa m'khosi. Pamene ndidadzilanga posala zakudya, anthu adandinyoza. Pamene ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni, ndidasanduka chinthu choŵaseketsa. Anthu okhala pa chipata amandinena, ndipo zidakwa zimandiimba nyimbo. Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta. Mundiyankhe pa nthaŵi yabwino, Inu Mulungu, chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, ndi chithandizo chanu chokhulupirika. Pulumutseni kuti ndisamire m'matope, landitseni kwa adani anga ndi ku madzi ozama. Musalole kuti chigumula chindikokolole, kapena kuti nyanja yakuya indimize. Musalole kuti manda atseke kukamwa atandimeza. Mundiyankhe, Inu Chauta, pakuti chikondi chanu chosasinthika nchabwino. Munditchere khutu chifukwa cha chifundo chanu chachikulu. Musandibisire ine mtumiki wanu nkhope yanu, fulumirani kundithandiza, pakuti ndili pa zovuta. Senderani pafupi, mundiwombole, mundipulumutse kwa adani anga. Inu mumadziŵa m'mene anthu amandinyozera, m'mene amandichititsira manyazi ndi kundichotsera ulemu. Adani anga onse mumaŵadziŵa. Ndamira m'thope lozama m'mene mulibe popondapo polimba. Ndaloŵa m'madzi ozama, ndipo mafunde andimiza.
Adagwira Chinjoka chija, ndiye kuti njoka yakale ija yotchedwa Mdyerekezi ndiponso Satana, nachimanga zaka chikwi chimodzi. Kenaka adachiponya m'Chiphompho muja, nachitsekera nkumatirira potsekerapo kuti chisadzanyengenso mitundu ya anthu mpaka zitatha zaka zija chikwi chimodzi. Zitatha zakazo ayenera kudzachimasulanso nthaŵi pang'ono.
Kalanga ine! Ndani adzandipulumutsa ku khalidwe langa lino londidzetsera imfa? Tiyamike Mulungu! Adzandipulumutsa ndiye kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Motero ineyo, ndi mtima wanga ndimatumikira Malamulo a Mulungu, chonsecho ndi khalidwe langa lokonda zoipa, ndimatumikira lamulo la uchimo.
Agalatiya opusa inu, adakulodzani ndani? Pamene tidakulalikirani Yesu Khristu, tidamuwonetsa poyera pamaso panu ngati wopachikidwa pa mtanda.
m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe.
“Choncho inu musamaopa anthu. Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululuka, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika. Zimene ndikukuuzirani m'chibisibisi, inu mukazilankhulire poyera, ndipo zimene mukuzimvera m'manong'onong'o, inu mukazilalikire pa madenga.
Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.
“Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ndi womwaza.
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
Inu atate, ndikukulemberani, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Inu achinyamata, ndikukulemberani, chifukwa mwampambana Woipa uja. Ndimakulemberani inu ana, chifukwa Atate mumaŵadziŵa. Ndimakulemberani inu atate, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Ndimakulemberani inu achinyamata, chifukwa ndinu amphamvu, mau a Mulungu amakhala mwa inu, ndipo mwampambana Woipa uja.
Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe adasanduka munthu wonga iwowo. Adachita zimenezi kuti ndi imfa yake aononge Satana amene anali ndi mphamvu yodzetsa imfa. Pakutero adafunanso kuti aŵamasule amene pa moyo wao wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa.
masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala.
Tsono Woyesa uja adadza namuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani miyala ili apayi kuti isanduke chakudya.”
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Kodi ndinenenso chiyani tsopano? Nthaŵi yachepa yoti ndinene za anthu enanso ambiri monga Gideoni, Balaki, Samisoni, Yefita, Davide, Samuele ndiponso aneneri. Pokhala ndi chikhulupiriro anthu ameneŵa adagonjetsa maufumu, adakhazikitsa chilungamo, ndipo adalandira zimene Mulungu adaaŵalonjeza. Ena adapuya mikango pakamwa, ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao.
Anthu ondineneza achite manyazi ndipo aonongeke. Anthu ofunafuna kundipweteka anyozedwe, ndipo achite manyazi kotheratu.
Tikudziŵa kuti aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamsunga, ndipo Woipa uja sangamkhudze.
Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni.
Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.