Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -



112 Mau a Mulungu Ponena za Kudandaula

112 Mau a Mulungu Ponena za Kudandaula

Mtima wanga ukondwera kwambiri Mulungu akaona ndikusunga mawu Anga. Ndimakondwa kwambiri ndikamuimbila nyimbo zotamanda ndi kuuza ena za ntchito zake zazikulu. Koma Mulungu sakondwera ndi bodza; sakondwera ndi anthu onamiza. Amatseka makutu Ake kwa anthu ochita zoyipa ndi kunenera anzawo. Izi n'zachilendo kwa Ambuye.

Kunena zoipa za anzanu, kukangana, kugawanika, kutukwana, ndi kunyinyirika, zonsezi zimatipweteka kwambiri. Zimatichokozera mavuto chifukwa sitimadya Mawu a Mulungu mokwanira ndipo timadzilola kuti Mdyerekezi atiipitse. Lilime lathu lingadalitse kapena lingatemberere. Choncho tiyenera kusamala kwambiri ndi zomwe tikulankhula.

Ndikofunikira kupempha Mulungu kuti atikhululukire machimo athu, makamaka tchimo la kunyinyirika, kuti tisataye chipulumutso chathu. Mulungu akufuna kuti tizidalitsa ena ndi mawu athu ngati mphepo yofewa pa mzimu wawo. Tiyenera kusiya kunena zoipa za anzathu. Tiyenera kupempha Yesu kuti atisambe ndi magazi ake oyera. Tiyenera kupewa zoyipa, kusamala ndi mawu athu, ndikudziwa nthawi yoyenera kukhala chete.

Tiyeni tikhale chitsanzo chabwino kwa anthu omatizungulira. Tiyeni tisinthe dziko ndi machitidwe athu abwino. Kumbukira, tingathe kuchita chilichonse mwa Khristu amene amatilimbitsa.




Aroma 1:30

amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:1

“Usachite umboni wonama. Munthu wolakwa usamthandize pakumchitira umboni wonama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:16

Koma nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, uzipewe, pakuti anthu olankhula zotere adzanka nanyozeranyozera Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:20

Moto umazima pakasoŵa nkhuni, chonchonso kumene kulibe kazitape, kulibenso ndeu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:19

Suwopa kulankhula zoipa pakamwa pako, lilime lako limapeka mabodza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:9

Munthu wosalabadirako za Mulungu amaononga mnzake ndi pakamwa pake; munthu wochita chilungamo amapulumuka chifukwa cha kudziŵa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:18

Wobisa chidani chake ndi munthu wonama, ndipo wochita ugogodi nchitsiru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:29

M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 16:7-8

m'maŵa mwake mudzaona ulemerero wa Chauta. Wamva madandaulo anu omuŵiringulira aja. Kodi ife ndife yani, kuti inu muzitiŵiringulira?” Ndipo Mose adati, “Ndi Chauta amene adzakupatsani madzulo nyama yoti mudye, ndi m'maŵa buledi woti nkukhuta, chifukwa choti wamva madandaulo anu onse omuŵiringulira aja. Ife ndife yani? Madandaulo anu simudaŵiringulire ife ai, koma Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:28

Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano, kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:8

Mau a kazitape ali ngati chakudya chokoma, anthu amaŵameza onse mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:8

Koma lilime palibe munthu amene angathe kuliŵeta. Ndi loipa, silidziŵa kupumula, ndipo ndi lodzaza ndi ululu wakupha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:2

Uŵauze kuti asamakamba zoipa za wina aliyense, apewe kukangana, akhale ofatsa, ndipo nthaŵi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:13

Amene amanka nachita ukazitape, amaulula zinsinsi. Koma wa mtima wokhulupirika, amasunga pakamwa pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:4

Wochita zoipa amamvera malangizo oipa, wabodza amamvera zochoka m'kamwa monyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:13

Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa, pakamwa pako pasakambe zonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 14:27

“Kodi anthu oipa chotereŵa, adzaleka liti kundiŵiringulira? Ndamva maŵiringulo ao amene akundichitira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:16

Musamangoyendayenda uku ndi uku kumachita ukazitape pakati pa anthu a mtundu wanu. Musachite kanthu kalikonse kamene kangathe kudzetsa imfa ya munthu wina. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:25

Adang'ung'udza m'mahema mwao ndipo sadamvere mau a Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:19

Amene amanka nachita ugogodi, amaulula zinsinsi. Nchifukwa chake usamagwirizane naye wolankhula zopusayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:23

Amene amagwira pakamwa ndi kusamala zokamba zake, sapeza mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:14

Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:4

Mau ofatsa amakhala ngati mtengo wopatsa moyo, koma mau oipa amapweteka mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 15:2-3

Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona. Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa, kapena kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:9

Abale musamanenerana zoipa pakati panu, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Onani, woweruza waima pa khomo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 11:1

Tsiku lina anthu adadandaula, Chauta alikumva. Chauta atamva zimenezo, adapsa mtima, ndipo moto wa Chautayo udayaka pa anthuwo, nupsereza mbali imodzi ya mahema ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:29-30

Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi, Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 16:2-3

Ndipo khamu lonse lidadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu muja kuti, Komabe ena mwa iwowo sadamvere zimene adaanena Mosezo, adasungako mpaka m'maŵa mwake. Koma kutacha, adaona kuti tonseto tagwa mphutsi, ndipo tikununkha. Apo Mose adaŵapsera mtima anthuwo. Ankatola m'maŵa mulimonse, ndipo aliyense ankatola monga m'mene ankasoŵera. Koma dzuŵa likatentha, tinthuto tinkasungunuka. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi ankatola chakudya cha masiku aŵiri, chokwanira malita anai ndi theka pa munthu mmodzi. Ndipo atsogoleri onse a Aisraele adabwera kwa Mose kudzamuuza zimenezo. Tsono Mose adaŵauza kuti, “Chauta walamula kuti, ‘Maŵa ndi tsiku lopumula, tsiku la Sabata, loperekedwa kwa Chauta. Wotchani yense amene mufuna kuwotcha, ndipo muphike yense amene mufuna kuphika. Wotsalako mumsunge padera mpaka maŵa.’ ” Mose atalamula zimenezi, anthuwo adasungadi totsalato mpaka m'maŵa mwake tosaonongeka, ndipo sitidagwe mphutsi. Pambuyo pake Mose adauza anthuwo kuti, “Idyani ameneyu lero, chifukwa lero ndi tsiku la Sabata loperekedwa kwa Chauta. Lero simumpezatu kunjaku. Mutole chakudya pa masiku asanu ndi limodzi. Koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, tsiku la Sabata, chakudyacho sichidzapezeka.” Pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo anthu ena adaapita kuti akatole chakudya, koma sadachipeze. Pamenepo Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi mudzakhalabe osamvera mau anga ndi malamulo anga mpaka liti? Kumbukirani kuti ndine Chauta, amene ndidakupatsani tsiku la Sabata. Tsono chifukwa cha chimenechi ndimakupatsani chakudya chokwanira masiku aŵiri pa tsiku lachisanu ndi chimodzi. Aliyense azingokhala komwe aliriko pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Asachoke ndi mmodzi yemwe pakhomo pake.” “Kukadakhala bwino Chauta akadatiphera ku Ejipito konkuja, kumene tinkakhala tikudya nyama ndi buledi, ndipo tinkakhuta. Koma inu mwatifikitsa kuchipululu kuno kuti mutiphe tonse ndi njala.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 12:1

Miriyamu ndi Aroni adayamba kumnena Mose chifukwa cha mkazi wachikusi amene Moseyo adamkwatira, poti adakwatiradi mkazi wa ku Kusi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:10

Musadandaule monga momwe adaadandaulira ena mwa iwo: paja adaphedwa ndi mngelo wodzetsa imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:16-17

Koma kwa munthu woipa Mulungu amati, “Ukuvutikiranji ndi kutchula malamulo anga? Bwanji pakamwa pako pakulankhula za chipangano changa? Iwe sufuna kulangizidwa, umaponya mau anga ku nkhongo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 1:27

Inu munkangodandaula m'mahema mwanu nkumati, “Chauta amadana nafe. Nchifukwa chake adatitulutsa ku dziko la Ejipito, natipereka kwa Aamori kuti atiphe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:11

Ndiye iwowo polandira, adayamba kuŵiringula,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:5

Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa. Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:12

Wonyada sakonda kumdzudzula, sapitako kwa anthu anzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:21-22

Usamasamala zonse zokamba anthu, mwinamwina udzamva wantchito wako akukutukwana. Mumtima mwako ukudziŵa kuti iweyonso udatukwanapo anthu ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:15

Pakati panu pasakhale ndi mmodzi yemwe wogwa m'mavuto chifukwa choti wapha munthu, kapena waba, kapena wachita choipa, kapena waloŵerera za eniake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:10

Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:3

Pamene ndinali ndisanaulule tchimo langa, thupi langa linali lofooka, chifukwa cha kubuula tsiku lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:15

Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:164

Ndimakutamandani kasanunkaŵiri pa tsiku, chifukwa cha malangizo anu olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 17:3

Koma anthu aja anali ndi ludzu loopsa, ndipo ankangoŵiringulira Mose, kuti “Chifukwa chiyani mudatitulutsa ku Ejipito kuti mutiphe ndi ludzu, ife pamodzi ndi ana athu ndi zoŵeta zathu?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 14:29

Mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu muno. Anthu onse, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, amene adandiŵiringulira,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36-37

Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:11

Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:30-31

Munthu wabwino amalankhula zanzeru, pakamwa pake pamatuluka zachilungamo. Malamulo a Mulungu amakhala mumtima mwake, motero sagwedezeka poyenda m'moyo uno.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 10:20

Ngakhale mumtima mwako usamainyoza mfumu. Ngakhale m'chipinda mwako momwe usamatukwana wolemera. Mwina kambalame kamumlengalenga kapena kachilombo kena kouluka nkukumvera, kenaka nkukaulula zonse kwa amene umaŵanenawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 16:11

Tsono kutereku nkukangana ndi Chauta, pamene iwe ndi gulu lako mwasonkhana chotere. Kodi Aroni ndiye yani kuti muzimuukira?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 59:12

Akodwe ndi kunyada kwao, chifukwa cha uchimo wa m'kamwa mwao, ndi mau a pakamwa pao. Chifukwa chakuti amatemberera ndipo amanama,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:1

Tsono woweruza enawe, kaya ndiwe yani, ulibe pozembera. Pakutitu pamene ukuweruza mnzako, ukudzitsutsa wekha, popeza kuti iweyo woweruzawe umachita zokhazokhazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 14:3

Koma ai, anthu onse ndi osokera, onsewo ndi oipa chimodzimodzi. Palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino, ai, palibiretu ndi mmodzi yemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:37

“Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:9

Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 41:6-7

Amene amabwera kudzandiwona, ndi wosakhulupirika, mumtima mwake amaganiza zoipa za ine, ndipo akatuluka, amakaziwanditsa. Onse odana nane amanong'onezana za ine, amayesa kuti zoipa zandigwera chifukwa cha kuipa kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1-2

“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha? Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa. “Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka. “Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu? Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai. Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto. M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:12-13

Nkhunzi zambiri zandizungulira. Adani amphamvu ngati nkhunzi za ku Basani andizinga. Andiyasamira kukamwa, ngati mkango wobangula wofuna kundikadzula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:19

Adalankhula motsutsana ndi Mulungu nati, “Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya m'chipululu muno?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 21:5

Anthu aja adayamba kuŵiringulira Mulungu ndiponso Mose, adati, “Chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito kuti tidzafere m'chipululu muno? Pakuti kuno kulibe ndi chakudya chomwe ngakhalenso madzi, ndipo chakudya chachabechi chatikola.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:19-20

Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso. Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:155

Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 12:2-3

Aliyense amangonamiza mnzake, amathyasika ndi pakamwa pake, amalankhula ndi mitima iŵiri. Inu Chauta, tsekani pakamwa ponse pothyasika letsani lilime lililonse lolankhula modzikuza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 11:4-6

Nthaŵi imeneyo anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraele adamva nkhuli yaikulu. Aisraelenso adayamba kudandaula, adati, “Ndani adzatipatsa nyama kuti tizidya? Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Ejipito, minkhaka ija, mavwende ndi anyezi wamitundu-mitundu. Koma tsopano mphamvu zathu zatha, ndipo sitikuwona kanthu kena kakudya koma mana basi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:15

Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 28:3

Musandichotsere kumodzi ndi anthu oipa, anthu amene amachita zonyenga, amene amalankhula zamtendere ndi anzao, koma mitima yao ndi yodzaza ndi chidani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:3

Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:15

“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:25

Munthu waumbombo amautsa mkangano, koma wokhulupirira Chauta adzalemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:28-32

Tsono popeza kuti iwo sadalabadireko za kumvera Mulungu, Mulunguyo adaŵasiya m'maganizo ao opusa, kotero kuti amachita zosayenera. Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi, Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao. Ndi opusa, osakhulupirika, okhakhala moyo, ndi opanda chifundo. Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:4

Munthu wotere ndi wodzitukumula ndi kunyada, sadziŵa kanthu. Mtima wake ngwodwala, wongofuna zotsutsanatsutsana ndi kukangana pa mau chabe. Zimenezi zimabweretsa kaduka, kusamvana, kusinjirirana, kuganizirana zoipa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:8-9

Amanyodola ndi kumalankhula zoipa, amadzikuza ndi kumaopseza ena kuti, “Tikupsinjani.” Pakamwa pao pamalankhula monyoza Mulungu kumwamba, ndipo lilime lao ndi losamangika pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 16:1-3

Kora mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, ndiponso Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Peleti, adzukulu a Rubeni, Ndiponso kodi Mulungu adakulolani kuti mubwere pafupi ndi Iye, inu pamodzi ndi abale anu Alevi, amene ali nanu? Kodi mukukhumbiranso ndi unsembe womwe? Tsono kutereku nkukangana ndi Chauta, pamene iwe ndi gulu lako mwasonkhana chotere. Kodi Aroni ndiye yani kuti muzimuukira?” Apo Mose adatuma munthu kukaitana Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu. Ndipo iwo adati, “Ife sitibwera kumeneko. Kodi zikukucheperani kuti mudatitulutsa ku dziko lamwanaalirenji ku Ejipito, kuti tifere m'chipululu muno? Kodi mukufunanso kuti mukhale mfumu yathu yotilamula? Kuwonjezera apo, simudatiloŵetse m'dziko lamwanaalirenji, ndipo simudatipatse polima kapena minda yamphesa, kuti ikhale choloŵa chathu. Kodi mukufuna kutigwira m'maso? Ife sitibwera kumeneko.” Apo Mose adapsa mtima kwambiri, ndipo adauza Chauta kuti, “Musalandire nsembe za anthu ameneŵa. Sindidaŵalande ndi bulu mmodzi yemwe, ndipo sindidalakwire ndi mmodzi yemwe mwa iwo.” Tsono Mose adauza Kora kuti. “Maŵa iwe pamodzi ndi anthu a gulu lako 250, mubwere ku hema lamsonkhano, iweyo ndi anthu akowo ndi Aroni. Aliyense mwa inu atenge chofukizira lubani, athiremo lubani. Nonsenu mubwere ku chihemacho, aliyense ndi chofukizira chake. Zofukizirazo zikhale 250, ndipo iweyo ndi Aroni mutenge aliyense chakechake.” Choncho munthu aliyense adatenga chofukizira lubani, naikamo moto, ndi kuthiramo lubani, ndipo adakaimirira pa chipata cha chihema chamsonkhano, pamodzi ndi Mose ndi Aroni. Kora adasonkhanitsa mpingo wonse pa chipata cha chihema chamsonkhano moyang'anana ndi Mose ndi Aroni. Ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera mpingo wonsewo. adakopa anthu. Adaukira Mose, iwowo pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele 250, osankhidwa ndi anthu pa msonkhano, anthu otchuka. Ndipo Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Chokani pakati pa mpingowu kuti ndiwononge onse nthaŵi imodzi.” Apo iwo adadziponya pansi, nati, “Inu Mulungu, Chauta mwini moyo wa anthu onse, kodi mukwiyira mpingo wonse chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi?” Chauta adauza Mose kuti, “Uza mpingo kuti achoke pafupi ndi mahema a Kora, Datani ndi Abiramu.” Tsono Mose adapita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akuluakulu a Aisraele adamtsatira. Mose adauza mpingowo kuti, “Ndapota nanu, chokani pakati pa mahema a anthu oipaŵa, ndipo musakhudze chinthu chao chilichonse, kuti angakuphereni kumodzi chifukwa cha zoipa zao.” Choncho anthuwo adachokapo pafupi ndi mahema a Kora, Datani ndi Abiramu. Pamenepo Datani ndi Abiramu adatuluka naima pakhomo pa mahema ao pamodzi ndi akazi ao, ana ao ndi makanda ao. Tsono Mose adati, “Pano muzindikira kuti ntchito zonse ndikuchitazi, adandituma ndi Chauta, si za m'mutu mwanga ai. Anthu aŵa akafa monga m'mene amafera anthu onse, Mulungu osaŵalanga, ndiye kuti Chauta sadanditume ai. Onsewo adasonkhana pamodzi ndipo adaukira Mose ndi Aroni, naŵauza kuti, “Inu mwankitsa nazo. Mpingo wonse ndi woyera, munthu aliyense mumpingomo ndi wa Chauta, ndipo Chauta ali pakati pathu. Chifukwa chiyani tsono mukudziyesa opambana pa msonkhano wa Chauta?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:18

Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:3

Ponseponse amandilankhula mau achidani, amandinena popanda chifukwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:21

Usamasamala zonse zokamba anthu, mwinamwina udzamva wantchito wako akukutukwana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:4

Kodi iweyo ndiwe yani kuti uweruze wantchito wamwini kuti walakwa? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza, popeza kuti Ambuye angathe kumkhozetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:26

Tisakhale odzitukumula, oputana, kapena ochitirana dumbo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:6

Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:21

Amagwirizana kuti aononge anthu osalakwa, nagamula kuti opanda mlandu aphedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:1

Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo, koma mau ozaza amakolezera ukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:22

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:24-25

Motero iwo adanyoza dziko lokoma, chifukwa sadakhulupirire malonjezo ake. Adang'ung'udza m'mahema mwao ndipo sadamvere mau a Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 11:1-3

Tsiku lina anthu adadandaula, Chauta alikumva. Chauta atamva zimenezo, adapsa mtima, ndipo moto wa Chautayo udayaka pa anthuwo, nupsereza mbali imodzi ya mahema ao. Mose adaŵamva anthu aja akulira m'mabanja mwao monse, aliyense atakhala pakhomo pa hema lake. Chauta adaapsa mtima kwambiri, ndipo nayenso Mose adaaipidwa nazo. Mose adafunsa Chauta kuti, “Chifukwa chiyani mwandivutitsa chotere mtumiki wanune? Chifukwa chiyani simudandikomere mtima, mpaka kundisenzetsa katundu wa anthu onseŵa? Kodi ndidaatenga pathupi pa anthu onseŵa ndine? Kodi ndidaŵabala ndine, kuti Inu muzindiwuza kuti ndiŵafungate pachifuwa panga, monga momwe mlezi amachitira poyamwitsa mwana, ndipo kuti ndipite nawo ku dziko limene mudalonjeza makolo ao molumbira kuti mudzaŵapatsa? Kodi nyama yoti ndiŵapatse anthu onseŵa, ndiitenga kuti? Iwowo akundilirira ine kuti, ‘Tipatseni nyama, tidye.’ Ine sindingathe kuŵasamala ndekha anthu onseŵa. Katundu ameneyu sindingathe kumsenza. Ndipotu mukafuna kundichita zimenezi, mungondipha basi, ngati mwandikomera mtima, kuti ndisaonenso mavutowo.” Chauta adauza Mose kuti, “Usonkhanitse amuna makumi asanu ndi aŵiri mwa akuluakulu a Aisraele, anthu amene ukuŵadziŵa kuti ndi atsogoleri ndi akapitao a anthu. Ubwere nawo ku chihema chamsonkhano, ndipo aime kumeneko pamodzi ndi iwe. Ine nditsika kudzalankhula nawe komweko. Ndidzatengako mzimu uli pa iwe ndi kuuika pa iwowo. Ndipo adzasenza nawe katundu wa anthuwo, kuti usasenzenso wekha. Uŵauze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera zamaŵa, ndipo mudzadya nyama. Inuyo mudalira Chauta alikumva, pamene munkati, “Ndani atipatse nyama tidye? Paja zinthu zinkatiyendera bwino ku Ejipito.” Nchifukwa chake Chauta adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya. Simudzaidya tsiku limodzi lokha, kapena masiku aŵiri okha, kapena masiku asanu okha, kapena masiku khumi okha, kapena masiku makumi aŵiri okha ai. Tsono anthu adalira kwa Mose, ndipo Moseyo atapemphera kwa Chauta, pompo motowo udazilala. Imeneyo mudzaidya mwezi wathunthu, mpaka izikachita kutulukira m'makutu, inuyo nkumadwala nayo. Zimenezi zidzachitika chifukwa choti mwakana Chauta amene amakhala pakati panu, ndipo mwadandaula pamaso pake nkumati, “Chifukwa chiyani tidatuluka ku Ejipito?” ’ ” Koma Mose adati, “Anthu amene ndikuyenda nawoŵa akukwanira 600,000. Ndipo Inu mwanena kuti, ‘Ndiŵapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu.’ Kodi zidzaphedwa nkhosa kapena ng'ombe zingati kuti ziŵakwanire? Ngakhale nsomba zonse zam'nyanja, kodi zingathe kukwanira?” Chauta adafunsanso Mose kuti, “Kodi dzanja la Chauta ndi lalifupi? Tsono uwona lero lomwe lino, ngati zichitikadi monga momwe ndanenera kapena ai.” Choncho Mose adatuluka nakauza anthu mau a Chauta aja. Adasonkhanitsa anthu makumi asanu ndi aŵiri mwa akuluakulu a Aisraele, naŵakhazika mozungulira chihema chamsonkhano. Tsono Chauta adatsika mu mtambo nayamba kulankhula ndi Mose. Ndipo adatengako mzimu umene unali pa Moseyo nauika pa akuluakulu makumi asanu ndi aŵiriwo. Anthuwo atalandira mzimu uja, adayamba kulosa. Koma sadapitirire kulosako. Anthu aŵiri adatsalira m'mahema, wina anali Elidadi, wina Meladi, ndipo mzimu udakhala pa iwowo. Anali nao m'gulu la olembedwa aja, koma sadapite nao ku chihema chamsonkhano, motero ankalosera m'mahema. Ndiye mnyamata wina adathamanga nakauza Mose kuti, “Elidadi ndi Meladi akulosa kumahemaku.” Apo Yoswa, mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose, mmodzi mwa anthu ake osankhidwa aja, adati, “Mbuyanga Mose, aletseni amenewo.” Koma Mose adamuuza kuti, “Kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikadakondwa anthu onse a Chauta akadakhala aneneri, ndipo Chauta akadaika mzimu wake pa iwo.” Motero malowo adaŵatcha Tabera, chifukwa choti moto wa Chauta udayaka pakati pao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:10

Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:13

Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 38:13-14

Koma ine ndili ngati gonthi, sindikumvako, ndili ngati mbeŵeŵe amene satha kulankhula. Inde ndili ngati munthu amene saamva, chifukwa sindingathe kuyankhapo kanthu, pamene akundilankhula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:1

Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:20

kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 141:3

Muike mlonda pakamwa panga, Inu Chauta. Mulonde pa khomo la milomo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 57:4

Ndimagona pakati pa anthu olusa amene ali ngati mikango. Mano ao ali ngati mikondo ndi mivi, lilime lao lili ngati lupanga lakuthwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:15

Kodi zinthu zanga ndisachite nazo monga ndifunira? Kapenatu ukuipidwa nawo ufulu wanga eti?’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:18

Onse onyada ndi onama olankhula mwamwano ndi monyoza kwa anthu abwino, muŵakhalitse chete.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:19

Mau oona amakhala mpaka muyaya, koma zabodza sizikhalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:13-14

M'kamwa mwao m'moopsa ngati manda apululu, ndi lilime lao amalankhula zonyenga, pamilomo pao pamatuluka mau aululu, ululu wake wonga wa mamba. M'kamwa mwao m'modzaza ndi matemberero, mumatuluka mau oŵaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:2

Usamafulumira kulankhula, ndipo usamalumbira msanga kwa Mulungu mumtima mwako. Paja Mulungu ali Kumwamba, iwe uli pansi pano, tsono usamachulukitsa mau ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:26

Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:20

Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:3

Kulankhula kwa chitsiru kumamuitanira ndodo pa msana, koma mau a munthu wanzeru amamteteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:22-23

popeza kuti sadadalire Mulungu, sadakhulupirire mphamvu zake zopulumutsa. Komabe Iye adalamula mitambo yamumlengalenga, natsekula zitseko zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:8

Koma pamene ophunzira ake adaona zimenezi, adaipidwa nazo nkumauzana kuti, “Chifukwa chiyani kusakaza zinthu chotere?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 28:3-4

Musandichotsere kumodzi ndi anthu oipa, anthu amene amachita zonyenga, amene amalankhula zamtendere ndi anzao, koma mitima yao ndi yodzaza ndi chidani. Muŵabwezere anthu otere molingana ndi ntchito zao, muŵalange molingana ndi zoipa zimene ankachita. Muŵabwezere molingana ndi ntchito zao, Muŵalange molingana ndi kuipa kwa ntchito zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 21:5-6

Anthu aja adayamba kuŵiringulira Mulungu ndiponso Mose, adati, “Chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito kuti tidzafere m'chipululu muno? Pakuti kuno kulibe ndi chakudya chomwe ngakhalenso madzi, ndipo chakudya chachabechi chatikola.” Tsono Chauta adatumiza njoka za ululu wonga moto pakati pa anthu aja, ndipo zidaŵaluma, kotero kuti Aisraele ambiri adafa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:16-19

Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa, mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa, mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:11

Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu. Onse olumbirira Iye, adzamtamanda, koma pakamwa pa anthu abodza padzatsekedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:1-2

Mulungu adzambatuke, adani ake amwazikane. Onse amene amamuda, athaŵe pamaso pake. Anthu anu adapezamo malo okhala. Inu Mulungu, mudapatsa anthu osauka zosoŵa zao mwa ubwino wanu. Ambuye apereka lamulo. Nchachikulu chiŵerengero cha amene abwera ndi uthenga wakuti, “Mafumu a magulu a ankhondo akuthaŵa, indedi akuthaŵa. Tsono azimai ku mudzi akugaŵana zofunkha, ngakhale atsalira pakati pa makola ankhosa. “Zofunkhazo zikuwoneka ngati mapiko a nkhunda okutidwa ndi siliva, nthenga zake nzokutidwa ndi golide wonyezemira.” Pamene Mphambe adabalalitsa mafumu kumeneko, ku Zalimoni kudagwa chisanu choopsa. Iwe phiri la Basani, phiri laulemerero, Iwe phiri la Basani, phiri la nsonga zambiri! Iwe phiri la nsonga zambiriwe, chifukwa chiyani ukuliyang'ana mwansanje phiri limene Mulungu adasankha kuti azikhalapo? Ndithu Chauta adzakhalapo mpaka muyaya. Ambuye adafika ku malo ao oyera kuchokera ku Sinai, ali ndi magaleta amphamvu zikwi zambirimbiri. Inu mudakwera kumwamba, mutatenga am'ndende ambiri, ndipo mudalandira mphatso kwa anthu, ngakhale kwa anthu oukira, kuti mudzakhale kumeneko, Inu Chauta Mulungu. Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku. Amwazeni iwowo monga m'mene mphepo imachitira utsi. Anthu oipa aonongeke pamaso pa Mulungu, monga m'mene sera amasungunukira pa moto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:10

“Aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira, koma wonyoza Mzimu Woyera ndi mau achipongwe, Mulungu sadzamkhululukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:18

Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 11:17-19

Tsopano pali mfundo ina imene sindingakuyamikireni. Ndiye kuti misonkhano yanu imabweretsa zoipa osati zabwino ai. Choyamba, ndikumva kuti mukamasonkhana mu mpingo, mumapatulana. Ndipo ndikhulupirira kuti zimenezi kwinaku nzoona. Nkofunika ndithu kuti pakhale kusiyana maganizo pakati panu, kuti amene ali okhoza pakati panu adziŵike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:8-9

Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse. Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu, amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wakumwamba, m'dzina la Yesu, ndikukuthokozani chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu pa moyo wanga, ngakhale ndine munthu wotani komanso zolakwa zomwe ndachita. Chikhulupiriro changa sichitha ndipo ndikudziwa kuti machimo anga m'nawataya kuya kwa nyanja. Mwa inu mulibe chiweruzo chifukwa mwandiyeretsa ndi magazi anu Yesu. Ndikukupemphani tsopano kuti mutsegule milomo yanga kuti ndisamanene bodza ndikuwonjezera mawu omwe amandiwononga ine ndi omwe ali pafupi nane. Mulungu wanga, yeretsani mtima wanga ndi hisopo kuti ndikonde choonadi chanu ndi kuunika kwanu. Mwa inu mulibe mdima ndipo ndikukupemphani mundimasule ku mzimu wa miseche. Ndikutsutsa nsanje, njiru, kukhumudwa ndi chidani. Ndikukupemphani Mzimu Woyera kuti mubwezeretse ubale wanga ndi Mulungu, chifukwa sindifunanso kumukhumudwitsa ndi mawu ambiri. Ndikukhulupirira ndi mtima wonse Ambuye kuti mawu a pakamwa panga ndi kuganizira kwa mtima wanga kukhale kokondweretsa inu. Munandiphunzitsa nthawi zonse kumenyana ndi choipa, chonde ndithandizeni kuti ndipamwamba ndipo ndisapereke mwayi ku zilakolako za thupi langa, gwirani lilime langa. Atate, ikani chotchinga pakamwa panga pamene ndikufuna kuvulaza mnzanga, kumbukirani mtima wanga kufunika kwanga pamene ndikumva wofooka, wochepa ndi wonyozeda. Ndikufuna mphamvu yanu, chikondi chanu, mawu anu ndi chilimbikitso chanu. Mundimasule ku choipa ichi kuti ndikupembedzeni ndi mtima woyera ndi milomo yoyera. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa