Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


102 Mau a m’Baibulo Okhudza Chigololo ndi Chisudzulo

102 Mau a m’Baibulo Okhudza Chigololo ndi Chisudzulo

Kuswa pangano kumabweretsa chisoni chachikulu mumtima. Masiku ano, kusakhulupirika kwafala kwambiri, ulemu ndi kukhulupirirana zikuoneka ngati zinthu zakale. Dziko likuoneka ngati likutinenera kuti kukhulupirika ndi nkhani yakale, koma izi zimam’bweretsa chisoni Mulungu.

M’masiku ovuta ano, njira yokha yopewera mayesero ndi ziwembu za mdani ndi kukhala paubwenzi wolimba ndi Mzimu Woyera. Kusakhulupirika ndi tchimo pamaso pa Mulungu, kwa mnzanu, komanso kwa Yesu. Ndikofunikira kusamala mtima wanu, maso anu, ndi makutu anu, kupewa njira zoyipa, ndikupempha thandizo ngati mukuyesedwa kusakhulupirika.

Mulungu anakhazikitsa ukwati mpaka imfa ikalekanitse, osati chinyengo kapena ziwembu za mdierekezi. Ngati mukuyesedwa kusakhulupirika, pitani kwa Mulungu, pemphani chikhululukiro, ndikupempha thandizo kwa anthu okhwima m’chikhulupiriro kuti akupempherereni. Mukatero, mudzaona mpamvu ya Mzimu Woyera ikukuthandizani kupulumutsa moyo wanu ndi ubale wanu.




Mateyu 5:27-28

“Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usachite chigololo.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:32

Amene amachita chigololo ndi wopanda nzeru, amangodziwononga yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:9

Tsono ndikunenetsa kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, nakwatira wina, akuchita chigololo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:4

Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:3-5

Paja mkazi wadama ali ndi pakamwa pokoma ngati uchi, mau ake ndi osalala koposa mafuta. Koma kotsiriza kwake ngwoŵaŵa ngati chivumulo, ngwolasa ngati lupanga lakuthwa konsekonse. Mapazi ake ndi oloza ku imfa, poyenda amaloŵera njira yakumanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:19

Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:11-12

Iye adaŵauza kuti, “Aliyense amene asudzula mkazi wake nakwatira wina, akuchita chigololo, ndipo akumchimwira mkazi wakeyo. Chimodzimodzinso ngati mkazi asudzula mwamuna wake, kenaka nkukwatiwa ndi wina, nayenso akuchita chigololo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 7:25-27

Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyo, musasokere potsata njira zakezo. Paja iye uja adagwetsa amuna ambiri, anthu amene adaŵaphetsa ngosaŵerengeka. Nyumba yake ndi njira yakumanda, yotsikira ku dziko la anthu akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:10-11

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:26

Ndidapeza china choŵaŵa kupambana imfa. Chinthucho ndi mkazi amene ali ngati msampha, amene mtima wake uli ngati ukonde, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu wokondweretsa Mulungu amamthaŵa mkaziyo, koma wochimwa amalolera kukhala kapolo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 5:7-8

Chauta akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji pa zonsezi? Ana anu adandisiya Ine, ndipo adapembedza milungu imene siili milungu konse. Ine ndidaŵapatsa zonse zimene ankasoŵa, komabe adakonda kumachita chigololo, namapita ku nyumba za akazi adama. Aliyense ankathamangira mkazi wa mnzake, monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 2:2

Akasirira minda, amailanda. Akakhumbira nyumba, amazilanda. Amavutitsa munthu ndi banja lake, naŵatengera zonse zimene ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:37

Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:4-6

Yesu adaŵayankha kuti, “Kodi simunaŵerenge kuti Mulungu amene adalenga anthu pa chiyambi, adalenga wina wamwamuna, wina wamkazi? Ndipo kuti Iye yemweyo adati, ‘Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ake ndi amai ake, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.’ Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 7:2-3

