Mawu a Mulungu ndi amphamvu ndipo amasintha moyo wanga. Pali mavesi ambiri amene timawamva kawirikawiri ndipo ali ndi mphamvu yosintha miyoyo yathu. Angasinthe maganizo athu, moyo wathu wonse. Mavesi amenewa timaphunzira nthawi zonse kuti tiwagwiritse ntchito pa moyo wathu watsiku ndi tsiku.
"Ndingathe kuchita zonse mwa Khristu amene amandipatsa mphamvu." (Afilipi 4:13) Uwu ndi umodzi mwa mavesi amene timaphunzira nthawi zonse, ndipo timaugwiritsa ntchito nthawi imene tikutaya mtima.
"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha." (Yohane 3:16) Uwu ndi umodzi mwa mavesi ofunika kwambiri, ndipo nthawi zambiri ndi umodzi mwa mavesi oyamba kumva ukayamba kumudziwa Ambuye Yesu. Pali mavesi ambiri ofunika, ndipo apa mutha kuwapeza.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.
Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.
Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.
Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano, koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru.
Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.
Amene amakonda nzeru amadzichitira zabwino mwiniwakeyo. Amene ali womvetsa, zinthu zidzamuyendera bwino.
Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziŵa zinthu, munthu wodekha mtima ndiye womvetsa zinthu.
Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.
Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe.
Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru.
Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.
Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu. Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba. Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali.
Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.
Kwa chitsiru kulakwa kumakhala ngati maseŵera, koma kwa munthu womvetsa zinthu kuchita zanzeru ndiye kumapatsa chimwemwe.
Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.
Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka.
Munthu wanzeru ngwochenjera, ndipo amalewa choipa, koma chitsiru chimadudukira zinthu mosasamalako.
Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.
Pali golide ndi miyala yambirimbiri yamtengowapatali, koma mau olankhula zanzeru ali ndi mtengo woposa zonsezo.
Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.
Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu, palibe ngakhale uphungu, zimene zingathe kupambana Chauta.
Utchere khutu lako, umve mau a anthu anzeru, uike mtima wako pa zophunzitsa zanga, kuti uzidziŵe.
Munthu wanzeru ndi wamphamvu kupambana munthu wa nyonga zambiri, munthu wophunzira amaposa munthu wamphamvu.
Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.
Wanzeru ukamlangiza, adzakhala wanzeru koposa. Munthu wochita chilungamo ukamuphunzitsa, adzadziŵa zambiri koposa.
Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.
Nzeru za munthu wochenjera zagona pa kuzindikira bwino njira zake, koma zitsiru zimanyengedwa nkupusa kwao komwe.
Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu kudziŵa zambiri, koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha!
Amene makutu ake amalandira bwino kudzudzula koyenera, adzakhala m'gulu la anthu anzeru.
Munthu wovomera malangizo, zinthu zidzamuyendera bwino, ndi wodala amene amadalira Chauta.
Munthu wanzeru amaika mtima pa nzeru, koma chitsiru chimangoti maso mwalamwala pa dziko lonse.
Mau a munthu angathe kukhala kasupe wa nzeru, ozama ngati nyanja yamchere yaikulu, omweka ngati a mu mtsinje wothamanga.
Mau a chitsiru amautsa mkangano, ndipo pakamwa pake pamaitana mkwapulo. Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake. Mau ake ali ngati msampha wodzikolera mwiniwakeyo.
Si bwino kuti munthu akhale wosadziŵa zinthu, ndipo munthu woyenda mofulumira dziŵi amasokera.
Anthu okhuta vinyo amanyodola anzao, omwa zaukali amautsa phokoso. Aliyense wosokera nazo zimenezi ndi wopanda nzeru.
Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.
Ugule choona, ndipo usachigulitse. Ugulenso nzeru, mwambo ndiponso mtima womvetsa zinthu.
Pafunika malangizo abwino kuti ukamenye nkhondo. Aphungu akachuluka, kupambana kuli pomwepo.
Kwa munthu womvetsera bwino, kudzudzula kuli ngati mphete yagolide, kapena chokongoletsera china chagolide.
Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi, pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono nkumaopa Chauta, kupambana kukhala ndi chuma chambiri nkupeza nacho mavuto.
Usaiŵale mau a pakamwa pangaŵa, usatayane nawo, Ukhale ndi nzeru, ndiponso khalidwe la kumvetsa zinthu. Usaisiye nzeru, ndipo idzakusunga. Uziikonda, ndipo idzakuteteza.
Mwana wanga, usunge nzeru yeniyeni usunge mkhalidwe wa kulingalira bwino, ziŵiri zimenezi zisakuthaŵe. Zimenezi zidzakupatsa moyo, moyo wake wokongola ngati mkanda wam'khosi.
Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.
Munthu wosapsa mtima msanga amapambana wankhondo, amene amadzigwira mtima amapambana msilikali wogonjetsa mzinda.
Woipa mtima amangodzithaŵira popanda wina wompirikitsa, koma wochita zabwino amalimba mtima ngati mkango.
Ukakonzekera kuchita zinthu, uziyamba wafunsa. Usanamenye nkhondo, uyambe wapempha malangizo oyenera.
Mkazi wabwino ali ngati chisoti chaulemu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda chamafinya kwa mwamuna wake.
Chinthu chochiyembekeza chikalephereka, chimafooketsa mtima, koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi, chili ngati mtengo wopatsa moyo.
Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.
Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.
Anthu ambiri amalankhula za kukhulupirika kwao, koma ndani angathe kumpeza munthu wokhulupirika kwenikweni?
Munthu wosadzimanga mtima ali ngati mzinda umene adani authyola nkuusiya wopanda malinga.
Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
Pajatu munthu wokondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamsandutsa waluntha, wanzeru ndi wosangalala. Koma wochimwa amampatsa ntchito yokunkha ndi younjika zinthu, kenaka zonsezo nkuzipatsa munthu wokondwetsa Mulungu. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
Kuli bwino kuti munthu azimva kudzudzula kwa anthu anzeru, kupambana kumvera nyimbo zotamanda za zitsiru.
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Kukwiya kwa munthu wopusa kumadziŵika msanga, koma munthu wanzeru salabadako za chipongwe.
Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
Amene amanka nachita ukazitape, amaulula zinsinsi. Koma wa mtima wokhulupirika, amasunga pakamwa pake.
Mumtima mwa anthu opangana zoipa mumakhala kunama, koma anthu olinga zabwino amakhala ndi chimwemwe.
Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe.
Usachite naye chibwenzi munthu wopsa mtima msanga, ndipo usamayenda naye munthu waukali, kuwopa kuti ungadzaphunzireko mayendedwe ake, ndi kukodwa mu msampha.
Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru, nanenso mtima wanga udzasangalala. Mtima wanga udzakondwa ndikadzakumva ukulankhula zolungama.
Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha, amene amakunkhuniza mwala, udzampsinja iye yemweyo.
Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
Nkhwangwa ikakhala yobuntha, nkupandanso kuinola, imalira mphamvu zambiri potema. Koma nzeru zimathandiza munthu kuti athedi kudula kanthu.
Wobisa machimo ake sadzaona mwai, koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo.
Kuwopa Chauta kumabweretsa moyo, ndipo amene amaopayo amakhala pabwino, ndiye kuti choipa sichidzamgwera.
Pamakhala njira ina yooneka yowongoka kwa munthu, koma kumapeto kwake imakhala njira ya ku imfa.
Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa, mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa, mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.
Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Chauta, nyaleyo imafufuza ziwalo zake zonse zam'kati.
Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti samkonda, koma amene amakonda mwana wake, sazengereza kumlanga.
Munthu wokhulupirika adzakhala ndi madalitso ambiri, koma wofunitsitsa kulemera msanga sadzalephera kupeza chilango.
Wolima munda wake mwakhama amapeza chakudya chambiri, koma wotsata zopanda pake ngwopanda nzeru.
Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, m'menemo munthu wakhama amalemera.
Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse, koma wochenjera amayang'ana m'mene akuyendera.
Kodi ukumuwona munthu wochita ntchito zake mwaluso? Iye adzatumikira mafumu, sadzatumikira anthu wamba.
Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.
Amene amasamalira mkuyu adzadya zipatso zake, chonchonso amene amasamalira mbuyake adzalandira ulemu.
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
Anthu oipa samvetsa kuti chilungamo nchiyani, koma amene amatsata kufuna kwa Chauta amachimvetsa kwathunthu.
Amene amatseka m'khutu wosauka akamalira, adzalira iyenso, koma kulira kwakeko sikudzamveka.
Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.
Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho. Usamuuze mnzakoyo kuti, “Pita, ukachite kubweranso, ndidzakupatsa maŵa,” pamene uli nazo tsopano lino.
Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo.
Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu. Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani.
Amene amakondetsa zosangalatsa, adzasanduka munthu wosauka. Amene amakondetsa vinyo ndi mafuta, sadzalemera.
Mtima wako usamachita nsanje ndi anthu ochimwa, koma upitirire kumaopa Chauta tsiku ndi tsiku. Ndithu, zakutsogolo zilipo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe.
Ndi Chauta amene amafuna kuti miyeso ndi masikelo zikhale zachilungamo. Miyala yonse yoyesera yam'thumba adaipanga ndi Chauta.
Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri. Pamene adatumphutsa madzi kuchoka kunsi kwa dziko, ndipo mitambo idagwetsa mvula, adaonetsa nzeru zodziŵa zinthu.
Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe, makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi, uŵalembe mumtima mwako. Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse. Usachite naye nsanje munthu wachiwawa, usatsanzireko khalidwe lake lililonse. Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa, koma olungama okha amayanjana nawo. Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa. Anthu onyoza, Iye amaŵanyoza, koma odzichepetsa Iye amaŵakomera mtima. Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi. Choncho udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi pa anthunso.