Mulungu akuitana ana ake kukhala oyera. Kukhala oyera ndiko kukhala opulidwa, odzipereka kwa Mulungu. Kuti tikhalebe oyera tiyenera kupewa chilichonse chomwe Mulungu sachikonda, ndipo Mawu ake ndiye chitsogozo chathu chabwino kwambiri choti tidziwe zimenezo. Werengani Mawu ake tsiku lililonse ndipo mudzamudziwa bwino Mulungu. Mukatero, mudzadziwa chabwino ndi choipa, chomwe chimakufikitsani pafupi ndi Ambuye komanso chomwe chimakutalikirani.
(Masalimo 119:9) Mnyamata adzayeretse bwanji njira yake? Ndi kusunga mawu anu. Yesu Khristu anapereka moyo wake chifukwa cha ife kuti atiyeretse ndi kutikhala oyera. Ngati mumakondadi Atate wanu wakumwamba, mudzapewa chilichonse chomwe chimakutalikirani kwa Iye. Mudzakhala osamala tsiku lililonse ndipo mudzafune kukhala oyera pa chilichonse chomwe muchita.
Tsiku lililonse muyenera kufunafuna kuyera kumene Mulungu akuitanani kuti mukaone Iye. Mawu ake amati: Fufuzani mtendere ndi onse, ndi chiyero; popanda icho palibe munthu adzaona Ambuye. (Ahebri 12:14) Atate wanu wakumwamba akuyuna kuti mukaonekere pamaso pake muli oyera, kuti muchotse chilichonse chomwe chimadetsa thupi lanu ndi mzimu wanu. Mu gawo lino mupeza mavesi ambiri okhudza kuyera ndi kufunika kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
Kulungama kwa anthu angwiro kumaŵathandiza pa moyo wao, koma kuipa mtima kumagwetsa mwiniwake yemweyo.
Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”
Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu? Ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera? Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa.
Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Angathe kutero ndi amene amachita zolungama ndi kulankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga, amene amakutumula manja ake kuti angagwire chiphuphu, amene amatseka makutu kuti angamve mau opangana za kupha anzao, amene amatsinzina kuti angaone zoipa. Munthu wotere adzakhala pa malo otetezedwa. Kothaŵirako iye kudzakhala ku malinga am'matanthwe. Chakudya azidzalandira, ndipo madzi sadzamsoŵa.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Mudzidzimuke mumtima mwanu, ndipo muleke kuchimwa. Ena mwa inu sadziŵa Mulungu konse. Ndikukuuzani zimenezi kuti muchite manyazi.
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe, makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi, uŵalembe mumtima mwako. Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse. Usachite naye nsanje munthu wachiwawa, usatsanzireko khalidwe lake lililonse. Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa, koma olungama okha amayanjana nawo. Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa. Anthu onyoza, Iye amaŵanyoza, koma odzichepetsa Iye amaŵakomera mtima. Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi. Choncho udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi pa anthunso.
Ngati mukudziŵa kuti Khristu ndi wolungama, musapeneke konse kuti aliyense wochita chilungamo, ndi mwana wa Mulungu.
Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.
“Mverani, inu amene mukudziŵa chilungamo, inu amene mukusunga malamulo anga mumtima mwanu. Musachite mantha anthu akamakudzudzulani, musataye mtima akamakulalatirani.
Paja Chauta ndi wolungama, amakonda ntchito zolungama, ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.
Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai,
Kukhulupirika kwanga ndi kulungama kwanga kunditeteze, popeza kuti ndakukhulupirirani.
Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.
Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira. Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye. Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse. Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi. Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera. Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.” Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite. Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,
Tsono leka zoipa, ndipo chita zabwino, motero udzakhala pa mtendere mpaka muyaya. Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu.
Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Ngakhale nthaŵi ya mdima, munthu wochita chilungamo ayenda m'kuŵala, chifukwa ngwokoma mtima, wachifundo ndi woongoka.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Ana anga, wina aliyense asakusokeretseni. Munthu amene amachita chilungamo, ngwolungama monga Khristu ali wolungama.
Ndimakonda kuchita zimene mumafuna, Inu Mulungu wanga, malamulo anu ali mumtima mwanga.”
kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,
Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.
Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.
Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni, ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro. Ndiye mlonda wa njira zolungama, amatchinjiriza njira ya anthu ake oyera mtima.
“Chenjerani, musachite ntchito zanu zabwino pamaso pa anthu ndi cholinga choti akuwoneni. Mukatero, simudzalandira mphotho kwa Atate anu amene ali Kumwamba.
Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira. Adzaonetsa poyera kusalakwa kwako, ndipo kulungama kwako kudzaŵala ngati usana.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu.
Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta.
Koma ngakhale mumve zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima,
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.
Mulungu ndiye adakulunzanitsani ndi Khristu Yesu, ndipo adamsandutsa kuti akhale nzeru yathu. Chifukwa cha Yesu, timapezeka olungama pamaso pa Mulungu. Ndi Yesuyo amene amatisandutsa anthu akeake a Mulungu, ndiye amatipulumutsa.
Inu Chauta, ndinu olungama, munditsogolere pakati pa adani ondizonda. Mundikonzere njira yoongoka kuti ndidzeremo.
