Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


117 Mau a m'Baibulo Okhudza Mafano ndi Kulambira Mafano

117 Mau a m'Baibulo Okhudza Mafano ndi Kulambira Mafano

M’buku la Ekisodo, Mulungu anapatsa anthu ake Malamulo Khumi, ndipo limodzi mwa malamulowo limatiletsa kupembedza mafano. Izi zimatikumbutsa kuti Mulungu yekha ndiye woyenera kulambiridwa ndi kukhulukidwa.

Komanso, m’Chipangano Chatsopano muli ziphunzitso zokhudza mafano zomwe zingatithandize masiku ano. Mtumwi Paulo analemba m’kalata yake yoyamba kwa Akorinto kuti mafano alibe mphamvu ndipo tiyenera kupewa kupembedza mafano.

Ndikufuna kuti tiganizire mozama za miyoyo yathu ndi kuona ngati pali chilichonse chimene tayika patsogolo pa Mulungu. Kodi ntchito yathu, ubale wathu ndi anthu ena, kapena zolinga zathu, zakhala zofunika kwambiri kuposa Mulungu? Kodi zinthu zakuthupi kapena kupambana padziko lapansi kwatilepheretsa kukhala paubwenzi ndi Mulungu?

Palibe cholakwika kukhala ndi zolinga ndi zokhumba, koma zikamakhala ngati mafano omwe amatilekanitsa ndi Mulungu, ndi nthawi yoti tiganizirenso. Tiyenera kukhala ndi miyoyo yabwino, yokumbukira kuti Mulungu ayenera kukhala pakati pa chilichonse chimene timachita.

M’buku la Deuteronomo 13:4 limati: “Muziyenda ndi Yehova Mulungu wanu, ndipo muzimuopa iye, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mawu ake, ndi kum’tumikira iye, ndi kumamatira kwa iye.”




1 Yohane 5:21

Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:23

Musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide, kuti muziipembedzera kumodzi ndi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:3-5

“Usakhale ndi milungu ina, koma Ine ndekha. “Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko. Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 13:4

Mutsate Chauta, Mulungu wanu, ndi kuwopa Iye yekha. Mutsate malamulo ake ndi kumvera mau ake. Mutumikire Iye ndi kuphathana naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:7-9

“Usapembedze Mulungu wina, koma Ine ndekha. “Usadzipangire fano kufanizira kanthu kolengedwa kalikonse kakumwamba, kapena ka pa dziko lapansi, kapena ka m'madzi a pansi pa dziko. Usagwadire fano lililonse kapena kulipembedza, chifukwa Ine, Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, sindilola kuti wina apikisane nane. Ndimalanga amene adana nane. Ndimalanganso zidzukulu zao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:14-15

Musamapembedza milungu ina, milungu imene amaipembedza anthu okhala mozunguliramu, popeza kuti mukatero, mkwiyo wa Chauta udzakuyakirani ngati moto, ndipo udzakuwonongani kwathunthu, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, amene amakhala pakati panu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:39

Choncho dziŵani ndipo musamaiŵala kuti Chauta ndiye Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, palibe wina ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:4-8

Koma mafano ao ndi asiliva ndi agolide, opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma salankhula. Maso ali nawo, koma sapenya. Makutu ali nawo, koma saamva. Mphuno ali nazo, koma sanunkhiza. Manja ali nawo, koma akakhudza, samva kanthu. Miyendo ali nayo, koma sayenda, ndipo satulutsa ndi liwu lomwe kukhosi kwao. Anthu amene amapanga mafanowo amafanafana nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5

Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 13:4

Chauta akuti “Ine ndakhala Chauta Mulungu wako kuyambira nthaŵi imene ndidakutulutsa ku Ejipito. Sudziŵa Mulungu wina, koma Ine ndekha, Mpulumutsi wako ndine ndekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 135:15-18

Mafano a mitundu ina ya anthu ndi asiliva ndi agolide chabe, ndi opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma salankhula, maso ali nawo, koma sapenya. Makutu ali nawo, koma saamva, ndipo alibe mpweya m'kamwa mwao. Anthu amene amapanga mafanowo afanefane nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:18-20

Kodi Mulungu mungathe kumuyerekeza ndi yani? Kodi mungamufanizire ndi chiyani? Likakhala fano, ndi munthu waluso amene amalipanga, kenaka mmisiri wa golide amalikuta ndi golide, nalipangira ukufu wasiliva. “Muŵalankhule mofatsa anthu a ku Yerusalemu. Muŵauze kuti nthaŵi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndaŵalanga moŵirikiza chifukwa cha machimo ao.” Mmphaŵi wosatha kupeza choperekera nsembe, amasankhula mtengo umene sudzaola. Amafunafuna mmisiri woti ampangire fano limene silingagwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 24:15

Ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene muti mudzamtumikire, kapena ndi milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m'dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:3-5

Ndithudi, miyambo ya anthu a mitundu inayo nzopanda pake. Iwo aja amakadula mtengo ku nkhalango, munthu waluso namausema ndi nsompho. Anthu ena amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide, kenaka nkuchikhomerera ndi misomali, kuti chisagwedezeke. Mafano aowo ali ngati kangamunthu woopsera mbalame m'munda wa minkhaka, sangathe nkulankhula komwe. Ayenera kuŵanyamula, poti sangayende okha. Musaŵaope, chifukwa sangakuchiteni choipa. Alibenso mphamvu zochitira zabwino.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 24:23

Yoswa adatinso, “Chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu, ndipo muzipembedza Chauta, Mulungu wa Israele, mokhulupirika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 14:3-5

“Iwe mwana wa munthu, anthu ameneŵa aika mtima pa mafano ao, aikanso maso ao pa zinthu zina zophunthwitsa. Kodi iwoŵa akuganiza kuti ndidzaŵayankha akadzapempha nzeru kwa Ine? Tsono uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ngati Mwisraele wina aliyense aika mtima pa mafano ake, naikanso maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, kenaka nkupita kwa mneneri, Ineyo Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha moyenerana ndi kuchuluka kwa mafano ake. Ndidzatero kuti mwina mwake nkukopanso mitima ya Aisraele amene andisiya chifukwa cha mafano ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:7

Ena amatamira magaleta ankhondo, ena amadalira akavalo, koma ife timatamira dzina la Chauta, Mulungu wathu, timamutama Iyeyo mopemba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:9

Iwo amakamba okha za m'mene mudatilandirira, ndi za m'mene mudasiyira mafano ndi kutembenukira kwa Mulungu weniweni wamoyo, kuti muzimtumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:8-9

Kale simunkadziŵa Mulungu, nchifukwa chake munkatumikira zomwe sizili milungu konse. Koma tsopano mukumdziŵa Mulungu, makamaka ndinene kuti Mulungu ndiye akudziŵa inu. Nanga bwanji mukubwereranso ku miyambo yachabe ndi yopanda phindu ija? Bwanji mukufuna kukhalanso akapolo ake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 26:1

“Musadzipangire mafano ndipo musaimike zithunzi zosema kapena miyala yachipembedzo. Musaimiritse miyala yosema mwachithunzi m'dziko mwanu kuti muziipembedza. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yona 2:8

Anthu opembedza milungu yachabe amataya kukhulupirika kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:4

Amene amasankhula milungu ina, amadzichulukitsira mavuto. Sindidzatsira nawo nsembe zao zamagazi kapena kutchula maina a milungu yaoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 32:1-4

Anthu ataona kuti Mose wakhalitsako kuphiri osatsikako, adasonkhana kwa Aroni, ndipo adamuuza kuti, “Tiyeni mutipangire milungu yotitsogolera ife, chifukwa sitikudziŵa chomwe chamugwera Moseyo, amene adatitsogolera potitulutsa ku Ejipito kuja.” Nchifukwa chake tsono, undileke kuti ndiŵaononge chifukwa ndili wokwiya kwambiri, koma iweyo ndidzakusandutsa mtundu waukulu wa anthu.” Koma Mose adapepesa Chauta wake, nati, “Inu Chauta, chifukwa chiyani mukukwiyira anthu anu chotere, anthu amene mudaŵatulutsa mu ukapolo ku Ejipito kuja ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lamphamvu? Kodi mukufuna kuti Aejipitowo azidzanena kuti, ‘Adaŵatulutsa ku Ejipito ndi cholinga choipa choti akaŵaphere ku mapiri ndi kuŵaonongeratu pa dziko lapansi?’ Ukali wanu woyaka ngati motowo ubwezeni, ndipo musaŵaononge anthu anu. Kumbukirani atumiki anu aja Abrahamu, Isaki ndi Israele ndiponso zija mudaŵalonjezazi molumbira pa dzina lanu, pamene mudaŵauza kuti, ‘Ndidzakupatsani zidzukulu zambiri, zochuluka ngati nyenyezi zakuthambo. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonse limene ndidalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lao mpaka muyaya.’ ” Choncho Chauta adaleka chilango choopsa chimene adaati agwetsere anthu akewo. Mose adabwerera natsika phiri atanyamula miyala iŵiri ija yaumboni, yolembedwa mbali zonse ziŵiri. Imeneyi inali ntchito ya Mulungu, ndipo zolembedwazo adaalemba ndi Mulungu mwini mozizokota pamiyalapo. Tsono Yoswa adamva anthu akufuula, nauza Mose kuti, “Ndikumva phokoso lankhondo kumahemako.” Koma Mose adati, “Phokoso limenelo silikumveka ngati phokoso la opambana pa nkhondo, kapenanso kulira kwa ogonjetsedwa. Ndikumva phokoso la kuimba.” Mose atafika pafupi ndi mahema aja, ndi kuwona mwanawang'ombe uja ndi anthu ovina, adakalipa kwambiri. Adaponya pansi miyala inali m'manja mwake ija, naiphwanya patsinde pa phiri paja. Tsono Aroni adauza anthuwo kuti, “Vulani nsapule zagolide kukhutu kwa akazi anu, kwa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi omwe, ndipo mubwere nazo kwa ine.” Pomwepo adakatenga mwanawang'ombe amene Aroni adapanga, namperapera ngati ufa, ndipo adakamtaya m'madzi. Tsono Aisraele aja adaŵamwetsa madziwo. Kenaka Mose adafunsa Aroni uja kuti, “Kodi anthu ameneŵa adakuchita zotani iwe, kuti uŵachimwitse koopsa chotere?” Aroni adayankha kuti, “Musakwiyire ine mbuyanga. Mumaŵadziŵa anthu ameneŵa kuti ngovuta. Iwoŵa adandiwuza kuti, ‘Tipangireni milungu yoti ititsogolere ife, chifukwa sitikudziŵa chomwe chamgwera Mose, amene adatitsogolera potitulutsa ku Ejipito.’ Tsono ine ndidaŵauza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi golide abwere naye.’ Ndipo amene anali nazo zinthu zopangidwa ndi golide adandipatsa. Ndidaziponya pa moto, ndipo ndidapanga fano la mwanawang'ombe lija.” Mose adaonadi kuti anthuwo ngosokonezeka, (chifukwa Aroni adaaŵalekerera, mpaka iwo kusanduka anthu oŵanyodola pakati pa adani ao). Moseyo adaimirira pa chipata cha mahema aja ndipo adafuula mokweza nafunsa kuti, “Kodi ndani akufuna Chauta? Bwerani kuno.” Pompo Alevi onse adadzasonkhana kwa iye, ndipo Mose adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Aliyense mwa inu atenge lupanga, ndipo mupite ku mahema ndi kuloŵa m'zipata zonse. Aliyense mwa inu akaphe mbale wake kapena bwenzi lake kapena mnansi.’ ” Aleviwo adachitadi monga momwe Mose adaŵalamulira, ndipo amuna 3,000 adaphedwa pa tsiku limenelo. Apo Mose adauza Aleviwo kuti, “Lero lino mwadzipatula nokha kuti mukhale ansembe otumikira Chauta, pakupha ana anu ndi abale anu omwe. Motero Chauta akudalitsani lero.” Anthuwo adavuladi nsapule zao, ndipo adabwera nazo kwa Aroni. M'maŵa mwake Mose adauza anthu kuti, “Inu mudachimwa koopsa. Koma tsopano ndidzapita kwa Chauta ku phiri, ndipo nditakupemphererani, kapena angathe kukukhululukirani machimo anu.” Tsono Mose adabwerera kwa Chauta nakanena kuti, “Anthu aŵa adachimwa koopsa. Adadzipangira milungu yagolide. Koma tsopano, chonde muŵakhululukire machimo ao. Mukapanda kuŵakhululukira, chonde mufafanize dzina langa m'buku m'mene mudalemba.” Apo Chauta adauza Mose kuti, “Yekhayo amene wandilakwira Ine, ndiye amene ndidzachotse dzina lake m'buku langa. Tsopano pita uŵatsogolere anthuwo ku malo amene ndidakuuza. Kumbukira kuti mngelo wanga adzakutsogolera, koma tsiku likubwera limene ndidzaŵalange iwowo chifukwa cha machimo ao.” Motero Chauta adatumiza nthenda pa anthuwo, chifukwa choti adakakamiza Aroni kuti aŵapangire fano la mwanawang'ombe. Tsono Aroni adalandira golideyo kumanja kwa anthuwo, ndipo adamsungunula, napanga fano la mwanawang'ombe m'chikombole. Ndipo anthu adayamba kufuula kuti, “Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:4

Musabwerere ku mafano, kapena kudzipangira nokha milungu ya zitsulo zosungunula. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:5

Paja milungu yonse ya mitundu ina ya anthu ndi mafano chabe. Koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 11:12

Anthu a m'mizinda ya ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adzapita kukalirira chithandizo kwa milungu imene ankaperekako nsembe. Koma singathe kuŵapulumutsa pa nthaŵi ya mavuto ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:14

Tsono okondedwa anga, pewani kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 135:15

Mafano a mitundu ina ya anthu ndi asiliva ndi agolide chabe, ndi opangidwa ndi manja a anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:13

“Palibe wantchito amene angathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkunyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 45:20

Chauta akuti, “Musonkhane pamodzi ndipo mubwere. Musendere pafupi, inu nonse amene mudapulumuka kwa anthu a mitundu ina! Ndi opanda nzeru amene amanyamula mafano amitengo, namapemphera kwa milungu imene singathe kuŵapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:21-23

Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima. Iwo amadziyesa anzeru, koma chikhalirecho ndi opusa. Adaleka kulemekeza Mulungu wosafa, nkumapembedza mafano ooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame ndi nyama zina, kapena zokwaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 9:20

Anthu ena onse otsala, amene sadaphedwe ndi miliri ija, sadatembenuke mtima kuti asiye ntchito za manja ao. Sadaleke kupembedza mizimu yoipa, ndi mafano agolide, asiliva, amkuŵa, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:16-31

Pamene Paulo ankadikira Silasi ndi Timoteo ku Atene, mtima wake udavutika kwambiri poona kuti mzinda wonse ngwodzaza ndi mafano. Tsono adakambirana m'nyumba yamapemphero ndi Ayuda ndi anthu ena opembedza Mulungu. Adakambirananso ndi anthu amene ankangokumana nawo pa msika tsiku ndi tsiku. Anzeru enanso a magulu a Aepikurea ndi Astoiki adadzatsutsana naye. Ena ankati, “Kodi mbutuma yolongololayi ikufunanso kunena chiyani?” Enanso ankati, “Ameneyu akukhala ngati wolalika za milungu yachilendo.” Ankanena zimenezi chifukwa iye ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Yesu, ndi za kuuka kwa akufa. Tsono adapita naye ku bwalo lamilandu lotchedwa Areopagi, namuuza kuti, “Ife timati mutidziŵitseko zatsopano zimene mukuphunzitsazi? Tsono Paulo adaloŵa nawo monga adaazoloŵera, ndipo adakambirana nawo za m'Malembo pa masabata atatu. Pakuti zina zimene mukutiwuzazi nzachilendo, ndipo tikufuna kudziŵa kuti zinthuzi nzotani.” Ndiye kuti nzika za ku Atene ndi alendo okhala kumeneko, inali ngati ntchito nthaŵi zonse kumangomvera zatsopano ndi kumazifotokozera. Paulo adaimirira pakati pa bwalo lija la Aeropagi nati, “Inu anthu a ku Atene, pa zonse ndikuwona kuti ndinu anthu opembedza kwambiri. Pakuti pamene ndinalikuyenda mumzindamu, nkumaona malo anu osiyanasiyana achipembedzo, ndinapezanso guwa lina lansembe pamene padalembedwa mau akuti, ‘Kwa Mulungu wosadziŵika.’ Tsonotu amene mumampembedza osamdziŵayo, ndi yemweyo amene ine ndikukulalikirani. Mulungu amene adalenga dziko lapansi ndiponso zonse zili m'menemo, ndiye Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi. Iye sakhala m'nyumba zachipembedzo zomangidwa ndi anthu ai. Anthu sangamtumikire ndi manja ao, ngati kuti Iye amasoŵa kanthu. Pajatu Iye ndiye amapatsa anthu onse moyo, mpweya ndi zina zonse. Kochokera mwa kholo limodzi Iye adalenga mitundu yonse ya anthu, kuti ikhale pa dziko lonse lapansi. Adakonzeratu nthaŵi ya moyo wao, ndiponso malire a pokhala pao. Mulungu adafuna kuti anthu amufunefune, ndipo kuti pomfufuzafufuza, mwina nkumupeza. Komabe Iye sali kutali ndi aliyense mwa ife. Paja “ ‘Mwa Iye ife timakhala ndi moyo, timayenda ndipo timakhala tilipo.’ Monga adanenera opeka ndakatulo anu ena kuti, “ ‘Ifenso ndife ofumira mwa Iye ngati ana ake.’ “Tsono popeza kuti tili ngati ana a Mulungu, sitiyenera kuganiza kuti umulungu wake umafanafana ndi fano lagolide kapena lasiliva kapena lamwala, lopangidwa mwa luso ndi nzeru za munthu. Adaŵamasulira za m'Malembomo ndi kuŵatsimikizira kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa kenaka nkuuka kwa akufa. Paulo adati, “Yesu amene ndikukulalikiraniyu, ndiye Mpulumutsiyo.” Mulungu adaaŵalekerera anthu pa nthaŵi imene iwo anali osadziŵa, koma tsopano akuŵalamula anthu onse ponseponse kuti atembenuke mtima. Chifukwa adaika tsiku pamene Iye adzaweruza anthu a pa dziko lonse lapansi molungama kudzera mwa Munthu amene Iye adamsankha. Adatsimikizira anthu onse zimenezi pakuukitsa Munthuyo kwa akufa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 23:13

nauza Efuroni pakhamu pa onse kuti, “Koma chonde, mundimvere, ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mtengo wake wa mundawu, kuti mkazi wanga ndidzamuike m'menemo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:6

Inu mumadana ndi opembedza mafano achabechabe. Koma ine ndimakhulupirira Inu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 11:2

Ine ndikamakangaza kumuitana, iye ndiye kumandithaŵa kunka kutali. Ankaperekabe nsembe kwa Baala ndi kulitenthera lubani fanolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:8

Dziko lao nlodzaza ndi mafano. Iwo amapembedza mafano opanga ndi manja ao, oumba ndi zala zao zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:23

Adaleka kulemekeza Mulungu wosafa, nkumapembedza mafano ooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame ndi nyama zina, kapena zokwaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 5:13

Ndidzaononga mafano anu onse pamodzi ndi miyala yoimika yopembedzerapo m'dziko mwanu. Simudzazigwadiranso zinthuzo zimene mudapanga ndi manja anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:36-39

Adatumikira mafano ao amene adasanduka msampha kwa iwo. Adapereka nsembe ana ao aamuna ndi aakazi kwa mizimu yoipa. Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo. Adadzidetsa ndi ntchito zao, nakhala osakhulupirika pa zochita zao ngati mkazi wachigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Habakuku 2:18

Kodi phindu la fano nchiyani? Adalipanga ndi munthu. Ndi chifanizo chabe, ndipo nchinthu chonyenga. Munthu wopangayo amakhulupirira zimene wachita, koma mafano akewo satha nkulankhula komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 18:21

Eliya adasendera pafupi ndi anthu onsewo, naŵafunsa kuti, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iŵiri mpaka liti? Ngati Chauta ndiye Mulungu, mtsateni. Koma ngati Baala ndiye Mulungu, tsatani iyeyo.” Anthuwo sadamuyankhe ndi liwu limodzi lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:16

Pamene Paulo ankadikira Silasi ndi Timoteo ku Atene, mtima wake udavutika kwambiri poona kuti mzinda wonse ngwodzaza ndi mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 17:15-17

Iwowo adanyoza malamulo a Chauta ndi chipangano cha Chauta chimene Iye adachita ndi makolo ao. Adanyozanso zochenjeza za Chauta. Adatsata milungu yachabechabe, ndipo iwo omwe adasanduka achabechabe. Ankatsata zitsanzo za anthu a mitundu ina okhala nawo pafupi, ngakhale Chauta anali atalamula kuti asamachite mofanana ndi mitundu imeneyo. Motero adasiya malamulo onse a Chauta Mulungu wao, nadzipangira mafano aŵiri osungunula anaang'ombe. Adapanganso mafano ena a Asera namapembedza zinthu zakumlengalenga ndiponso Baala. Anthuwo adapereka ngati nsembe ana ao aamuna ndi ana ao aakazi, ndipo ankaombeza maula, namachitanso zanyanga. Adadzipereka kuti azichita zoipa zochimwira Chauta, namkwiyitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:13

Mukamafuula kufuna chithandizo, mafano anuwo akupulumutseni! Mphepo idzaiyalula milunguyo, mpweya udzaiwulutsa. Koma amene amakhulupirira Ine, adzalandira dziko lokhalamo, ndi kumapembedza pa phiri langa loyera.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 8:5-6

Pamenepo Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayang'ana kumpoto.” Ine nkuyang'anadi kumpoto. Kumeneko, pafupi ndi guwa pa khomo la chipata, ndidaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija. Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuwona zimene Aisraele akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene akuchita kuno, zondichotsa ku Nyumba yanga yoyera? Ndipotu udzaona zonyansa zina zazikulu kuposa zimenezi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 51:17-18

Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza, mwa iwo mulibe konse moyo. Mafanowo ngachabechabe, oyenera kuŵaseka, ndipo pamene anthuwo adzalangidwe, mafanowo adzaonongedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:4

Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:17

“Musadzipangire milungu yosungunula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:25-26

Mudzatenthe mafano ao ofanizira milungu yao. Musadzakhumbire siliva kapena golide amene iwo adapangira mafanowo. Musadzatengeko zimenezi kuti mungagwe mu msampha, popeza kuti zimenezo zimamnyansa Chauta, Mulungu wanu. Musadzaloŵe nazo m'nyumba mwanu zimenezi, kuti tsoka limene lili pa iwowo lingadzakhale pa inu. Mudzadane ndi mafanowo ndi kuŵanyoza, chifukwa Chauta adaŵatemberera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:2

Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:29

Ndithudi, milungu yonseyi njachabe, zochita zake si kanthu konse. Mafano ake osungunula ali ngati mphepo yachabechabe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:6-7

Chauta, Mfumu ndi Momboli wa Israele, Chauta Mphambe, akunena kuti, “Ine ndine woyamba ndi womaliza. Palibenso Mulungu wina, koma Ine ndekha. Ndani nanga akulingana ndi Ine? Aimirire, alankhule, andifotokozere. Kuyambira kalekale ndani adalosa zakutsogolo? Atidziŵitsetu zimene zikudzachitika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:14

Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza mwa iwo mulibe konse moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:8

Anthu amene amapanga mafanowo amafanafana nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 8:4-6

Ndinene tsono za chakudya choperekedwa kwa mafano. Tikudziŵa kuti fano si kanthu konse, ndiponso kuti palibe mulungu wina, koma Mulungu mmodzi yekha. Ena amati kuli zinthu zina kumwambaku, kapena pansi pano, zimene iwo amazitchula milungu, ndipo anthuwo ali nayodi milungu yambiri, ndi ambuye ambiri. Koma kwa ife, Mulungu ndi mmodzi yekha, ndiye Atate, amene adalenga zonse, ndipo moyo wathu umalinga kwa Iye. Tilinso ndi Ambuye amodzi okha, Yesu Khristu. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo ife tili ndi moyo chifukwa cha Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 46:1-2

Nayu Beli wapendekeka, Nebo waŵerama! Mafano ameneŵa a Babiloni aŵaika pa abulu ndi ng'ombe. Zinthu zimene kale munkanyamula ndinu, tsopano mukuziika ngati katundu wolemera pamsana pa nyama zotopa. Ndidaneneratu zakumathero kuchokera pa chiyambi pomwe. Kuyambira kalekale ndidaloseratu zimene zidakali zosachitikabe. Ndidaanena kuti, ‘Maganizo anga sadzalephera, ndidzachitadi zonse zimene ndidafuna kuchita.’ Ndikuitana chiwombankhanga kuchokera kuvuma, ndiye kuti munthu wofumira ku dziko lakutali, amene adzapherezetsa zimene ndikufuna kuchita. Zimene ndalankhula, ndidzazifitsa, zimene ndafuna kuchita ndidzazichitadi. “Mundimvere, inu ouma mitunu, inu amene muli kutali ndi chipulumutso. Tsiku la chipulumutso ndalisendeza pafupi, layandikira, sindidzachedwa kukupulumutsani. Ndidzapulumutsa Ziyoni, ndipo ndidzapatsa dziko la Israele ulemerero.” Nyamazo zikuŵerama ndi kufuna kugwa naye katunduyo, sizikutha kumpulumutsa. Izo zomwe zikupita ku ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 2:8-9

Tandipempha uwone, ndidzasandutsadi mitundu ya anthu kuti ikhale choloŵa chako, ndipo dziko lonse lapansi lidzakhala lako. Udzaŵaphwanya ndi ndodo yachitsulo, ndi kuŵatekedza zidutswazidutswa monga mbiya.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:25

Adasiya zoona za Mulungu namatsata zabodza. Adayamba kupembedza ndi kutumikira zolengedwa m'malo mwa kupembedza ndi kutumikira Mlengi mwini, amene ali woyenera kumlemekeza mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:41-43

Tsono masiku amenewo iwo adapanga fano la mwanawang'ombe. Adapereka nsembe kwa fanoli, nakondwerera ntchito za manja ao. Pamenepo Mulungu adaŵafulatira, naŵapereka ku machimo akupembedza nyenyezi, monga akunenera mau olembedwa m'buku la aneneri kuti, “ ‘Inu Aisraele, musayese kuti munkapereka kwa Ine nyama zimene munkapha ndi kuzipereka ngati nsembe pa zaka makumi anai zija m'chipululu. Munkanyamula hema la Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani, mafano amene mudaŵapanga kuti muziŵapembedza. Ndidzakuchotsani kukutayani kutali, kupitirira dziko la Babele.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 33:7-9

Tsono m'Nyumba ya Chauta adaikamo fano lopanga iyeyo, Nyumba imene Mulungu adaauza Davide ndi Solomoni mwana wake kuti, “M'nyumba imeneyi, mu Yerusalemu muno, malo amene ndaŵasankhula pakati pa mafuko onse a Aisraele, ndimo m'mene adzatamandira dzina langa mpaka muyaya. Ndipo sindidzachotsa phazi la Israele m'dziko limene ndidapatsa makolo anu, pokhapokha akamasamala ndi kuchita zonse zimene ndidaŵauza pakumvera malamulo ndi malangizo onse amene ndidaŵapatsa kudzera mwa Mose.” Manase adachimwitsa anthu a ku Yuda pamodzi ndi anthu okhala mu Yerusalemu. Ankachita zoipa zambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵaononga pofika Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 97:7

Onse opembedza milungu yonama, amene amanyadira mafano achabechabe, amachititsidwa manyazi, pakuti milungu ina yonse imagonjera Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 9:21

Chinthu chimene mudachipangacho, fano lachitsulo la mwanawang'ombelo, ndidaliponya pa moto. Tsono ndidaliphwanya pafupipafupi ndi kuliperapera, ndipo ndidataya phulusa lake ku mtsinje wotsika m'phiri uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:22

Pamenepo mudzatenga mafano anu, ena okutidwa ndi siliva, ena okutidwa ndi golide, ndipo mudzaŵataya ngati zinyalala, ndikunena kuti, “Zichoke zonsezi!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 14:7

Ngati munthu wina aliyense, Mwisraele kapena mlendo wongokhala nao, andikana Ine, naika mtima pa mafano ake, ndi kuika maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, munthu woteroyo akabwera kudzapempha nzeru kwa Ine, kudzera mwa mneneri, Ine Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:24

Tsono musagwadire milungu yao kapena kuipembedza. Musamachita nao zimene amachita anthu amenewo. Mukaonongeretu milungu yao, ndiponso mukaphwanye miyala yao yopembedzerapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:37

Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:30-31

Chauta ataiwononga mitunduyo inu mukuwona, mukachenjere kuti musakatsate zipembedzo zao. Musadzayese kufunsafunsa za milungu yao kuti, “Kodi mitundu ya anthu iyi imapembedza bwanji milungu yao, kuti ifenso tichite chimodzimodzi?” Musadzapembedze Chauta, Mulungu wanu, mofanafana ndi m'mene iwo amapembedzera milungu yaoyo. Iwo adachita zoipa zoopsa zambiri zimene Chauta amadana nazo, mpaka kutentha ana ao aamuna ndi aakazi pa moto pakuŵapereka kwa milungu yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:38

Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:10

Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:19

Palibe wolingalira, palibe wanzeru kapena womvetsa woti anganene kuti, “Chigawo china cha mtengo ndidatentha pa moto, pa makala ake ndidaphikapo buledi, ndidaotchapo nyama ndipo ndidadya. Tsopano chigawo chotsalachi ndipangira chinthu chonyansa! Monga ine ndizipembedza mtengo?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 14:15

“Anthuni, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Tikukulalikirani Uthenga Wabwino wakuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo amene adalenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'menemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 34:33

Kenaka Yosiya adachotsa zinthu zonyansa zonse ku maiko onse a Aisraele, nakakamiza anthu onse okhala ku Israele kuti azitumikira Chauta, Mulungu wao. Motero anthuwo sadaleke kutsata Chauta, Mulungu wa makolo ao, pa masiku onse a Yosiya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:39

Adadzidetsa ndi ntchito zao, nakhala osakhulupirika pa zochita zao ngati mkazi wachigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:12

Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 1:16

Ndidzatulutsa mlandu wanga wotsutsa anthu anga, chifukwa cha zoipa zimene adachita pakundisiya Ine. Adafukiza lubani kwa milungu ina, namapembedza zimene adapanga ndi manja ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 42:8

Ine ndine Chauta, dzina langa nlimenelo. Ulemerero wanga sindidzapatsa wina aliyense. Mayamiko oyenera Ine, sindidzalola kuti mafano alandireko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:1

Komabe panali aneneri ena onama ngakhale pakati pa Aisraele omwe. Momwemonso pakati pa inu padzaoneka aphunzitsi onama. Iwowo adzaloŵetsa mwachinsinsi zophunzitsa zonama ndi zoononga, ngakhale kukana kumene Mbuye wao amene adaŵaombola, ndipo motero adzadziitanira chiwonongeko mwamsanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:20-22

Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana. Simungathe kumwera m'chikho cha Ambuye nkumweranso m'chikho cha Satana. Simungathe kudyera pa tebulo la Ambuye nkudyeranso pa tebulo la Satana. Kodi tichite kuŵaputa dala Ambuye? Kodi mphamvu zathu nkupambana zao?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:27

Onse amene ali kutali ndi Inu adzaonongeka, Inu mumaŵaononga amene ali osakhulupirika kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 46:9

Mukumbukire zamakedzana zija. Mulungu ndine ndekha, palibenso wina ai. Ndithudi, Mulungu ndine, ndipo palibenso wina wonga Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:4

Musakapembedze Chauta, Mulungu wanu, monga m'mene amachitira anthu ameneŵa popembedza milungu yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:16

Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:13

Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:10

Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:8

Musadedere, musaope. Suja kuyambira kale lomwe ndakhala ndikukuuzani ndi kutsimikiza zimenezi? Inuyo ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine? Iyai, palibenso Thanthwe lina, sindikudziŵa lina lililonse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:3-4

Mulungu wathu ali kumwamba, amachita chilichonse chimene afuna. Koma mafano ao ndi asiliva ndi agolide, opangidwa ndi manja a anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:8

Kale simunkadziŵa Mulungu, nchifukwa chake munkatumikira zomwe sizili milungu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 24:1-2

Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta, dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake. Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta Wamphamvuzonse. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero. Pakuti iye ndi amene adaika dziko lapansi pa nyanja yaikulu, adalikhazika pa mitsinje yozama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:18

Mafano onse adzatheratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 5:19

Ndipo mukamafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta Mulungu wathu watichita zimenezi?’ Iwe Yeremiya uzidzayankha kuti, ‘Monga momwe mudasiyira Chauta, ndi kumatumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemonso ndimo m'mene inuyo muzidzatumikira anthu a m'dziko lachilendo.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:21

Inu mumadzudzula onyada, amene ali otembereredwa, amene amasiya malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 16:31-33

Adachita ngati sadakhutire ndi kuchimwa konga kwa Yerobowamu, mwakuti adaonjeza tchimo pakukwatira Yezebele, mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni, nayamba kutumikira fano lotchedwa Baala, ndi kumalipembedza. Adamanga nyumba ku Samariya yopembedzeramo Baala, ndipo m'nyumbamo adamangamo guwa la Baalayo, naimikamo fano la Asera. Motero Ahabu adachita zinthu zambiri zoputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, kupambana mafumu onse a ku Israele amene adaalipo kale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:1

Ndikupereka mtima wanga kwa Inu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 44:17-19

Koma tidzachitadi zonse zimene tidalumbira. Tidzaifukizira ndithu lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuiperekera nsembe zazakumwa, monga tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akalonga athu, m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Nthaŵi imeneyo tinali ndi chakudya chambiri, ndipo tinkakhuta, osapeza zovuta. Koma kuchokera nthaŵi imene tidaleka kuifukizira lubani mfumukazi yakumwamba, ndi kumaiperekera nsembe zazakumwa, takhala tikusoŵa zonse, ndipo taonongeka ndi nkhondo ndi njala.” Akaziwo adapitirira ponena kuti, “Pamene tinkaifukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kumaiperekera nsembe zazakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza m'mene tinkapangira mfumukaziyo makeke abwino olembapo chithunzi chake, ndiponso m'mene tinkaiperekera nsembe zazakumwa?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 46:5

“Kodi Ine mungandifanizire ndi yani, kapena kundilinganiza ndi yani? Kodi mungandiyerekeze ndi yani, kuti Ine ndi iyeyo tikhale ofanana?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 28:1-3

Ahazi anali wa zaka 20 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Iyeyo sadachite zolungama pamaso pa Chauta, monga m'mene ankachitira Davide kholo lake. Tsono mukufuna kuti mupondereze anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, amuna ndi akazi omwe, kuti akhale akapolo anu. Kodi inuyo mulibe anu machimo pamaso pa Chauta, Mulungu wanu? Mverani tsono, ndipo muŵabweze akapolo amene mudaŵatenga pakati pa abale anuwo, kuti apite kwao, poti Chauta wakwiya nanu koopsa.” Atsogoleri enanso a anthu a ku Efuremu, monga Azariya mwana wa Yohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, adaimirira kuti amenyane ndi anthu amene ankachoka ku nkhondo. Adaŵauza kuti, “Musati mubwere nawo kuno akapolowo, poti inuyo mukufuna kuti ife tichimwire Chauta kuwonjezera pa machimo athu amene tili nawo, ndiponso kuwonjezera pa zolakwa zathu. Ndithu kulakwa kwathu nkwakukulu ndipo mkwiyo woopsa uli pa Israele.” Motero anthu ankhondo aja adaŵasiya akapolowo, pamodzi ndi zofunkhazo, pamaso pa atsogoleriwo ndi pamaso pa msonkhano wonse. Kenaka anthu amene taŵatchula maina aja, adanyamuka natenga akapolowo. Amene anali maliseche adaŵaveka zovala zimene adaafunkha. Adaŵaveka, naŵapatsa nsapato. Adaŵapatsa zakudya ndi zakumwa. Tsono atanyamula anthu onse ofooka pa abulu, adabwera nawo kwa abale ao ku Yeriko, mzinda wamigwalangwa. Kenaka adabwerera ku Samariya. Pa nthaŵi imeneyo Mfumu Ahazi adatumiza mau kwa mfumu ya ku Asiriya, kupempha chithandizo. Paja Aedomu anali atathiranso nkhondo ku Yuda, ndipo adaagonjetsa Yudayo, natenga anthu kuti akhale akapolo. Afilisti nawonso anali atathira nkhondo mizinda yakuchigwa ndiponso Megebu wa ku Yuda. Ndipo adalanda Betesemesi, Aiyaloni, Gederoti ndiponso Soko pamodzi ndi midzi yake yomwe, Timna pamodzi ndi midzi yake yomwe, ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yake yomwe, nakhazikika komweko. Zoonadi Chauta adalitsitsa dziko la Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi, popeza kuti adaaipitsa ku Yuda, ndipo anali wosakhulupirika kwa Chauta. Koma adatsata zitsanzo za mafumu a ku Israele. Adapanga zifanizo zosungunula za Abaala. Motero Tiligati-Pilinesere, mfumu ya ku Asiriya, adadzamenyana naye nkhondo, ndipo adamvutitsa m'malo momlimbikitsa. Ahazi ankatenga katundu ku Nyumba ya Chauta, ku nyumba ya mfumu ndi ku nyumba za nduna, namakampereka kuti akakhomere msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya. Koma zonsezo sizidamthandize. Pa nthaŵi yake yamavutoyo, Ahazi adapitirirabe kukhala wosakhulupirika kwa Chauta. Ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko imene idamgonjetsayo, ndipo ankati, “Chifukwa chakuti milungu ya mafumu a ku Siriya yaŵathandiza iwowo, ine ndidzapereka nsembe kwa milunguyo kuti indithandizenso ine.” Koma milunguyo idamuwononga pamodzi ndi anthu ake onse. Tsono Ahazi adasonkhanitsa ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta, naziphwanyaphwanya. Kenaka adatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, nadzimangira maguwa pa malo ambirimbiri mu Yerusalemu. Adamanga akachisi opembedzerako ku mzinda uliwonse wa Yuda, kuti azifukizako lubani kwa milungu ina, kuputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa makolo ake. Tsono ntchito zonse ndi makhalidwe ake kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Yuda ndi mafumu a ku Israele. Ahazi adamwalira, naikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sadamuike m'manda enieni a mafumu. Ndipo Hezekiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Adafukiza lubani ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza, potsata miyambo yonyansa ya anthu a mitundu ina imene Chauta adaaipirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:28-32

Tsono popeza kuti iwo sadalabadireko za kumvera Mulungu, Mulunguyo adaŵasiya m'maganizo ao opusa, kotero kuti amachita zosayenera. Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi, Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao. Ndi opusa, osakhulupirika, okhakhala moyo, ndi opanda chifundo. Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:9

Musandibisire nkhope yanu. Musandipirikitse ine mtumiki wanu mokwiya, Inu amene mwakhala mukundithandiza. Musanditaye, musandisiye ndekha, Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:14

Musadzapembedze mulungu wina aliyense, chifukwa Chauta amene dzina lake ndi Kansanje, ndi Mulungu wansanjedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:28

Musamale zonse zimene ndakulamulanizi, ndipo mumvere mokhulupirika. Muchite zabwino zokhazokha zokondweretsa Chauta, Mulungu wanu, kuti zonse zidzakuyendereni bwino, inu ndi zidzukulu zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:11

Inu amene mumaopa Chauta, mkhulupirireni. Chauta ndiye mthandizi wanu ndi chishango chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:10-11

Atsogoleri onse a Israele ndi akhungu, onsewo ndi opanda nzeru konse. Ali ngati agalu opanda mau, osatha kuuwa. Ntchito nkulota, kugona pansi, kukondetsa tulo. Ali ngati agalu a njala yaikulu, amene sakhuta konse. Abusa nawonso ndi opanda nzeru. Aliyense amachita monga m'mene afunira, ndipo amangofuna zokomera iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:15-19

“ ‘Koma udadzitama nako kukongola kwako ndi kutchuka kwako, ndipo udayamba kuchita zadama. Unkachita chigololo, kumangodzipereka kwa aliyense amene wabwera. Udatengako zovala zako zina nukakongoletsera akachisi akoako, ndipo kumeneko unkakachitirako zigololo. Zotere sizinachitikepo, ndipo sizidzachitikanso. Udatenganso zokongoletsera, zopangidwa ndi golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndidakupatsa, ndipo udapangira mafano achimuna amene udachita nawo chigololo. Mafanowo udaŵaveka zovala zako zopetapeta, ndipo udapereka mafuta anga ndi lubani wanga kwa iwo. Udatenga chakudya chimene ndidakupatsa, ufa, mafuta ndi uchi zimene ndinkakudyetsa, nuzipereka kwa iwo ngati nsembe za fungo lokoma. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:18

Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:14

Muzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene munkalakalaka pamene munali osadziŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:15

imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 17:8

Sadzakhulupiriranso maguwa amene iwo omwe adamanga, kapenanso kudalira zimene adapanga ndi manja ao, ngakhale mafano ofanizira Asera kapena maguwa ofukizapo lubani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga, ndinu woyenera ulemerero wonse, landirani kukwezedwa ndi kutamandidwa konse. Ndikudziwa kukula kwanu ndipo ndikudziwa bwino kuti palibe Mulungu wina koma inu, ndinu wamkulu ndi woopsa, wopanga zodabwitsa ndi zozizimiritsa, yekhayo woyenera ulemerero. Mzimu wanga ukukutamandani ndi kukudalitsani Ambuye, thupi langa lonse likulambira chiyero ndi kukongola kwanu, dziko lonse lidziwe kuti muli moyo ndipo mukhala kudzanja lamanja la Mulungu. Inu Ambuye, ndinu thanthwe langa ndi linga langa, ndikudzicepetsa pamaso panu kuti mundimasule ku maunyolo a mafano ndi kukonzanso mtima wanga mu chilungamo ndi chiyero, ndithandizeni kusiya zachabe za dziko lino ndi kufunafuna chifuniro chanu chokha. Ndimakukhulupirirani Mulungu wanga, kuti munditsogolere panjira ya choonadi ndi kulambira koona. Zonse zimene ndichita zikhale za ulemerero ndi ulemu wa dzina lanu. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa