Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


MAVESI OKHUDZA MASIKU APADERA

MAVESI OKHUDZA MASIKU APADERA

Mulungu ndi wodabwitsa, amatipatsa nthawi yoti tisekerere ndi kusangalala ndi achibale ndi anzathu. Nthawi ngati kubadwa, chikumbutso cha ukwati, ukwati wokha, ndi masiku ena apadera amenewa, timasangalala nawo kwambiri. Koma dziwani ichi, Mulungu amatipatsa chifundo chake chatsopano m'mawa uliwonse ndipo zimapangitsa tsiku lililonse kukhala lapばadera; tsiku loti tisangalale ndi Ambuye athu Yesu Khristu ndikusangalala ndi zodabwitsa zake.

Mukasekerera ndi okondedwa anu, nthawi zonse mutha kugawana nawo mawu a Mulungu ndikusinkhasinkha zabwino zake.




Zefaniya 3:17

Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 6:24-26

Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 1:11

Chauta, Mulungu wa makolo anu, akulitse chiŵerengero chanu pochichulukitsa ndi chikwi chimodzi, ndipo akudalitseni monga momwe adalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:4-7

Muzikondwa mwa Ambuye nthaŵi zonse. Ndikubwerezanso kuti, “Muzikondwa.” Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi. Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:8

Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:14

Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:12

“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:26

Amalankhula mwanzeru, ndipo amaphunzitsa anthu ndi mau okoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3

Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:4-7

Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:2-4

Akutumizire chithandizo kuchokera ku malo ake oyera, akuchirikize kuchokera ku Ziyoni. Alandire zopereka zako zonse, akondwere ndi nsembe zako zopsereza. Akupatse zimene mtima wako ukukhumba, akuthandize kuti zonse zimene wakonza zichitikedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:1

Mkazi wanzeru amamanga banja lake, koma wopusa amalipasula ndi zochita zake zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:16

Mkazi wa mkhalidwe wabwino amalandira ulemu, koma amuna ankhanza amangopata chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:25-28

Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake. Amaganiza zakutsogolo mosangalala. Amalankhula mwanzeru, ndipo amaphunzitsa anthu ndi mau okoma. Amayang'anira makhalidwe a anthu a pabanja pake, ndipo sachita ulesi mpang'ono pomwe. Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala. Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:2-3

Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:8-9

Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa. Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluŵa pamutu pako, zili ngati mkanda wa m'khosi mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:20

Anthu osauka amaŵachitira chifundo, amphaŵi amaŵapatsa chithandizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:10-31

Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali. Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasoŵa phindu. Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa. Amanka nafunafuna ubweya ndi thonje, ndipo amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu. Ali ngati zombo za anthu amalonda, zakudya zake amakazitenga kutali. Amadzuka usikusiku nkuyamba kukonzera chakudya anthu a pabanja pake, ndi kuŵagaŵira ntchito adzakazi ake. Amalingalira za munda, naugula. Amalima munda wamphesa ndi ndalama zozipeza ndi manja ake. Amavala dzilimbe ndipo sachita manja khoba pogwira ntchito. Amazindikira kuti malonda ake ndi aphindu, choncho nyale yake sizima usiku wonse. Thonje amadzilukira yekha, ndipo nsalu amadziwombera yekha. Nchiyani, mwana wanga? Nchiyani, mwana wa m'mimba mwanga? Nchiyani, mwana wanga amene ndidachita kukupempha polonjeza ndi malumbiro? Anthu osauka amaŵachitira chifundo, amphaŵi amaŵapatsa chithandizo. A pabanja pake saŵaopera kuti nkufa nacho chisanu, poti amadziŵa kuti onsewo amavala zovala zofunda. Amadzipangira yekha zofunda, ndipo iye amavala zovala zabafuta ndi za mtengo wapatali. Mwamuna wake ndi wodziŵika ndithu ku mabwalo, akakhala pakati pa akuluakulu a dziko. Mkazi ameneyu amasoka zovala za nsalu yabafuta, nazigulitsa, amaperekanso mipango kwa anthu amalonda. Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake. Amaganiza zakutsogolo mosangalala. Amalankhula mwanzeru, ndipo amaphunzitsa anthu ndi mau okoma. Amayang'anira makhalidwe a anthu a pabanja pake, ndipo sachita ulesi mpang'ono pomwe. Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala. Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati, “Inde alipo akazi ambiri olemerera kwabasi, koma kuyerekeza ndi iwe, onsewo nchabe.” Mphamvu zako usathere pa akazi, usamayenda nawo ameneŵa, amaononga ndi mafumu omwe. Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda. Muzimlemekeza chifukwa cha zochita zake, ntchito zake zizimpatsa ulemu ku mabwalo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13-14

Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:5

Ndimakumbukira chikhulupiriro chako chosanyenga. Chikhulupiriro chimenechi adaayamba ndi agogo ako aLoisi kukhala nacho. Amai ako aYunisi anali nachonso, ndipo tsopano sindikukayika konse kuti iwenso uli nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 2:7-8

Koma tidakhala ofatsa pakati panu ngati mai wosamalira ana ake. Tinkakukondani, ndipo chifukwa cha kukulakalakani kwambiri, tidatsimikiza zogaŵana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso ngakhale moyo wathu womwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:1-2

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake. Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse. Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-3

Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 3:20

Adamu adatcha mkazi wake Heva, chifukwa choti iyeyu anali mai wa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:4-5

kuti choncho athe kuphunzitsa azimai achitsikana kukonda amuna ao ndi ana ao. Aŵaphunzitse kukhala a maganizo anzeru, opanda dama, osamala bwino zapabanja, ndi omvera amuna ao. Pamenepo anthu sanganyoze mau a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:4

Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 8:6

Umatirire mtima wako kuti musaloŵe winanso koma ine ndekha, ndipo sudzakumbatira winanso koma ine ndekha. Paja chikondi nchamphamvu ngati imfa, nsanje njaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti laŵilaŵi ngati malaŵi a moto, ndipo nchotentha koopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:20

Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-14

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:11

Bwerani ana anga, mundimvere, ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:3-4

Kudzikongoletsa kwanu kusangokhala kwa maonekedwe akunja pakuluka tsitsi, ndi kuvala zamakaka zagolide ndi zovala zamtengowapatali. Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:11

Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:5

Mulungu ali m'kati mwa mzindawo, sudzaonongeka konse. Mulungu adzauthandiza dzuŵa lisanatuluke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:4

Mibadwo ndi mibadwo idzatamanda ntchito zanu, idzalalika ntchito zanu zamphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:17-18

Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:5

Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:4

Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:12

Inu Ambuye, Mulungu wanga, ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse, ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:15-16

Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse. Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:7

Tsono muzipereka kwa onse zimene zikukhalira iwowo: msonkho kwa okhometsa msonkho, zolipira kwa oyenera kuŵalipira. Muzilemekeza oyenera kuŵalemekeza, ndi kuchitira ulemu oyenera kuŵachitira ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 131:2

Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:2-3

Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai, ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu. Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni. Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu. Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni. Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa. M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo. ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:28

Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala. Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:10

Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:29

“Inde alipo akazi ambiri olemerera kwabasi, koma kuyerekeza ndi iwe, onsewo nchabe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:30

Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13

Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:22

Wopeza mkazi, wapeza chinthu chabwino, Chauta wamukomera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:20-21

Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako. Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 19:26

Pamene Yesu adaona amai ake ndi wophunzira uja amene Iye ankamukonda kwambiri, akuimirira pafupi, adauza amai ake kuti, “Mai, nayu mwana wanu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 113:9

Amapatsa banja mkazi wosabala, namsandutsa mai wosangalala wa ana. Tamandani Chauta!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:13

Ndidzakusangalatsani ku Yerusalemu monga momwe mai amasangalatsira mwana wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga wokondedwa, landirani ulemu ndi chiyamiko chifukwa ndinu nokha woyenera. Zikomo chifukwa cha kukhala kasupe wa zonse, chikondi, chimwemwe, mgwirizano, mtendere ndi kukhuta kwa mzimu wanga zimachokera kwa inu nokha. Dalitsani tsiku lapaderali, tisinthireni ife ndi banja langa ndi Mzimu wanu. Sinthani mtima wanga kukhala guwa lanu lokulambirani nthawi zonse, chikondi chanu chilamulire pa chikondwerero chilichonse, pamavuto aliwonse, kapena chilambero chilichonse. Ambuye, sungani ndi kudalitsa miyoyo ya onse amene ali ndi ine lerolino, ndi kuwadzaza ndi kukhalapo kwanu. Zikomo chifukwa chakuti mwakhala thandizo langa ndi pothawirapo panga mosasamala kanthu za tsiku kapena nthawi. Ndikukupemphani kuti ndiziyenda motsogozedwa ndi Mzimu wanu Woyera kuti ndithane ndi mavuto ndi mayesero onse molimba mtima ndi kupambana. Ambuye, ndisungeni ku ziwembu ndi misampha yonse ya mdani. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa