Ndi zodabwitsa bwanji kuika Mulungu pa chilichonse, ngakhale pamene muli ndi mwambo ndipo mukufuna kuti ukhale ndi vesi la m'Baibulo pa chiitano chanu, kaya ndi ukwati, tsiku lobadwa, maphunziro otsiriza… Ndizokongola kukhala ndi kapena kupeza vesi m'mawu a Mulungu. Apa mupeza vesi la mwambo uliwonse umene muli nawo, ndikuyembekeza kuti likhale lodalitsa komanso lothandiza.
Taganizirani mmene zilili zolimbikitsa kuika Mulungu patsogolo pa zochita zathu. Monga mmene Baibulo limatiphunzitsira, zonse zimene timachita, tizichita monga kuti tizichitira Ambuye. Ndipo chifukwa chake kuika vesi la m’Baibulo pa chiitano chanu ndi njira yabwino yosonyezera kuti Mulungu ndiye maziko a chikondwerero chanu.
Palibe chimene chimakhala chokoma mtima kuposa kudziwa kuti Mulungu ali nafe nthawi zonse. Kaya ndi mwambo wotani, kukhala ndi vesi la m'Baibulo kumatikumbutsa kuti Mulungu ali nafe paulendo wathu. Ndi chikumbutso choti sitingayende okha, ndipo chikondi Chake ndi mphamvu Zake zidzatithandiza nthawi zonse.
Ndikukhulupirira kuti vesi limene mwasankha lidzakubarikiitsani komanso kudzakuthandizani. Mulungu akhale nanu pa mwambo wanu ndipo akudalitseni m'njira zonse.
Umatirire mtima wako kuti musaloŵe winanso koma ine ndekha, ndipo sudzakumbatira winanso koma ine ndekha. Paja chikondi nchamphamvu ngati imfa, nsanje njaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti laŵilaŵi ngati malaŵi a moto, ndipo nchotentha koopsa.
Wokondedwa wangayo ndi wangadi, ndipo ine ndine wake. Amadyetsa gulu lake la ziŵeto pakati pa akakombo.
Momwemonso amuna azikonda akazi ao, monga momwe eniakewo amakondera matupi ao. Amene amakonda mkazi wake, ndiye kuti amadzikonda iye yemwe.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
Chikondi nchosatha. Uneneri udzatha, kulankhula zilankhulo zosadziŵika kudzalekeka, ndipo nzeru za anthu zidzatha.
Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo.
Umatirire mtima wako kuti musaloŵe winanso koma ine ndekha, ndipo sudzakumbatira winanso koma ine ndekha. Paja chikondi nchamphamvu ngati imfa, nsanje njaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti laŵilaŵi ngati malaŵi a moto, ndipo nchotentha koopsa. Ngakhale madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, ngakhale madzi a chigumula sangachikokolole. Ngakhale munthu atapereka chuma chonse cha m'nyumba chifukwa chofuna kugula chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu. Alongo a Mkazi
Ngakhale madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, ngakhale madzi a chigumula sangachikokolole. Ngakhale munthu atapereka chuma chonse cha m'nyumba chifukwa chofuna kugula chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu. Alongo a Mkazi
Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe.
Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai, ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu. Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni. Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu. Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni. Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa. M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo. ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.
Chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika zidzakumana. Chilungamo ndi mtendere zidzagwirizana.
Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira.
Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.
Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe, makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi, uŵalembe mumtima mwako. Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse. Usachite naye nsanje munthu wachiwawa, usatsanzireko khalidwe lake lililonse. Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa, koma olungama okha amayanjana nawo. Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa. Anthu onyoza, Iye amaŵanyoza, koma odzichepetsa Iye amaŵakomera mtima. Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi. Choncho udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi pa anthunso.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Lolani kuti m'maŵa ndimve za chikondi chanu chosasinthika, chifukwa ndimakhulupirira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiziyendamo, pakuti ndimapereka mtima wanga kwa Inu.
Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.
Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Paja mau a Mulungu akuti, “Nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amai ake, nkukaphatikizana ndi mkazi wake, kuti aŵiriwo asanduke thupi limodzi.”
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, wangoti mtima wangawu kwe! Wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi mphande imodzi ya mkanda wa m'khosi mwako.
Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali.
Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi. Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”
Ndidangoti iwo aja ntaŵapitirira pang'ono, ndampeza amene mtima wanga umamkonda. Ndidamgwira, osamlola kuti achoke, mpaka nditamloŵetsa m'nyumba ya amai anga, m'chipinda cha amene adandibala.
Tamandani Chauta. Ndidzathokoza Chauta ndi mtima wanga wonse pa msonkhano wa anthu olungama mtima.
Ndidzasimba za chikondi chosasinthika cha Chauta. Ndidzamtamanda chifukwa cha zonse zimene watichitira. Wadalitsa kwambiri anthu a ku Israele, potsata chifundo ndi kukula kwa chikondi chake chosasinthika.
Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi. Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Akazi
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.
Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.
Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, chikondi chako nchosangalatsa. Chikondi chako nchosangalatsa kupambana vinyo, mafuta ako ndi onunkhira bwino kupambana zonunkhira zabwino zonse.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.
Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Yesu adaŵayankha kuti, “Kodi simunaŵerenge kuti Mulungu amene adalenga anthu pa chiyambi, adalenga wina wamwamuna, wina wamkazi? Ndipo kuti Iye yemweyo adati, ‘Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ake ndi amai ake, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.’ Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”
Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera. koma changwiro chikadzaoneka, chopereŵeracho chidzatha. Pamene ine ndinali mwana, ndinkalankhula mwachibwana, ndinkaganiza mwachibwana ndipo zinthu ndinkazitengera chibwana. Koma nditakula, ndidazileka zachibwanazo. Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu. Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi. Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri, ngakhale nditamadziŵa zobisika zonse, ndi kumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikhulupiriro chachikulu chakuti ndingathe kusuntha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse. Ndipo ngakhale nditagaŵira amphaŵi chuma changa chonse, kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ndiye kuti changa palibe.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Kuli bwino kudyera masamba pali chikondi, kupambana kudyera nyama ya ng'ombe yonenepa pali chidani.
Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Pambuyo pake Chauta adati, “Sibwino kuti munthuyu akhale yekha. Ndipanga mnzake woti azimthandiza.”
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Cholinga changa pokupatsa malangizo ameneŵa, nchakuti pakhale chikondi chochokera mu mtima woyera, mu mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndiponso m'chikhulupiriro chopanda chiphamaso.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Paja Chauta amakondwera ndi anthu ake, amaŵalemekeza anthu odzichepetsa poŵagonjetsera adani ao.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
Milomo yake njosangalatsa kwambiri, munthuyo amanditenga mtima kwabasi. Ameneyutu ndiye wokondedwa wanga, ndiponso bwenzi langa, inu akazi a ku Yerusalemu.
Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake. Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza.
Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aŵiriwo amakhala thupi limodzi.
Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.