Moyoyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, Iye ndiye amene amatipatsa chifukwa chokhalira ndi moyo. Ngakhale mdani amayesa kutiletsa, Mlengi wathu nthawi zonse amafunira zabwino kwa ife. Kuyambira pachiyambi, cholinga chake chinali chakuti anthu achuluke padziko lapansi. Choncho, ndikofunikira kumvetsa kuti chilichonse chimene chimabweretsa imfa sichinali m’dongosolo la Mulungu. Kuchotsa mimba sichinali m’dongosolo lake la dziko lino.
Ziribe kanthu kuti wakumana ndi zotani mpaka kufika pano, ndikofunikira kudziwa kuti thandizo la Mulungu lili pafupi. Kaya wakumana ndi mimba yosakonzekera kapena yochokera muzochitika zopetsa mtima, moyo umene uli m’kati mwako uyenera kupatsidwa mwayi wokula. Kuchotsa mimba si yankho ndipo kungakubweretsere mavuto a m’maganizo amene angasokoneze moyo wako.
Khulupirira kuti Mulungu angakuchiritse ndi kukumasula, kukupatsa tsogolo lodzala ndi chiyembekezo kwa iwe ndi mwana wako. Yandikirani kwa Iye, muuzeni mavuto anu ndipo mupemphe chikhululukiro. Taya maganizo aliwonse okukutsogolera ku kuchotsa mimba ndipo ulape ndi mtima wonse. Mulungu ali ndi dongosolo labwino kwa iwe. Ngakhale utamva kuti uli wekha, kumbukira kuti Mzimu Woyera ali nawe, akukutsimikizira ndi kukulimbitsa panthawi yovutayi.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi.
Chauta, Mpulumutsi wako, amene adakupanga m'mimba mwa mai wako, akunena kuti, “Ndine Chauta, amene ndidapanga zinthu zonse. Pamene ndinkayalika zakuthambo, ndinali ndekha. Pamene ndinkalenga dziko lapansi, kodi analipo amene adandithandiza?
Ndakhala ndikudalira Inu chibadwire changa, Inu mwakhala Mulungu wanga kuyambira pamene mai wanga adandibala. Musandikhalire kutali, pakuti mavuto ali pafupi kundigwera, ndipo palibe wina wondithandiza.
Pamene Elizabeti adamva malonje a Maria, mwana adayamba kutakataka m'mimba mwake. Elizabeti adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adalankhula mokweza mau kuti, “Ndinu odala kupambana akazi ena onse, ngwodalanso Mwana wanu. Ine ndine yani kuti inu, mai wa Ambuye anga, mudzandiyendere? Chifukwatu pamene ndinamva malonje anu, mwana anayamba kutakataka ndi chimwemwe m'mimba mwanga.
Mverani inu anthu a ku maiko a m'mphepete mwa nyanja, tcherani khutu, inu anthu akutali. Chauta adandiitana ndisanabadwe, adanditchula dzina ndidakali m'mimba mwa amai anga.
“Anthu aamuna akamayambana, ndipo nkupweteka mai wapathupi, maiyo napititsa padera, koma osafa, amene adampwetekayo adzalipira mtengo uliwonse umene mwamuna wa maiyo angadzatchule. Ndipo adzalipira monga momwe anthu oweruza anganenere. Koma maiyo akampweteka, chilango chake chidzakhala chotere: moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, kutentha ndi moto kulipa kutentha ndi moto, bala kulipa bala, ndipo mkwingwirima kulipa mkwingwirima.
Tsono Chauta adatenga dothi pa nthaka, ndipo adaumba munthu ndi dothilo. Adamuuzira mpweya wopatsa moyo m'mphuno zake, ndipo munthuyo adakhala wamoyo.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo,
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa,
Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
“Mundimvere, inu zidzukulu za Yakobe, inu nonse otsala a m'nyumba ya Israele. Ndakhala ndikukusamalani chibadwire chanu, ndidakunyamulani kuyambira m'mimba mwa amai anu. Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.
Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene.
ndimadzifunsa kuti, “Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?” Ndiyetu mudamlenga mochepera pang'ono kwa Mulungu amene, mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu.
Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai, adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.
M'mene mzimu umaloŵera m'thupi la mwana m'mimba mwa mkazi wodwala, inu simudziŵa. Chonchonso ntchito ya Mulungu amene amapanga zonse, inu simungaidziŵe.
Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.”
Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Anthu ena ankabwera ndi ana omwe kwa Yesu kuti aŵakhudze. Ophunzira ake poona zimenezi, ankaŵazazira. Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.
Kodi ine ndidzafikitsa anthu anga mpaka nthaŵi yobala, koma osalola kuti abaledi?” Akuterotu Chauta. “Kodi Ine, amene ndili wobalitsa, ndingatseke mimba nthaŵi imeneyo?” Akuterotu Mulungu wako.
Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Ulewe zabodza, zosinjirira. Usaphe munthu wosalakwa ndi wosapalamula, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.
Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa. Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Manja anu adandilenga ndi kundiwumba. Patseni nzeru zomvetsa, kuti ndiziphunzira malamulo anu.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.
“Aliyense wopha munthu, nayenso adzaphedwa, pakuti munthu adalengedwa muchifaniziro cha Mulungu.
Inu Chauta, mukadaŵerengera machimo, ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye? Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani.
Ine ndine Chauta amene ndidakulengani ndi kukuumbani m'mimba mwa amai anu, amenenso ndinkakuthandizani. Usaope iwe Yakobe, mtumiki wanga. Inu ndinu anthu anga okondedwa amene ndidakusankhulani.
Zoonadi, ndidabadwa mu uchimo, ndinali mu uchimo kuyambira pamene mai wanga adatenga pathupi pa ine.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.
Makolo asafere zolakwa za ana ao. Momwemonso ana asafere zolakwa za makolo ao. Munthu aphedwe chifukwa cha zoipa za iye mwini.
Musanditayire kumodzi ndi anthu ochimwa, musandichotsere moyo pamodzi ndi anthu ofuna kupha anzao,
Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Aliyense wodana ndi mnzake, ndi wopha anthu. Ndipo mukudziŵa kuti aliyense wopha anthu, alibe moyo wosatha mumtima mwake.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo.
Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika.
Ndidaonanso kuzunza kulikonse kochitika pansi pano. Ndipo ndidaona ozunzidwa akulira misozi, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti aŵatonthoze. Panalibe oŵatonthoza chifukwa ozunzawo anali ndi mphamvu.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko, ndimadzifunsa kuti, “Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?”
Adzakukondani ndi kukudalitsani, kotero kuti mudzachuluka ndi kubereka ana ambiri. Minda yanu adzaidalitsa, kotero kuti tirigu, vinyo ndi mafuta, mudzakhala nazo zonsezo. Adzakudalitsaninso pa zoŵeta pokupatsani ng'ombe zambiri ndi zoŵeta zina zomwe. Madalitso onseŵa, adzakupatsani muli m'dziko limene adalonjeza makolo anu. Pa dziko lapansi, palibe anthu amene adzakhale odala ngati inu. Sipadzaoneka mwamuna kapena mkazi wosabala pakati panu, ndiponso pakati pa zoŵeta zanu.
Zitatha izo Mulungu adati, “Tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam'nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoŵeta, ndi zokwaŵa zonse za pa dziko lapansi.” Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi.
Tsoka kwa amene amakangana ndi mlengi wake, ngakhale ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake. Kodi mtapo ungafunse munthu woumba kuti, “Kodi ukuumba chiyani?” Kapena kunena kuti, “Woumbawe, ulibe luso!”
Ndithu iyo idzalanditsa anthu osoŵa amene amaiitana, idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda woŵathandiza. Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osoŵa, ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphaŵi. Idzaombola moyo wao kwa anthu oŵapsinja ndi kwa oŵachita zankhanza, pakuti magazi ao ndi amtengowapatali pamaso pake.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Ngakhale anthu ambiri akamachita choipa, usamavomerezana nawo. Ndipo usamapereka umboni wopotoza chiweruzo m'bwalo lamilandu, kuti ukondweretse anthu ambiri.
Tsono poti mkazi wa Isaki anali wosabereka, Isakiyo adapempherera mkazi wake kwa Chauta. Chauta adamva pemphero lake, ndipo Rebeka adatenga pathupi. Koma pamene ana aŵiriwo anayamba kulimbana m'mimba mwake, adati, “Ngati umu ndimo m'mene zikhalire zinthu, ndikhaliranji ndi moyo?” Ndipo adakafunsa Chauta kuti amuyankhe.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse. Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene amakhala moyo chifukwa cha iye yekha, kapena kufa chifukwa cha iye yekha. Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.
Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.
“Bwanji sindidangobadwa wofaifa! Bwanji sindidangoti badwu nkufa! Chifukwa chiyani mai wanga adandifukata? Chifukwa chiyani adandiyamwitsa?
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu: Ndaziwona ntchito zimene Mulungu adapatsa anthu kuti azizigwira. Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira. Ndikudziŵa kuti kwa anthu palibe chabwino china choposa kukhala osangalala ndi kumadzikondweretsa nthaŵi yonse ya moyo wao. Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa. Ndikudziŵa kuti zimene Mulungu amazichita zimakhazikika mpaka muyaya. Palibe zimene zingathe kuwonjezedwa kapena kuchotsedwapo pa zimenezo. Mulungu adazipanga motero, kuti choncho anthu azimumvera. Zimene zilipo tsopano zidaaliponso kale. Zimene zidzakhalepo kutsogolo, zidaaliponso kale. Mulungu amabwezanso zakale zimene zidapita kuti zichitikenso. China chimene ndidachiwona pansi pano ndi ichi: Koyenera kukhala chiweruzo chabwino, komwekonso kumapezeka kuipa mtima. Koyenera kukhala chilungamo, komwekonso kumapezeka zoipa. Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.” Kunena za anthu, ndinkalingaliranso kuti, “Mulungu amaŵayesa ndi cholinga choti aŵaonetse kuti iwowo sasiyana konse ndi nyama. Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake. pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo.
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Nanji munthu, amene amaposa nkhosa kutalitali! Ndiye kutitu Malamulo amalola kuchita zabwino pa tsiku la Sabata.”
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo, Tsono inuyo ndi zidzukulu zanu mudzabwerera kwa Chauta, ndipo mau ake amene ndikukupatsani leroŵa mudzaŵamvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake. Chauta adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili m'menemo. Amasunga malonjezo ake nthaŵi zonse.
Kodi inu zikukukomerani kuti mundizunze ndi kundinyoza ine, ntchito ya manja anune, chonsecho mukukondera upo wa anthu oipa? Kodi maso anu ali ngati a munthu? Kodi mumaona zinthu monga m'mene amaziwonera munthu?
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wachita chiyani? Magazi a mng'ono wako akulira kwa Ine kuchokera m'nthaka. Tsopano watembereredwa, sudzailimanso nthaka yomwe yamwa magazi a mng'ono wako, amene waŵakhetsa ndi manja ako.
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali. Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa. Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani? Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga. Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya. Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse. Ngakhale mau anga asanafike pakamwa panga, Inu Chauta mumaŵadziŵa onse. Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo, ndipo mumandisanjika dzanja lanu. Nzeru zimenezi nzopitirira nzeru zanga, nzapamwamba, sindingathe kuzimvetsa.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate. Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao.
Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.
Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri. Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
“Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziŵa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
Ndakhala ndikudalira Inu chibadwire changa, Inu mwakhala Mulungu wanga kuyambira pamene mai wanga adandibala.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.
Kodi amene adapanga ine m'mimba mwa amai anga si yemwe adapanganso iyeyo? Kodi si mmodzi yemweyo amene adatilenga tonsefe?
Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.