Tsiku lobadwa ndi nthawi yopatulika yothokoza Mulungu chifukwa cha moyo wina wowonjezera. Ndi nthawi yosangalala ndi madalitso Ake ndi mphatso ya chaka china. Mulungu wakulonjeza zinthu zambiri zabwino, ndipo tsiku labwino lino ndi nthawi yabwino yokumbukira malonjezo amenewa. Kugawana Mawu a Mulungu ndi okondedwa ako kungakupatseni chimwemwe chowonjezera pa nthawi yosangalatsayi.
Pa tsiku lako lobadwila, ndikufunira thanzi labwino tsiku lililonse, ndipo moyo wako utsogoleredwe ndi nzeru za Mulungu. Mulungu atumize angelo Ake kuti akuzungireni ndi kukutetezerani. Akwaniritse zokhumba za mtima wako mogwirizana ndi chifuniro Chake changwiro. Pakuti “ndi Ine masiku ako adzachuluka, ndi zaka zako za moyo zidzawonjezeka.” (Miyambo 9:11)
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.
“Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziŵa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo ndidzaonjezera zaka pa moyo wako.
Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”
Pakutha pa chaka mumapereka zokolola zambiri mwa ubwino wanu, kulikonse kumene Inu mupita, kumapezeka dzinthu dzambiri.
Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.
Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka.
Akupatse zimene mtima wako ukukhumba, akuthandize kuti zonse zimene wakonza zichitikedi.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe. Monga pa masiku achikondwerero, ndidzakuchotsera tsoka, limene lingokuvutitsa ndi kukunyozetsa.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha. M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.
Koma Inu mwandisangalatsa mtima kwambiri, kupambana anthu a zakudya ndi zakumwa zambiri!
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
“Ndakuuzani zimenezi kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Inu Chauta, mwandisangalatsa ndi ntchito zanu. Motero ndikufuula ndi chimwemwe chifukwa cha zimene Inu mwachita.
Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.
Motero, uzikonda Chauta, Mulungu wakoyo, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse.’
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo, Tsono inuyo ndi zidzukulu zanu mudzabwerera kwa Chauta, ndipo mau ake amene ndikukupatsani leroŵa mudzaŵamvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chimafika mpaka kumwamba, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Ndidzaimbira Chauta moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Chauta, nthaŵi zonse pamene ndili moyo. Mapemphero anga amkomere Chauta, popeza kuti ndimakondwa mwa Iye.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu wonse ukhale wolunzana naye. Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Muzikondwa mwa Ambuye nthaŵi zonse. Ndikubwerezanso kuti, “Muzikondwa.” Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi. Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Munthu wozunzika masiku ake onse amakhala oipa, koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthaŵi zonse.