Dziko lauzimu lilipoli, ndipo mmenemo timayenera kuchita nkhondo ndi pemphero komanso ndi mawu a Mulungu. Nkhondo zazikulu zimamenyedwa m’dziko lauzimu limeneli. M’dziko lauzimuli ndi kumene mphamvu zodabwitsa za Mulungu zimaonekera. Si kumene timangomenyana ndi mizimu yoipa yokha ayi, komanso kumene umapezera zodabwitsa ndi chipambano m’moyo wako.
Pakuti nkhondo yathu si yolimbana ndi anthu, koma ndi olamulira, ndi akuluakulu, ndi mafumu a dziko la mdima lino, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba. (Aefeso 6:12) Apa Mulungu akutiuza za dziko lauzimu limeneli, kumene ukhoza kupambana pokhapokha wodzazidwa ndi mphamvu zake.
Ngakhale kuti timakhala m’dzikoli, sitimenya nkhondo monga mmene dziko limamenyera. Zida zathu za nkhondo si za dziko lino, koma zili ndi mphamvu ya Mulungu yogumula mipanda. (2 Akorinto 10:3-4)
Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.
Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake, koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake.
Musamazunze akazi amasiye ndi ana amasiye, alendo ndiponso amphaŵi. Musamaganizirane zachiwembu m'mitima mwanu.
Nchifukwa chake Woyera uja wa Israele akunena kuti, “Inu mumanyozera zimene ndimakuuzani, mumakhulupirira zopsinja anzanu ndipo mumadalira mabodza. Nchifukwa chake tchimo lanuli lidzakhala ngati mng'ankha pa chipupa chachitali choŵinuka, chimene kugwa kwake nkwadzidzidzi.
Mmphaŵi usamubere, chifukwa choti iyeyo ndi wosauka. Anthu ozunzika usaŵapondereze pa bwalo la milandu. Pakuti Chauta adzaŵateteza pa mlandu wao, ndipo adzaŵalanda moyo amene amalanda zinthu zao.
Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”
Ine ndamva ndithu kulira kwa Aisraele, ndipo ndaŵaonadi mazunzowo amene Aejipito akuŵapsinja nawo.
Mfumu idzateteza anthu osauka, idzapulumutsa anthu osoŵa, koma idzaononga anthu ozunza anzao.
Tsoka kwa amene amapanga malamulo opanda chilungamo, ndi kwa alembi amene amalemba zongovutitsa anzao. Ine ndidakantha mafumu a anthu opembedza mafano, amene mafano ao ndi aakulu kupambana a ku Yerusalemu ndi a ku Samariya. Ndiye ndingalephere kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake omwe, monga momwe ndidachitira Samariya ndi mafano ake?” Ambuye atamaliza ntchito yao yolanga onse pa phiri la Ziyoni ndiponso ku Yerusalemu, adzalanganso mfumu ya ku Asiriya, chifukwa cha kudzitama kwake ndi kunyada kwake. Pakuti mfumuyo ikuti, “Ndachita zimenezi ndi mphamvu zanga ndiponso ndi nzeru zanga, pakuti kumvetsa nkwanga. Ndachotsa malire a mitundu ya anthu, ndipo ndafunkha chuma chao. Ndaŵatsitsa amene anali pa mipando yaufumu. Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu, monga momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame. Monga momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, ndimo m'mene Ine ndidasonkhanitsira dziko lonse lapansi. Ndipo panalibe mbalame ndi imodzi yomwe yoti mapiko phephere-phephere, kapena yoti kukamwa yasa kapena yolira kuti psepsepse.” Koma Chauta akuti: “Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Kodi sowo ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti mkwapulo ukuzunguza munthu, kapena ndodo yanyamula munthu!” Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzatumiza matenda oondetsa kwa ankhondo amphamvu a mfumu ya ku Asiriya. Ndipo mfumuyo kunyada kwake kudzapsa ndi moto wosazimika. Mulungu, Kuŵala kwa Israele, adzakhala ngati moto. Mulungu, Woyera Uja wa Israele, adzakhala ngati malaŵi a moto. Motowo udzaŵatentha ndi kuŵapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi. Adzaononga nkhalango yaikulu ndi nthaka yachonde. Zidzaonongeka m'kati ndi kunja kwake, ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuwonda. Mitengo yotsalira yam'nkhalangomo idzakhala yochepa kwambiri, yoti ndi mwana yemwe nkuiŵerenga. Pakutero amapotoza malamulo poweruza amphaŵi mosalungama. Amaŵalanda zoŵayenerera anthu anga osauka, amafunkha za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye!
Amene amalalatira mmphaŵi, amanyoza Mlengi wake. Amene amakondwerera tsoka la mnzake adzalangidwa.
Anthu ako akhala akunyoza atate ao ndi amai ao. Akhala akuzunza alendo okhala nawe, akhalanso akusautsa ana amasiye ndi akazi amasiye.
Ndidaonanso kuzunza kulikonse kochitika pansi pano. Ndipo ndidaona ozunzidwa akulira misozi, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti aŵatonthoze. Panalibe oŵatonthoza chifukwa ozunzawo anali ndi mphamvu.
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Israele akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo amagulitsa anthu achilungamo ndi siliva, amagulitsa anthu osauka ndi nsapato.
Mumapondereza anthu osauka ndi kuŵabera pa msonkho. Nchifukwa chake ngakhale mwamanga nyumba za miyala yosema, simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, simudzamumwa vinyo wake.
“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse.
Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu, amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa. Akadzuka m'maŵa amakazichitadi, pakuti mphamvu zake ali nazo. Nyamukani, chokani, ano simalo opumulirapo. Zonyansa zanu zaŵaipitsa, zadzetsapo chiwonongeko choopsa. Munthu wina atamapita uku ndi uku akulalika zabodza kuti, ‘Ndithudi mudzakhala ndi vinyo ndi zakumwa zamphamvu zambiri,’ mlaliki wotere ndi amene anthu aŵa angamkonde. “Koma inu banja lonse la Yakobe, ndidzakusonkhanitsani. Onse otsala a ku Israele ndidzaŵasonkhanitsa pamodzi ngati nkhosa m'khola, ngati gulu la zoŵeta pa busa lake. Malowo adzakhala thithithi ndi chinamtindi cha anthu.” Woŵapulumutsa adzaŵatsogolera, ndipo onse adzathyola pa chipata nathaŵa. Idzayambira ndi mfumu yao kudutsa, Chauta adzakhala patsogolo pao. Akasirira minda, amailanda. Akakhumbira nyumba, amazilanda. Amavutitsa munthu ndi banja lake, naŵatengera zonse zimene ali nazo. Nchifukwa chake zimene akunena Chauta ndi izi: “Imvani, ndidzakufitsirani tsoka chifukwa cha zoipa zonsezi. Ndidzakuvekani goli m'khosi mwanu, limene simungathe kulivula. Apo simudzayendanso monyada, chifukwa nthaŵi imeneyo idzakhala yoipa.
Amene amapondereza osauka kuti aonjezere pa chuma chake, kapena amene amangopatsa zinthu olemera okha, adzasanduka wosauka.
Amateteza ana amasiye ndi akazi amasiye. Amakonda anthu achilendo amene amakhala pakati panu, ndipo amaŵapatsa chakudya ndi zovala zomwe.
Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake, ali ngati mvula yamkuntho yosasiya konse chakudya m'minda.
“Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, cha timbeu tokometsera chakudya, ndiponso cha mbeu zakudimba za mtundu uliwonse. Koma simulabadako kuchita chilungamo, kapena kukonda Mulungu. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.
Chauta, mumamva zimene odzichepetsa amapempha. Mudzalimbitsa mitima yao, mudzaŵatchera khutu. Potero mudzaŵateteza amasiye ndi opsinjidwa, kuti anthu amene ali a pansi pano, asadzathe kuwopsezanso.
Chifukwa choti osauka alandidwa zao ndipo osoŵa akudandaula, Chauta akunena kuti, “Ndichitapo kanthu tsopano, ndiŵapulumutsa monga momwe akufuniramo.”
“Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m'phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito. Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. Mukamaŵazunza, Ine ndidzaŵamva iwowo akamalira kwa Ine.
Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.
Wantchito wolembedwa amene ali mmphaŵi ndi wosoŵa, musamamdyerera, ngakhale akhale mnansi wanu kapena mlendo wokhala mumzinda mwanu m'dziko lanulo. Tsiku lililonse dzuŵa lisanaloŵe, muzimlipira malipiro a tsikulo. Ndalamazo akuzisoŵa iyeyo ndipo akuŵerengera zomwezo. Mukapanda kumlipira, adzakulirirani kwa Mulungu ndipo mudzatsutsidwa kuti ndinu ochimwa.
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Anthu a ku Israele akuzunzidwa pamodzi ndi anthu a ku Yuda. Onse amene adaŵagwira ukapolo aŵagwiritsa, osafuna kuŵamasula. Koma mpulumutsi wao ndi wamphamvu, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Adzaŵaimira pa mlandu, kuti apatse mtendere dziko lonse lapansi, koma adzavutitsa okhala ku Babiloni.
Akasirira minda, amailanda. Akakhumbira nyumba, amazilanda. Amavutitsa munthu ndi banja lake, naŵatengera zonse zimene ali nazo.
Koma Mulungu amateteza amphaŵi kwa adani oŵasinjirira, amapulumutsa osauka kwa anthu ofuna kuŵapanikiza.
Tsono inu mudzaŵauze kuti, “Ife tidaali akapolo a mfumu ya dziko la Ejipito, koma Mulungu adatipulumutsa ndi mphamvu zake zazikulu.
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsono ndidzakufikani pafupi kuti ndikuzengeni mlandu. Mosataya nthaŵi ndidzanena mau otsutsa mfiti, anthu achigololo, a umboni wonama, odyerera antchito ao, ovutitsa akazi ndi ana amasiye, ochita alendo zosalungama ndipo onse amene sandiwopa Ine.
Ndidzasangalala ndi mtima wonse ndi kunena kuti. “Ndani angafanefane ndi Inu Chauta, Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka kwa munthu wopambana pa mphamvu, Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka ndi wosoŵa kwa munthu wolanda zinthu zake?”
Ukamaona anthu osauka akuzunzika m'dziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzao ndi kuŵalanda ufulu wao mwankhanza, usadabwe nazo zimenezo. Paja woyang'anira wokulapo ali naye wina wamkulu kwambiri amene amamuyang'anira. Ndipo palinso akuluakulu enanso oyang'anira iwowo.
Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa.
Chautatu akuti uziweruza molungama ndi mosakondera. Munthu amene adambera zake uzimpulumutsa kwa womsautsa. Usavutitse mlendo, mwana wamasiye kapena mkazi wamasiye. Usakhetse magazi a anthu osachimwa pa malo ano.
Chauta adzakupumitsani ku zoŵaŵa ndi mavuto, ndiponso ku ntchito yakalavulagaga imene anthu ankakugwiritsani. “Osauka zedi adzapeza chakudya, amphaŵi adzakhala pabwino. Koma mtundu wanu Afilistinu ndidzauwononga ndi njala, ndi otsalira omwe ndidzaŵapha. “Lirani kwamphamvu inu apachipata! Pemphani chithandizo mofuula, inu amumzinda! Njenjemerani ndi mantha nonse Afilisti! Onani fumbi likuchita kuti kodoo kuchokera kumpoto, ndipo mwa ankhondo akubwerawo palibe wamantha.” Kodi tidzaŵayankhanji amithenga a ku Filistiyawo? Tidzati, “Chauta adakhazikitsa kale Ziyoni, ndipo mu mzinda umenewu anthu ake ozunzika amapeza populumukira.” Motero mudzanyodola mfumu ya ku Babiloni, mudzati, “Watha bwanji wopsinja uja? Kwatha bwanji kudzikuza kwake kuja?
Ndidzaumiriza okuzunzani kuti adzadye mnofu wao womwe. Ndipo adzaledzera nawo magazi ao omwe, monga momwe adakachitira ndi vinyo watsopano. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mpulumutsi wanu, ndine Momboli wanu, Wamphamvu uja wa Yakobe.”
Ndaona ndithu kuvutika kwa anthu anga amene ali ku Ejipito. Ndamva kudandaula kwao, ndipo ndabwera kudzaŵapulumutsa. Tiye tsopano, ndikutume ku Ejipito.’
Koma Mulungu amateteza amphaŵi kwa adani oŵasinjirira, amapulumutsa osauka kwa anthu ofuna kuŵapanikiza. Choncho amphaŵi amaŵalimbitsa mtima, koma anthu oipa amaŵatseka pakamwa.
Tsono Aisraele adalira kwa Chauta kuti aŵathandize, pakuti Sisera anali ndi magaleta achitsulo okwanira 900, ndipo adaazunza Aisraele mwankhalwe zaka makumi aŵiri.
Munthu wosalankhula umlankhulire ndiwe. Anthu osiyidwa uŵalankhulire pa zoŵayenerera. Uzilankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uziteteza amphaŵi ndi osauka.
Mundichitire chifundo Inu Mulungu, mundichitire chifundo, pakuti mtima wanga ukudalira Inu. Ndidzathaŵira pansi pa mapiko anu, mpaka chiwonongeko chitandipitirira.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi. “Landitsani ofooka ndi osoŵa. Apulumutseni kwa anthu oipa.”
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende. Chauta amatsekula maso a anthu osapenya, Chauta amakweza anthu otsitsidwa. Chauta amakonda anthu ochita chilungamo. Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
Angathe kutero ndi amene amachita zolungama ndi kulankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga, amene amakutumula manja ake kuti angagwire chiphuphu, amene amatseka makutu kuti angamve mau opangana za kupha anzao, amene amatsinzina kuti angaone zoipa.
“Mtheradi ndikudziŵa kuti Momboli wanga alipo, ndipo pa nthaŵi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Nchifukwa chake anthu amene amamva zoŵaŵa monga Mulungu afunira, adzipereke m'manja mwa Mlengi wao wokhulupirika, ndi kumachitabe ntchito zabwino.
Koma kuweruza kwanu kwangwiro kuziyenda kosalekeza ngati madzi, kulungama kwanu kukhale ngati mtsinje wosaphwa.
Pamene amphaŵi ndi osauka akufunafuna madzi, koma osaŵapeza, ndipo kum'mero kwao kwangoti gwa ndi ludzu, Ine Chauta ndidzayankha pemphero lao, Ine Mulungu wa Israele sindidzaŵasiya.
Koma Mulungu amapulumutsa ovutika mwa njira ya mazunzo ao omwe, amaŵatsekula makutu poŵagwetsa m'mavuto.
Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. “Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.
Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga! Fuula ndi chimwemwe, iwe dziko lapansi! Yambani nyimbo, inu mapiri! Chauta watonthoza mtima anthu ake, ndi kuŵamvera chifundo anthu ake ovutika.
Munthu wokoma mtima amasamalira zoyenerera osauka, koma munthu woipa salabadako za zimenezo.
Amatswanya anthu anu, Inu Chauta, amazunza anthu anu osankhidwa. Amapha akazi amasiye ndi alendo okhala nawo m'dziko mwao, amaphanso ana amasiye.
Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni. Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu. Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu. Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu, bulu wake kamwana tsono.
“Musazunze mlendo. Inu nomwe mukudziŵa m'mene amamvera mlendo, poti paja inunso munali alendo ku Ejipito kuja.
Pamene anthu ake chiŵerengero chao chidachepa, ndipo pamene adatsitsidwa chifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni, Ena adasokera m'chipululu, osapeza njira yopita ku mzinda woti akakhalemo. apo Chauta adagwetsa manyozo pa mafumu oŵapsinja naŵasokeretsa, m'chipululu. Koma anthu osoŵa adaŵatulutsa m'mavuto ao, adachulukitsa mabanja ao ngati magulu a nkhosa.
Chauta akunena kuti, “Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima. Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa, mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu? Kodi ndinu yani kuti muziiŵala Chauta, Mlengi wanu, amene adayalika zakuthambo, ndi kuika maziko a dziko lapansi? Kodi ndinu yani kuti nthaŵi zonse muziwopa ukali wa anthu okuzunzani, amene angofuna kukuwonongani? Ukali wa anthu okuzunzaniwo tsopano uli kuti?
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Israele akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo amagulitsa anthu achilungamo ndi siliva, amagulitsa anthu osauka ndi nsapato. Anthu osauka iwo amaŵadyera masuku pa mutu, anthu ozunzika iwo safuna kuŵayang'ana. Bambo ndi mwana amakagona ndi mdzakazi mmodzimmodzi, mwakuti amanyoza dzina langa loyera.
Tsono adaika akapitao ao oŵagwiritsa mwankhanza ntchito yolimba Aisraelewo, kuti pakutero aŵafooketse. Aisraele adamangira Faraoyo mizinda ya Pitomu ndi Ramsesi, kumene Aejipito ankasunga chakudya chao. Koma Aisraele ankati akamaŵazunza kwambiri, ndi pamene iwo tsono ankachulukirachulukira, mpaka adabalalikira m'dziko lonselo. Motero Aejipito ankaŵaopa Aisraele, ndipo ankaŵakakamiza mwankhalwe kugwira ntchito yaukapolo. Moyo wa Aisraele unali woŵaŵa chifukwa cha ntchito yakalavulagaga youmba njerwa, ndiponso ntchito zosiyanasiyana zam'minda. Ankaŵakakamiza mwankhanza kugwira ntchito zonse zolemetsa.
Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’ Apo olungama aja adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, ife nkukupatsani chakudya, kapena muli ndi ludzu, ife nkukupatsani chakumwa? Ndi liti tidaakuwonani muli mlendo, ife nkukulandirani kunyumba kwathu, kapena muli wamaliseche, ife nkukuvekani? Ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife nkudzakuchezetsani?’ Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m'nsupa zao. Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’
Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Kuweruza kolungama kwalekeka, ndipo kuchita zaungwiro kwaiŵalika. Zoona sizikupezekanso m'mabwalo a milandu, ndipo chilungamo sichikutha kupezeka kumeneko. Zoona zikusoŵa kumeneko, ndipo wina aliyense akapanda kuchita nawo zoipa, amapeza mavuto.” Chauta adaziwona zimenezi ndipo zidamunyansa kuti palibe chilungamo.
“Pakuti sadanyoze munthu wozunzika, sadaipidwe ndi masautso ake, sadamubisire nkhope yake, koma adamumvera pamene adamdandaulira.”
“Chilango chimene Mulungu amasungira munthu woipa, choloŵa chimene munthu wozunza anzake amalandira kwa Mphambe ndi ichi: ana ake ngakhale achuluke chotani, adzaphedwa ndi lupanga, zidzukulu zake zidzasoŵa chakudya. Amene adzamtsalireko adzafa ndi matenda, akazi ao amasiye sadzaŵalira. Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi, kapena kukundika zovala ngati mchenga, koma olungama ndiwo amene adzavala zimenezo, ndipo anthu osachimwa adzagaŵana siliva ameneyo.
Mulungu akutsogolera msonkhano wakumwamba. Akugamula mlandu milungu ya pansi pano. Akuti, “Mudzakhalabe mukuweruza mopanda chilungamo mpaka liti? Bwanji mukupitirizabe kumakondera anthu oipa? Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi. “Landitsani ofooka ndi osoŵa. Apulumutseni kwa anthu oipa.”
Chauta amapasula nyumba ya munthu wonyada, koma amasamalira kadziko ka mkazi wamasiye.
Chauta akuŵaimba mlandu akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake. Akuŵazenga kuti, “Ndinu amene mwaononga munda wanga wamphesa. Nyumba zanu zadzaza ndi zinthu zolanda kwa amphaŵi. Mukuŵapsinjiranji anthu anga? Chifukwa chiyani mukuŵadyera masuku pamutu amphaŵi?” Akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
Pakuti inu mwathyola goli limene linkaŵalemera, ndodo zimene ankamenyera mapewa ao, ndiponso mikwapulo ya anthu oŵazunza, monga mudaachitira pogonjetsa Amidiyani.
“Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo, womanga zipinda zake monyenga, pogwiritsa ntchito anthu, koma osaŵapatsa malipiro a ntchito yao.
Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Amosi adati, “Imvani izi, inu amene mumapondereza osoŵa, amene mufuna kuwononga anthu osauka am'dzikomu. Inu mumadzifunsa kuti, ‘Kodi chikondwerero cha kukhala kwa mwezi chidzatha liti, kuti tigulitse dzinthu? Kodi tsiku lopumula la Sabata litha liti kuti tigulitsenso tirigu, kutinso tipeze mpata wochepetsera miyeso ndi kukweza mitengo, ndiponso kuti tichenjeretse anthu ndi masikelo onama, kuti osauka tiŵagule ndi siliva, amphaŵi tiŵagule ndi nkhwaŵiro, kutinso tigulitse ndi mungu womwe wa tirigu?’ ” Chauta, Mulungu amene ana a Yakobe amamnyadira walumbira kuti, “Ndithudi, sindidzaiŵala zochita zao zonse.
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake. Chauta adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili m'menemo. Amasunga malonjezo ake nthaŵi zonse. Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.
Ziwawa sizidzamvekanso. Dziko lako silidzaonongekanso. Ndidzakhala ngati linga lokuteteza, ndipo udzanditamanda chifukwa chokupulumutsa.”
“Usachite umboni wonama. Munthu wolakwa usamthandize pakumchitira umboni wonama. “Muzibzala mbeu zaka zisanu ndi chimodzi m'munda mwanu, ndi kumakolola mbeuzo. Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe. “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu. Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula. “Muzikhala ndi tsiku lachikondwerero katatu pa chaka, kuti mundilemekeze Ine. Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha Masika pokolola mbeu zoyamba zochokera ku zobzala zanu. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pa chaka, pamene muika m'nkhokwe dzinthu dzanu dzonse. Anthu aamuna onse aziwonekera pamaso pa Ine Chauta pa masiku atatu ameneŵa. “Mukamapereka magazi a nyama ngati nsembe kwa Ine, musapereke pamodzi ndi buledi wofufumitsa, ndipo mafuta a nyama yopereka pa tsiku langa lachikondwerero asakhale mpaka m'maŵa. “Muzibwera ndi zokolola zoyamba zabwino kwambiri za kumunda kwanu ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu. “Musamaphika kamwanakanyama mu mkaka wa make. Ngakhale anthu ambiri akamachita choipa, usamavomerezana nawo. Ndipo usamapereka umboni wopotoza chiweruzo m'bwalo lamilandu, kuti ukondweretse anthu ambiri. “Ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu, kuti akutchinjirizeni pa njira ndi kukufikitsani ku malo amene ndakukonzerani. Mumvere iyeyo, ndipo mumvetse zimene akunena. Musamchite zaupandu, chifukwa sadzakhululukira tchimo lotere. Iye akuchita zimenezi m'dzina langa. Koma mukamvera iyeyo ndi kuchita zonse zimene ndinena, Ineyo ndidzadana ndi adani anu, ndipo onse amene atsutsana nanu ndidzalimbana nawo. “Mngelo wanga adzapita patsogolo panu, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Aamori, Ahiti, Aperizi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzaŵaononga onsewo. Tsono musagwadire milungu yao kapena kuipembedza. Musamachita nao zimene amachita anthu amenewo. Mukaonongeretu milungu yao, ndiponso mukaphwanye miyala yao yopembedzerapo. Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse. Palibe mkazi amene adzapititse padera m'dziko mwanumo, ndipo wosabala sadzaoneka. Ndidzakupatsani moyo wautali. Anthu onse olimbana nanu ndidzaŵachititsa mantha kuti andiwope Ine. Ndidzadzetsa chisokonezo pakati pa anthu amene mukumenyana nawo. Ndipo adani anu onse ndidzaŵathamangitsa liŵiro lamtondowadooka. Ndidzapirikitsa Ahivi, Akanani ndi Ahiti, inu musanafike, ndipo adzathaŵa monga ngati ndaŵatumira mavu. Sindidzaŵapirikitsa chaka chimodzinchimodzi, kuti dzikolo lingadzakhale lopanda anthu ndi kukusiyirani nyama zakuthengo zokhazokha. Munthu wosauka ukamuweruza, usaweruze mokondera.
Zidatero chifukwa choti ndinkapulumutsa amphaŵi olira, ndinkalanditsa ana amasiye opanda woŵathandiza. Anthu amene anali pa zoopsa kwambiri ankanditamanda, akazi amasiye ndinkaŵasangalatsa. Nthaŵi zonse ndinkachita zoyenera, ntchito zanga zonse zinali zangwiro. Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya, ndinali ngati mapazi kwa anthu opunduka. Osauka ndinali ngati bambo wao, anthu osaŵadziŵa konse ndinali mtetezi wao pa milandu. Ndinkaononga mphamvu za anthu ankhalwe, ndinkalanditsa amene anali atagwidwa.
Othaŵa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu. Mukhale populumukira pao kwa woononga uja.” Nthaŵi ikudza pamene kupsinja sikudzakhalaponso, kuwononga kudzaleka, ndipo amene amaŵapondereza adzachoka m'dzikomo.
“Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu. Muzichitirana zolungama. Musazunze alendo kapena ana amasiye kapena akazi amasiye. Musaphe anthu osachimwa pa malo ano. Musamatsate milungu ina, kuti ingakuwonongeni. Mukamvera mau anga, ndidzakulolani kuti mukhale pa malo ano, m'dziko limene ndidapatsa makolo anu mpaka muyaya.
Inu mwakhala ngati ngaka kwa anthu osauka, mwakhala ngati linga kwa anthu osoŵa pa nthaŵi yamavuto. Mwakhala ngati pobisalirapo namondwe, ndiponso ngati mthunzi wousirapo dzuŵa. Anthu ankhalwe ali ngati namondwe woomba pa khoma, ngati chitungu m'dziko louma.
“Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja. Mukatenga mwinjiro wa munthu wina ngati chigwiriro kuti adzakulipireni, muubweze dzuŵa lisanaloŵe, poti chofunda nchokhacho, ndicho chotetezera thupi lake. Nanga adzafunda chiyani? Akalira kwa Ine iyeyu kuti ndimthandize, ndidzamuyankha chifukwa ndine wachifundo.
“Musachenjeretse mnzanu kapena kumubera zinthu zake. Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka m'maŵa.
Ndidzatonthoza mtima Ziyoni, ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake. Ngakhale dziko lake ndi chipululu, ndidzalisandutsa ngati Edeni. Ngakhale dziko lake ndi thengo, ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta. Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala, adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza. “Mverani, inu anthu anga, tcherani khutu, inu mtundu wanga. Malamulo adzachokera kwa Ine, ndipo chilungamo changa chidzaunikira anthu onse.
Paja Chauta amaimirira pafupi ndi munthu wosoŵa, amafuna kumpulumutsa kwa anthu ogamula kuti iyeyo aphedwe.
“Atembereredwe aliyense woweruza mopotoza milandu ya alendo, ya ana amasiye, ndi ya akazi amasiye.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
Chauta akuyankha kuti, “Ndithudi, ankhondo adzaŵalanda akaidi ao, ndipo mfumu yankhalwe adzailanda zofunkha zake. Ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu, ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
Ndidzakusandutsa wolimba ngati linga lamkuŵa kwa anthuwo. Iwo adzalimbana nawe, koma sadzakupambana, pakuti Ine ndili nawe, ndidzakulanditsa ndi kukupulumutsa. Ndidzakulanditsa kwa anthu oipa, ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza,” akuterotu Chauta.
Mumapondereza anthu osauka ndi kuŵabera pa msonkho. Nchifukwa chake ngakhale mwamanga nyumba za miyala yosema, simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, simudzamumwa vinyo wake. Ine ndikudziŵa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumazunza anthu ochita chilungamo, mumalandira ziphuphu ndiponso mumapotoza milandu ya anthu osauka.
Chauta si wosoŵa mphamvu, kuti angalephere kukupulumutsani, ndipo si gonthi, kuti nkupanda kumva zimene mukupempha. Timapapasapapasa ngati anthu akhungu, tili ngati anthu opanda maso. Timaphunthwa masana ngati usiku. Ndife amoyo ndithu, komabe tili ngati anthu akufa. Tonse timabangula ngati zimbalangondo, ndipo timalira modandaula ngati nkhunda. Timayembekeza kuweruza kolungama, koma sitikupeza. Timadikiranso chipulumutso, koma chili nafe kutali. Inu Chauta, takuchimwirani kwambiri. Machimo athu akutitsutsa, zolakwa zathu zili pa ife, ndipo sitingakanepo nchimodzi chomwe. Takupandukirani, takukanani, Inu Chauta, ndipo takana kukutsatani. Tapanikiza anzathu, takupandukirani Inu. Maganizo athu ndi abodza, mau athu ndi onama. Kuweruza kolungama kwalekeka, ndipo kuchita zaungwiro kwaiŵalika. Zoona sizikupezekanso m'mabwalo a milandu, ndipo chilungamo sichikutha kupezeka kumeneko. Zoona zikusoŵa kumeneko, ndipo wina aliyense akapanda kuchita nawo zoipa, amapeza mavuto.” Chauta adaziwona zimenezi ndipo zidamunyansa kuti palibe chilungamo. Chauta adaona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe adadabwa kuti palibe wochitapo kanthu. Tsono adapambana ndi mphamvu zakezake, ndipo adadzilimbitsa ndi kulungama kwake. Adavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake adavala chisoti chachipulumutso. Adavala kulipsira ngati mkanjo, ndipo mkwiyo udakhala ngati chofunda chake, Chauta adzalanga adani a anthu ake molingana ndi zochita zao: adzaonetsa ukali kwa omuukira, ndipo adzalipsira adani ake. Adzalanga ngakhale okhala m'maiko akutali. Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho. Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho saamva zimene inu mumanena.
Anthu am'dzikomo amasautsa anzao ndiponso amaba. Amazunza osoŵa ndi osauka. Amavutitsa alendo posaŵachitira zinthu mwachilungamo. Unene kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Wadziitanira tsoka iwe mzinda umene umakhetsa magazi a anthu ake ambiri. Ndiwe mzinda umene umadziipitsa ndi mafano amene udadzipangira! Ndidafunafuna munthu pakati pao woti amange linga, woti pamaso panga aime pamene padagumuka, kuti ateteze dziko ndi kundipepesa kuti ndisaliwononge. Koma munthu woteroyo sindidampeze. Nchifukwa chake ndidaŵakwiyira kwambiri. Ndidzaŵaononga kotheratu ndi mkwiyo wanga woyaka ngati moto. Motero ndidzaŵalanga monga kuŵayenera.” Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Potero mudzaŵateteza amasiye ndi opsinjidwa, kuti anthu amene ali a pansi pano, asadzathe kuwopsezanso.
Patapita nthaŵi yaitali ndithu, mfumu ya ku Ejipito ija idamwalira. Monsemo Aisraele ankangolira nawo ukapolo wao uja, namapempha chithandizo, ndipo kulira kwao kudamveka kwa Mulungu. Mulungu adamva kudandaula kwaoko, nakumbukira chipangano chake chija chimene adachita ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Mulungu ataŵapenya Aisraelewo, adaŵamvera chifundo.
“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.
Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira. Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Koma anthu osoŵa adaŵatulutsa m'mavuto ao, adachulukitsa mabanja ao ngati magulu a nkhosa. Anthu olungama mtima amaona zimenezo, nkumasangalala, koma oipa onse amaŵakhalitsa chete.
Koma ngati wina afuna kunyadira, anyadire ichi chakuti amamvetsa za Ine, ndipo amandidziŵa. Amadziŵa kuti Ine ndine Chauta wokonda chifundo, chilungamo, ndi ungwiro pa dziko lapansi. Ndithudi, pazimenezi ndipo pali mtima wanga.”
Koma amphaŵi adzaŵaweruza mwachilungamo, ndipo anthu otsika a pa dziko lapansi adzaŵagamulira mlandu wao mosakondera. Mau ochokera m'kamwa mwake adzakhala ngati ndodo yokanthira ochimwa, atalamula iyeyo anthu oipa adzaphedwa.
Pamenepo mpando wachifumu udzakhazikitsidwa mwachikondi, mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika. Iyeyo poweruza adzatsata zachilungamo, ndipo adzalimbikira kuchita zaungwiro.
Yesu adaŵaphera fanizo pofuna kuŵaphunzitsa kuti azipemphera nthaŵi zonse, osataya mtima. Adati, “Anthu aŵiri adaapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera. Wina anali Mfarisi, wina anali wokhometsa msonkho. Mfarisiyo adaimirira nayamba kupemphera motere mumtima mwake: ‘Mulungu, ndikukuyamikani kuti ine sindili monga anthu ena onse ai. Iwowo ndi anthu akuba, osalungama ndi adama. Sindilinso monga wokhometsa msonkho uyu ai. Ine ndimasala zakudya kaŵiri pa mlungu, ndipo ndimapereka chachikhumi pa zonse zimene ndimapata.’ Koma wokhometsa msonkho uja adaima kutali, osafuna nkuyang'ana kumwamba komwe. Ankangodzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumanena kuti, ‘Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwane.’ ” Yesu popitiriza mau adati, “Kunena zoona, wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.” Anthu ena ankabwera ndi ana omwe kwa Yesu kuti aŵakhudze. Ophunzira ake poona zimenezi, ankaŵazazira. Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere. Ndithu ndikunenetsa kuti amene salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzaloŵamo.” Mkulu wina adafunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?” Yesu adamuyankha kuti, “Ukunditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi. Adati, “M'mudzi mwina mudaali woweruza wina amene sankaopa Mulungu kapena kulabadako za munthu. Malamulo ukuŵadziŵa: Usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, lemekeza atate ako ndi amai ako.” Munthu uja adati, “Zonsezi ndakhala ndikuzitsata kuyambira ndili mwana.” Pamene Yesu adamva zimenezi, adamuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Koma pamene munthu uja adamva zimenezi, adavutika mu mtima, pakuti adaali wolemera kwambiri. Yesu adamuyang'ana, nanena kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu. Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” Anthu amene adamva zimenezi adafunsa kuti, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?” Yesu adati, “Zimene zili zosatheka ndi anthu, zimatheka ndi Mulungu.” Pamenepo Petro adati, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena makolo, kapena ana chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, M'mudzi momwemo mudaalinso mai wamasiye. Iyeyu ankabwera kwa woweruza uja kudzampempha kuti, ‘Mundiweruzireko mlandu umene uli pakati pa ine ndi mdani wanga.’ ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.” Yesu adatengera ophunzira ake pambali, naŵauza kuti, “Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu, ndipo zonse zidzachitika zimene aneneri adalemba zokhudza Mwana wa Munthu. Akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamnyazitsa, ndi kumthira malovu. Akamkwapula, nkumupha, koma mkucha wake Iye adzauka.” Ophunzira aja sadamvetse konse zimenezi. Tanthauzo la mau ameneŵa linali lobisika kwa iwo, nchifukwa chake sadamvetsetse zimene Yesu ankanenazo. Pamene Yesu ankayandikira ku Yeriko, munthu wina wakhungu adaakhala pamphepete pa mseu akupemphapempha kwa anthu. Atamva anthu ambirimbiri akupita mumseumo, adafunsa kuti, “Kodi kuli chiyani?” Adamuyankha kuti, “Kukupita Yesu wa ku Nazarete.” Apo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!” Anthu amene anali patsogolo adamzazira, adati, “Khala chete!” Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide, chitireni chifundo!” Kwa nthaŵi yaitali woweruza uja ankakana, koma pambuyo pake adaganiza kuti, ‘Ngakhale sindiwopa Mulungu kapena kusamala munthu, Yesu adaima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atafika pafupi, Yesu adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Iye adati, “Ambuye, ndikufuna kuti ndizipenyanso.” Yesu adamuuza kuti, “Penya. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthaŵi yomweyo adapenyanso nayamba kutsata Yesu, akuthokoza Mulungu. Anthu onse aja ataona zimenezi, adatamanda Mulungu. komabe chifukwa mai wamasiyeyu akundivuta, ndimuweruzira mlandu wake, kuwopa kuti angandilemetse nako kubwerabwera kwake.’ ” Tsono Ambuye adati, “Mwamvatu mau a woweruza wosalungama uja. Nanga Mulungu, angaleke kuŵaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangoŵalekerera? Iyai, kunena zoona adzaŵaweruzira mlandu wao msanga. Komabe Mwana wa Munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”
Alendo kapena ana amasiye musaŵalande zao zoŵayenera, poŵapotozera mlandu wao. Ndipo mkazi wamasiye musamlande chovala kuti chikhale pinyolo ya ngongole.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa.
Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.”
Muuze onse a mtima wamantha kuti, “Limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.”
Ine ndidati, “Imvani inu akuluakulu a Yakobe, olamulira a banja la Israele! Kodi oyenera kudziŵa chilungamo sindinu? Mumamanga Ziyoni ndi chuma chochipata pakupha anthu, Yerusalemu mumammanga ndi kuipa kwanu. Atsogoleri ake saweruza popanda chiphuphu, ansembe ake saphunzitsa popanda malipiro, aneneri ake salosa popanda ndalama. Komabe amagonera pa Chauta ndi kunena kuti, “Kodi suja Chauta ali pakati pathu? Tsoka silingatigwere ai.” Tsono chifukwa cha inu Ziyoni adzatipulidwa ngati munda, Yerusalemu adzasanduka bwinja, ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango. Mumadana ndi zabwino, mumakonda zoipa. Anthu anga mumaŵasenda amoyo, ndi kukangadzula mnofu wao. Mumandidyera anthu anga, mumachita ngati kumaŵasenda, kuphwanya mafupa ao, ndi kumaŵachekera mumphika ngati nyama. “Nthaŵi ikubwera pamene mudzalira kwa Chauta, koma sadzakuyankhani. Nthaŵi imeneyo adzakufulatirani chifukwa ntchito zanu nzoipa.”
Bango lopindika sadzalithyola, moto wozilala sadzauzima. Adzabweretsa chilungamo mokhulupirika.