Munthu abwino amakhala mwachilungamo, ndipo Mulungu amadalitsa ana amene amatsata njira yake.
Koma tsopano mwamasulidwa ku uchimo, ndipo ndinu otumikira Mulungu. Phindu lake ndi kuyera mtima, ndipo potsiriza pake kulandira moyo wosatha.
Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima?
Munthu sakhazikika bwino pochita uchimo, koma maziko a munthu wochita zabwino sadzagwedezeka.
Mulungu adachita zimenezi, kuti chilungamo chimene Malamulo a Mose amatipempha, chiwoneke kwathunthu mwa ife amene sitimveranso khalidwe lathu lopendekera ku zoipa, koma timamvera Mzimu Woyera.
Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Inunso kale mudaali mu mdima, koma tsopano muli m'kuŵala, popeza kuti ndinu ao a Ambuye. Tsono muziyenda ngati anthu okhala m'kuŵala. Pajatu pamene pali kuŵala, pamapezekanso ubwino wonse, chilungamo chonse ndi choona chonse.
Wolungama wanga adzakhala ndi moyo pakukhulupirira. Koma akamachita mantha nkubwerera m'mbuyo, Ine sindikondwera naye.”
Koma Chauta Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chilungamo chake, Mulungu Woyera adzaonetsa kuyera kwake pochita zaungwiro.
Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya. Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka.
Koma anthu okhulupirika am'dziko, ndidzaŵayang'ana moŵakomera mtima, ndipo adzakhala ndi ine. Oyenda m'njira yopanda cholakwa adzanditumikira.
Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama.
Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu, koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.
Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.
“Mukatero, mudzaŵala ngati mbandakucha, ndipo mabala anu adzapola msanga. Ine, kulungama kwanu, ndidzakutsogolerani, ndipo ulemerero wanga udzakutchinjirizani kumbuyo kwanu.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.
Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.
Chauta adandipatsa mphotho molingana ndi ntchito zanga zabwino, adandifupa molingana ndi ungwiro wanga.
Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.
Nchifukwa chake monga Atate anu akumwamba ali abwino kotheratu, inunso mukhale abwino kotheratu.
Udzakhazikika m'chilungamo chenicheni. Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa palibe choopa, sudzakhalanso ndi mantha, chifukwa manthawo sadzakufikira.
Munthu wosauka amene amayenda mwaungwiro amaposa kwambiri munthu wolemera amene ali wonyenga.
Ndi amene sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja, amene salandira chiphuphu kuti azunze munthu wosalakwa. Munthu wochita zimenezi, palibe chilichonse chimene chidzamgwedeze.
Tsono muzipereka kwa onse zimene zikukhalira iwowo: msonkho kwa okhometsa msonkho, zolipira kwa oyenera kuŵalipira. Muzilemekeza oyenera kuŵalemekeza, ndi kuchitira ulemu oyenera kuŵachitira ulemu.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Ndipo moyo wanu udzakhala wodzaza ndi zipatso za chilungamo zimene mudzaonetsa mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti anthu onse alemekeze ndi kutamanda Mulungu.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Kusiyana kwake pakati pa ana a Mulungu ndi ana a Satana kumaoneka motere: aliyense wosachita chilungamo, ndiponso wosakonda mnzake, sali mwana wa Mulungu.
Nsembe ya anthu oipa mtima imamuipira Chauta, koma pemphero la anthu olungama limamkondweretsa.
Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.
Sambani, dziyeretseni, chotsani pamaso panga ntchito zanu zoipa. Inde, lekani kuchita zoipa. Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”
Anthu athunso aziphunzira kudzipereka pa ntchito zabwino, kuti azithandiza pamene pali kusoŵa kwenikweni. Azitero kuti moyo wao usakhale wopanda phindu.
Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni. Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu.
Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu.
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Ndipotu Mwana wa Munthu adzabwera ndi angelo ake ali ndi ulemerero wa Atate ake. Pamenepo adzabwezera aliyense molingana ndi zochita zake.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Njira ya munthu woipa ndi yokhotakhota, koma khalidwe la munthu wosachimwa ndi lolungama.
Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’
Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.
Iye adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Anthu amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pakuchita ntchito zabwino molimbikira, Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha.
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.
Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.
Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.”
“Mufunefune Chauta pamene angathe kupezeka, mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi. Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”
Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa.
Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera. Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
Munthu akamati amakhala mwa Mulungu, zochita zake zizilingana ndi zimene Yesu ankachita.
Munthu woyenda mwaungwiro, amayenda mosatekeseka. Koma woyenda njira zoipa, adzadziŵika.
Ndi amene amachita zabwino ndi manja ake, ndipo amaganiza zabwino mumtima mwake. Ndi amene salingalira zonama, ndipo salumbira monyenga. Adzalandira madalitso kwa Chauta, ndipo Mulungu Mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
Tsekulireni zipata za Nyumba ya Mulungu, kuti ndifike ku malo ake achilungamo, ndikathokoze Chauta. Aisraele anene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.” Ichi ndicho chipata cha Chauta, anthu okhawo ochita chifuniro chake adzaloŵera pamenepa.
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.
Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira.
Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.
Khulupirira Chauta, ndipo usunge njira zake. Motero adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako. Udzaona anthu oipa akuwonongeka.