Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


107 Mau a m'Baibulo Okhudza Zonyansa

107 Mau a m'Baibulo Okhudza Zonyansa

Ndikufuna tikambirane za zinthu zimene Mulungu amaziona ngati zonyansa. M'buku lakale la chipangano, nthawi zambiri Mulungu ankalankhula za mafano ndi miyambo ya anthu osamudziwa Iye, monga kupembedza milungu yabodza. Izi zinali zonyansa kwa Iye. Mulungu ankauza anthu ake kuti asiye zimenezi, chifukwa sizinali zimene amawafunira.

Mwachitsanzo, m'buku la Deuteronomio 18:9-121, Mulungu amatitchula zamatsenga ndi ufiti ngati zinthu zomunyansa pamaso pake. Ngakhale m'chipangano chatsopano, Yesu anatiphunzitsa kufunika kwa moyo woyera. M'buku la Mateyu 15:18-202, Iye ananena kuti zinthu zotuluka m'kamwa mwathu, monga mabodza ndi mawu otukwana, zimatichititsa kukhala onyansa, chifukwa zimachokera mumtima. Mulungu amaona kuipa kulikonse mumtima mwathu ngati konyansa.

Mulungu amafuna kuti tikhale oyera ndi omvera mawu ake. Tiziyesetsa kupewa zinthu zimene Iye amaziona ngati zonyansa. Kuphunzira Baibulo n'kofunika kwambiri kuti tidziwe zimene Mulungu amafuna ndikupewa kuchita zinthu zomunyansa pamaso pake. Tikatero, tidzakhala paubwenzi wabwino ndi Iye.




Luka 16:15

Ndipo Iye adaŵauza kuti, “Inu mumadziwonetsa olungama pamaso pa anthu, koma Mulungu amaidziŵa mitima yanu. Pajatu zimene anthu amaziyesa zamtengowapatali, m'maso mwa Mulungu zimaoneka zonyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:1

Muyeso wonyenga umanyansa Chauta, koma muyeso wachilungamo umamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 23:18

Ndalama zozipeza mwa njira yadama yotereyi, yochitika ndi mkazi kapena mwamuna, musabwere nazo ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, kuti mukwaniritsire malonjezo anu, poti zimenezi Chauta, Mulungu wanu, amadana nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:16-19

Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa, mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa, mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:22

Usagone ndi mwamuna ngati mkazi. Chimenecho ndi chinthu chonyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:12

Chauta, Mulungu wanu, amadana nawo anthu ochita zoipa zimenezi. Chimene Mulungu akupirikitsira anthuŵa pamene inu mukufika ndi chifukwa chakuti anthuwo ankachita zoipa zoterezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:13

Munthu akagona ndi munthu wamwamuna mnzake ngati mkazi, onsewo achita chinthu chonyansa, ndipo ayenera kuphedwa. Magazi ao akhale pa iwowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:25-26

Mudzatenthe mafano ao ofanizira milungu yao. Musadzakhumbire siliva kapena golide amene iwo adapangira mafanowo. Musadzatengeko zimenezi kuti mungagwe mu msampha, popeza kuti zimenezo zimamnyansa Chauta, Mulungu wanu. Musadzaloŵe nazo m'nyumba mwanu zimenezi, kuti tsoka limene lili pa iwowo lingadzakhale pa inu. Mudzadane ndi mafanowo ndi kuŵanyoza, chifukwa Chauta adaŵatemberera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:27

Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 17:1

Musadzapereke ng'ombe kapena nkhosa yachilema ngati nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu. Musadzapereke nyama iliyonse yopunduka, chifukwa Mulungu wanu amadana nazo zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:10-12

Pakati panu pasadzapezeke wopereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto ngati nsembe. Pasaoneke munthu woombeza kapena woyeseza kulosa zam'tsogolo, kapena wogwiritsa ntchito nyanga kapena zithumwa. Pasapezekenso munthu wopempha nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Chauta, Mulungu wanu, amadana nawo anthu ochita zoipa zimenezi. Chimene Mulungu akupirikitsira anthuŵa pamene inu mukufika ndi chifukwa chakuti anthuwo ankachita zoipa zoterezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:5

Akazi asamavale zovala za amuna, chimodzimodzi amuna asamavale zovala za akazi. Chauta, Mulungu wanu, amanyansidwa nawo anthu ochita zotere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:13-14

