Ambuye watipatsa madalitso ambiri, tsiku lililonse tili ndi zambiri zoti tiyamike. Mulungu ndi wabwino ndipo amatidzaza ndi madalitso ake tsiku lililonse. Mu Mulungu timawona ndi kusangalala ndi madalitso amenewa monga: kukhala ndi pogona, kukhala ndi thanzi labwino, kukhala ndi banja, kukhala ndi ntchito. Pali zinthu zambiri zomwe timawona madalitso a Mulungu, kotero nthawi zonse padzakhala chifukwa choyamikira Mulungu. Nthawi zina timaganizira kwambiri mavuto athu kapena zinthu zomwe tilibe m'malo motamanda ndi kuyamikira Mulungu pazinthu zonse zabwino zomwe zili m'miyoyo yathu.
Mulungu wathu ndiye wopereka zinthu zonse zabwino! Yambani chizolowezi choyamika Mulungu tsiku lililonse chifukwa cha ubwino wake wonse. Conco, popeza tilandira ufumu wosagwedezeka, tiyeni tikhale oyamikira. Ndi chiyamiko chimenechi, tiyeni tilambire Mulungu momusangalatsa, ndi mantha ndi ulemu. (Ahebri 12:28) Apa mupeza mavesi ambiri oyamika Mulungu.
Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Muziyamika Mulungu Atate nthaŵi zonse chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima.
Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.
Ndidzatamanda dzina la Mulungu pomuimbira nyimbo, ndidzalalika ukulu wake pomuthokoza.
Ndipo timapemphera kuti muziyamika Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungira anthu ao mu ufumu wa kuŵala.
Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta, anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani.
Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, ndi nsomba zija, adathokoza Mulungu, nazinyemanyema nkuzipereka kwa ophunzira ake, iwowo nakazigaŵira anthu aja.
Inu Ambuye, Mulungu wanga, ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse, ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.
“Koma perekani nsembe zanu zothokozera kwa Mulungu, ndipo muchite zimene mudalumbira kwa Wopambanazonse.
Ndimadzuka pakati pa usiku kuti ndikutamandeni, chifukwa cha malangizo anu olungama.
Timathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kumakutchulani m'mapemphero athu.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi. Kumwamba amaimba nyimbo zotamanda ulemerero wanu.
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.
Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe.
Ndidzaimbira Chauta moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Chauta, nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Tamandani Chauta, inu angelo ake, inu amphamvu amene mumamva mau ake, amene mumachita zimene amalamula. Tamandani Chauta, inu magulu a ankhondo ake onse, atumiki ake ochita zimene Iye afuna.
Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Tikukuthokozani Inu Mulungu, ndithu tikukuthokozani. Tikutchula dzina lanu mopemphera ndipo tikulalika ntchito zanu zodabwitsa.
Ndikugwada moŵerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera. Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, chifukwanso cha kukhulupirika kwanu. Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu kupambana chinthu china chilichonse.
Tamandani Chauta! Nkwabwino kuimba nyimbo zotamanda Mulungu wathu, nkokondwetsa mtima kumtamanda moyenera.
Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta.
Tamandani Chauta. Ndidzathokoza Chauta ndi mtima wanga wonse pa msonkhano wa anthu olungama mtima.
Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera. Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse.
Ine ndidzathokoza Chauta chifukwa cha kulungama kwake, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Chauta, Wopambanazonse uja.
Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha.
Tamandani Chauta, inu zolengedwa zake zonse, ku madera onse a ufumu wake. Nawenso mtima wanga, tamanda Chauta!
Thokozani Chauta, tamandani dzina lake, lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta amene amakhala ku Ziyoni. Lalikani za ntchito zake kwa anthu a mitundu yonse.
Tamandani Chauta. Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Ndidzapambana adani anga ondizungulira, ndipo ndidzapereka nsembe m'Nyumba mwake ndili kufuula ndi chimwemwe. Ndidzaimba nyimbo yotamanda Chauta.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Tsiku limenelo mudzati: “Thokozani Chauta, tamandani dzina lake. Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
Ndidzamveketsa mbiri ku mibadwo yonse, nchifukwa chake mitundu ya anthu idzakutamandani mpaka muyaya.
Anthu onse a pa dziko lapansi amakupembedzani, amaimba nyimbo zotamanda Inu, amaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
Nchifukwa chake Davide adatamanda Chauta pamaso pa msonkhano wonse. Adati, “Mutamandike mpaka muyaya Inu Chauta, Mulungu wa Israele, kholo lathu.
Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse. Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu.
Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga. Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu. Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa mokhulupirika ndi motsimikiza, zinthu zimene mudakonzeratu kalekale.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.
Ndidzakuyamikani, Inu Mulungu wanga, mfumu yanga, ndidzalemekeza dzina lanu nthaŵi zonse mpaka muyaya.
Nkwabwino m'maŵa kulalika za chikondi chanu chosasinthika, ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu,
Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta, inu anthu ake oyera mtima, mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera.
Ndidzazipereka m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, mu mzinda wa Yerusalemu. Tamandani Chauta!
Anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Chauta, mabanja a mitundu ina ya anthu adzampembedza.
Chauta ndi wamkulu, ndi woyenera kumutamanda kwambiri. Timuyamike mu mzinda wake, pa phiri lake loyera,
Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.
Ndiponso akuti, “Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye, anthu a mitundu yonse amtamande.”
Thokozani Chauta, tamandani dzina lake, lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Inde momwemo. Inde momwemo.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Ombani m'manja inu anthu a mitundu yonse. Fuulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe.
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Okhulupirika akondwerere chigonjetso chopambanachi, aziimba mokondwa ali gone pa mabedi.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Pakamwa panga padzafuula ndi chimwemwe, pamene ndikukuimbirani nyimbo zotamanda. Nawonso mtima wanga umene mwauwombola, udzaimba moyamika.
Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera.
Iye amatchera khutu kuti andimve, nchifukwa chake ndidzampempha nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.