Timatamanda Mulungu chifukwa cha tsiku lililonse lapadera limene timakumana nalo, ndi masiku osangalala ndi kukondwerera. Mulungu amasangalala tikamayenda mu mtendere ndi chimwemwe. Muzimutamanda Yehova m'masiku amenewa ndipo musaiwale kuti ndi Mulungu amene amakuchititsani kukhala ndi nthawi zapadera.
Masalimo 30:11-12 amati, “Munasintha kulira kwanga kukhala kuvina; Munandichotsa chiguduli, n’kundiveka chokondwerera; kuti moyo wanga uziyimba nyimbo zotamanda Inu, osakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakutamandani nthawi zonse.” M’Baibulo muli mavesi ambiri okhudza zochitika zapadera.
Pambuyo pake msonkhano wonse udavomerezana zopitiriza chikondwererocho masiku asanu ndi aŵiri ena. Choncho adachitadi chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri ena mosangalala.
“Muzichita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa monga ndidakulamulirani. Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, chifukwa ndi mwezi umenewu pamene inu mudachokako ku Ejipito kuja.
Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja.
Aisraele azisunga tsiku la Sabatalo, ndipo mibadwo yonse yakutsogoloko izidzalisunga ngati pangano losatha.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Tsono adapeza kuti m'buku la Malamulo mudalembedwa kuti Chauta adalamula kudzera mwa Mose kuti Aisraele azikhala m'zithando nthaŵi yonse ya chikondwerero cha pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Motero adafalitsa ndi kulengeza m'midzi yao yonse ndiponso m'Yerusalemu, kuti, “Pitani ku mapiri, mukatengeko nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wakuthengo, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa, ndiponso za mitengo ina ya masamba ambiri, kuti mumangire misasa monga momwe zidalembedwera.”
Ndidzathetsa chimwemwe chake chonse, zikondwerero zake za pokhala mwezi, za masabata ndi za masiku ena onse opatulika.
Musabwere nazonso nsembe zanu zachabechabe. Utsi wake umandinyansa. Sindingapirire misonkhano yanu yamapemphero, kapenanso zikondwerero za pokhala mwezi ndi za Sabata, sindingapirire mapemphero oipitsidwa ndi machimo. Zikondwerero zanu za pokhala mwezi ndi masiku anu oyera ndimadana nazo. Zasanduka katundu wondilemera, ndatopa nako kuŵapirira.
Aroniyo ataona zimenezi, adapanga guwa patsogolo pa mwanawang'ombe wagolideyo. Tsono adalengeza kuti, “Maŵa padzakhala chikondwerero cholemekeza Chauta.”
Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala mwezi, ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Chauta.
mwina muzidzapereka ng'ombe kapena nkhosa kwa Chauta kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, kapena yopsereza, kapena yopembedzera, kuti mukwaniritse zimene mudalonjeza molumbira. Mwina mudzazipereka kuti zikhale nsembe yaufulu kapena nsembe yopereka pa nthaŵi ya zikondwerero zosankhidwa, kuti zikhale nsembe zotulutsa fungo lokomera Chauta.
Adaŵalamula onsewo kuti, “Kamodzi pa zaka zisanu ndi ziŵiri zilizonse, pamene chaka cha kumasulidwa chafika, muŵerenge malamuloŵa pa chikondwerero cha misasa. Muŵaŵerenge kwa Aisraele onse, pamene adzabwere kudzapembedza Chauta pa malo oŵasankha Iyeyo.
“Mukamapereka magazi a nyama ngati nsembe kwa Ine, musapereke pamodzi ndi buledi wofufumitsa, ndipo mafuta a nyama yopereka pa tsiku langa lachikondwerero asakhale mpaka m'maŵa.
Chachikhumi muziika padera, ndiye kuti limodzi mwa magawo khumi a zokolola zanu za chaka ndi chaka. Tsono pitani mukakhale pa malo amodzi amene Chauta, Mulungu wanu, adzasankhula kuti anthu azidzampembedzerapo. Ndipo magawo achachikhumi ameneŵa mudyere pa malo amenewo, pamaso pa Mulungu wanu. Magawo ameneŵa ndi a tirigu, vinyo ndi mafuta aolivi, ndiponso ana oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a nkhosa. Muzichita zimenezi masiku onse, kuti motero muphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu.
Zikondwerero zanu ndidzazisandutsa kulira, nyimbo zanu ndidzazisandutsa zamaliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu pathupi panu, ndipo mitu yanu yonse idzachita dazi. Mudzakhala ngati anakubala olira mwana wao mmodzi yekha. Tsiku limenelo lidzakhaladi loŵaŵa mpaka kutha kwake.”
“Muziŵerenga masabata asanu ndi aŵiri a zaka, zaka zisanu ndi ziŵiri kuchulukitsa kasanunkaŵiri, kuti nyengo ya masabata asanu ndi aŵiri a zakayo ikwanire zaka 49 pamodzi. Tsono pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, mulize lipenga mokweza. Tsiku lochita mwambo wopepesera machimo, ndilo tsiku limene mulize lipengalo m'dziko lanu lonse.
Ndipo tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku la chikondwerero cha buledi wosafufumitsa, lolemekezera Chauta. Pa masiku asanu ndi aŵiri muzidya buledi wosafufumitsa.
“Tsono mfumu ichitenso chimodzimodzi pa tsiku la khumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Chikondwerero chimenecho chizichitika masiku asanu ndi aŵiri. Izipereka nsembe za mtundu womwewonso, zopepesera machimo, nsembe zopsereza, ndiponso nsembe zaufa ndi zamafuta zomwe.”
“Pa tsiku la khumi ndi chinai la mwezi woyamba, muzichita chikondwerero cha Paska, chikondwerero chake cha masiku asanu ndi aŵiri. Masiku amenewo muzidya buledi wosatupitsa.
Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe kudalembedwera. Masiku onse ankaperekanso nsembe zopsereza potsata chiŵerengero chake chofunika tsiku ndi tsiku, monga kudalembedwera.
Tsono anthu a ku Israele amene analipo ku Yerusalemu kuja, adachita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa masiku asanu ndi aŵiri, ndipo adasangalala kwambiri. Alevi pamodzi ndi ansembe ankatamanda Chauta tsiku ndi tsiku, akumuimbira ndi mphamvu zao zonse.
monga momwe zinkafunikira pa tsiku lililonse. Ankapereka potsata malamulo a Mose okhudza masiku a Sabata, masiku a pokhala mwezi watsopano, ndiponso masiku achikondwerero atatu a chaka ndi chaka: Chikondwerero cha buledi wosafufumitsa, chikondwerero cha masabata ndiponso chikondwerero cha mahema.
Anthu aamuna onse a mtundu wanu azidzabwera kudzapembedza Chauta, Mulungu wanu, ku malo achipembedzo, katatu pa chaka. Azidzafika pa nthaŵi ya Paska, pa nthaŵi ya chikondwerero cha kholola ndiponso pa nthaŵi ya chikondwerero cha misasa.
“Aisraele azichita Paska pa nthaŵi yake. Nthaŵi zina mtambowo unkaphimba masiku oŵerengeka, ndipo Aisraele ankakhalabe m'mahema potsata malamulo a Chauta. Tsono ankanyamuka ulendo Chauta akaŵalamula. Nthaŵi zina mtambowo unkangophimba chihemacho kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. M'maŵa mwake mtambowo ukachoka, iwo ankanyamuka ulendo wao. Mwina mtambowo unkaphimba chihema chija tsiku lonse ndi usiku womwe, koma ukangochokapo, iwowo ankanyamuka ulendo wao. Ngakhale mtambowo uphimbe pamwamba pa chihema cha Mulungu nkumakhala pomwepo masiku aŵiri kapena mwezi, kapena chaka, kapena nthaŵi yopitirirapo, Aisraele ankakhalabe m'mahema, ndipo sankanyamuka. Koma mtambowo ukangochokapo, iwo ankanyamuka ulendo. Aisraele ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula, ndipo ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula. Ankasunga lamulo la Chauta, loŵafikira kudzera mwa Mose. Muzichita Paska tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo ake. Muzichita Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake onse.”
“Pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, mutakolola dzinthu m'dziko mwanu, muchite chikondwerero cha Chauta pa masiku asanu ndi aŵiri. Tsiku loyamba likhale tsiku lalikulu lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu likhalenso tsiku lalikulu lopumula.
“Uza Aisraele kuti, ‘Kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, pa masiku asanu ndi aŵiri, pazikhala chikondwerero chamisasa cholemekeza Chauta.
‘Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku lochita mwambo wopepesera machimo. Imeneyo ikhale nthaŵi yanu yochita msonkhano wopatulika. Musale zakudya, ndipo mupereke nsembe yopsereza kwa Chauta.
“Uza Aisraele kuti, ‘Pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzilisunga kuti likhale tsiku lalikulu lopumula, tsiku lachikumbutso, lolengezedwa ndi malipenga, tsiku la msonkhano wopatulika.
“Kuyambira tsiku lotsatana ndi la Sabata lija, pamene mudadzapereka mtolo wanu uja wa chopereka choweyula pamaso pa Chauta, muŵerenge milungu isanu ndi iŵiri yathunthu, ndiye kuti masiku asanu mpaka tsiku lotsatana ndi la Sabata lachisanu ndi chiŵiri. Patapita masiku amenewo, mupereke chopereka cha chakudya chatsopano kwa Chauta.
“Uza Aisraele kuti, ‘Mukakaloŵa m'dziko limene ndikukupatsanilo ndi kukakolola za m'minda mwanu, mudzabwere kwa wansembe ndi mtolo wa zoyambirira kucha mwa zokolola zanu. Wansembeyo auweyule mtolowo pamaso pa Chauta, kuti inuyo mulandiridwe. Auweyule tsiku lotsatana ndi la Sabata.
“Masiku achikondwerero osankhidwa a Chauta, masiku oyera amisonkhano amene mudzaŵalengeza pa nthaŵi yake, ndi aŵa:
“Uza Aisraele kuti, ‘Masiku achikondwerero osankhidwa olemekeza Chauta, amene mudzaŵalengeza kuti akhale masiku oyera amisonkhano, masiku achikondwerero amene Ine ndaŵasankha, ndi aŵa:
Muziŵamvera malamulo ameneŵa inuyo ndi ana anu mpaka muyaya. Ndipo mukadzaloŵa m'dziko limene Chauta akukupatsanilo, monga momwe adalonjezera, muzidzasunga mwambo umenewu. Ana anu azidzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza chiyani?’ Pamenepo inu muzidzayankha kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Chauta, chifukwa chakuti adapitirira nyumba za Aisraele ku Ejipito; pamene ankapha Aejipito, nyumba zathu adazisiya.’ ” Atamva zimenezi, anthu adaŵerama pansi, napembedza.
Ndipo pa tsiku la 15 la mwezi umenewu, ndi tsiku lachikondwerero. Azidya buledi wosafufumitsa masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku loyamba pazikhala msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito yotopetsa,
“Pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, muzichita msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa. Tsiku limeneli muziliza malipenga.
“Tsiku limeneli muzidzalisunga. Tsiku limeneli muzidzalikumbukira, ndipo muzidzachita chikondwerero, kupembedza Chauta. Mibadwo yonse izidzakumbukira tsikuli, kuti likhale lamulo lamuyaya, lakuti muzidzachita chikondwerero pa tsiku limenelo.”
Muzilemekeza Chauta, Mulungu wanu, pakuchita chikondwerero cha Paska pa mwezi wa Abibu. Chifukwa usiku wina mwezi umenewu, mpamene Chauta adakutulutsani ku Ejipito.
Muzichita chikondwerero cha masabata, ndi chikondwerero cha kukolola tirigu woyambirira, ndi chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pake pa chaka.
“Muzikhala ndi tsiku lachikondwerero katatu pa chaka, kuti mundilemekeze Ine. Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha Masika pokolola mbeu zoyamba zochokera ku zobzala zanu. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pa chaka, pamene muika m'nkhokwe dzinthu dzanu dzonse.
Mutatuta tirigu wanu yense, ndiponso mutafinya mphesa zanu, muzidzachita chikondwerero cha misasa masiku asanu ndi aŵiri. Musangalale pa chikondwererocho, inuyo pamodzi ndi mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mtumiki wanu wamwamuna, mdzakazi wanu, Alevi amene ali m'mizinda mwanu, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, amene amakhala nanu m'mizinda mwanu.
Tsono muchite chikondwerero cha kholola, cholemekeza Chauta, Mulungu wanu, pakumpatsa chopereka chaufulu, molingana ndi madalitso amene Iye wakupatsani.
Zitatha zimenezi anthu onse otsala mwa adani amene ankamenyana ndi Yerusalemu, azidzabwera chaka ndi chaka kudzapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, ndiponso kudzachita chikondwerero chamisasa.
Itayandikira nthaŵi ya Paska, chikondwerero cha Ayuda, Yesu adanyamuka kupita ku Yerusalemu.
Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m'nyumba imodzi.
Ndipo ataona kuti zimenezi zidakondweretsa Ayuda, adapitiriza ndithu nkugwiranso Petro. Zimenezi zidachitika pa masiku a Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa. Atamgwira, adamtsekera m'ndende, nampereka kwa magulu anai a asilikali kuti azimlonda, gulu lililonse asilikali anai. Tsono Herode ankafuna kuzenga mlandu wake pamaso pa anthu onse, chikondwerero cha Paska chitapita.
Mupatule chaka cha 50, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu m'dziko lonselo kwa onse amene ali m'menemo. Kwa inu chaka chimenecho chidzakhale chokondwerera zaka 50, pamene aliyense adzayenera kubwerera pa mtunda wake, ndipo aliyense mwa inu abwerere ku banja lake.
Onani Ziyoni, mzinda wa zokondwerera zathu zachipembedzo. Maso anu adzaona Yerusalemu, mzinda wamtendere, hema losasunthika. Zikhomo zake sizidzazuka, ndipo zingwe zake sizidzaduka.
Chikondwerero cha Paska chija chinkayandikira. Choncho anthu ambiri ochokera ku midzi adapita ku Yerusalemu kukachita mwambo wa kudziyeretsa, Paska isanayambe.
Umu ndimo m'mene Mose adafotokozera kwa Aisraele za masiku achikondwerero osankhidwa, olemekeza Chauta.
“Pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri womwewo, muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa, ndipo muchite chikondwerero cholemekeza Chauta masiku asanu ndi aŵiri.
Motero pa masiku asanu ndi aŵiri adasangalala pa chikondwerero cha buledi wosatupitsa. Zidatero chifukwa Chauta adaŵakondweretsa, ndipo adaatembenuza mtima wa mfumu ya ku Asiriya, kotero kuti idaŵakomera mtima niŵathandiza pa ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu, Mulungu wake wa Aisraele.
Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kuperekedwanso kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nyengo yozizira.
Pa tsiku lanu losangalala, pa masiku osankhidwa a zikondwerero zanu, ndi pa masiku oyamba a miyezi, mulize malipenga pamene mukupereka nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu zachiyanjano. Malipengawo adzakuthandizani kumkumbukira Mulungu wanu. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”
“Pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri womwewo, muchite msonkhano wopatulika, ndipo musale zakudya. Musagwire ntchito iliyonse,
Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri, lidzakhala la Sabata, tsiku lanu lopumula, loperekedwa kwa Chauta. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo, adzaphedwa.
Koma ife tidayenda pa chombo kuchokera ku Filipi, itatha Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa. Ndipo patapita masiku asanu, tidakumana nawo ku Troasi. Kumeneko tidakhalako masiku asanu ndi aŵiri.
Tsono mfumu Yosiya adalamula anthu onse kuti, “Muchite chikondwerero cha Paska, kulemekeza Chauta, Mulungu wanu, potsata zimene zidalembedwa m'buku lachipangano.”
Likhale ngati tsiku lalikulu la Sabata lopumula kwa inu, ndipo musale zakudya. Pa tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, kuyambira madzulo ake mpaka madzulo ena otsatira, musunge tsikulo monga ngati la Sabata.’ ”
Chikondwerero chimenechi cha buledi wosafufumitsa, mudzachisunge ndithu, chifukwa pa tsiku limeneli mpamene ndidzatulutse magulu anu onse kuchoka m'dziko la Ejipito. Tsono muzidzasunga tsiku limeneli pa mibadwo yanu yonse, ngati lamulo lamuyaya.
Tsiku lotsiriza la chikondwerero chija linali lalikulu. Pa tsikulo Yesu adaimirira nkunena mokweza kuti, “Ngati pali munthu ali ndi ludzu, abwere kwa Ine kuti adzamwe.
Kusala zakudya pa mwezi wachinai, wachisanu, wachisanu ndi chiŵiri ndi wakhumi, kudzakhala nthaŵi yachimwemwe ndi yachisangalalo ku banja la Yuda. Muzikonda zoona ndiponso mtendere.”
Koma munthu amene sadadziipitse ndipo sali paulendo, komabe akana kuchita Paska, ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraele, chifukwa sadabwere ndi zopereka zake kwa Chauta pa nthaŵi yake. Ameneyo adzalangidwa chifukwa cha tchimo lake.
Choncho Aisraele amene anali pamenepo adachita Paska nthaŵi imeneyo, ndipo pa masiku asanu ndi aŵiri adachita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa.
Pa phiri ili la Ziyoni Chauta Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse phwando la zakudya zokoma ndi la vinyo wabwino, phwando la nyama yonona ndi la vinyo amene wafikapo.
Koma inu anthu a Mulungu, mudzakondwa ndi kuimba monga m'mene mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika. Mudzasangalala ngati anthu opita naimba toliro ku phiri la Chauta, thanthwe la Israele.
Choncho kunali chikondwerero chachikulu ku Yerusalemu, pakuti kuyambira nthaŵi ya Solomoni, mwana wa Davide, mfumu ya Israele, sizidachitikepo zotere ku Yerusalemu.
Mtima wanga umaŵawa ndikamakumbukira m'mene ndinkayendera ndi chinamtindi cha anthu, poŵatsogolera ku Nyumba ya Mulungu. Panali khwimbi la anthu ofuula mosangalala, akuimba nyimbo zothokoza ndipo akuchita chikondwerero.
Nthaŵi yaikulu idapita, ndipo ngakhale nthaŵi yosala zakudya inali itapita kale. Nthaŵiyo ulendo wapamadzi unali woopsa. Pamenepo Paulo adaŵachenjeza kuti,
Inuyo pitani kuchikondwereroko. Ine sindipitako ku chikondwerero chimenechi, chifukwa nthaŵi yanga yoyenera siinafike.”
Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.”
Pambuyo pake kunali chikondwerero chachipembedzo cha Ayuda, ndipo Yesu adapitako ku Yerusalemuko.
“Pa masiku achikondwerero, anthu am'dzikomo akabwera kudzapembedza Chauta, munthu woloŵera pa chipata chakumpoto azidzatulukira pa chipata chakumwera. Munthu woloŵera pa chipata chakumwera, azidzatulukira pa chipata chakumpoto. Munthu aliyense asadzatulukire pomwe waloŵera, koma azipita chakutsogolo.
“Ameneŵa ndi masiku achikondwerero osankhidwa olemekeza Chauta, amene muziŵalengeza kuti ndi nthaŵi ya msonkhano wopatulika. Masiku ameneŵa muzipereka kwa Chauta nsembe zapamoto, monga nsembe zopsereza, nsembe zaufa, nsembe zanyama, ndi zopereka za chakumwa, iliyonse pa tsiku lake.
Imbani lipenga mwezi ukaoneka chatsopano, ukaoneka kwathunthu, pa tsiku lathu lachikondwerero.
Tsiku ndi tsiku kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lotsiriza, Ezara ankaŵerenga buku la Malamulo a Mulungu. Anthu adachita chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu padachitika mwambo wotseka msonkhano, potsata buku la Malamulo lija.
Chaka chimenecho cha 50 chikhale chaka chachikondwererodi. Pa chaka chimenechi musabzale kanthu, kapena kukolola mphulumukwa, kapenanso kuthyola mphesa pa mitengo yosathenera.
“Upange malipenga aŵiri asiliva, uchite kusula. Uziimba malipengawo poitana mpingo, ndi pochoka pa mahema.
Ndipo Yerobowamu adakhazikitsa tsiku lachikondwerero, pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chitatu, lofanafana ndi tsiku lachikondwerero limene ankachita ku Yuda, napereka nsembe pa guwa nthaŵi imeneyo. Adachita zimenezi ku Betele, namapereka nsembe kwa mafano a anaang'ombe, amene iyeyo adapanga. Ndipo ku Beteleko adaikako ansembe pa malo achipembedzo amene adamanga.
Ndipo mfumu izipereka zofunikira ku nsembe zopsereza, nsembe zatirigu ndi nsembe zazakumwa pa masiku achikondwerero, ndi a pokhala mwezi, masiku a Sabata, ndiponso pa masiku ena amene Aisraele amaŵasunga. Mfumuyo ipereke zofunikira ku nsembe zopepesera machimo, nsembe zatirigu, nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kuti zonsezo zikhale zopepesera machimo a Aisraele.
Lizani lipenga ku Ziyoni. Lengezani mwambo wa kusala zakudya. Muitanitse msonkhano waukulu.
Chimenechi ndi chaka chokondwerera zaka 50. Chikhale chaka chopatulika kwa inu ndipo mudye zam'likale.
Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska, ophunzira a Yesu adamufunsa kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”
Tsiku la buledi wosafufumitsa lidafika, ndiye kuti tsiku limene anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska.
Nthaŵi yochitira chikondwerero cha buledi wosafufumitsa inkayandikira. Chikondwererocho chimatchedwa Paska.
Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, ophunzira aja adadza nafunsa Yesu kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”