Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


111 Mau a m'Baibulo Okhudza Kuba

111 Mau a m'Baibulo Okhudza Kuba

Mulungu amatiphunzitsa m’Mawu ake kuti kuba n’koletsedwa, ndi tchimo lolakwiridwa ndi malamulo a Mulungu komanso a dziko. Kuba sikuli koyenera ndipo sikubweretsa mphotho, koma chilango kwa ochita zimenezi. Choncho, konzani mitima yanu, musiye njira zoyipa zobweretsa imfa.

Kuba sikubweretsa phindu lililonse pa moyo wanu, koma kungofanana ndi kudzimangirira chingwe m’khosi. Kukula kwa chinthu chobedwacho sikofunika, chifukwa kungotenga chokhala cha wina kukupangitsani kukhala olakwa. Palibe chodzikhuza pamaso pa Mulungu, ngakhale muli pa umphawi.

Choncho, ndikukulangizani kuti: “Wakuba asabenso; koma agwire ntchito moona mtima ndi manja ake, kuti akhale ndi chofunikira chopatsa wosowa.” M’malo motengera ena, Yesu akufuna mukhale opatsa ndipo nthawi zonse mukhale ndi chogawana ndi ena. N’chifukwa chake muyenera kugwira ntchito ndipo musamaone ngati zinthu zopanda pake katundu wa anthu amene agwira ntchito molimbika kuti akapeze.

Ngakhale simunagwidwe mukuba koyamba, dziwani kuti zonse zidzadziwika ndipo mukhoza kukhala m’ndende zaka zambiri. Ganizirani zomwe zili zabwino pa moyo wanu, musatsatire zilakolako za kanthawi kochepa kapena kulola mavuto kukupusitsani. Fufuzani Mulungu, chifukwa m’chifundo chake chosatha adzakupatsani malinga ndi chuma ndi ulemerero wake.

Musagwere m’msampha wa mdani, funani thandizo, siyani zizolowezi zoipa zimenezo ndipo lolani Mzimu Woyera akutsogolereni. Musaswe malamulo, khalani olimba m’Mawu ake ndipo mudzaona momwe amakusamalirani tsiku lililonse.




Masalimo 62:10

Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:2

Chuma chochipeza monyenga sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:6

Chuma chomachipeza monyenga chimangoti wuzi ngati nthunzi, ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:21

Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:11

“Musabe, musachite zinthu zonyenga, ndipo musaname.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:22-23

Mmphaŵi usamubere, chifukwa choti iyeyo ndi wosauka. Anthu ozunzika usaŵapondereze pa bwalo la milandu. Pakuti Chauta adzaŵateteza pa mlandu wao, ndipo adzaŵalanda moyo amene amalanda zinthu zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 5:3-4

Tsono adandiwuza kuti, “Pamenepo palembedwa temberero limene lidzagwera dziko lonse lapansi. Aliyense wakuba adzachotsedwa m'dziko potsata zimene zalembedwa mbali iyi, ndipo aliyense wolumbira zabodza nayenso adzachotsedwa potsata zimene zalembedwa mbali inai. Chauta Wamphamvuzonse wanena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza m'nyumba ya munthu wakuba ndi m'nyumba ya munthu wolumbira zabodza potchula dzina langa. Lidzakhala m'nyumbamo mpaka kuiwonongeratu, mitengo yake ndi miyala yake yomwe.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:10

mbala, aumbombo, zidakwa, augogodi, kapena achifwamba, ameneŵa sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:18

Iye adati, “Malamulo ake oti?” Yesu adayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:19

Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:8

Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:22

Mmphaŵi usamubere, chifukwa choti iyeyo ndi wosauka. Anthu ozunzika usaŵapondereze pa bwalo la milandu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:70

Anthu otere ndi opulukira, koma ine ndimakondwa ndi malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:21

Tsono iwe wophunzitsa ena, bwanji sukudziphunzitsa wekha? Iwe wolalika kuti, “Osamaba,” bwanji iwenso umaba?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:10

kapena kumaŵabera, koma makamaka adziwonetse kuti ngokhulupirika pa zonse zabwino. Motero pa zochita zao zonse adzaonetsa kukoma kwake kwa zophunzitsa zonena za Mulungu, Mpulumutsi wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:6

Pa zimenezi munthu asachimwire mbale wake kapena kumpezera. Monga tidakuuzani kale monenetsa, Ambuye adzalanga anthu onse ochita zotere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 23:30

“Nchifukwa chake ndikuŵakana aneneri amene amaberana mau iwo okhaokha nkumati mauwo ndi a Ineyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:1