Musabwere nazonso nsembe zanu zachabechabe. Utsi wake umandinyansa. Sindingapirire misonkhano yanu yamapemphero, kapenanso zikondwerero za pokhala mwezi ndi za Sabata, sindingapirire mapemphero oipitsidwa ndi machimo. Zikondwerero zanu za pokhala mwezi ndi masiku anu oyera ndimadana nazo. Zasanduka katundu wondilemera, ndatopa nako kuŵapirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:22

Pakamwa pabodza pamamnyansa Chauta. Koma anthu ochita zinthu mokhulupirika amamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:8

Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:5

Anthu amenewo mudzaŵachite izi: mudzaphwanye maguwa ao, mudzaphwanye miyala yoimiritsa yopembedzapo, mudzagwetse mafano ao aja a Aserimu, ndipo mudzatenthe mafano ao osema.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:26

Maganizo a anthu oipa amamnyansa Chauta, koma mau a anthu olungama amamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 25:16

Chauta amadana ndi anthu onyenga mwa njira yotereyi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:4-5

“Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko. Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 14:24

Kuwonjezera pamenepo, m'dzikomo munkapezeka anthu ena ochitana zadama potsata chipembedzo chao. Anthu ankachita zonyansa zonse zimene inkachita mitundu ya anthu amene Chauta adaaipirikitsa pofika Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 32:35

Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala m'chigwa cha Benihinomu, kuti apereke ana ao aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Sindidalamule zimenezo ndine, ndipo sindidaganizeko kuti iwo nkuchita zonyansa zoterezi, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda pakutero.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:15

“Mudzaona ‘Chosakaza chonyansa chija’ chimene mneneri Daniele adaanena, atachiimika m'Nyumba ya Mulungu. (Amene ukuŵerengawe, umvetse bwino.)

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 11:10-13

Koma zamoyo zonse zam'nyanja kapena zam'mitsinje zopanda zilimba ndi mamba, tizilombo tonse tam'madzi ndi zamoyo zonse zopezeka m'menemo, nzonyansa kwa inu. Zimenezo zikhale zonyansa kwa inu, ndipo musadye. Zikafa zikhalebe zonyansa kwa inu. Zamoyo zonse zam'madzi zopanda zilimba ndi mamba, nzonyansa kwa inu. “Ndipo mbalame zimene muyenera kuziyesa zonyansa, zoti simuyenera kudya, popeza kuti nzonyansa kwa inu, ndi izi: mphungu, nkhwazi, ndi muimba,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 27:15

“Atembereredwe aliyense wopanga fano losema kapena loumba, namalipembedza mobisa. Chauta amanyansidwa nacho chinthu chopanga mmisiricho.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:3

“Koma pali ena amene amangochita zoŵakomera. Kwa iwo nchimodzimodzi kupereka ng'ombe yamphongo ngati nsembe kapena kupha munthu, kupha mwanawankhosa kuti aperekere nsembe kapena kupha galu, kupereka chopereka cha chakudya kapena kupereka magazi a nkhumba, kupereka lubani ku nsembe yachikumbutso kapena kupembedza fano. Anthu ameneŵa mtima wao umakondwera nazo zonyansa zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:8

Nsembe ya anthu oipa mtima imamuipira Chauta, koma pemphero la anthu olungama limamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:5

Munthu aliyense wodzikuza amanyansa Chauta, ndithu ameneyo sadzalephera kulangidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:32

Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa, koma olungama okha amayanjana nawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:31

Musadzapembedze Chauta, Mulungu wanu, mofanafana ndi m'mene iwo amapembedzera milungu yaoyo. Iwo adachita zoipa zoopsa zambiri zimene Chauta amadana nazo, mpaka kutentha ana ao aamuna ndi aakazi pa moto pakuŵapereka kwa milungu yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:20

Anthu a mtima woipa amamnyansa Chauta, koma anthu a makhalidwe abwino amamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:15

Woweruza munthu woipa mtima kuti ndi wosalakwa, amanyansa Chauta, nayenso wopasa mlandu munthu wosalakwa amaipira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:10

Masikelo ndi miyeso ina yoyesera zinthu zikakhala zonyenga, zonsezo zimamunyansa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 2:11

Anthu a ku Yuda akhala osakhulupirika, ku Israele ndi ku Yerusalemu akhala akuchita zinthu zonyansa. Anthu a ku Yuda aipitsa Nyumba ya Chauta imene Iye amaikonda. Akhala akukwatira akazi opembedza milungu yachikunja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:13

Kuwopa Chauta nkudana ndi zoipa. Kunyada, kudzitama, kuchita zoipa ndi kulankhula zonyenga, zonsezo ndimadana nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:50

Ankadzitukumula kwambiri namachita zonyansa zambiri pamaso panga. Nchifukwa chake ndidaