Kodi ndani amene anganamize kuti Yesu si Khristu? Iyeyu ndiye wotsutsana ndi Khristu, wokanira Atate ndi Mwana. Munamva bwanji zimene Yohane anatiuza? (1 Yohane 2:22)
Nkhani ya wotsutsana ndi Khristu, yomwe ili m'Baibulo, yakhala ikukopa chidwi cha anthu ambiri kwa nthawi yaitali. Malemba Opatulika amatiuza za munthu uyu amene adzadza m'masiku otsiriza, kudzionetsera ndi mphamvu zake ndi kunyengetsa osakhazikika m'chikhulupiriro, ngakhale osankhidwa. Ndikofunika kwambiri kukhala maso, kuzindikira choonadi ndi chinyengo, podziwa kuti tikukhala m'dziko lomwe Satana nayenso alipo ndipo tiyenera kuzindikira machenjerero ake.
Ndikulimbikitsani kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Mulungu ndikukhala olimba m'Mawu Ake, kuti tisagwere mumsampha wonyengedwa ndi malonjezo abodza a wotsutsana ndi Khristu. Taganizirani izi: kodi ndili wolimba m’chikhulupiriro changa? Kodi ndine wokonzeka kuchitira umboni Yesu ngakhale pakati pa mavuto?
Tiyeni tilimbikire m'pemphero, tiphunzire Mawu a Mulungu, ndipo tidalire mphamvu ya Mzimu Woyera kuti atitsogolere m'njira ya choonadi. Mulungu ndiye mphamvu yathu.
Wabodzayo ndani? Kodi si amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi wolonjezedwa uja? Wokana Atate ndi Mwana, ameneyo ndiye Woukira Khristu.
Koma aliyense wosavomereza Yesu, ameneyo ndi wosachokera kwa Mulungu. Maganizo akewo ndi ochokera kwa Woukira Khristu, yemwe uja mudamva kuti akubwerayu; ndipotu wafika kale m'dziko lapansi.
Ananu, ino ndi nthaŵi yotsiriza. Mudamva kuti kukubwera Woukira Khristu, ndipo tsopano aoneka kale ambiri oukira Khristu. Zimenezi zikutizindikiritsa kuti ino ndi nthaŵi yotsirizadi.
Paja pakuwoneka anthu ambiri onyenga pa dziko lapansi. Iwo savomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu. Munthu wosavomereza zimenezi ndi wonyenga, ndiponso woukira Khristu.
Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti, ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
Anthuwo adachita kuchoka pakati pathu, komabe sanali a gulu lathu kwenikweni. Pakuti akadakhala a gulu lathu, bwenzi akali nafebe. Koma adatichokera, kuti aonekere poyera kuti panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene anali wa gulu lathu.
Pambuyo pake ndidaona chilombo chikuvuuka m'nyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iŵiri. Pa nyanga iliyonse chidaavala chisoti chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu.
Koma aliyense wonyoza Mzimu Woyera, sadzakhululukidwa konse. Tchimo lakelo limakhala mpaka muyaya.”
Musalole kuti wina akupusitseni mwa njira iliyonse. Pajatu lisanafike tsikulo, kudzayamba kwachitika zoti anthu ochuluka akupandukira Mulungu, ndipo kudzaoneka Munthu Woipitsitsa uja, woyenera kutayikayu. Ameneyu ndi mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti mwiniwakeyo adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
Chilombo chimene ndidaaonacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati a chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chidaapatsa chilombocho mphamvu zake, mpando wake wachifumu, ndiponso ulamuliro waukulu. Umodzi mwa mitu yake unkaoneka ngati uli ndi bala lofa nalo, koma balalo linali litapola. Pamenepo anthu onse ankachitsata chilombocho ali odabwa.
Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.
Musalole kuti wina akupusitseni mwa njira iliyonse. Pajatu lisanafike tsikulo, kudzayamba kwachitika zoti anthu ochuluka akupandukira Mulungu, ndipo kudzaoneka Munthu Woipitsitsa uja, woyenera kutayikayu.
Chilombo chija chidaloledwa kulankhula mau onyada ndi onyoza Mulungu mwachipongwe. Ndipo chidapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42. Tsono chidayamba kunena mau achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo ake okhalamo, ndi onse okhala Kumwamba.
Zimenezitu si zododometsa ai, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu. Motero si chodabwitsa ngati atumiki ake omwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati otumikira chilungamo. Potsiriza adzalandira molingana ndi zimene ankachita.
Chidaloledwa kuŵathira nkhondo anthu a Mulungu ndi kuŵagonjetsa. Chidapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi a chilankhulo chilichonse.
Chidaaloledwa kuuzira mpweya wopatsa moyo mu fano la chilombo choyamba chija, kuti mpaka lizilankhula, ndi kuphetsa aliyense wosalipembedza.
Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine,’ ndipo adzasokeza anthu ambiri.
Chinkakakamiza anthu onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, ndiye kuti dzina la chilombo choyamba chija, kapena nambala yotanthauza dzina lake.
Chilombocho chidagwidwa pamodzi ndi mneneri wonama uja amene anali atachita zozizwitsa pamaso pake. Zozizwitsazo, iye anali atanyenga nazo anthu amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, ndiponso anthu amene anali atapembedza fano lake lija. Chilombo chija ndi mneneri wonama uja, onse aŵiri adaŵaponya m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala yoyaka ya sulufure.
Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya.
Tsono pamenepo Munthu Woipitsitsa uja adzaululuka. Ndipo Ambuye Yesu adzamthetsa ndi mpweya wa m'kamwa mwake, nkumuwonongeratu ndi maonekedwe ake aulemerero a kubwera kwake.
“Mudzaona ‘Chosakaza chonyansa chija’ chimene mneneri Daniele adaanena, atachiimika m'Nyumba ya Mulungu. (Amene ukuŵerengawe, umvetse bwino.)
“Chosakaza chonyansa chija chidzakhala atachiimika pamalo pomwe sichiyenera kukhalapo. (Umvetse bwino amene ukuŵerengawe.) Mukadzaona zimenezi, pamenepo amene ali m'Yudeya adzathaŵire ku mapiri.
Chilombo chimene unachiwona chija, kale chidaali chamoyo, koma tsopano sichilinso chamoyo. Chiyenera kutuluka kuchokera m'chiphompho chija kupita kukaonongedwa. Anthu onse okhala pa dziko lapansi, amene chilengedwere dziko lapansi maina ao sadalembedwe m'buku la amoyo, azidzadabwa poona chilombocho. Azidzadabwa poona kuti kale chidaali chamoyo koma tsopano sichilinso chamoyo, komabe m'tsogolo muno chidzaonekanso.
“Nyanga khumi zimene unaona, zikufanizira mafumu khumi amene asanayambebe kulamulira. Koma adzalandira mphamvu zolamulira ngati mafumu pa ora limodzi, pamodzi ndi chilombo chija. Mafumu khumi ameneŵa, cholinga chao ndi chimodzi, ndipo amapereka mphamvu zao ndi ulamuliro wao m'manja mwa chilombo chija.
Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse. Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu. Inu okondedwa, ngati Mulungu adatikonda kwambiri chotere, ifenso tiyenera kumakondana. Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife. Tikudziŵa kuti timakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera. Ife taona, ndipo tikuchita umboni, kuti Atate adatuma Mwana wake kuti adzakhale Mpulumutsi wa anthu a pa dziko lonse lapansi. Aliyense wovomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye, ndipo iye amakhala mwa Mulungu. Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye. Pamene chikondi chafikira pake penipeni mwa ife ndi apa pakuti moyo wathu pansi pano uli wonga moyo wa Khristu, kotero kuti tingathe kukhala olimba mtima pa tsiku la chiweruzo. Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye. Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda. Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: aliyense wovomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu, ameneyo ndi wochokera kwa Mulungu.
Tikudziŵa kuti ndife ake a Mulungu, ndipo kuti onse odalira zapansipano ali m'manja mwa Woipa uja.
pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.
Kenaka ndidaona mizimu yonyansa itatu, yonga achule, ikutuluka wina m'kamwa mwa chinjoka chija, wina m'kamwa mwa chilombo chija, wina m'kamwa mwa mneneri wonama uja. Imeneyi ndi ija timati mizimu yoipa imene imachita zozizwitsa. Imapita ponseponse kwa mafumu a pa dziko lapansi kukaŵaitana kuti adzabwere ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu lija la Mulungu Mphambe.
Motero mngelo woyamba adakakhuthulira za mumkhate mwake pa dziko lapansi. Pamenepo zilonda zonyansa ndi zopweteka zidabuka pa anthu onse aja, amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, napembedza fano lake.
Nchifukwa chake Mulungu adzatumiza mphamvu zoŵasokoneza, kuti akhulupirire zonama. Motero adzalangidwa onse amene sadakhulupirire choona, koma adakondwerera kusalungama.
Chinjoka chachikulu chija chidagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakale ija yotchedwa “Mdyerekezi” ndiponso “Satana”, wonyenga anthu a pa dziko lonse lapansi. Chidagwetsedwa pa dziko lapansi pamodzi ndi angelo ake onse.
Onse okhala pa dziko lapansi adzachipembedza, ndiye kuti aliyense amene, chilengedwere dziko lapansi, dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo la Mwanawankhosa adaphedwa uja.
Popeza kuti mwasunga mau anga oti mupirire mosatepatepa, Inenso ndidzakusungani pa nthaŵi yamayeso imene ilikudza m'dziko lonse lapansi, kuti anthu onse okhalamo adzayesedwe.
“Pa nthaŵi imeneyo wina akadzakuuzani kuti, ‘Ali panotu Khristu uja! Uyo ali apoyo!’ musadzakhulupirire. Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
Pambuyo pake ndidaona chilombo chija pamodzi ndi mafumu a pa dziko lapansi, ndi magulu ao ankhondo. Adaasonkhana kuti amenyane nkhondo ndi wokwera pa kavalo uja, pamodzi ndi gulu lake la ankhondo. pakuti chiweruzo chake chilichonse nchoona ndi cholungama. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene ankaipitsa dziko lapansi ndi chigololo chake, wamlanga chifukwa cha kupha atumiki ake.” Chilombocho chidagwidwa pamodzi ndi mneneri wonama uja amene anali atachita zozizwitsa pamaso pake. Zozizwitsazo, iye anali atanyenga nazo anthu amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, ndiponso anthu amene anali atapembedza fano lake lija. Chilombo chija ndi mneneri wonama uja, onse aŵiri adaŵaponya m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala yoyaka ya sulufure.
Nditayang'ana, ndidaona kavalo woyera. Wokwerapo wake anali ndi uta, ndipo adaapatsidwa chisoti chaufumu. Adatulukira ngati wogonjetsa kuchokera kumwamba, kuti akagonjetsenso ena pa dziko lapansi.
Mfumu yake inali mngelo wolamulira Chiphompho chija. Pa Chiyuda dzina lake ndi Abadoni, pa Chigriki ndi Apoliyoni (tanthauzo lake ndiye kuti, “Woononga uja”.)
Yesu adati, “Chenjerani kuti anthu angakusokezeni. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine.’ Azidzatinso, ‘Nthaŵi yayandikira.’ Amenewo musadzaŵatsate.
m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe.
Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Chilombo chachiŵirichi chinkachita zozizwitsa kwambiri, mpaka kumadzetsa moto pa dziko lapansi kuchokera kumwamba, anthu akuwona. Chinkanyenganso anthu okhala pa dziko lapansi ndi zozizwitsa zimene chidaaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Chinkauza anthu okhala pa dziko lapansiwo kuti apange fano lolemekezera chilombo chimene chidaavulazidwa ndi lupanga, koma nkukhalabe moyo.
“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda.
Komabe panali aneneri ena onama ngakhale pakati pa Aisraele omwe. Momwemonso pakati pa inu padzaoneka aphunzitsi onama. Iwowo adzaloŵetsa mwachinsinsi zophunzitsa zonama ndi zoononga, ngakhale kukana kumene Mbuye wao amene adaŵaombola, ndipo motero adzadziitanira chiwonongeko mwamsanga.
Woyenera kutengedwa ku ukapolo, kuukapoloko akapitadi. Woyenera kuphedwa ku nkhondo, kunkhondoko akaphedwadi. Pamenepa ndiye pamene anthu a Mulungu ayenera kuwonetsa kupirira ndi kulimbika m'chikhulupiriro.
Ameneyu ndi mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti mwiniwakeyo adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.
Paja nthaŵi idzafika pamene anthu azidzakana chiphunzitso choona. M'malo mwake, chifukwa cholakalaka kumva zoŵakomera zokha, adzadzisankhira aphunzitsi ochuluka omaŵauza zimene iwo akufuna. Adzafulatira choona, osafunanso kuchimva, ndipo adzangotsata nthano chabe.
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.
Pambuyo pake mmodzi mwa angelo asanu ndi aŵiri aja, amene anali ndi mikhate isanu ndi iŵiri ija, adadzalankhula nane. Adati, “Tiye kuno ndikakuwonetse m'mene akukaweruzidwira mkazi wadama wotchuka uja, amene akukhala pambali pa madzi ambiri. Ikufaniziranso mafumu asanu ndi aŵiri. Mwa iwo, asanu adagwa, imodzi ikulamulirabe, imodzi inayo siinafikebe. Koma ikadzafika, idzayenera kungokhala kanthaŵi. Tsono chilombo chija chimene kale chidaali chamoyo, koma tsopano si chamoyonso, chikufanizira mfumu yachisanu ndi chitatu ichocho, komabe ndi imodzi mwa mafumu asanu ndi aŵiri aja, ndipo ikupita kukaonongedwa. “Nyanga khumi zimene unaona, zikufanizira mafumu khumi amene asanayambebe kulamulira. Koma adzalandira mphamvu zolamulira ngati mafumu pa ora limodzi, pamodzi ndi chilombo chija. Mafumu khumi ameneŵa, cholinga chao ndi chimodzi, ndipo amapereka mphamvu zao ndi ulamuliro wao m'manja mwa chilombo chija. Iwoŵa adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa uja. Koma Mwanawankhosayo adzaŵagonjetsa, pakuti ndi Mbuye wa ambuye onse, ndi Mfumu ya mafumu onse. Ndipo anthu ake oitanidwa, osankhidwa ndi okhulupirika, nawonso adzapambana pamodzi naye.” Mngelo uja adandiwuzanso kuti, “Madzi unaona aja amene mkazi wadama uja wakhalapo, akufanizira mitundu ya anthu, makamu a anthu, mafuko a anthu ndiponso anthu a zilankhulo zosiyanasiyana. Tsono nyanga khumi unaona zija, pamodzi ndi chilombo chija, zidzadana naye mkazi wadamayo. Zidzamlanda zake zonse ndi kumsiya maliseche. Zidzadyako mnofu wake, kenaka nkumuponya pa moto kuti apserere. Zidzaterodi, pakuti Mulungu adazipatsa mtima wofuna kuchita zimene Iye adazikonzeratu. Zimenezi nzakuti zidzagwirizana pakupereka mphamvu zake zolamulira kwa chilombo chija, mpaka zitachitika zonse zimene Mulungu adanena. “Mkazi unaona uja akufanizira mzinda waukulu uja wolamulira mafumu onse a pa dziko lapansi.” Mafumu a pa dziko lapansi ankachita naye chigololo, ndipo anthu okhala pa dziko lapansi ankaledzera naye vinyo wa dama lakelo.”
Mwa iwe simudzaonekanso konse kuŵala kwa nyale. Mwa iwe simudzamvekanso konse mau a mkwati wamwamuna kapena wamkazi. Amalonda anali anthu otchuka kwambiri aja a pa dziko lapansi. Unkanyenga anthu a mitundu yonse ndi maula ako.”
Iwoŵa adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa uja. Koma Mwanawankhosayo adzaŵagonjetsa, pakuti ndi Mbuye wa ambuye onse, ndi Mfumu ya mafumu onse. Ndipo anthu ake oitanidwa, osankhidwa ndi okhulupirika, nawonso adzapambana pamodzi naye.”
Tsono mbonizo zikadzatsiriza umboni waowo, chilombo chotuluka m'Chiphompho chija chidzachita nazo nkhondo. Chidzazigonjetsa nkuzipha.
Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
Choyamba mumvetse izi: pa masiku otsiriza kudzafika anthu olalata, otsata zilakolako zao zoipa. Azidzalalata nkumanena kuti, “Kodi suja Ambuye adalonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nkale adamwalira makolo athu, koma zonse zili monga momwe Mulungu adazilengera poyamba paja.”
Chifukwa chokondetsa chuma, iwo adzayesa kupeza phindu pakukuuzani mau onyenga. Komatu chilango chao nchokonzeratu kale, ndipo chiwonongeko chao chikuŵadikira.
Paja adakuuzani kuti, “Pa masiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, otsata zilakolako zao zoipa.”
“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna. Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’ Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’
Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.” Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda.
Munthu wina aliyense asakupusitseni ndi mau onyenga, pakuti zinthu zotere ndizo zimadzetsa ukali wa Mulungu pa anthu omupandukira.
Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo. Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu.
Koma inu abale, simuli m'chimbulimbuli kuti tsikulo nkukudzidzimutsani ngati mbala. Paja nonsenu zanu zonse ndi zam'kuŵala, ndiye kuti zausana. Ife zathu si zausiku kapena zamumdima ai. Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera.
Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.
Paja anthu ena osasamala za Mulungu adaloŵa mobisika pakati panu. Iwo amapotoza kukoma mtima kwa Mulungu, ndi kukuyesa ufulu wochitira zonyansa. Amakana Yesu Khristu, amene Iye yekha ndiye Mbuye wathu ndi Mfumu yathu. Zakuti anthu ameneŵa adzalangidwa zidalembedwa kale lomwe.
Adachipembedza chinjoka chija chifukwa chidaapatsa ulamuliro wake kwa chilombo chija. Nachonso chilombo chija adachipembedza nkumanena kuti, “Ndani angafanane ndi chilombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”
Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta. Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu. Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino, opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu. Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.
“Monga momwe zidaachitikira pa nthaŵi ya Nowa, zidzateronso pa nthaŵi ya Mwana wa Munthu. Masiku amenewo anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kumakwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Pamenepo chigumula chidafika nkuŵaononga onse. Monga momwe zidaachitikiranso pa nthaŵi ya Loti. Anthu ankangodya ndi kumwa, ankagulitsana malonda, ankabzala mbeu, ankamanga nyumba. Koma tsiku limene Loti adatuluka m'Sodomu, Mulungu adagwetsa moto ndi miyala yoyaka ya sulufule nkuŵaononga onsewo. Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke.
Zidzaterodi, pakuti Mulungu adazipatsa mtima wofuna kuchita zimene Iye adazikonzeratu. Zimenezi nzakuti zidzagwirizana pakupereka mphamvu zake zolamulira kwa chilombo chija, mpaka zitachitika zonse zimene Mulungu adanena.
Momwemonso, mukadzaona zonse ndanena zija, mudzadziŵe kuti Mwana wa Munthu ali pafupi, ali pakhomo penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse.
Zimenezi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire nkukweza mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”
Pambuyo pake ndidamva mau ena ochokera Kumwamba. Adati, “Inu anthu anga, tulukanimo mumzindamo, kuti mungachimwire nawo pamodzi, miliri yao ingakugwereniko.
Pambuyo pake ndidamva ngati mau amphamvu a chinamtindi cha anthu Kumwamba. Mauwo ankati, “Aleluya! Chipulumutso, ulemerero ndi mphamvu ndi zake za Mulungu wathu, Apo ndidadzigwetsa ku mapazi ake kuti ndimpembedze. Koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ndiponso ngati abale ako amene amachitira Yesu umboni. Iwe pembedza Mulungu.” Pajatu kuchitira Yesu umboni ndiye thima la uneneri. Pambuyo pake ndidaona Kumwamba kutatsekuka, kavalo woyera nkuwoneka. Wokwerapo wake dzina lake ndi “Wokhulupirika”, ndiponso “Woona.” Poweruza, ndi pomenya nkhondo, amachita molungama. Maso ake anali psuu ngati malaŵi a moto, ndipo pamutu pake panali zisoti zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lolidziŵa iye yekha, osati wina aliyense. Chovala chake chinali choviika m'magazi, ndipo ankatchedwa, “Mau a Mulungu.” Magulu a ankhondo a Kumwamba ankamutsatira atakwera akavalo oyera, ndipo iwowo atavala zabafuta, zoyera ndi zangwiro. M'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa lotulukira kunja, loti adzalangire mitundu ya anthu. Adzaŵalamulira ndi ndodo yachitsulo, ndipo m'chopondera mphesa adzaponda mphesa za vinyo wa mkwiyo waukali wa Mulungu Mphambe. Pa mkanjo wake, ndi pantchafu pake padaalembedwa dzina loti, “Mfumu ya mafumu onse, ndi Mbuye wa ambuye onse.” Kenaka ndidaona mngelo mmodzi ataimirira pa dzuŵa. Adafuula mokweza mau, nauza mbalame zonse zouluka mu mlengalenga kuti, “Dzasonkhaneni ku mgonero waukulu wa Mulungu. Bwerani, mudzadye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi wa okwerapo, mnofu wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, ang'onoang'ono ndi akuluakulu.” Pambuyo pake ndidaona chilombo chija pamodzi ndi mafumu a pa dziko lapansi, ndi magulu ao ankhondo. Adaasonkhana kuti amenyane nkhondo ndi wokwera pa kavalo uja, pamodzi ndi gulu lake la ankhondo. pakuti chiweruzo chake chilichonse nchoona ndi cholungama. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene ankaipitsa dziko lapansi ndi chigololo chake, wamlanga chifukwa cha kupha atumiki ake.”
Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona. Mulungu amaŵakwiyira, chifukwa zimene munthu angathe kudziŵa zokhudza Mulungu iwo akuzidziŵa bwino lomwe, popeza kuti Mulungu mwini ndiye adaŵaululira zimenezi. Uthengawu Iye adaulonjeza kale kudzera mwa aneneri ake ndipo udalembedwa m'Malembo Oyera. Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Ndiye kuti pamene anthu osamala za Mulungu akuyesedwa, Iye amadziŵa kuŵapulumutsa kwake. Koma amadziŵanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona. Mulungu adakuitanirani zimenezi kudzera mwa Uthenga Wabwino umene tidakulalikirani. Adakuitanani kuti mulandire nao ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. Tsono abale, khalani olimbika, ndipo mugwiritse miyambo imene tidakuphunzitsani ndi mau apakamwa kapena am'makalata.