Muyeso wonyenga umanyansa Chauta, koma muyeso wachilungamo umamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:8

“Ine Chauta ndimakonda chilungamo, ndimadana ndi zakuba ndi zoipa. Anthu anga ndidzaŵapatsa mphotho mokhulupirika, ndidzapangana nawo chipangano chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:1-4

“Munthu akaba ng'ombe kapena nkhosa, nkuipha kapena kuigulitsa, alipire ng'ombe zisanu pa ng'ombe imodzi, kapena nkhosa zinai pa nkhosa imodzi. “Munthu akapereka ng'ombe, nkhosa kapena choŵeta chilichonse kwa munthu wina kuti amsungire, tsono choŵeta chija nkufa, kapena kupweteka kapena kutengedwa, wina osaona, zitsimikizike pakulumbiritsa wosungayo pamaso pa Chauta kuti sadatenge chamwinicho. Ngati sichidabedwe, mwini wakeyo adzangoti zagwa zatha, ndipo wosungayo asalipire. Koma ngati choŵetacho chidabedwa, mwiniwakeyo adzalipidwa. Ngati chidajiwa ndi zilombo, atengeko zotsalira zake kuti zikhale mboni, koma asalipire chimene chidajiwa ndi zilombocho. “Munthu akabwereka choŵeta kwa mnzake, tsono choŵeta chija nkupweteka mpaka kufa pamene sichili kwa mwiniwakeyo, wobwerekayo alipire ndithu choŵetacho. Koma ngati chili kwa mwiniwakeyo, wobwereka uja asalipire. Choŵetacho akachibwereka, tsono nkuwonongeka, mtengo wolipira pobwereka ndiwo udzakonze mlanduwo. “Munthu akanyenga namwali wosadziŵa mwamuna, yemwe sanatomeredwe, nagona naye, alipire chiwongo, ndipo amkwatire. Koma ngati bambo wake wa namwaliyo akana kuti mwana wakeyo asakwatiwe, munthuyo adzangolipirabe ndalama za chiwongo cha namwali. “Munthu wamkazi wochita zaufiti, musamlole kuti akhale moyo. “Aliyense wogona ndi nyama aphedwe basi. “Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo ikanthidwa nkufa, asalipsire magazi chifukwa cha mbalayo. “Aliyense wopereka nsembe kwa milungu, osati kwa Chauta yekha, aphedwe ameneyo. “Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m'phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito. Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. Mukamaŵazunza, Ine ndidzaŵamva iwowo akamalira kwa Ine. Ndidzakukwiyirani, ndipo ndidzakuphani ku nkhondo. Akazi anu adzasanduka amasiye, ndipo ana anunso adzasanduka amasiye. “Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja. Mukatenga mwinjiro wa munthu wina ngati chigwiriro kuti adzakulipireni, muubweze dzuŵa lisanaloŵe, poti chofunda nchokhacho, ndicho chotetezera thupi lake. Nanga adzafunda chiyani? Akalira kwa Ine iyeyu kuti ndimthandize, ndidzamuyankha chifukwa ndine wachifundo. “Musanyoze Mulungu, ndipo musatemberere mtsogoleri wa anthu anu. “Musachedwe kundipatsa zopereka zotapa pa zokolola zanu zambiri ndiponso pa vinyo wanu wochuluka. “Mundipatse ana anu achisamba aamuna. Koma ikaphedwa dzuŵa litatuluka, apo padzakhala kulipsira magazi. Pajatu wakuba aliyense ayenera kulipira ndithu. Ngati mbala igwidwa, ndipo ilephera kulipira mlandu, aigulitse chifukwa cha kubako. Mundipatsenso ana oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwayo adzangokhala ndi mai wake masiku asanu ndi aŵiri, ndipo mudzampereka kwa Ine pa tsiku lachisanu ndi chitatu. “Mudzakhale anthu operekedwa kwa Ine. Motero musadzadye nyama ya choŵeta chilichonse chojiwa ndi zilombo ku thengo. Nyama imeneyo mudzapatse agalu. Ngati chinthu yabacho chipezeka chamoyo m'manja mwake, kaya ndi ng'ombe, kaya ndi bulu, kaya ndi nkhosa, mbalayo ilipire moŵirikiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 24:1

Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta, dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:27

Munthu wofunafuna phindu monyenga amavutitsa banja lake, koma munthu wodana ndi ziphuphu adzapeza bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:7

Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-21

“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:1

“Usachite umboni wonama. Munthu wolakwa usamthandize pakumchitira umboni wonama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:61

Ngakhale anthu oipa anditchere msampha, sindiiŵala malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 24:7

Aliyense woba Mwisraele mnzake ndi kumsandutsa kapolo kapena kumgulitsa ngati kapolo, aphedwe ndithu. Motero mudzachotsa choipa chimenechi pakati pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:9

Pajatu malamulo amene amati, “Usachite chigololo, usaphe, usabe, usasirire”, ndiponso malamulo ena onse, amaundidwa mkota m'lamulo ili lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:24

Wobera atate ake kapena amai ake namanena kuti kutero sikulakwa, ameneyo ndi mnzake wa munthu woononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 24:2

Anthu ena amasendeza malire, kuti akuze dziko lao, amalanda ziŵeto namakazidyetsa ku mabusa ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 49:6-7

Anthu otero amangokhulupirira chuma chao, amanyada chifukwa ali ndi chuma chambiri. Zoonadi, palibe munthu amene angadziwombole, kapena kupatsa Mulungu mtengo wa moyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:11

Ngati ife tidafesa zabwino zauzimu pakati panu, nanga tilekerenji kulandira kwa inu zotisoŵa m'moyo wathu wathupi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:2

Anthu oipa amazunza anthu osauka modzikuza. Akodwe m'misampha yotcha iwo omwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:10

Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:18

“Ukaona mbala umasanduka bwenzi lake, ndipo umayenda ndi anthu achigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:12

Onani, umu ndimo m'mene aliri anthu oipa. Nthaŵi zonse ali pabwino, ndipo amangolemera kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:43-44

Koma dziŵani kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba. Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene inu simukuyembekeza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:23

Atsogoleri ako apanduka, ndipo amagwirizana ndi mbala. Aliyense amakonda chiphuphu, ndipo amathamangira mphatso. Satchinjiriza ana amasiye, ndipo samvera madandaulo a akazi amasiye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:23

Pa ntchito iliyonse pali phindu lake, koma kumangolakatika kumabweretsa umphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:10

anthu amene manja ao amachita zoipa, ndipo anthu amene dzanja lao lamanja ndi lodzaza ndi ziphuphu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:29-30

Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi, Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:12

Nsanja yolimba ya anthu oipa mtima imaonongeka, koma maziko a munthu wabwino ngosagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:28

Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:11

Ali ngati agalu a njala yaikulu, amene sakhuta konse. Abusa nawonso ndi opanda nzeru. Aliyense amachita monga m'mene afunira, ndipo amangofuna zokomera iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:11

Chuma chochipeza mofulumira chidzanka chitha pang'onopang'ono, koma chochipeza pang'onopang'ono chidzanka chichulukirachulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 2:1

Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu, amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa. Akadzuka m'maŵa amakazichitadi, pakuti mphamvu zake ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:14

Asilikali omwe adamufunsa kuti, “Nanga ifeyo tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Musamalanda za munthu aliyense pakuwopseza kapena pakumnamizira. Muzikhutira ndi malipiro anu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:17

Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:3

Paja munthu woipa amanyadira zokhumba za mtima wake, wokonda chuma amanyoza ndi kukana Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:40-42

Munthu akakuzenga mlandu nafuna kukulanda mkanjo wako, umlole atengenso ndi mwinjiro wako womwe. Munthu akakukakamiza kuyenda naye mtunda umodzi, uyende naye mitunda iŵiri. Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:10

Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:119

Anthu onse oipa a pa dziko lapansi, mumaŵayesa ngati zakudzala, nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:8

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 49:16-17

Usavutike munthu wina akamalemera, pamene chuma cha m'nyumba mwake chikukulirakulira. Chifukwa pamene munthuyu amwalira, sadzatengapo kanthu. Chuma chake sichidzapita naye limodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:17

Chakudya chochipeza monyenga chimamkomera munthu, koma pambuyo pake chimakasanduka ngati lubwe m'kamwa mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:70-72

Mulungu adasankhula Davide mtumiki wake, ndipo adakamtenga ku makola a nkhosa. Adamtenga kumene ankaŵeta nkhosa zimene zinali ndi ana, kuti adzakhale mbusa wa Yakobe, fuko lake, wa Israele, choloŵa chake. Davide adaŵasamala ndi mtima wolungama, naŵatsogolera ndi dzanja lake mwaluso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 7:10

Musamazunze akazi amasiye ndi ana amasiye, alendo ndiponso amphaŵi. Musamaganizirane zachiwembu m'mitima mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:19

“Usabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:16-17

Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka, kupambana kukhala nazo zokoma zambiri zimene munthu woipa ali nazo. Pakuti Chauta adzathetsa mphamvu za anthu oipa, koma adzalimbikitsa anthu onse abwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:7

“Munthu akasungiza mnzake ndalama kapena zina zamtengowapatali, ndipo zibedwa m'nyumba mwa munthumo, mbalayo ilipire moŵirikiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 4:8

Panali munthu amene anali yekha, wopanda mwana kapena mbale, komabe ntchito yake yolemetsa sinkatha. Maso ake sankakhutitsidwa nacho chuma chake. Motero sankadzifunsa konse kuti, “Kodi ntchito yolemetsa ndikuigwirayi ndiponso mavuto a kudzimana zokondweretsaŵa, ndikuchitira yani?” Zimenezi nzopanda phindu ndiponso nzosakondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:28

Amabisalira ngati mbala yachifwamba, ndipo chifukwa cha iyeyo amuna ambiri amasanduka osakhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:27

Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 82:3

Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:6

“Ngati mmodzi mwa anthu ako osauka aimbidwa mlandu, umuweruze molungama ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:19

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:94

Ndine wanu, pulumutseni, pakuti ndasamala malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:24

Woyenda ndi mbala ndi wodana ndi moyo wake, amamva kutemberera, koma osaulula kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:10

Amene amasokeza anthu olungama kuti azitsata njira yoipa, adzagwa m'dzenje lake lomwe. Koma anthu amene alibe cholakwa adzalandira choloŵa chabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:11

Wokongoza ndalama amlande zonse zimene ali nazo. Alendo afunkhe zimene adapindula ndi ntchito yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:1-3

Mverani tsono, inu anthu achumanu. Lirani ndi kufuula chifukwa cha zovuta zimene zikudzakugwerani. Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m'dzina la Ambuye. Iwo adamva zoŵaŵa, komabe adapirira. Anthu amene timaŵatchula odala, ndi amene anali olimbika. Mudamva za kulimbika kwa Yobe, ndipo mudaona m'mene Ambuye adamchitira potsiriza, pakuti Ambuye ngachifundo ndi okoma mtima. Koma koposa zonse abale anga, musamalumbira. Musalumbire potchula Kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. Pofuna kutsimikiza kanthu, muzingoti, “Inde”. Pofuna kukana kanthu, muzingoti, “Ai”. Muzitero, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni kuti ndinu opalamula. Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu. Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye. Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo. Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe. Eliya anali munthu monga ife tomwe. Iye uja adaapemphera kolimba kuti mvula isagwe, ndipo mvula siidagwedi pa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi. Atapempheranso, mvula idagwa, nthaka nkuyambanso kumeretsa mbeu zake. Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza, Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu. dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa. Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 33:15

Angathe kutero ndi amene amachita zolungama ndi kulankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga, amene amakutumula manja ake kuti angagwire chiphuphu, amene amatseka makutu kuti angamve mau opangana za kupha anzao, amene amatsinzina kuti angaone zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:13-14

M'kamwa mwao m'moopsa ngati manda apululu, ndi lilime lao amalankhula zonyenga, pamilomo pao pamatuluka mau aululu, ululu wake wonga wa mamba. M'kamwa mwao m'modzaza ndi matemberero, mumatuluka mau oŵaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:155

Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:13

Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 12:5

Chifukwa choti osauka alandidwa zao ndipo osoŵa akudandaula, Chauta akunena kuti, “Ndichitapo kanthu tsopano, ndiŵapulumutsa monga momwe akufuniramo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:7

Ndeu za anthu oipa zidzaŵaononga, poti amakana kuchita zolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:30-37

Apo Yesu adati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira achifwamba adamgwira. Adamuvula zovala, nammenya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa. “Ndiye zidangochitika kuti wansembe wina ankapita pa njira yomweyo. Pamene adaona munthu uja, adangolambalala. Chimodzimodzinso Mlevi wina adafika pamalopo, ndipo pamene adaona munthuyo, nayenso adangolambalala. Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni. Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino. M'maŵa mwake adatulutsa ndalama ziŵiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘Msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.’ ” Tsono Yesu adafunsa katswiri wa Malamulo uja kuti, “Inu pamenepa mukuganiza bwanji? Mwa anthu atatuŵa, ndani adakhala ngati mnzake wa munthu uja achifwamba adaamugwirayu?” Iye adati, “Amene adamchitira chifundo uja.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:21-22

Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa. Anthu amene Chauta adaŵadalitsa, adzalandira dziko kuti likhale lao, koma amene Chauta adaŵatemberera adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:6

Ukonde wa kangaude sangauvale ngati nsalu, chimene anthu amapangacho sangafunde konse. Ntchito zao nzoipa ndipo amakonda kuchita zandeu ndi manja ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:3

Ungwiro wa anthu olungama umaŵatsogolera, koma makhalidwe okhota a anthu onyenga ngoononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 18:30

“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:118

Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu, zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:22

Chofunika kwa munthu nkukhulupirika. Kukhala wosauka nkwabwino koposa kukhala wonama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 79:12

Inu Ambuye, kunyoza kuja kumene anthu a mitundu ina adakunyozani, muŵabwezere kasanunkaŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:2

Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi, munthu amene amalimbikira kuzichita, amene amalemekeza tsiku la Sabata, osaliwononga, ndipo amadziletsa kuchita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 52:1

Bwanji ukunyadira ntchito zako zoipa, munthu wamphamvuwe?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:17

Munthu akadziŵa zabwino zimene ayenera kuchita, napanda kuzichita, ndiye kuti wachimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:25

Kulakalaka kwa munthu waulesi kumamupha, poti amangokhala manja ali khoba, osagwira ntchito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:10

Masikelo ndi miyeso ina yoyesera zinthu zikakhala zonyenga, zonsezo zimamunyansa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:13

Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 53:4

Kani anthu oipaŵa alibe nzeru chotere? Iwo amameza anthu anga, kuŵayesa chakudya, ndipo samutama Mulungu mopemba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:21

dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:16

Amene amapondereza osauka kuti aonjezere pa chuma chake, kapena amene amangopatsa zinthu olemera okha, adzasanduka wosauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:11

Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 9:17

“Madzi akuba ndiwo amatsekemera, buledi wodya mobisa ndiye amakoma.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 3:8

Ine ndikuti, Kodi munthu angathe kubera Mulungu? Komabe inu mumandibera. Inu mumati, ‘Kodi timakuberani bwanji?’ Ine ndikuti, Mumandibera pa zachikhumi zanu ndi zopereka zina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:1

“Kunena zoona, munthu woloŵa m'khola la nkhosa osadzera pa khomo, koma kuchita kukwerera pena, ameneyo ndi wakuba ndi wolanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:9

Mumaba, mumapha, mumachita zigololo, mumalumbira zonama, mumapereka nsembe zopsereza kwa Baala, mumatsata milungu ina imene kale simunkaidziŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:30

Paja anthu sainyoza mbala, ikaba chifukwa cha njala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:15

“Usabe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:1

“Munthu akaba ng'ombe kapena nkhosa, nkuipha kapena kuigulitsa, alipire ng'ombe zisanu pa ng'ombe imodzi, kapena nkhosa zinai pa nkhosa imodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 2:26

“Banja la Israele lidzachita manyazi, monga momwe mbala imachitira manyazi akaigwira. Aisraele, mafumu ao ndi akalonga ao, ansembe ao ndi aneneri ao, onsewo adzachita manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:19

Malamulo ukuŵadziŵa: Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, usadyerere mnzako, lemekeza atate ako ndi amai ako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:28

Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Mzimu Woyera wokondedwa wanga, Inu ndinu mtsogoleri wanga, chitonthozo changa, ndi amene amandisintha. Ndikukupemphani mundithandize ndi kundimasula ku chilichonse chomwe chimandimanga ku uchimo. Mawu anu amati: "Wakubayo asabenso, koma agwire ntchito, akuchita zabwino ndi manja ake, kuti akhale ndi chogawana ndi wosowa." Ambuye Yesu, ndikhululukireni munthu aliyense amene ndidamuwopseza ndi kumunyoza kuti ndimubwere, ndikhululukireni chilichonse chomwe ndidaba, kaya chifukwa cha kusowa kapena chifukwa cha ulesi, konzani ndi kulimbitsa munthu wamkati mwanga, ndithandizeni kuvua munthu wakale amene ali ndi zilakolako zonyenga kuti ndisapatse malo uchimo m'moyo mwanga. Ndikutsutsa chilakolako chilichonse ndi chilichonse chomwe chimandikakamiza kubera, chotsani Ambuye, anthu onse omwe amandilimbikitsa molakwika ndi omwe akufuna choipa changa achotsereni pa njira yanga. Mawu anu amati: "Indetu, indetu, ndikukuuzani, kuti aliyense wochita uchimo, ndi kapolo wa uchimo." Ambuye, ndithandizeni kupambana ndi kutseka zitseko za uchimo, kuti mtima wanga udane ndi kutaya kuba, kuba, dama, zolaula, bodza, chilakolako, umbombo, chigololo ndi chonyansa chilichonse. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa