Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


107 Mau a m'Baibulo Okhulupirira Kubwezera

107 Mau a m'Baibulo Okhulupirira Kubwezera

M’malemba Oyera muja, tikuphunzitsidwa kuti kubwezera sikuli kwathu ife anthu, koma ndi kwa Mulungu yekha.

Mu Aroma 12:19, Baibulo limatiuza momveka bwino kuti, “Musabwezere choipa ndi choipa, okondedwa anga, koma patukani mtima; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.” Izi zikutanthauza kuti sitiyenera kutenga chilungamo m’manja mwathu, koma kudalira Mulungu yekha amene angachigwiritse ntchito mwachilungamo.

Tikapwetekedwa kapena kuchitiridwa zoipa, n’zachibadwa kuti mtima wathu uzifuna kubwezera. Komabe, Baibulo limatilimbikitsa kudalira Mulungu ndi kukhululukira m’malo mofuna kubwezera. Monga mmene lemba la Miyambo 20:22 limatiuzira, “Usanene, Ndidzabwezera choipa; dikira Yehova, ndipo adzakupulumutsa iwe.”

Kubwezera kungawoneke ngati njira yobwezeretsera ulemu wathu kapena kuyika chilungamo pamalo pake. Koma Baibulo limatiphunzitsa kuti si udindo wathu kufuna kubwezera. M’malomwake, tiyenera kudalira mphamvu ndi nzeru za Mulungu kuti achite chilungamo pa nthawi yake yoyenera.

Tikasiya kubwezera ndi kutsatira ziphunzitso za m’Baibulo, timapeza ufulu weniweni ndi kuona mphamvu ya chikondi ndi chisomo cha Mulungu m’miyoyo yathu.




Masalimo 94:1-2

Inu Chauta, ndinu Mulungu wolipsira, Inu Mulungu wolanga, dziwonetseni. Kodi wolangiza mitundu ya anthu, sangathe kulanga? Kodi wophunzitsa anthu onse, alibe nzeru? Chauta amadziŵa maganizo a anthu kuti ndi mpweya chabe. Inu Chauta, ngwodala munthu amene mumamlangiza, amene mumamphunzitsa ndi malamulo anu. Mumampumitsa pa nthaŵi yamavuto, mpaka woipa ataloŵa m'dzenje. Chauta sadzaŵataya anthu ake, sadzaŵasiya okha osankhidwa ake. Chilungamo chidzaŵabwereranso kwa anthu ake, ndipo onse oongoka mtima adzachitsata. Ndani amalimba mtima kuti andimenyere nkhondo ndi anthu oipa? Ndani amaimira mbali yanga, kuti alimbane ndi anthu ochita zoipa? Chauta akadapanda kundithandiza, bwenzi posachedwa nditapita ku dziko lazii. Pamene ndinkaganiza kuti, “Phazi langa likuterereka,” nkuti chikondi chanu chosasinthika chikundichirikiza. Pamene nkhaŵa zikundichulukira, Inu mumasangalatsa mtima wanga. Dzambatukani, Inu Muweruzi wa dziko lapansi, apatseni anthu onyada zoŵayenerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:18

Musabwezere choipa, ndipo musakwiyire anthu a mtundu wanu, koma mukonde mnzanu monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:35

Kulipsira nkwanga, kubwezera zoyenerera nkwanganso, nthaŵi yoti agwe idzakwana. Tsiku la masoka ao layandikira, chiwonongeko chao chikudza mofulumira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:43

Inu mitundu yonse ya anthu, tamandani anthu a Chauta. Chauta amalanga onse opha anthu ake, amalipsira adani ake, ndipo amachotsa tchimo m'dziko la anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:9

Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:22

Usamanena kuti, “Ndidzabwezera choipa ndine.” Udikire Chauta, ndipo adzakuthandiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:17-20

Usamakondwerera kugwa kwa mdani wako, mtima wako usamasangalala iyeyo akaphunthwa. Ukatero Chauta adzaziwona zimenezo nadzaipidwa nazo, kenaka adzaleka kumkwiyira mdani wakoyo. Usamavutika chifukwa cha anthu ochita zoipa, usachite nawo nsanje anthu oipa. chifukwa mitima yao imalingalira zandeu, ndipo pakamwa pao pamalankhula zoutsa mavuto. Pajatu munthu woipa zinthu sizidzamuyendera bwino m'tsogolo, moyo wa anthu oipa adzauzima ngati nyale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:29

Usamanena kuti, “Ndidzamchitira monga momwe iye wandichitira ine, ndidzamlipsira chifukwa cha zomwe iye wandichitira ine.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nahumu 1:2-3

Chauta ndi Mulungu wansanje ndiponso wolipsira. Chauta amalanga, ndipo ndi wamkali. Chauta amalipsira amaliwongo ake amakwiyira adani ake. Chauta ndi wamphamvu zedi. Ndi wosakwiya msanga, komabe sadzalola kuti munthu wochimwa akhale wosalangidwa. Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu ndi mphepo yamkuntho, mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:44

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:38-39

“Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Diso kulipa diso, dzino kulipa dzino.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu woipa osalimbana naye. Ngati munthu akumenya pa tsaya la ku dzanja lamanja, upereke linalonso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:17-18

Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 11:25

Ndipo pamene mukuti mupemphere, muziyamba mwakhululukira mnzanu ngati muli naye nkanthu. Mukatero, Atate anunso amene ali Kumwamba adzakukhululukirani machimo anu.” [

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:27-28

“Koma inu amene mukumva mau anga, ndikukuuzani kuti, Muzikonda adani anu, muziŵachitira zabwino amene amadana nanu. Muziŵafunira madalitso amene amakutembererani, muziŵapempherera amene amakuvutitsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:17-18

Usamakondwerera kugwa kwa mdani wako, mtima wako usamasangalala iyeyo akaphunthwa. Ukatero Chauta adzaziwona zimenezo nadzaipidwa nazo, kenaka adzaleka kumkwiyira mdani wakoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:30

Paja tikumdziŵa kale amene adati, “Kulipsira nkwanga, ndidzakhaulitsa ndine.” Adatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:14

Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:1

Inu Chauta, ndinu Mulungu wolipsira, Inu Mulungu wolanga, dziwonetseni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:19

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:15

Onetsetsani kuti wina aliyense mnzake akamchita choipa, asabwezere choipacho. Koma nthaŵi zonse muziyesetsa kuchitira zabwino anzanu ndi anthu ena onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 13:11

Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:7

“Anthu adamsautsa ndi kumzunza, koma iye sadalankhule kanthu. Monga momwe amachitira mwanawankhosa wopita naye kuti akamuphe, ndiponso monga momwe nkhosa imakhalira duu poimeta, nayenso adangokhala chete.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 26:10-11

Ndipo adalamulira kuti, “Pali Chauta wamoyo, Chautayo ndiye adzamkanthe kapena pamene lidzafike tsiku lake lakumwalira, kapena pamene adzapite ku nkhondo nakaphedwa. Chauta andiletse kuti ndisapweteke wodzodzedwa wake. Koma tsono tingotenga mkondo umene uli kumutu kwakewu ndi mtsuko wa madziwu, ndipo tizipita.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 4:15

Koma Chauta adamuyankha kuti, “Iyai, aliyense wopha iwe Kaini adzalangidwa, ndipo Ineyo ndidzamulipsira kasanunkaŵiri.” Motero Chauta adaika chizindikiro pa Kaini kuchenjeza aliyense kuti asamuphe Kainiyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:21-22

Mdani wako akakhala ndi njala, umpatse chakudya, akamva ludzu, umpatse madzi akumwa. Potero udzamchititsa manyazi aakulu, ndipo Chauta adzakupatsa mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:8-9

Lewa kupsa mtima ndi kukwiya. Usachite zimenezi, pakuti sudzapindula nazo kanthu. Pajatu anthu oipa adzaonongeka, koma okhulupirira Chauta adzalandira dziko kuti likhale lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:10-12

Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze. Paja Malembo akunena kuti, “Ambuye akuti, ‘Pali Ine ndemwe, anthu onse adzandigwadira ndi kuvomereza kuti ndine Mulungu.’ ” Motero aliyense mwa ife adzadzifotokozera yekha kwa Mulungu zimene adazichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:52

Apo Yesu adamuuza kuti, “Bwezera lupangalo m'chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzaphedwa ndi lupanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 35:1

Inu Chauta, mulimbane nawo anthu olimbana nane, Mumenyane nawo omenyana nane.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 7:11-13

Mulungu ndiye muweruzi wolungama, amalanga anthu oipa nthaŵi zonse. Ngati munthu salapa, Mulungu adzanola lupanga lake, adzakunga ndi kukoka uta wake. Wakonza zida zake zoopsa, waika mivi yamoto ku uta wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 1:6-8

Paja Mulungu mwa chilungamo chake, adzaŵalanga ndi masautso anthu amene amakusautsani inu. Koma inu amene mukusauka tsopano, adzakupatsani mpumulo pamodzi ndi ife tomwe. Adzachita zimenezi, Ambuye Yesu akadzabwera kuchokera Kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu. Adzabwera ndi moto woyaka, nadzalanga anthu amene sadziŵa Mulungu, ndi amene sadamvere Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:7

Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Chauta, ngakhale adani ake omwe amakhala naye mwamtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 35:4

Muuze onse a mtima wamantha kuti, “Limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:5

Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 23:34

Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:4

pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:4-5

“Ukaona ng'ombe ya mdani wako ikusokera, kapena bulu wake, utenge ukampatse. Bulu wa mdani wako akagwa ndi katundu, usabzole ndi kumsiya, koma umthandize kuti adzuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:12

Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10-11

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa. Motero onse amene akukupsera mtima adzachita manyazi ndi kunyazitsidwa. Amene akumenyana nawe adzakhala ngati salinso kanthu, ndipo adzafa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:1-2

Usamavutika ndi anthu oipa. Usamakhumbira kukhala ngati ochita zoipa, Kanthaŵi pang'ono ndipo munthu woipa sadzakhalaponso, ngakhale muyang'ane bwino pamalo pamene analiri, simudzampezapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka. Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino, namamtuzulira maso mwachidani. Koma Chauta amamseka munthu woipayo, poti amaona kuti tsiku lake la kuwonongeka likubwera. Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama. Koma lupanga lao lidzalasa mitima ya eniake omwewo, ndipo mauta ao adzaŵathyokera m'manja. Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka, kupambana kukhala nazo zokoma zambiri zimene munthu woipa ali nazo. Pakuti Chauta adzathetsa mphamvu za anthu oipa, koma adzalimbikitsa anthu onse abwino. Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya. Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka. pakuti mosachedwa amanyala ngati udzu, ndipo amafota ngati masamba aaŵisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:29

Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:19-20

Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso. Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:1

Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo, koma mau ozaza amakolezera ukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:27-29

Tsono leka zoipa, ndipo chita zabwino, motero udzakhala pa mtendere mpaka muyaya. Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa. Anthu a Mulungu adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala m'menemo mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:47-48

Mulungu ndiye adandithandiza kuti ndilipsire, adagonjetsa anthu a mitundu ina, kuti akhale mu ulamuliro wanga. Ndiye amene adandipulumutsa kwa adani anga. Zoonadi Inu mudandikweza pamwamba pa ondiwukira, mudandilanditsa kwa anthu ankhanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:84-86

Kodi mtumiki wanune ndipirire mpaka liti? Kodi anthu ondizunza mudzaŵalanga liti? Anthu osasamala za Mulungu, osatsata malamulo anu, andikumbira mbuna. Malamulo anu onse ndi osasinthika. Anthuwo amandizunza ndi mabodza ao; thandizeni!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:13

Munthu akamabwezera zoipa kwa zabwino, tsoka silidzachoka pabanja pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:14-15

“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:18

Munthu wopsa mtima msanga amautsa mkangano, koma munthu woleza mtima amabweretsa mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:23

Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sadabwezere chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 14:14

Chauta ndiye amene akumenyereni nkhondo. Inuyo simuchitapo kanthu konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:8

Uzingopenya ndi maso ako, ndipo udzaona m'mene amalangidwira anthu ochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:1-2

Usamachitira nsanje anthu ochimwa, kapena kumalakalaka kuti uzimvana nawo, Ukataya mtima pamene upeza zovuta, ndiye kuti mphamvu zako ndi zochepa. Uŵapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe. Uŵalanditse amene akuyenda movutikira popita kukaŵapha. Ukanena kuti, “Ife sitidazidziŵe zimenezi,” kodi iye amene amayesa mtima, zimenezi saziwona? Kodi amene amayang'anira moyo wako sazidziŵa? Kodi sadzambwezera munthu potsata ntchito zake? Mwana wanga, uzidya uchi poti ndi wabwino, madzi a m'chisa cha njuchi ndi ozuna ukaŵalaŵa. Udziŵe kuti nzeru ndi yoteronso mumtima mwako. Ukaipeza, zinthu zidzakuyendera bwino m'tsogolo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe. Nyumba ya munthu wabwino usaichite zachifwamba ngati munthu woipa mtima, usachite nayo nkhondo nyumba yake. Munthu wabwino amagwa kasanunkaŵiri, koma amadzukirira ndithu, m'menemo anthu oipa tsoka limaŵagwera chonse. Usamakondwerera kugwa kwa mdani wako, mtima wako usamasangalala iyeyo akaphunthwa. Ukatero Chauta adzaziwona zimenezo nadzaipidwa nazo, kenaka adzaleka kumkwiyira mdani wakoyo. Usamavutika chifukwa cha anthu ochita zoipa, usachite nawo nsanje anthu oipa. chifukwa mitima yao imalingalira zandeu, ndipo pakamwa pao pamalankhula zoutsa mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 31:29-30

“Sindidakondwerere kuwonongeka kwa mdani wanga. Sindidasekere tsoka litamgwera. Wosalungama tsoka limamgwera, wochita zoipa amaonongeka. Sindidachimwe ndi pakamwa panga, potemberera mdani wanga kuti aonongeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:3-4

Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke. “Tsiku limenelo, amene ali pa denga, asadzatsike kukatenga katundu wake m'nyumba. Chimodzimodzinso amene ali ku munda, asadzabwerere ku nyumba. Kumbukirani za mkazi wa Loti. Aliyense woyesa kudzisungira moyo wake, adzautaya, koma woutaya adzausunga. Kunena zoona, usiku umenewo, padzakhala anthu aŵiri pa bedi limodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Azimai aŵiri adzakhala akusinja pamodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya, Anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.” Apo ophunzira ake adamufunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti, Ambuye?” Yesu adati, “Kumene kwafera chinthu, nkumeneko kumasonkhana miphamba.” Akakuchimwira kasanunkaŵiri pa tsiku, nabwera kasanunkaŵiri kudzanena kuti, ‘Pepani,’ umkhululukire ndithu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:26-27

Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:17

Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 10:3-4

Ndi zoona kuti ndife anthu, koma sitimenya nkhondo motsata za anthu chabe. Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:22

Koma mukamvera iyeyo ndi kuchita zonse zimene ndinena, Ineyo ndidzadana ndi adani anu, ndipo onse amene atsutsana nanu ndidzalimbana nawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:4-5

M'malo mwa chikondi changa, iwo amandibwezera zondineneza, ngakhale pamene ndikuŵapempherera. Motero amandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino, amandiwonetsa chidani m'malo mwa chikondi changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:21-22

Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:29

Ngati munthu akumenya pa tsaya, uperekere linalonso. Ndipo munthu akakulanda mwinjiro wako, umlole atenge ndi mkanjo womwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:23

Adzaŵalanga chifukwa cha machimo ao, adzaŵaononga chifukwa cha kuipa kwao, zoonadi, Chauta, Mulungu wathu, ndiye amene adzaŵafafanize.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:15

Chilungamo chikachitika, nzika zabwino zimakondwera, koma zimadederetsa atambwali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:24

Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, Wamphamvu uja wa Israele, akunena kuti: “Ha! Olimbana nane ndidzaŵatha, adani anga ndidzaŵalipsira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:1-2

Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha. Akutinso, “Inu anthu a mitundu ina, kondwani pamodzi ndi anthu ake a Mulungu.” Ndiponso akuti, “Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye, anthu a mitundu yonse amtamande.” Nayenso mneneri Yesaya akuti, “Mmodzi mwa zidzukulu za Yese adzabwera. Iye adzadzambatuka kuti alamule anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzaika chikhulupiriro chao pa Iyeyo.” Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana. Komabe m'kalata ino zina ndakulemberani mopanda mantha konse, kuti ndikukumbutseni zimenezo. Ndalemba motere popeza kuti Mulungu adandikomera mtima pakundipatula kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Adandipatsa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu ngati wansembe, kuti anthuwo akhale ngati nsembe yokomera Iye ndi yoperekedwa mwa Mzimu Woyera. Tsono pokhala ndine wake wa Khristu Yesu, ndikunyadira ntchito imene ndikugwirira Mulungu. Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga, ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko. Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:16

Kukwiya kwa munthu wopusa kumadziŵika msanga, koma munthu wanzeru salabadako za chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:13

Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:7-8

Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu. Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:28

Munthu wosadzimanga mtima ali ngati mzinda umene adani authyola nkuusiya wopanda malinga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:14

Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino. Funafuna mtendere ndi kuulondola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:14-15

Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:11-13

Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:12

Chidani chimautsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:5

Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:8

Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:39-40

Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:18-19

Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye. Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:22

Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:11

Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 57:3

Mulungu adzandiyankha ali kumwamba, ndipo adzandipulumutsa. Iye adzasokoneza amene andipondereza. Adzaonetsa chikondi chake chosasinthika, adzaonetsa kukhulupirika kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:1

“Usachite umboni wonama. Munthu wolakwa usamthandize pakumchitira umboni wonama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 35:3-4

Mulimbitse manja ofooka, ndi kuŵapatsa mphamvu maondo olobodoka. Muuze onse a mtima wamantha kuti, “Limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36-37

Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:36

Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:21

Zoonadi, anthu oipa chilango sichidzamuphonya, koma anthu a Mulungu adzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:6-7

Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake. Amaonetsa chikondi chake kwa anthu zikwi zambirimbiri, ndipo amaŵakhululukira mphulupulu zao, zoipa zao, ndi machimo ao. Koma sadzalekerera ochimwa, ndipo adzalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha zoipa za atate ao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:4

Chauta ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro, njira zake zonse ndi zolungama, ndi Mulungu wokhulupirika ndi wosaipa konse, wachilungamo ndi wosalakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:5

Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:3-4

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:2

Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:7-8

Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1-2

“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha? Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa. “Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka. “Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu? Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai. Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto. M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:34

Khulupirira Chauta, ndipo usunge njira zake. Motero adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako. Udzaona anthu oipa akuwonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:1-2

Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu oipa. Tchinjirizeni kwa anthu ankhanza. Makala amoto aŵagwere, aponyedwe m'maenje ozama, asatulukemonso. Musalole kuti woononga mbiri ya mnzake akhazikike m'dziko. Choipa chimlondole munthu wankhanza mpaka kumuwononga. Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa. Zoonadi, anthu ochita zabwino adzatamanda dzina lanu. Anthu amenewo adzakhala pamaso panu. Iwo amalingalira mumtima mwao kuti achite zoipa, amautsa nkhondo nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:34-35

Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31-32

Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse. Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:18

Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:15

Masiku anga ali m'manja mwanu. Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:3

Nchaulemu kwa munthu kumalewa mikangano, koma aliyense wopusa amakonda kulongolola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:6

Chauta amaweruza mwachilungamo onse opsinjidwa amaŵachitira zolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wakumwamba, moyo wanga ukukutamandani ndi kukupatsani ulemerero chifukwa cha chikondi chanu ndi chifundo chanu pa moyo wanga. Zikomo chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu lomwe limandilimbitsa ndi kundipatsa mtendere pakati pa mkuntho. Zikomo pa zonse zomwe mumachita tsiku lililonse. Mzimu Woyera, ndikupemphani kuti munditsogolere mu pemphero langa, kuti ndipeze bata lomwe ndikufuna kuti lisakhale ndi chidani mu mtima mwanga. Ndiloleni ndizindikire kuti kukhululukira ndi njira yopita ku machiritso ndi kumasulidwa ku njiru iliyonse. Mundithandize kukumbukira kuti ndinu Woweruza Wamkulu, ndipo kudalira chilungamo chanu n’kofunika kwambiri kuposa kufuna kubwezera choipa. Ndikupemphera kuti mundipatse nzeru ndi bata kuti ndithane ndi chipongwe chilichonse ndi chifundo ndi kumvetsetsa. Chikondi chanu chosatha chindidzaze kwathunthu, kuti ndiyankhe mavuto ndi chikondi, osati ndi mkwiyo. M’manja mwanu ndikuyika chikhumbo changa cha kubwezera choipa, ndipo ndikupemphani kuti muchisinthire kukhala chifundo ndi chisoni. Ndikukuthokozani chifukwa cha kukhalapo kwanu kosalekeza m'moyo wanga ndi kundithandiza kugonjetsa malingaliro anga oipa. M’dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa