Atate wathu wakumwamba watilangiza kuti tizipemphera nthawi zonse. Ndi m’pemphero momwe timayanjana ndi Mulungu wathu. Pemphero ndi njira yolankhulirana ndi Mulungu. Ndi m’pemphero momwe timaperekera mapempho athu onse pamapazi a Mlengi wathu. Ndi komwe timapita zinthu zikavuta, tili ndi nkhawa, kapena titakhala achisoni.
Mulungu amadziwa kale zosowa zathu, ndipo ankadziwa miyoyo yathu tisanabadwe. Koma amafuna kuti tizilankhula naye, kuti timufunefune. Mukapemphera, mumayamba kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu. Mumapanga ubale wolimba naye. Pemphero ndi chida champhamvu kwa ife okhulupirira Yesu. Ndi chida chodzitetezera pa nkhondo iliyonse. Ndi m’pemphero momwe mumapezera chipambano pa chilichonse.
Mphamvu ya pemphero sichokera kwa inu, koma kwa Yesu. Iye ndiye amayankha mapemphero ndi kuchititsa zinthu zomwe sizingatheke kwa anthu. Mukapemphera ndi mtima wonse, mumapeza chitonthozo, mtendere, ndi chikondi cha Atate. Yandikirani kwa Mulungu ndi mtima wodzichepetsa ndi wachisoni, ndipo sadzakukanani. (Aefeso 6:18)
Pemphani mwa Mzimu nthawi zonse, ndi mapempho osiyanasiyana. Khalani maso, ndipo pempherani nthawi zonse chifukwa cha oyera mtima onse. Mukapemphera, yambani ndi kuyamika Mulungu. Osangopereka mapempho anu okha, komanso khalani chete pamaso pake. (Atesalonika 1 5:16-18) Khalani okondwa nthawi zonse, pempherani nthawi zonse, ndipo yamikani Mulungu pa chilichonse, pakuti ichi ndi chifuniro chake kwa inu mwa Khristu Yesu.
Ukadzapemphera kwa Iye adzakumvera, udzapereka kwa Iye zija udalumbira kuti udzaperekazi.
Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
Imvani pemphero langa, Inu Chauta. Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga. Mundiyankhe chifukwa cha kukhulupirika kwanu ndi kulungama kwanu.
Nanga Mulungu, angaleke kuŵaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangoŵalekerera?
Apo Ambuye adamuuza kuti, “Nyamuka, upite ku mseu wa mumzindamu umene amati, ‘Njira Yolunjika.’ Ndipo ku nyumba ya Yudasi ukafune munthu wina wa ku Tariso, dzina lake Saulo. Panopa akupemphera,
Nchifukwa chake sindilekeza kuthokoza Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani m'mapemphero anga,
Akukupatsani moni Epafra, amene ali mmodzi mwa inu, ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu. Nthaŵi zonse iyeyo amalimbikira kukukumbukirani m'mapemphero ake. Amatero pofuna kuti inuyo mukhale okhazikika, angwiro, ndipo kuti muzichilimikira kuchita zonse zimene Mulungu afuna.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.
Iye adayang'anitsitsa mngeloyo mantha atamgwira, ndipo adamufunsa kuti, “Nkwabwino, Ambuye?” Mngeloyo adati, “Mulungu wakondwera nawo mapemphero ako ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo zako.
Komabe Chauta amaonetsa chikondi chake chosasinthika tsiku ndi tsiku, Nchifukwa chake nthaŵi zonse ndimamuimbira nyimbo, ndi kumpemphera Mulungu wondipatsa moyo.
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
Masiku amenewo Yesu adapita ku phiri kukapemphera, ndipo adachezera usiku wonse akupemphera kwa Mulungu.
Koma ife tidzadzipereka ku ntchito ya kupemphera ndi kulalika mau a Mulungu.”
Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi.
Ndikufuna kuti paliponse amuna popemphera azikweza manja ao kwa Mulungu momchitira ulemu, mopanda mkwiyo kapena kukangana.
Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.
Ndikamaitana, mundiyankhe Inu Mulungu, Mtetezi wanga. Mudabwera kudzandithandiza pamene ndinali m'mavuto. Mundichitire chifundo, ndi kumvera pemphero langa.
Tsono atatsazikana nawo anthu aja, Iye adakwera ku phiri yekha kukapemphera. M'mene kunkayamba kuda, nkuti ali komweko yekhayekha.
Yesu, pa nthaŵi imene anali munthu pansi pano, mofuula ndi molira misozi, adapereka mapemphero ndi madandaulo kwa Mulungu, amene anali nazo mphamvu zompulumutsa ku imfa. Ndiye popeza kuti Yesu adaadzipereka modzichepetsa, Mulungu adamvera mapemphero ake.
Ndikupemphera kwa Inu Mulungu, chifukwa mudzandiyankha. Tcherani khutu kuti mumve mau anga.
Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.
Pemphero langa likwere kwa Inu ngati lubani, kukweza kwa manja anga kukhale ngati nsembe yamadzulo.
Muzimva mapemphero opemba a mtumiki wanu ndiponso a anthu anu Aisraele, akamapemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mutikhululukire.
Koma inu okondedwa, muzithandizana kuti uzikulirakulira moyo wanu, umene udakhazikika pa maziko a chikhulupiriro chanu changwiro. Muzipemphera ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Mulungu ndi mboni yanga. Ndimamtumikira ndi mtima wanga wonse, pakulalika Uthenga Wabwino wonena za Mwana wake. Akudziŵa kuti ndimakukumbukirani kosalekeza m'mapemphero anga onse.
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera.
Tsono adapatukana nawo kadera, kutalika kwake ngati pamene mwala ungafike munthu atauponya. Apo adagwada pansi nayamba kupemphera.
Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo.
Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta. Mundiyankhe pa nthaŵi yabwino, Inu Mulungu, chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, ndi chithandizo chanu chokhulupirika.
Komabe Inu Chauta, Mulungu wanga, imvani pemphero la ine mtumiki wanu ndi kupemba kwanga. Mverani kulira kwanga ndiponso pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu lero lino.
Ndi mtima wonse timapemphera usana ndi usiku kuti tiwonane nanunso maso ndi maso, kuti tikakwaniritse zimene zikusoŵa pakuwonetsa chikhulupiriro chanu.
Nchifukwa chake timakupemphererani nthaŵi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera moyo umene Iye adakuitanirani. Timapemphanso kuti ndi mphamvu zake akulimbikitseni kuchita zabwino zonse zimene mumalakalaka kuzichita, ndiponso ntchito zotsimikizira chikhulupiriro chanu.
Koma Ine ndakupempherera, kuti usaleke kundikhulupirira. Ndipo iweyo utatembenuka mtima, ukaŵalimbitse abale akoŵa.”
Motero Petro ankasungidwa m'ndende. Koma Mpingo unkamupempherera kwa Mulungu kosalekeza.
Choncho Chauta ankalankhula ndi Mose pamasompamaso, monga momwe munthu amalankhulira ndi bwenzi lake. Tsono pambuyo pake Mose ankabwerera kumahema komweko. Koma mnyamata wina, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, amene anali mtumiki wa Mose, sankachoka kuchihemako.
Timakondwa pamene ife tili ofooka koma inu muli amphamvu. Chimene tikupempha Mulungu nchakuti mudzasanduke angwiro.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Chimalizo cha zonse chayandikira. Nchifukwa chake khalani ochenjera ndi odziletsa, kuti muthe kupemphera.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga. Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.
Mpaka tsopano simunapemphe kanthu potchula dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.”
Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo.
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu.
Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu.
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Koma iwe, pamene ukuti upemphere, loŵa m'chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.”
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
M'maŵa, Inu Chauta, mumamva mau anga. M'maŵa ndimapemphera kwa Inu, ndi kudikira kuti mundiyankhe.
Akuti: Unditame mopemba, ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziŵa.
Mulungu adaŵathandiza pomenya nkhondoyo, ndipo Ahagiriwo pamodzi ndi onse amene adaaphatikana nawo, adaperekedwa m'manja mwao. Ankalira kwa Mulungu pomenya nkhondoyo, tsono Mulungu adaŵapatsa zimene ankapemphazo, popeza kuti adaamkhulupirira.
Inu Chauta, tcherani khutu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu ena amene amakonda kulemekeza dzina lanu. Lolani kuti ine mtumiki wanu zinthu zindiyendere bwino lero, ndipo kuti mfumu indichitire chifundo.” Pa nthaŵi imeneyo nkuti ine ndili woperekera zakumwa kwa mfumu.
Ndimakonda Chauta chifukwa amamva mau anga omupemba. Ndidakhulupirirabe ngakhale pamene ndinkati, “Ndazunzika koopsa.” Pamene ndinkachita mantha, ndidati, “Anthu ndi osakhulupirika.” Ndidzambwezera chiyani Chauta pa zabwino zonse zimene adandichitira? Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta. Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse. Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta, ndi yamtengowapatali pamaso pake. Chauta, ine ndine mtumiki wanu, mtumiki wanu weniweni, mwana wa mdzakazi wanu. Inu mwamasula maunyolo anga. Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta. Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse. Ndidzazipereka m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, mu mzinda wa Yerusalemu. Tamandani Chauta! Iye amatchera khutu kuti andimve, nchifukwa chake ndidzampempha nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.
Nchifukwa chake, kuyambira tsiku limene tidamva zimenezi, sitileka kukupemphererani. Timapempha Mulungu kuti akudzazeni ndi nzeru ndi luntha, zimene Mzimu Woyera amapatsa, kuti mumvetse zonse zimene Iye afuna.
M'mamaŵa ndithu, kusanache, Yesu adadzuka napita kumalo kosapitapita anthu. Kumeneko adakapemphera.
Popeza kuti timakhulupirira Iyeyu, tingathe kulimba mtima kuyandikira kwa Mulungu mosakayika konse.
Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.
Komanso kunena za ine, sindifuna kuchimwira Chauta, pakuleka kukupemphererani. Ndidzakuphunzitsani zimene zili zabwino ndi zolungama kuti muzizichita.
Onseŵa ankalimbikira kupemphera ndi mtima umodzi, pamodzi ndi akazi ena, ndi Maria amai ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.
Koma zoonadi, Mulungu wandimvera, wasamala mau a pemphero langa. Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu. Mulungu atamandike chifukwa sadakane pemphero langa, sadachotse chikondi chake chosasinthika kwa Ine.
Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.
“Pamene mukupemphera, musamangobwerezabwereza mau monga amachitira anthu akunja. Iwowo amayesa kuti akachulukitsa mau choncho, ndiye pamene Mulungu aŵamvere.
ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”