Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -



MAVESI OKHUDZA CHItonthozo

MAVESI OKHUDZA CHItonthozo

Zimakhala zovuta kudziwa kuti simudzakumananso ndi munthu amene wamwalirayu, munthu amene mumamukonda kwambiri ndipo anali wofunika pa moyo wanu. Simudzakumananso naye kuti mucheze, museke, ndiponso mugawane nthawi zosaiwalika. Tonse timadutsamo m'nthawi yachisoni, nthawi yomvetsa chisoni. M'nthawi ngati imeneyi tingalire ndikumva kuwawa ndipo si tchimo. Yesu nayenso analira atamva kuti Lazaro, mnzake, wamwalira (Yohane 11:35). Ndikofunika kuulula zakukhosi kwanu m'nthawi yachisoni.

Koma ngakhale muli pachisoni, musalole kuti chisonicho chikulepheretseni kupitiriza ndi moyo. Mulungu ali nanu kuti apukute misozi yanu, atonthoze mtima wanu, ndikubwezeretsanso chimwemwe pa nkhope yanu. Ingomulolani Mulungu achite zimenezi. (2 Akorinto 1:3) Dalitsani Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wachifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.




Masalimo 27:1

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:23-24

Koma chonsecho ndili ndi Inu nthaŵi zonse. Inu mumandigwira dzanja lamanja. Mumandiwongolera ndi malangizo anu, pambuyo pake mudzandilandira ku ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 19:25-26

“Mtheradi ndikudziŵa kuti Momboli wanga alipo, ndipo pa nthaŵi yomaliza adzabwera kudzanditeteza. Khungu langa litatha nkuwonongeka, m'thupi langa lomweli ndidzamuwona Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:15-16

Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:1

Ine ndimathaŵira kwa Inu Chauta. Musandichititse manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:29

Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:22

Chomwecho inunso mukuvutika tsopano, koma ndidzakuwonaninso. Pamenepo mtima wanu udzakondwa, ndipo palibe munthu amene adzakulandani chimwemwe chanucho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-5

Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 60:20

Chokuunikira ngati dzuŵa sichidzaloŵanso, ndipo chokuunikira ngati mwezi sichidzazimiriranso, chifukwa ndi Chauta amene adzakhala kuŵala kwako mpaka muyaya. Choncho masiku ako olira adzatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:5

Pakuti monga tikumva zoŵaŵa kwambiri pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatilimbitsa mtima kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:24

Khalani amphamvu ndipo mulimbe mtima, inu nonse okhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:3-4

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:21

Kwa inetu moyo ndi Khristu amene, ndipo nayonso imfa ili ndi phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:12

Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 3:22-23

Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha. M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:13

Pambuyo pake ndidamva mau ochokera Kumwamba. Adati, “Lemba kuti, Ngodala anthu akufa amene kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno afa ali otumikira Ambuye.” Mzimu Woyera akuti, “Inde, ngodaladi. Akapumule ntchito zao zolemetsa, pakuti ntchito zaozo zimaŵatsata.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:20-21

Mudzanditsitsimutsanso Inu amene mwandiwonetsa mavuto ambiri oŵaŵa, mudzanditulutsanso m'dzenje lozama la pansi pa nthaka. Inu mudzaonjezera ulemu wanga ndipo mudzandisangalatsanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:26

Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:10

“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:13

Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:9

koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:76

Chikondi chanu chosasinthika chindisangalatse ine mtumiki wanu, monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:15

Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:4

Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1-2

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:11-12

Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:12

Inu mudalola kuti adani atikwere pa mutu, tidaloŵa m'moto ndiponso m'madzi, komabe Inu mwatifikitsa ku malo opulumukirako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:18

Tsono popeza kuti iye yemwe adazunzikapo ndi kuyesedwapo, ndiye kuti angathe kuŵathandiza anthu amene amayesedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:20

Mulungu wathu ndi Mulungu wotilanditsa, ndi Mulungu, Ambuye amene amatipulumutsa ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:13

Anamwali adzavina mokondwa, achinyamata ndi okalamba omwe adzasangalala. Kulira kwao kuja ndidzakusandutsa chimwemwe. Ndidzaŵasangalatsa, ndidzaŵakondwetsa, nkuchotsa chisoni chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:39

Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 7:17

Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakatikati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wao, adzaŵatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Ndipo Mulungu adzaŵapukuta misozi yonse m'maso.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:21

“Ndinu odala, inu amene mukumva njala tsopano, chifukwa mudzakhuta. “Ndinu odala, inu amene mukulira tsopano, chifukwa mudzakondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:2

Anthu amene ankayenda mumdima aona kuŵala kwakukulu. Amene ankakhala m'dziko la mdima wandiweyani, kuŵala kwaŵaonekera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 4:8

Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:3-4

“Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, lidule nkulitaya. Ndi bwino kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kupambana kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.” “Anthu akale aja adaaŵalamulanso kuti, ‘Ngati munthu asudzula mkazi wake, ampatse mkaziyo kalata yachisudzulo.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, akumchititsa chigololo mkaziyo ngati akwatiwanso. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo. “Mudamvanso kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usalumbire monama, koma uchitedi zimene udaŵalonjeza Ambuye molumbira.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muleke nkulumbira komwe. Usalumbire kuti, ‘Kumwambadi!’ Paja Kumwamba kuli mpando waufumu wa Mulungu. Usalumbire kuti, ‘Pali dziko lapansi!’ Paja dziko lapansi ndi chopondapo mapazi ake. Usalumbire kuti, ‘Pali Yerusalemu!’ Paja Yerusalemu ndi mzinda wa Mfumu yaikulu. Usalumbire ngakhale pa mutu wako, pakuti sungathe kusandulitsa ndi tsitsi limodzi lomwe kuti likhale loyera kapena lakuda. Muzingoti, ‘Inde,’ kapena ‘Ai.’ Zimene muwonjezerepo nzochokera kwa Satana, Woipa uja. “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Diso kulipa diso, dzino kulipa dzino.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu woipa osalimbana naye. Ngati munthu akumenya pa tsaya la ku dzanja lamanja, upereke linalonso. Ngodala anthu amene akumva chisoni, pakuti Mulungu adzaŵasangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:9

Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 130:5

Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 38:17

Chimene ndidamvera zoŵaŵa nkuti ndipeze bwino. Mwapulumutsa moyo wanga ku manda, mwataya machimo anga onse kumbuyo kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 20:36

Iwo adzakhala ngati angelo, mwakuti sangafenso ai. Iwo ndi ana a Mulungu popeza kuti Iye adaŵaukitsa kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 12:23

Koma tsopano mwanayo wafa. Nanga ndizikaniranjinso zakudya? Kodi ndingathe kumbwezanso? Ine ndidzapitadi kumene kuli iyeko, koma iyeyo sadzabwereranso kwa ine.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:10

Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:7

Iwe mtima wanga, bwerera ku malo ako opumulira, chifukwa Chauta wakuchitira zokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 51:11

Amene mudaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa. Chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pankhope pao. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chisangalalo. Chisoni ndi kubuula zidzatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:5

Ngati takhala amodzi ndi Khristu mu imfa yake, momwemonso tidzakhala amodzi naye pa kuuka kwa akufa, monga momwe adaukira Iyeyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:7-8

Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu. Mtima wanga ukukangamira Inu, dzanja lanu lamanja likundichirikiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:8-9

Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima. Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:14

Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:20-22

Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu. Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera. Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:6

Ndipo ndimati, “Ndikadakhala ndi mapiko onga a njiŵa, bwenzi nditauluka kupita kutali kukapuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:4

Ngodala anthu amene akumva chisoni, pakuti Mulungu adzaŵasangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 25:8

Chauta adzathetsa imfa mpaka muyaya, adzapukuta misozi m'maso mwa aliyense, ndipo adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi. Watero Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:22

Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 3:31-32

Ndithudi Ambuye sadzataya atumiki ao mpaka muyaya. Angathe kulanga mwankhalwe, komabe adzaonetsa chifundo, chifukwa chikondi chao nchochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:7

Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:2

Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:8

Ndithu tikulimba mtima, ndipo makamaka tikadakonda kutuluka m'thupi lathu lino ndi kukakhala kwa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:9

Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28

“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:1-2

Anthu a Mulungu okhulupirira amafa, ndipo palibe amene amasamalako. Anthu okhulupirika amatengedwa, ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake. Anthu olungama amachotsedwa, kuti tsoka lisaŵagwere, Mudatopa nawo mtunda wouyenda, koma osanena kuti, “Ndingoleka!” Mudapezera zina mphamvu, mwakuti simudalefuke konse. “Kodi ndi milungu yanji imene mudaiwona nkuchita nayo mantha, kotero kuti mudandinamiza nkundiiŵaliratu, osalabada konse za Ine? Kodi mwaleka kundiwopa chifukwa choti ndakhala chete pa nthaŵi yaitali? Mukuganiza kuti zimene mumachita nzolungama, koma makhalidwe anu ndidzaŵaonetsa poyera, ndipo mafano sadzakuthandizani. Mukamafuula kufuna chithandizo, mafano anuwo akupulumutseni! Mphepo idzaiyalula milunguyo, mpweya udzaiwulutsa. Koma amene amakhulupirira Ine, adzalandira dziko lokhalamo, ndi kumapembedza pa phiri langa loyera.” Padzamveka mau akuti, “Lambulani, lambulani ndi kukonza mseu. Chotsani chitsa chilichonse pa njira yodzeramo anthu anga.” Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima. “Ndine amene ndidalenga anthu anga ndi kuŵapatsa mpweya wa moyo, motero sindidzapitirira kukangana nawo kapena kuŵakwiyira mpaka muyaya. “Ndidaŵakwiyira chifukwa anali okonda chuma dziŵi. Tsono ndidaŵalanga, ndi kuŵafulatira mokwiya. Koma iwowo adakhalabe ouma mitu, ndipo adapitirira kuchita ntchito zao zoipa. “Ndidaona m'mene ankachitira, komabe ndidzaŵachiritsa. Ndidzaŵatsogolera ndi kuŵatonthoza. Anthu olira nao adzandiyamika ndi milomo yao. Anthu onse akutali ndi apafupi, ndidzaŵapatsa mtendere. Ndidzachiritsa anthu anga. ndipo amafa mwamtendere. Amene ali olungama amapumula bwino pogona pao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:18

Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:1

Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Akuchiritsa a mtima wachisoni, ndipo akumanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:27

“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:18

Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:3-4

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:4

Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:13-14

Abale, tifuna kuti mudziŵeko za anthu amene adamwalira, kuti chisoni chanu chisakhale ngati cha anthu ena amene alibe chiyembekezo. Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:4

Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 11:25-26

Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:55

“Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:50

Chimene chimandisangalatsa m'masautso anga nchakuti malonjezo anu amandipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:19

Pamene nkhaŵa zikundichulukira, Inu mumasangalatsa mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:35-39

Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.” Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda. Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:11

Koma Chauta amakondwera ndi anthu omuwopa, amene amadalira chikondi chake chosasinthika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:13

Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga! Fuula ndi chimwemwe, iwe dziko lapansi! Yambani nyimbo, inu mapiri! Chauta watonthoza mtima anthu ake, ndi kuŵamvera chifundo anthu ake ovutika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:15

Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta, ndi yamtengowapatali pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:19

Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:26

Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:13

Ndidzakusangalatsani ku Yerusalemu monga momwe mai amasangalatsira mwana wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:8

Inu mwaona kupiripita kwanga, mudziŵa kuchuluka kwa misozi yanga. Kodi zonsezi sizidalembedwe m'buku lanu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:16-18

Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku. Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:8

Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:13-14

Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta m'dziko la amoyo. Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:7-8

Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro. Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira. Ambuye amene ali Woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphothoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1-2

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:7

Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:11

Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:1-2

Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye. Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima. Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu, chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:34

Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:18

Nchifukwa chake tsono muzithuzitsana mtima pokambirana zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Zikomo Ambuye, chifukwa ndinu wochiritsa wanga, wopereka wanga, ndi wolinda wanga. Ndinu amene mumalungama nkhondo zanga, ndipo mumanditsogolera kuchoka mu ulemerero kupita mu ulemerero wina. Mu dzina lamphamvu la Yesu, ndikupempherani Mulungu wanga wamphamvu, kuti ndikuthokozani chifukwa pakati pa mavuto, mwakhala thandizo langa ndi mphamvu yanga. Pakati pa kusowa, mwandipatsa zonse zimene ndikufuna. Mundidzaze ndi kukhalapo kwanu ndi Mzimu Woyera wanu waulemerero. Mtendere wanu wopambana luntha lonse usunge mtima wanga ndi maganizo anga. Pakati pa mavuto, ndikhale ndi chikhulupiriro chonse kuti mukuwongolera zonse. Sungani mtima wanga ku zowawa zonse. Ndipo nthawi zovuta pamene ambiri anandisiya, inu munali nane. Zikomo chifukwa pakati pa mantha, Mzimu wanu Woyera wandipatsa mphamvu kuti ndithane ndi mavuto ndi mayesero, ndipo ndapeza chigonjetso mu dzina la Yesu. Ambuye, pakati pa chete ndi chikhulupiriro, ndadziwa kuti ndinu Mulungu amene mumalungama nkhondo zanga. Mawu anu amati: “Ngakhale nditayenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; chifukwa inu muli ndi ine; ndodo yanu ndi chikwakwa chanu zinditonthoza.” Mu dzina lamphamvu la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa