Kondwerani ndi masiku anu a unyamata, muzitsatira zomwe Mulungu wakukonzerani. Gwiritsani ntchito mphamvu zomwe muli nazo tsopano. Musamadziganizire zochepa chifukwa cha unyamata wanu. Nthawi zina mukadali aang'ono mukhoza kutaya mtima mukaganizira zam'tsogolo, ndipo mwina mungamve kupsinjika maganizo. Koma dziwani kuti Mulungu, Mlengi wanu, ali ndi inu ndipo amayang'anira moyo wanu. Muzimufunafuna ndi mtima wonse, ndipo muziyeretsa tsiku ndi tsiku mwa Iye.
Khalani chitsanzo chabwino kulikonse kumene mungapite, m'chikondi, m'mawu, m'khalidwe, m'chikhulupiriro, ndi m'kuyera. Mulungu amanena m'Mawu ake kuti wachinyamata adzayeretsa njira yake ndi mawu ake. Fufuzani Mawu ake tsiku ndi tsiku ndipo mudzakhala ndi chipambano m'moyo wanu.
Gwiritsani ntchito nthawi iliyonse kukhala pafupi ndi Atate wanu wakumwamba, masiku asanafike pamene simudzakhalanso ndi chimwemwe, kapena mphamvu zomwe muli nazo lero, kapena nthawi yomwe muli nayo lero. Ndinu ofunika kwa Mulungu, Iye ali ndi dongosolo labwino pa moyo wanu ndipo akufuna kulikwaniritsa mwa inu. Mukamamufunafuna Iye, adzakuyikani dongosolo lake mwa inu. (1 Timoteo 4:12) Munthu asanyoze unyamata wanu, koma khalani chitsanzo kwa okhulupirira m'mawu, m'khalidwe, m'chikondi, m'mzimu, m'chikhulupiriro, ndi m'kuyera.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Uzikumbukanso Mlengi wako pa masiku a unyamata wako, masiku oipa asanafike, zisanafikenso zaka zoti uzidzati, “Moyowu wandikola.”
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri, koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.
Pambuyo pake adauza onse amene anali pamenepo kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake tsiku ndi tsiku nkumanditsata.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.” Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”
Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga. Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina. Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha. Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta. Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.” Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.” Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.”
Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama. Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa.
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira.
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza. Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen.
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu. Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.
Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta. Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu. Ndili ndi nzeru kupambana okalamba, pakuti ndimatsata malamulo anu. Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu. Sindisiyana nawo malangizo anu, pakuti Inu mudandiphunzitsa mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga. Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga. Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza kuti ndidzamvera malangizo anu olungama. Ndazunzika koopsa, Chauta, patseni moyo, molingana ndi mau anu aja. Chauta, landirani mapemphero anga oyamika, ndipo mundiphunzitse malangizo anu. Moyo wanga uli m'zoopsa nthaŵi zonse, komabe sindiiŵala malamulo anu. Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni. Anthu oipa anditchera msampha, komabe sindisokera kuchoka m'njira ya malamulo anu. Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga. Mtima wanga muuphunzitse kuti uzikonda malamulo anu nthaŵi zonse. Ndimadana nawo anthu apaŵiripaŵiri, koma ndimakonda mau anu. Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu. Chokereni inu, anthu ochita zoipanu, kuti ine ndizitsata malamulo a Mulungu wanga. Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika. Chirikizeni kuti ndipulumuke, kuti nthaŵi zonse ndizitsata malamulo anu. Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu, zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake. Anthu onse oipa a pa dziko lapansi, mumaŵayesa ngati zakudzala, nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu. Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu. Thupi langa limanjenjemera chifukwa chokuwopani, ndimachita mantha ndi kuweruza kwanu. Ndachita zimene zili zolungama ndi zabwino. Musandisiye m'manja mwa ondizunza. Lonjezani kuti mudzandichitira zabwino mtumiki wanune, musalole anthu osasamala za Mulungu kuti andizunze. Maso anga atopa chifukwa cha kuyembekeza chipulumutso chanu, chifukwa cha kudikira kuti malonjezo anu olungama aja achitikedi. Komereni mtima mtumiki wanune, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Ndine mtumiki wanu, mundipatse nzeru zomvetsa, kuti ndizidziŵa malamulo anu. Yakwana nthaŵi yakuti Inu Chauta muchitepo kanthu, popeza kuti anthu aphwanya malamulo anu. Koma ine ndimasamala malamulo anu kupambana golide, golide wosungunula bwino. Malamulo anu onse amalungamitsa mayendedwe anga. Ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. Malamulo anu ndi abwino, nchifukwa chake ndimaŵatsata ndi mtima wanga wonse. Ndimalalika ndi mau anga malangizo onse a pakamwa panu. Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru. Ndimapuma mwaŵefuŵefu nditatsekula pakamwa, chifukwa ndimalakalaka malamulo anu. Yang'aneni, ndipo mundikomere mtima monga m'mene mumachitira ndi anthu okukondani. Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira. Pulumutseni kwa anthu ondizunza, kuti ndizitsata malamulo anu. Yang'anireni ine mtumiki wanu ndi chikondi chanu, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Maso anga akudza misozi yambiri ngati mitsinje, chifukwa anthu satsata malamulo anu. Ndinu olungama Chauta, ndipo kuweruza kwanu nkolungama. Malamulo amene mwatipatsa, ndi olungama ndi okhulupirika ndithu. Changu changa chikuyaka ngati moto mumtima mwanga, chifukwa adani anga amaiŵala mau anu. Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse. Malonjezo anu ndi otsimikizika, ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda. Ine ndine wamng'ono ndi wonyozeka, komabe sindiiŵala malamulo anu. Kulungama kwanu nkwamuyaya, ndipo malamulo anu ndi oona. Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe, koma malamulo anu amandisangalatsa. Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya, patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo. Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu. Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu. Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu. Ndimakhala maso usiku wonse, ndikusinkhasinkha za malonjezo anu. Imvani liwu langa chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Inu Chauta, sungani moyo wanga chifukwa cha chilungamo chanu. Ndidzasinkhasinkha za malamulo anu, ndipo ndidzatsata njira zanu. Anthu ankhanza ondizunza akuyandikira. Iwo ali kutali ndi malamulo anu. Koma Inu Chauta muli pafupi, ndipo malamulo anu onse ndi oona. Poŵerenga malamulo anu ndidadziŵa kale lomwe kuti Inu mudaŵakhazikitsa mpaka muyaya. Yang'anani masautso anga, ndipo mundipulumutse, popeza kuti sindiiŵala malamulo anu. Munditchinjirize pa mlandu wanga, ndipo mundiwombole. Mundipatse moyo molingana ndi malonjezo anu aja. Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu. Chifundo chanu nchachikulu, Inu Chauta, mundipatse moyo molingana ndi chilungamo chanu. Anthu ondizunza ndiponso adani anga ngochuluka, koma sindisiyana nawo malamulo anu. Ndimanyansidwa ndikamayang'ana anthu osakhulupirika, chifukwa satsata malamulo anu. Onani m'mene ndimakondera malamulo anu, sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika Ndidzakondwera ndi malamulo anu, ndipo mau anu sindidzaŵaiŵala. mau anu ndi oona okhaokha, malangizo anu onse olungama ngamuyaya. Mafumu amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umaopa mau anu. Ndimakondwa ndi mau anu monga munthu amene wapeza chuma chambiri. Ndimadana ndi anthu abodza, zoonadi, ndimanyansidwa nawo, koma ndimakonda malamulo anu. Ndimakutamandani kasanunkaŵiri pa tsiku, chifukwa cha malangizo anu olungama. Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa. Ndimakhulupirira kuti mudzandipulumutsa, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu. Mzimu wanga umatsata malamulo anu, pakuti ndimaŵakonda ndi mtima wanga wonse. Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu, pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona. Kulira kwanga kumveke kwa Inu, Chauta. Mundipatse nzeru zomvetsa potsata mau anu aja. Komereni mtima ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo ndi kusunga mau anu. Kupempha kwanga kumveke kwa Inu. Mundipulumutse potsata malonjezo anu. Pakamwa panga padzakutamandani, chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu. Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu, chifukwa malamulo anu onse ndi olungama. Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza, chifukwa ndatsata malamulo anu. Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa. Lolani kuti ndikhale moyo, kuti ndizikutamandani, ndipo malangizo anu azindithandiza. Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu. Tsekulani maso anga kuti ndiwone zodabwitsa zochokera m'malamulo anu. Ndine munthu wongokhala nawo pa dziko lapansi, musandibisire malamulo anu. Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,
Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”
Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi.
Monga inu simudziŵa kuti pa mpikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti nkukalandira mphothoyo. Aliyense wothamanga pa mpikisano wa liŵiro amadziletsa pa zonse. Iwowo amachita zimenezi kuti akalandire mphotho ya nkhata yamaluŵa yotha kufota. Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota.
“Inu anthu onse a pa dziko lapansi, tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke. Paja Ine ndine Mulungu, palibenso wina ai.
Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse. Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Uzisamala m'mene mukupita mapazi ako, ndipo njira zako zonse zidzakhala zosapeneketsa. Usapatukire kumanja kapena kumanzere, usayende pamene pali choipa chilichonse.
Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Moyo wosathawo ndi wakuti akudziŵeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziŵenso Yesu Khristu amene mudamtuma.
“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Adzakupatsani mtendere wokhazikika pa nthaŵi yanu. Adzakuninkhaninso chipulumutso chachikulu, luntha lambiri ndi nzerunso zambiri. Kuwopa Chauta ndiko kumapezetsa chuma chimenechi.
Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha. Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa. Ozunzikawo atayang'ana kwa Chauta, nkhope zao zidasangalala, sadachite manyazi.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”
Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Chakudya, kwake nkuloŵa m'mimba, ndipo mimba, kwake nkulandira chakudya. Koma Mulungu adzaononga ziŵiri zonsezo. Thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo.
Tonsefe, opanda chophimba nkhope yathu, timaonetsa ulemerero wa Ambuye, monga momwe galasi limaonetsera nkhope ya munthu. Monsemo Ambuye, amene ali Mzimu, amatisandutsa kuti tifanefane naye, ndi kukhala nawo ulemerero wake mochulukirachulukira.
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Yesu adaŵauza kuti, “Chakudya chopatsa moyocho ndine. Munthu aliyense wodza kwa Ine, sadzamva njala. Ndipo aliyense wokhulupirira Ine, sadzamva ludzu konse.
popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola.
Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.