Mawu a Mulungu ndiyenera kuwaphunzitsa ana anga kuyambira ali aang'ono. Ndiyenera kuwaphunzitsa kuopa Mulungu ndi malonjezo ake. Baibulo limatiphunzitsa kulangiza mwana njira yoyenera, ndipo akafika ukalamba sadzachoka pa njira imeneyo.
Kuti tilowe kumwamba, Yesu anatiuza kuti tiyenera kukhala ngati ana. Ana sakhala ndi mkwiyo, amaiwala zolakwa, ndipo ali ndi mtima woyera, wosavuta, komanso wodziwa kuyamikira. Yesu anati: “Leke ana aang'ono abwere kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Kumwamba ndi wa otere.” (Mateyu 19:14). Choncho, ntchito yathu ndiyo kulola ana athu, adzukulu athu, abale athu aang'ono, kapena mwana aliyense kutsogozedwa ndi mawu a Mulungu ndi kuphunzira mavesi okongola awa kuyambira ali aang'ono.
Mulungu amakonda ana kuyambira ali m'mimba mwa amayi awo. Mulungu anakonzeratu kale dongosolo labwino la mwana aliyense ndipo amafuna kuti likwaniritsidwe m'miyoyo yawo. Ana ndi cholowa chochokera kwa Ambuye; zipatso za m'mimba ndi mphoto yochokera kwa Mulungu. “Maso anu adandiona ine ndisanakhale munthu; ndipo m’buku mwanu munalembedwa masiku onse adandiikidwira, pamene panalibe ngakhale limodzi la iwo.” (Masalimo 139:16).
“Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziŵa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
“Aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Ndipo wondilandira Ine bwino, ndiye kuti akulandira bwino osati Ineyo, koma Atate amene adandituma.”
Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake. Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Ndidzathira madzi pa dziko louma, ndidzayendetsa mitsinje m'chipululu. Ndidzatumizira ana anu Mzimu wanga, ndidzatsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
Chauta, Mpulumutsi wako, amene adakupanga m'mimba mwa mai wako, akunena kuti, “Ndine Chauta, amene ndidapanga zinthu zonse. Pamene ndinkayalika zakuthambo, ndinali ndekha. Pamene ndinkalenga dziko lapansi, kodi analipo amene adandithandiza?
Ndakhala ndikudalira Inu chibadwire changa, Inu mwakhala Mulungu wanga kuyambira pamene mai wanga adandibala.
Esau atayang'ana, adaona akazi ndi ana omwe aja, ndipo adamufunsa kuti, “Anthu aŵa ali ndi iweŵa nga yani?” Yakobe adayankha kuti, “Aŵa, mbuyanga, ndi ana amene Mulungu adandipatsa mwa chifundo chake.”
Koma mngeloyo adaŵauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Usiku womwe uno m'mudzi wa Davide wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako.
Palibe mkazi amene adzapititse padera m'dziko mwanumo, ndipo wosabala sadzaoneka. Ndidzakupatsani moyo wautali.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake. Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.
Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.”
Ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufika, ndi kukuziriza malire a dziko lanu. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kulanda dziko lanulo nthaŵi zitatuzo za pa chaka, pamene mudzadziwonetse pamaso pa Ine Chauta, Mulungu wanu.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chimafika mpaka kumwamba, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.
Pakuti mwalanditsa moyo wanga ku imfa. Inde mwandichirikiza mapazi kuti ndisagwe, kuti motero ndiziyenda pamaso pa Mulungu m'kuŵala kwa amoyo.
“Nchifukwa chake musamada nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Tidzadyanji? Tidzamwanji? Tidzavalanji?’ Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu akunja. Atate anu akumwamba amadziŵa kuti mukuzisoŵa zonsezi. Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse. Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndinu Mulungu wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndi wokhulupirika kotheratu.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse. Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Tsono Chauta adatenga dothi pa nthaka, ndipo adaumba munthu ndi dothilo. Adamuuzira mpweya wopatsa moyo m'mphuno zake, ndipo munthuyo adakhala wamoyo.
“Mundimvere, inu zidzukulu za Yakobe, inu nonse otsala a m'nyumba ya Israele. Ndakhala ndikukusamalani chibadwire chanu, ndidakunyamulani kuyambira m'mimba mwa amai anu. Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.
Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa. Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Chauta amene amakhala ku Ziyoni akudalitse. Uwone m'mene Yerusalemu zinthu zidzamuyendere bwino masiku onse a moyo wako. Ukhale ndi moyo wautali kuti uwone zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israele.
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.
Nawonso ana ndi makanda omwe amauimbira. Mwamanga linga chifukwa cha adani anu, kuti mugonjetse onse okuukirani.
Adamu adakhala ndi mkazi wake Heva ndipo mkaziyo adatenga pathupi. Tsono adabala mwana wamwamuna, ndipo adati, “Ndalandira mwana wamwamuna mwa chithandizo cha Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Kaini.
Uzimlanga mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere mu mtima, adzakondweretsa mtima wako m'tsogolo.
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.
Akudalitseni Chauta amene amakhala ku Ziyoni, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
“Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.”
Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Chauta adalumbirira Davide momtsimikizira, ndipo sadzasintha, adati, “Ndidzakhazika pa mpando wachifumu mmodzi mwa ana ako aamuna. Ngati ana ako aamuna asunga chipangano changa ndi malamulo anga amene ndidzaŵaphunzitsa, ana aonso adzakhala pa mpando wako wachifumu mpaka muyaya.”
Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima, ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe. Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga, ndipo ndimakukonda, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina, mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Ndithu iyo idzalanditsa anthu osoŵa amene amaiitana, idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda woŵathandiza. Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osoŵa, ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphaŵi. Idzaombola moyo wao kwa anthu oŵapsinja ndi kwa oŵachita zankhanza, pakuti magazi ao ndi amtengowapatali pamaso pake.
Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Anthu ako ndidzaŵaphunzitsa ndekha, Ine Chauta, ana ako ndidzaŵadalitsa ndi kuŵapatsa mtendere waukulu.
Sitidzabisira ana ao, koma tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo ntchito zotamandika za Chauta, tidzaŵasimbira mphamvu zake ndi zodabwitsa zimene wakhala akuchita.
Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa.
Chauta adzadalitsa ana anu ndi zokolola zanu, ndi ana a zoŵeta zanu, ndipo adzakupatsani ng'ombe ndi zoŵeta zina zambiri.
Pakuti Chauta ndiye muweruzi wathu. Chauta ndiye wotilamula, Chauta ndiye mfumu yathu, ndiye amene adzatipulumutsa.
“Ndani wazikhulupirira zimene tamvazi? Ndani wazindikira mphamvu za Chauta pa zimenezi? Komabe ndi Chauta yemwe amene adaafuna kuti amuzunze, ndipo adamsautsadi. Iye adapereka moyo wake kuti ukhale nsembe yokhululukira machimo. Choncho adzaona zidzukulu zake, adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Chauta chidzachitika mwa iye. Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula. Motero Ine ndidzampatsa ulemu woyenerera akuluakulu. Adzagaŵana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza kuti adapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo. Adasenza machimo a anthu ambiri, ndipo adaŵapempherera ochimwawo kuti akhululukidwe. Pajatu mtumiki wake uja adakula ngati chiphukira pamaso pa Mulungu, ndiponso ngati muzu m'nthaka youma. Iye analibe maonekedwe enieni kapena nkhope yabwino, kuti ife nkumamuyang'ana. Analibe kukongola koti ife nkukokeka naye.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Chauta amapasula nyumba ya munthu wonyada, koma amasamalira kadziko ka mkazi wamasiye.
Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Koma ine ndili ngati mtengo wauŵisi wa olivi m'Nyumba ya Mulungu. Ndimaika mtima nthaŵi zonse pa chikondi chosasinthika cha Mulungu.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka. Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.
Koma Chauta amakondwera ndi anthu omuwopa, amene amadalira chikondi chake chosasinthika.
Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe. Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.
Inu Ambuye, Mulungu wathu, mutikomere mtima, ndi kudalitsa zonse zimene timachita, ndithu mudalitse ntchito zonse za manja athu.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate. Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse.
Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”
Pajatu chilichonse chimene Mulungu adalenga nchabwino, palibe chilichonse choti munthu asale, akamachilandira moyamika Mulungu,
Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.
Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu
Inu Chauta, Mulungu wanga, mwatichitira zodabwitsa zambiri, mwatikonzera zabwino zambiri zakutsogolo. Palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulingana nanu. Ndikati ndisimbe ndi kulongosola za zimenezo, sindingathe kuziŵerenga zonse chifukwa cha kuchuluka kwake.
Tsoka kwa wofunsa bambo wake kuti, “Mwabereka chiyani,” kapena mai wake kuti, “Mwabala chiyani?”
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere, ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.”
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Komabe pakuti Mulungu ngwachifundo, adaŵakhululukira machimo ao, ndipo sadaŵaononge. Kaŵirikaŵiri ankadziletsa kukwiya, sadalole kuti mkwiyo wake wonse uyake.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
“Suja amagulitsa atimba asanu tindalama tiŵiri? Komabe Mulungu saiŵala ndi mmodzi yemwe. Ndipo tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.”
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Cholinga cha Mulungu ndi cha kudziŵitsa anthuwo kukoma kwake kwa chinsinsicho ndi ulemerero wake pakati pa anthu akunja. Chinsinsicho nchakuti Khristu ali mwa inu, ndipo Iye amakupatsani chiyembekezo cha kudzalandira ulemerero.
Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
Ndi waukulu ubwino wanu umene mwaŵasungira anthu okumverani, umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu, aliyense waona zimenezi.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
Sindichita mantha ngakhale adani anga ndi osaŵerengeka, ngakhale andizinge ndi kundithira nkhondo.
“Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala? Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Mundisunge Inu Mulungu, pakuti ndikuthaŵira kwa Inu. chifukwa simudzandisiya ku malo a anthu akufa, simudzalola kuti wokondedwa wanune ndikaole kumeneko. Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja. Ndimamuuza Chauta kuti, “Inu ndinu Ambuye anga. Ndilibe chinthu china chabwino koma Inu nokha.”
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.