Mwachitsanzo, malamulo amati mkazi wokwatiwa ngwomangidwa kwa mwamuna wake, nthaŵi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi uja amamasuka ku malamulo okhudza za mwamuna wake aja. Ngati ndichita zimene sindizifuna, sindinenso amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine. Motero ndimaona kuti chimene chimachitika nchakuti pamene ndifuna kuchita zabwino, zoipa zili nane pomwepo. Mtima wanga umakondwa ndi Malamulo a Mulungu, koma m'kati mwanga ndimaona lamulo lina lolimbana ndi lamulo limene mtima wanga wavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa kapolo wa lamulo la uchimo lokhala m'kati mwanga. Kalanga ine! Ndani adzandipulumutsa ku khalidwe langa lino londidzetsera imfa? Tiyamike Mulungu! Adzandipulumutsa ndiye kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Motero ineyo, ndi mtima wanga ndimatumikira Malamulo a Mulungu, chonsecho ndi khalidwe langa lokonda zoipa, ndimatumikira lamulo la uchimo. Nchifukwa chake ngati adzipereka kwa mwamuna wina, pamene mwamuna wake ali moyo, mkaziyo amati ngwachigololo. Koma mwamuna wake akamwalira, mkazi uja wamasuka ku malamulo a ukwati, kotero kuti sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:27

Onse amene ali kutali ndi Inu adzaonongeka, Inu mumaŵaononga amene ali osakhulupirika kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:32-34

Mkazi wadama iwe, unkakonda amuna achilendo kupambana mwamuna wako. Amuna amapereka ndalama kwa akazi onse adama. Koma iwe zibwenzi zako zonse unkazipatsa mphatso. Potero unkazinyengerera kuti zizibwera kuchokera mbali zonse kudzagona nawe. Choncho udaali wosiyana ndi akazi ena pochita zadama, chifukwa panalibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye amene unkapereka ndalama, osati ena kukupatsa ndalama ai. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:16-17

Udzapulumuka kwa mkazi wadama, kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika, amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta, kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:15-16

Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:155

Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:20

M'mene amachitira mkazi akachita chigololo amatere: amati akadya nkupukuta pakamwa, namanena kuti, “Palibe chimene ndalakwa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:6

Iwe Israele, Chauta wakuitananso. Uli ngati msungwana wosiyidwa, amene ali wodzaza ndi chisoni mu mtima, ngati mkazi wapaunyamata amene wachotsedwa, akuterotu Mulungu wako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:12

Tsono amene akuganiza kuti waimirira molimba, achenjere kuti angagwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5

Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:13

Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:26

Munthu wochita zabwino amatsogolera anzake pa njira yokhoza, koma njira ya munthu woipa imaŵasokeretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:3

Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chachabechabe. Ndimadana ndi zochita za anthu okusiyani, sizindikomera konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:113

Ndimadana nawo anthu apaŵiripaŵiri, koma ndimakonda mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:14

Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:15

Pakati panu pasakhale ndi mmodzi yemwe wogwa m'mavuto chifukwa choti wapha munthu, kapena waba, kapena wachita choipa, kapena waloŵerera za eniake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:26

Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:17

“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:3

Senderani kuno, inu anthu ochita zoipa, pakuti muli ngati zidzukulu zam'chigololo, zochokera m'zadama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:20

kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:11

Koma ndidaakulemberani kuti musamayanjane ndi munthu amene amati ndi mkhristu, pamene chikhalirecho ndi munthu wadama, kapena waumbombo, wopembedza mafano, waugogodi, chidakwa, kapena wachifwamba. Munthu wotere musamadye naye nkomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:16-17

Koma kwa munthu woipa Mulungu amati, “Ukuvutikiranji ndi kutchula malamulo anga? Bwanji pakamwa pako pakulankhula za chipangano changa? Iwe sufuna kulangizidwa, umaponya mau anga ku nkhongo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 10:20

Ngakhale mumtima mwako usamainyoza mfumu. Ngakhale m'chipinda mwako momwe usamatukwana wolemera. Mwina kambalame kamumlengalenga kapena kachilombo kena kouluka nkukumvera, kenaka nkukaulula zonse kwa amene umaŵanenawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:3-9

Afarisi ena adadza kwa Iye. Tsono kufuna pomupezera chifukwa, adamufunsa kuti, “Kodi nkololedwa kuti munthu asudzule mkazi wake pa chifukwa chilichonse?” Komatu ambiri amene ali oyambirira adzakhala otsirizira, ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.” Yesu adaŵayankha kuti, “Kodi simunaŵerenge kuti Mulungu amene adalenga anthu pa chiyambi, adalenga wina wamwamuna, wina wamkazi? Ndipo kuti Iye yemweyo adati, ‘Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ake ndi amai ake, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.’ Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.” Afarisi aja adamufunsa kuti, “Nanga bwanji Mose adalamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo kenaka nkumuchotsa?” Yesu adaŵayankha kuti, “Mose adaakulolani kusudzula akazi anu chifukwa cha kukanika kwanuku. Komatu pa chiyambi sizinali choncho ai. Tsono ndikunenetsa kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, nakwatira wina, akuchita chigololo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:10-11

Kwa anthu am'banja lamulo langa, limenetu kwenikweni ndi lochokera kwa Ambuye, ndi ili: Mkazi asalekane ndi mwamuna wake. Koma ngati amuleka, akhale wosakwatiwanso, kapena ayanjane nayenso mwamuna wakeyo. Chimodzimodzinso mwamuna asasudzule mkazi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 2:16

Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndimadana ndi kusudzulana. Ndimadana ndi munthu wochita zankhalwe zotere kwa mkazi wake. Choncho chenjerani, musakhale osakhulupirika. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 2:24

Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aŵiriwo amakhala thupi limodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:6

Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:7

Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:1

Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:20

Onse amene amakonda Chauta, amaŵasunga, koma Chauta adzaononga oipa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:2-4

Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi. Ndilibenso wina wonga amene ali ndi mtima wosamala za inu kwenikweni. Paja ena onse amangofuna zokomera iwo okha, osati zokomera Yesu Khristu. Koma mukudziŵa kuti mkhalidwe wa Timoteo ndi wotsimikizika kale kuti ngwabwino. Mukudziŵanso kuti adagwira mogwirizana nane ntchito yofalitsa Uthenga Wabwino, monga mwana ndi bambo wake. Ndikuyembekeza tsono kumtumiza kwa inu msanga, nditadziŵa za m'mene ziyendere zanga. Koma ndikhulupirira kuti, Ambuye akalola, inenso ndidzafika kwanuko msanga. Ndaganiza kuti nkofunikadi kuti ndikutumizireni mbale wathu uja, Epafrodito. Mudaamtuma kuti adzandithandize pa zosoŵa zanga, ndipo wagwiradi ntchito ndi kumenya nkhondo yachikhristu pamodzi ndi ine. Tsonotu akukulakalakani nonsenu, ndipo ndi wokhumudwa podziŵa kuti inu mudamva zoti iye ankadwala. Nzoonadi adaadwala zedi mpaka pafupi kufa. Mwai kuti Mulungu adamchitira chifundo. Ndipotu sadangochitira chifundo iye yekhayu, komanso ineyo, kuti chisoni changa chisakhale chosanjikizana. Nchifukwa chake ndikufunitsitsa ndithu kumtumiza kwa inu, kuti podzamuwonanso mudzasangalale, kutinso nkhaŵa yanga ichepeko. Mlandireni mwachikhristu ndi chimwemwe chachikulu. Anthu otere muziŵachitira ulemu. Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:14

Koma ndimadalira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu Mulungu wanga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:19

Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:31-32

“Anthu akale aja adaaŵalamulanso kuti, ‘Ngati munthu asudzula mkazi wake, ampatse mkaziyo kalata yachisudzulo.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, akumchititsa chigololo mkaziyo ngati akwatiwanso. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:12-15

Kwa ena mau anga, osati a Ambuye ai, ndi aŵa: Ngati mkhristu ali ndi mkazi wachikunja, ndipo mkaziyo avomera kukhala naye, mwamunayo asathetse ukwatiwo. Momwemonso ngati mkhristu wamkazi ali ndi mwamuna wachikunja, ndipo mwamunayo avomera kukhala naye, mkaziyo asathetse ukwatiwo. Pakuti mwamuna wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mkazi wakeyo. Nayenso mkazi wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mwamuna wakeyo. Pakadapanda apo, bwenzi ana anu atakhala akunja, koma monga zilirimu, ndi ana a Mulungu. Koma ngati wakunja uja afuna kuleka mkhristu, amuleke. Zikatero, ndiye kuti mkhristu wamwamunayo kapena wamkaziyo ali ndi ufulu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale ndi moyo wamtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:31

Paja mau a Mulungu akuti, “Nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amai ake, nkukaphatikizana ndi mkazi wake, kuti aŵiriwo asanduke thupi limodzi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:18

Uzikhutira ndi mkazi wako, uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:4-5

Yesu adaŵayankha kuti, “Kodi simunaŵerenge kuti Mulungu amene adalenga anthu pa chiyambi, adalenga wina wamwamuna, wina wamkazi? Ndipo kuti Iye yemweyo adati, ‘Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ake ndi amai ake, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:14

Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:12

Chidani chimautsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:17

Kuli bwino kudyera masamba pali chikondi, kupambana kudyera nyama ya ng'ombe yonenepa pali chidani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:8

Yesu adaŵayankha kuti, “Mose adaakulolani kusudzula akazi anu chifukwa cha kukanika kwanuku. Komatu pa chiyambi sizinali choncho ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:9

Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:13

Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:14

Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:10-12

Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali. Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasoŵa phindu. Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:19

Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:7

“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:22

Wopeza mkazi, wapeza chinthu chabwino, Chauta wamukomera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:39

Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati, nthaŵi yonse pamene mwamuna wake ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi mwamuna amene iye afuna, malinga ukwatiwo ukhale wachikhristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:176

Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 24:67

Tsono Isaki adatenga Rebeka kuti akhale mkazi wake naloŵa naye m'hema mwake. Isaki adamkonda kwambiri Rebekayo, mwakuti zimenezi zidamtonthoza pa imfa ya mai wake ija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:2

Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:10

Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:14

Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7-8

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:30

Pajatu pouka akufa, palibenso za kukwatira kapena kukwatiwa ai. Onse ali ngati angelo Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:1

Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:13

Koma ntchito za munthu aliyense zidzaonekera poyera, pamene tsiku la chiweruzo lidzaziwonetsa. Pakuti tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito za munthu aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:28

Tsono popeza kuti iwo sadalabadireko za kumvera Mulungu, Mulunguyo adaŵasiya m'maganizo ao opusa, kotero kuti amachita zosayenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:5

Mlengi wako ali ngati mwamuna wako. Chauta Wamphamvuzonse ndiye dzina lake. Woyera Uja wa Israele ndiye Momboli wako, dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:32

Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:8

Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:4

Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:32

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, akumchititsa chigololo mkaziyo ngati akwatiwanso. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:18

“Aliyense amene asudzula mkazi wake, nakwatira wina, akuchita chigololo. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:26

Paja mkazi wachiwerewere ungathe kumgula ndi buledi, koma wadama wokwatiwa amakulanda ndi moyo wako womwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:18

Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:28

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:14

“Usachite chigololo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:20

Usagone ndi mkazi wa mnzako ndi kudziipitsa naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:22

Munthu akagwidwa akuchita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, aphedwe onsewo, mwamuna ndi mkazi yemwe. Choncho mudzachotsa choipa pakati pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 3:8

Adaona kuti Israele wosakhulupirika uja ndidamsudzula ndi kumpirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda, mbale wake, sadaope. Iyenso adakhala wosakhulupirika, adapita kukachita zadama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:26

Udachita zigololo ndi Aejipito adama oyandikana nawe, ndipo udandikwiyitsa chifukwa udachulukitsa zigololo zako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga Wamuyaya, Wamkulu, Wamphamvu, chifundo chanu n'chopanda malire pa moyo wanga! Ndikudalirani chilichonse, ndipo chifukwa cha ichi, ndikupereka mtima wanga pamaso panu kuti ndikulemekezeni ndi kukudalitsani. Ndikulumbira Ambuye, ndili ndi chisoni chachikulu chifukwa cha kusakhulupirika kwa mkazi/mwamuna wanga, mtima wanga uli ndi udani ndi mkwiyo, chonde ndithandizeni kumukhululukira kuti inunso mundikhululukire. Inu munatipanga ndipo mukudziwa zobisika za mitima yathu, chifukwa cha ichi ndikupemphani kuti muchitire chifundo banja lino ndi kutsanulira Mzimu Woyera pa mkazi/mwamuna wanga amene walakwira kwambiri ndi munthu wina. Ndithandizeni Ambuye kukhala chiwonetsero cha chikondi chanu nthawi iliyonse ndikamalankhula naye. Inu munatiyang'ana ndipo munkadziwa zomwe zidzachitike, chiritsani mabala anga ndi kubwezeretsa ubwenzi wanga ndi inu kuti ndikwanitse kubwezeretsa mgwirizano wanga ndi munthu amene wandilakwira. Mzimu Woyera ndithandizeni kumuona mwa maso anu, ndi chikondi, chifundo ndi mtima wowona. Ndipatseni nzeru zomulankhulira ndi kumvetsera. Ndikutsutsa chilakolako cha kubwezera, mkwiyo, nsanje ndi ndewu. Yesu, inu munavutika, munanyengedwa ndi kugwidwa popanda chifukwa, ndithandizeni kupambana mayesero akulu amenewa omwe abwera m'nyumba mwanga. Pakuti mawu anu amati: «Thaŵani dama. Uchimo wina uliwonse umene munthu angachite uli kunja kwa thupi; koma wochita dama, uchimwira thupi lake lomwe.» Mulungu wokondedwa, sungani mtima wanga pamalo anu otetezeka kuti usawonongeke ndi mayesero a satana kapena ntchito za anthu. Ndilanditseni kwa mkazi wopanda nzeru ndi wachipanduko ndi mwamuna wonyenga ndi woipa. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa