Madalitso a Mulungu pa moyo wanga amabwera nthawi zonse mokwanira ndipo amafika panthawi yake, sakhala mochedwa. Mulungu amadziwa nthawi yoyenera yotumizira madalitso amene mumapempha m’pemphero.
Tizunguliridwa ndi madalitso okongola a Mulungu, tili ndi thanzi, tili ndi pogona, tili ndi chakudya, tili ndi thanzi la maganizo, tili ndi anthu amene amatikonda ndipo koposa zonse tili ndi Mulungu m’miyoyo yathu, timasangalala ndi mphatso yabwino ya chipulumutso, amenewa ndi madalitso amene nthawi zina sitimazindikira, koma amene anthu ambiri akusowa, ndipo tiyenera kuyamikira zinthu zimenezi, ndi kusangalala chifukwa chifundo cha Mulungu chimakhala chatsopano m’mawa uliwonse.
Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu zonse mogwirizana ndi chuma chake cha ulemerero mwa Khristu Yesu (Afilipi 4:19). Mulungu amalankhula m’mawu ake kuti madalitso ochokera kwa Iye ndi amene amalimbitsa ndipo saonjezera chisoni, Mulungu amadziwa zimene tikufuna ndipo amasamalira ife.
Tikhale oleza mtima kuti madalitso ake adzafika pamene simukuyembekezera. Lambirani Ambuye Mulungu wanu, ndipo adzadalitsa chakudya chanu ndi madzi anu. Ine ndidzachotsa matenda onse pakati panu (Ekisodo 23:25). Khalani ndi moyo womvera Mulungu ndipo madalitso adzabwera nawo.
Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”
Mulungu amene amapatsa mbeu kwa wobzala, ndiponso chakudya choti adye, adzakupatsani mbeu zoti mubzale, ndipo adzazichulukitsa. Adzachulukitsanso zipatso zake za chifundo chanu.
Paja anthu amati, ‘Ikapita miyezi inai, ndiye kuti yafika nyengo yokolola.’ Koma ndithu, taonani m'mindamu, kodi simukuwona kuti mbeu zacha kale kudikira kholola?
Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.
Mwana womakolola nthaŵi yachilimwe ndiye wanzeru, koma womangogona nthaŵi yokolola amachititsa manyazi.
Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo.
Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe. Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.
Tayani mtima, inu alimi, lirani, inu olima mphesa, chifukwa tirigu ndi barele, ndi zonse zam'minda zalephera.
“Mukamayenda motsata njira zanga ndi kumamvera malamulo anga onse ndi kuŵatsatadi, Ndidzaononga akachisi anu opembedzerako mafano ku mapiri ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo lubani, ndipo ndidzaponya mitembo yanu pa mafano opanda moyo, ndipo ndidzadana nanu. Ndidzasandutsa mizinda yanu kuti ikhale mabwinja, ndidzasandutsanso malo anu achipembedzo kuti akhale opanda anthu, ndipo sindidzalolanso kumva fungo lokoma la zopereka zanu. Ndidzaononga dziko lanu kotero kuti adani anu amene adzakhale m'menemo adzadabwa. Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzakupirikitsani, lupanga lili pambuyo. Dziko lanu lidzasanduka chipululu, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja. “Pa nyengo imeneyo nthaka idzakondwerera zaka zoipumitsa nthaŵi yonse pamene m'dzikomo mulibe anthu, inu muli m'dziko la adani anu. Pamenepo nthaka idzapuma ndi kukondwerera zaka zopumazo. Nthaŵi zonse pamene dzikolo lilibe anthu, nthaka idzapuma, kupuma kwake kumene sidapumepo pa zaka zonse pamene inu munkakhalamo. Ndipo ngakhale ena amene mudzatsalenu, ndidzaika mtima wa mantha mwa inu pamene muli m'dziko la adani anu. Mtswatswa wa tsamba louluka udzakuthaŵitsani. Mudzathaŵa monga m'mene munthu amathaŵira lupanga, ndipo mudzagwa pansi popanda okuthamangitsani. Mudzaphunthwitsana monga ngati mukuthaŵa nkhondo, ngakhale palibe amene akukupirikitsani. Ndipo simudzakhala ndi mphamvu zoti mulimbane ndi adani anu. Mudzatha, kuchita kuti psiti, pakati pa mitundu ya anthu, ndipo dziko la adani anu lidzakudyani. Ngakhale ena amene mudzatsalenu, nanunso mudzazunzika m'dziko la adani anu chifukwa cha machimo anu, ndipo mudzazunzikanso chifukwa cha machimo a makolo anu. ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake, ndipo nthaka idzakubalirani zokolola zochuluka, ndipo mitengo yam'minda idzakubalirani zipatso.
Anthu anjala amamdyera zokolola zake, amamtengera ndi zapaminga zomwe. Anthu akhwinthi amafunkha chuma chake.
“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Chauta adalumbira motsimikiza, ndipo adzasunga malumbirowo ndi mphamvu zake. Adati, “Adani ako sadzadyanso tirigu wako, ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako. Koma inu amene mudabzala ndi kukolola tiriguyo, ndiye amene mudzadye buledi, ndipo mudzatamanda Chauta. Inu amene munkasamala mitengo yamphesa ndi kumathyola mphesa, ndiye amene mudzamwe vinyo m'mabwalo a Nyumba yanga.”
Sadanenepo m'mitima mwao kuti, ‘Tiyeni tizimvera Chauta Mulungu wathu, amene amatipatsa mvula pa nthaŵi yake, mvula yachizimalupsa ndi yam'masika. Ndipo salephera kutipatsa nthaŵi ya kholola.’ ”
Mdani wodzafesa namsongole uja ndi Satana. Kudula kuja nkutha kwake kwa dziko lino lapansi, ndipo odula aja ndi angelo.
Mudzifesere m'chilungamo, ndipo mudzakolola madalitso a chikondi changa chosasinthika. Tipulani tsala lanu pakuti nthaŵi yofunafuna Chauta yakwana. Funafunani Chautayo mpaka atabwera kudzakugwetserani mvula ya madalitso.
Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri chikhale chaka chopumuza nthaka, chaka chopatulikira Chauta, ndipo musalime minda yanu kapena kuthenera mitengo yanu yamphesa. Akhale ngati wantchito wako, ndiponso ngati mlendo wako. Azikugwirira ntchito mpaka chaka chokondwerera zaka 50. Pambuyo pake achoke kwa iwe, pamodzi ndi ana ake omwe, apite ku banja lake, ndi kubwerera ku choloŵa cha makolo ake. Aisraele ndi atumiki anga amene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, asagulitsidwe ngati akapolo. Usaŵalamule mwankhalwe, koma uziwopa Mulungu wako. Kunena za akapolo aamuna kapena aakazi oti muzikhala nawo, mungathe kuŵagula kwa mitundu ina ya anthu okuzungulirani. Mungathenso kuŵagula pakati pa alendo amene akukhala pakati panu ndiponso pakati pa mabanja okhala nanu amene adabadwira m'dziko mwanu. Amenewo angathe kukhala anu. Akapolowo mungathe kuŵasiya m'manja mwa ana anu, inu mutafa, kuti akhale choloŵa chao nthaŵi zonse. Amenewo mungathe kuŵayesa akapolo, koma abale anu Aisraele musaŵalamule mwankhalwe. “Mlendo kapena munthu wodzangokhala nanu akalemera, ndipo mbale wanu wokhala naye pafupi akakhala wosauka, nadzigulitsa yekha kwa mlendoyo kapena kwa munthu wodzangokhala nanu uja, kapena kwa aliyense wa banja la mlendolo, mbale wanu wodzigulitsayo angathe kuwomboledwa. Wina mwa abale ake angathe kumuwombola, kapena mbale wa bambo wake, kapena mwana wa mbale wa bambo wake, kapena wachibale wa pabanja pake, onseŵa angathe kumuwombola. Koma wodzigulitsayo akalemera, angathe kudziwombola yekha. Musakolole zimene zidamera zokha m'munda mwanu, ndipo musathyole mphesa za mitengo yanu yosathenera. Chaka chimenechi chikhale chopumuza nthaka.
Ndakupatsani mafuta onse abwino kopambana, vinyo yense ndi mbeu zonse zabwino kwabasi, ndi zipatso zonse zoyamba zimene anthu amapereka kwa Chauta. Mwa zinthu zonse za m'dziko mwako, zipatso zoyambirira kupsa zimene amapereka kwa Chauta, zimenezo zikhale zanu. Munthu aliyense wosaipitsidwa m'nyumba mwanu angathe kudyako.
Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha Masika pokolola mbeu zoyamba zochokera ku zobzala zanu. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pa chaka, pamene muika m'nkhokwe dzinthu dzanu dzonse.
Mukamakolola dzinthu m'minda mwanu, zina pang'ono nkuiŵalika, musabwerere kukatenga zoiŵalikazo. Zimenezo muzisiyire alendo okhala nanu, ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.
Muzichita chikondwerero cha masabata, ndi chikondwerero cha kukolola tirigu woyambirira, ndi chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pake pa chaka.
Tsono mbeuzo zikacha, munthu uja amatenga mpeni wodulira, pakuti nyengo yokolola yafika.”
Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo akukondwa pamaso panu monga m'mene anthu amakondwera nthaŵi ya masika, monganso m'mene anthu amakondwera pogaŵana zofunkha.
“Samulani zenga wodulira tirigu, pakuti mbeu zacha kale kudikira kholola. Bwerani, dzapondeni mphesa, poti mopondera mphesa mwadzaza, ndipo mbiya zikusefukira. Chonchonso zolakwa za mitundu ina ya anthu zachuluka zedi.”
“Nthaŵi zonse m'mene dziko lapansi lidzakhalire, padzakhala nyengo yobzala ndi nyengo yokolola. Padzakhala nyengo yachisanu ndi nyengo yotentha, nyengo yachilimwe ndi nyengo yadzinja, ndipo usana ndi usiku zidzakhalapo kosalekeza.”
Kwa anthu amene amtuma, wamthenga wokhulupirika ali ngati madzi ozizira pa nthaŵi yotentha, amaziziritsa mtima wa mbuyake.
Zilekeni zikulire pamodzi zonse mpaka nyengo yodula. Pa nthaŵi imeneyo ndidzauza odula kuti, Yambani mwazula namsongole, mummange m'mitolo kuti mukamtenthe. Kenaka musonkhanitse tirigu ndi kukamthira m'nkhokwe yanga.’ ”
Mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu nafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala pamtamboyu. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chako, yambapo kudula dzinthu. Tsopano nyengo yamasika yafika, ndipo dzinthu dza pa dziko lapansi dzidacha kale.”
Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.
“Muzigwira ntchito pa masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, musagwire ntchito iliyonse, ngakhale pa nthaŵi yolima kapena yokolola. Muzichita chikondwerero cha masabata, ndi chikondwerero cha kukolola tirigu woyambirira, ndi chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pake pa chaka.
Munthu woipa amalandira malipiro achabechabe, koma wochita zolungama amalandira mphotho yeniyeni.
Mumati zikule tsiku lomwe mwabzalalo, mumati zituluke maluŵa m'maŵa momwe mwazibzalamo, komabe zimene mudzakololezo zidzatha pa tsiku lamavuto, ndipo mazunzo ake adzakhala osatha.
Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino, ndipo zidabereka. Ngala zina zinali ndi njere makumi khumi, zina makumi asanu ndi limodzi, zina makumi atatu.”
Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.
Muzidzatamanda Chauta, Mulungu wanu, pochita chikondwerero chimenechi masiku asanu ndi aŵiri, pa malo amene Iye adzasankhule, chifukwa chakuti Chauta, Mulungu wanu, adzakhala atadalitsa kholola lanu ndi ntchito zanu zonse, kuti chimwemwe chanu chikhale chodzaza ndithu.
Tsono abale, khazikani mtima pansi mpaka Ambuye adzabwere. Onani m'mene amachitira mlimi. Amadikira kuti zipatso zokoma ziwoneke m'munda mwake. Amangoyembekeza mokhazika mtima kuti zilandire mvula yachizimalupsa ndi yachikokololansanu.
Ineyo ndidabzala mbeu, Apolo nkuzithirira, koma amene adazimeretsa ndi Mulungu. Motero wobzala kapenanso wothirira sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amameretsa, ndiye ali kanthu. Tsono wobzala sasiyana ndi wothirira, ndipo aliyense adzalandira mphotho yake molingana ndi ntchito imene adaigwira.
Koma mbeu zofesedwa pa nthaka yabwino zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu naŵamvetsa. Munthu wotere amaberekadi zipatso, mwina makumi khumi, mwina makumi asanu ndi limodzi, mwina makumi atatu.”
Mlimi wogwira ntchitoyo molimbika, ndiye ayenera kukhala woyamba kulandira nao zipatso.
Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa.
Koma mbeu zogwera pa nthaka yabwino zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, naŵasunga mu mtima woona ndi wabwino, ndipo amalimbikira mpaka kubereka zipatso.”
Isaki adabzala mbeu m'dzikomo, ndipo chaka chimenecho adakolola dzinthu dzochuluka koposa, chifukwa Chauta adaamudalitsa.
“Mvula ndi chisanu chambee zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko, koma zimathirira nthaka. Zimameretsa ndi kukulitsa zomera, kenaka nkupatsa alimi mbeu ndi chakudya. Ndimonso amachitira mau ochokera m'kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidaŵatumira zidzayenda bwino.
Mudzalimanso minda yamphesa pa mapiri a Samariya. Alimi adzabzala mphesa ndipo adzadya zipatso zake.
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene mlimi adzabzola wokolola, ndipo woponda mphesa adzabzola wobzala mbeu. M'mapiri mudzatuluka vinyo wokoma, azidzachita kuyenderera pa zitunda zonse.
Adzakukondani ndi kukudalitsani, kotero kuti mudzachuluka ndi kubereka ana ambiri. Minda yanu adzaidalitsa, kotero kuti tirigu, vinyo ndi mafuta, mudzakhala nazo zonsezo. Adzakudalitsaninso pa zoŵeta pokupatsani ng'ombe zambiri ndi zoŵeta zina zomwe. Madalitso onseŵa, adzakupatsani muli m'dziko limene adalonjeza makolo anu.
Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali.
Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino. Zidamera bwino nkukula, ndipo zidabereka. Ngala zina zinali ndi njere makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi, zina makumi khumi.”
Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaafesa mbeu zabwino m'munda mwake. Koma anthu onse ali m'tulo, mdani wake adabwera, nkufesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. Tsono pamene mmera udakula nkuyamba kuchita njere, namsongole uja nayenso adayamba kuwoneka. Antchito a mwinimunda uja adadzamufunsa kuti, ‘Bwana, kodi suja mudaafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga bwanji mukuwonekanso namsongole?’ Iye adaŵayankha kuti, ‘Ndi mdani amene wachita zimenezi.’ Antchito aja adamufunsa kuti, ‘Bwanji tikamzule?’ Koma iye adati, ‘Iyai, mungakazulire kumodzi ndi tirigu pozula namsongoleyo. Yesu adalankhula nawo zambiri m'mafanizo. Adati, “Munthu wina adaapita kukafesa mbeu. Zilekeni zikulire pamodzi zonse mpaka nyengo yodula. Pa nthaŵi imeneyo ndidzauza odula kuti, Yambani mwazula namsongole, mummange m'mitolo kuti mukamtenthe. Kenaka musonkhanitse tirigu ndi kukamthira m'nkhokwe yanga.’ ”
Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”
Anthu adzakondwa kwambiri chifukwa adzakhala ndi madzi ambiri, ndipo abulu ndi ng'ombe zao azidzadya paliponse.
Mudzabzala, koma simudzakolola, Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzaŵadzola. Mudzaponda mphesa, koma vinyo wake simudzamulaŵa.
“Inu anthu a ku Ziyoni, kondwani ndi kusangalala chifukwa cha zimene Chauta, Mulungu wanu, wakuchitirani. Wakukomerani mtima pokupatsani mvula mofulumira. Wakupatsani mvula yochuluka, kumayambiriro ndi kumathero, monga pa masiku amekedzana. “Pa malo opunthira padzadzaza tirigu. Mopondera mphesa mudzasefukira vinyo watsopano, mafutanso adzachuluka.
Wolima munda wake mwakhama amapeza chakudya chambiri, koma wotsata zopanda pake ngwopanda nzeru.
Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”
Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.
Waulesi sasoseratu pa nthaŵi yoyenera. Pa nthaŵi yokolola adzafunafuna dzinthu, koma sadzapeza kanthu.
Chopetera chake chili m'manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m'nkhokwe, koma mankhusu adzaŵatentha m'moto wosazimika.”
Tsiku limenelo Chauta mwini wake adzasonkhanitsa anthu ake mmodzimmodzi, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Ejipito.
Kunena zoona, mbeu ya tirigu imakhalabe imodzi yomweyo ngati siigwa m'nthaka nkufa. Koma ikafa, imabala zipatso zambiri.
“Muzibzala mbeu zaka zisanu ndi chimodzi m'munda mwanu, ndi kumakolola mbeuzo. Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.
Kopanda ng'ombe, kumakhalanso kopanda dzinthu, koma kwa ng'ombe zamphamvu, dzinthu dzimachuluka.
Zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi. Angelo adzabwera nadzachotsa anthu ochimwa pakati pa anthu olungama,
Paja Malembo akuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe imene ikupuntha tirigu.” Penanso akuti, “Wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake.”
Yesu adaŵaphera fanizo, adati, “Munthu wina anali ndi mkuyu wobzalidwa m'munda wake wamphesa. Adakafunamo zipatso, koma osazipeza. Tsono adauza wosamala mundawo kuti, ‘Papita zaka zitatu tsopano ndikufuna zipatso mu mkuyu uwu, koma osazipeza. Udule tsono. Ukugugitsiranji nthaka?’ Koma iye adati, ‘Ambuye, baulekani chaka chino chokha. Ndiukumbira pa tsinde nkuuthira manyowa. Ukadzabala zipatso chaka chamaŵa, zidzakhala bwino. Koma ukakapanda kubala, apo mudzaudule.’ ”
Ntamuimbirako bwenzi langa nyimbo yokamba za wokondedwa wanga ndi munda wake wamphesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa pa phiri la nthaka yachonde. Munda wamphesa wa mahekitara khumi, vinyo wake adzangodzaza mbiya imodzi. Kufesa madengu khumi a mbeu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.” Tsoka kwa amene amadzuka m'mamaŵa nathamangira chakumwa choledzeretsa, amene amamwa mpaka usiku kufikira ataledzera kotheratu. Amangoimba zeze, pangwe, ng'oma ndi chitoliro, nkumamwa vinyo pa maphwando ao. Koma sasamala ntchito za Chauta, sapenya ntchito za manja ake. Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo chifukwa cha kusamvetsa zinthu. Atsogoleri ao olemekezeka adzafa ndi njala, ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu. Nchifukwa chake kumanda sikukhuta, kwangoti kukamwa yasa kuti kulandire aliyense. Anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka, adzagweramo ali wowowo, m'kuledzera kwaoko. Munthu aliyense adzatsitsidwa, onse adzachepetsedwa, anthu odzikuza adzaŵachititsa manyazi. Koma Chauta Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chilungamo chake, Mulungu Woyera adzaonetsa kuyera kwake pochita zaungwiro. Tsono anaankhosa adzadya pamenepo ngati pabusa pao, ndipo anaambuzi adzadya m'mabwinja. Tsoka kwa amene amadzikokera machimo ambiri ndi kunama kwao, amene amalephera kudzimasula ku machimo awo. Amanena kuti, “Chauta afulumire, agwire ntchito yake mwamsanga, kuti ntchitoyo tiiwone. Zimene Woyera uja wa Israele afuna kuchita, zichitiketu kuti tizidziŵe.” Adautipula nachotsa miyala yonse, ndipo adaokamo mipesa yabwino kwabasi. Adamanga nsanja pakati pa mundawo, nasema mopondera mphesa m'kati momwemo. Adaayembekeza kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ai, udabala mphesa zachabechabe.
“Ndinenso amene ndidamanga mvula patangotsala miyezi itatu kuti mukolole. Ndine amene ndinkagwetsa mvula pa mudzi wina, koma pa mudzi wina ai. Mvula inkagwa pa munda wina, koma munda wina nkumakhala gwa, chifukwa chosoŵa mvula.
Pamenepo adauza mtengowo kuti, “Mtengo iwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya wina aliyense asadzadyekonso zipatso zako.” Mau ameneŵa ophunzira ake aja adaŵamva.
Anthu adafesa tirigu, koma adakolola minga. Adadzitopetsa pogwira ntchito, koma osapindula nkanthu komwe. Zokolola zao nzochititsa manyazi, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Chauta.”
Khalani m'nyumba yomweyo. Mudye ndi kumwa zimene akupatsani, pakuti wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake. Musamachoka kumene mwafikirako nkukaloŵa ku nyumba zina ai.
Kalanga ine! Ndasanduka ngati wokunkha wosapeza zotsalira. Sipadatsalenso mphesa zoti nkudya. Sipadatsaleko nkhuyu zimene ndimazikonda.
“Musachedwe kundipatsa zopereka zotapa pa zokolola zanu zambiri ndiponso pa vinyo wanu wochuluka. “Mundipatse ana anu achisamba aamuna.
Ngakhale mwana yemwe amadziŵika ndi ntchito zake, kuti zimene amachitazo ndi zabwino ndi zolungama.
“Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu. Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu?
Iwo ali ngati mbeu zobzala posachedwa, kapena zofesa chatsopano, zongoyamba kumene kuzika mizu. Mbeuzo Chauta akaombetsa mphepo zimauma, ndipo mkuntho umaziwulutsa ngati mankhusu.
Okolola ayamba kale kulandira malipiro, ndipo akututira mbeu ku moyo wosatha, kuti obzala ndi okolola akondwere pamodzi. Paja amanenadi zoona aja amati, ‘Wobzala ndi wina, wokolola ndi winanso.’ Ine ndidakutumani kukakolola mbeu zimene simudagwirirepo ntchito. Anthu ena ndiwo adagwira ntchito, inu mwangolandirapo phindu la ntchito yaoyo.”
Kodi sankanena zimenezi makamaka chifukwa cha ife? Adazilembadi chifukwa cha ife, pakuti wolima ndiponso wopuntha, onsewo amagwira ntchito yao ndi chiyembekezo chakuti nawonso adzalandirako kanthu pa zokolola.
pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo.
Mau a Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Akunkheni ndi kuŵalanda zonse anthu otsala a Aisraele, monga momwe anthu amachitira, populula mphesa ku nthambi zake.”
“Uza Aisraele kuti, ‘Mukakaloŵa m'dziko limene ndikukupatsanilo ndi kukakolola za m'minda mwanu, mudzabwere kwa wansembe ndi mtolo wa zoyambirira kucha mwa zokolola zanu.
Ndinkakuwopani, popeza kuti ndinu munthu wankhwidzi. Mumalonjerera zimene simudaikize, ndiponso mumakolola zimene simudabzale.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa, ndikutsutsa ndi mau ako omwe. Kani unkadziŵa kuti ndine munthu wankhwidzi, amene ndimalonjerera zimene sindidaikize, ndipo ndimakolola zimene sindidabzale. Nanga bwanji osaiika ku banki ndalama yangayo, kuti ine pobwera ndiilandire pamodzi ndi chiwongoladzanja chake?’
Antchito okolola m'minda mwanu simudaŵalipire. Ndalama zamalipirozo zikulira mokutsutsani. Ndipo kufuula kwa okololawo kwamveka m'makutu a Chauta Mphambe.
Nchifukwa chake ndidzaŵalanga koopsa mwaukali. Mkwiyo wanga udzagwera Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi mbeu zomwe. Mkwiyowo udzayaka ngati moto wosazimika.”
Tsono Yesaya adauza mfumu Hezekiya kuti, “Chizindikiro cha zimene zidzachitika ndi ichi: Chaka chino mudzadya tirigu wa mphulumukwa. Chaka chamaŵa mudzadya tirigu wongodzimerera. Tsono chaka chamkucha mudzabzala tirigu ndi kukolola, mudzaoka mitengo yamphesa nkudya zipatso zake.
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
Aliyense amene akupatsani chikho cha madzi chifukwa chakuti ndinu ake a Khristu, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
“Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m'munda. Munthu wina atachitumba, amachibisanso. Kenaka mokondwa amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula munda uja.
M'dziko mukhale chakudya chambiri, pamwambanso pa mapiri pakhale dzinthu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni, anthu ake achuluke m'mizindamo ngati udzu wakuthengo.
Yesu adaŵauza kuti, “Koma tsopano amene ali ndi thumba la ndalama, asalisiye. Chimodzimodzinso thumba lake lapaulendo. Ndipo amene alibe lupanga, agulitse mwinjiro wake nkugula lupanga.
Chauta adzadalitsa ntchito zanu, ndipo nkhokwe zanu zidzadzaza. Adzakudalitsani m'dziko limene akukupatsanilo.
M'maŵa uzifesa mbeu zako, ndipo madzulo usamangoti manja lende. Sudziŵa chimene chidzapindula, kaya ndi ichi kaya ndi chinachi, mwinanso ziŵiri zonsezo zitha kukhala zabwino.
“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaalaŵirira m'mamaŵa kukalemba anthu okagwira ntchito m'munda wake wamphesa. Tsono pamene olembedwa poyamba aja adabwera, ankaganiza kuti alandira pakulu. Koma nawonso adangolandira aliyense ndalama imodzi. Ndiye iwowo polandira, adayamba kuŵiringula, adati, ‘Aa! Anzathu otsiriziraŵa angogwira ntchito kanthaŵi pang'ono, bwanji mwaŵapatsa malipiro olingana ndi athu, pamene ifeyo tathyoka nayo ntchito tsiku lathunthu, ndi chidzuŵa chonse chija?’ Koma mwinimunda uja adayankha mmodzi mwa iwo kuti, ‘Iwe, inetu sindidakubere ai. Kodi suja tinapangana ndalama yasiliva imodzi? Tenga malipiro ako, uzipita. Mwiniwakene ndafuna kuti ndipatse wolembedwa potsirizayu molingana ndi iwe. Kodi zinthu zanga ndisachite nazo monga ndifunira? Kapenatu ukuipidwa nawo ufulu wanga eti?’ ” Tsono Yesu adati, “Choncho amene ali oyambirira adzakhala otsirizira. Ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.”
Kodi mlimi wofuna kubzala amangokhalira kutipula kokhakokha? Kodi amangokhalira kugaula ndi kugalauza? Akasalaza mundawo, suja amafesa maŵere ndi chitoŵe? Suja amafesa tirigu ndi barele m'mizere, nabzala mcheŵere m'mphepete mwa mundawo?
“Muzikhala ndi tsiku lachikondwerero katatu pa chaka, kuti mundilemekeze Ine. Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha Masika pokolola mbeu zoyamba zochokera ku zobzala zanu. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pa chaka, pamene muika m'nkhokwe dzinthu dzanu dzonse.
“Pamene muloŵa m'dzikomo ndi kubzala mitengo yamitundumitundu ya zipatso, zipatsozo zikhale zoletsedwa. Zikhale zoletsedwa kwa inu zaka zitatu, musadye pa nthaŵi imeneyo. Pa chaka chachinai, zipatso zonse zidzakhala zopatulikira Chauta ngati nsembe yomtamandira. Koma pa chaka chachisanu mudzatha kudya zipatso zake, kuti choncho mitengoyo idzakubalireni kwambiri. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
Adafesa mbeu m'minda, namaoka mipesa, ndipo adakolola dzinthu dzambiri. Chifukwa cha madalitso a Chauta, anthuwo adachuluka kwambiri, Chauta sadalole kuti zoŵeta za anthuwo zichepe.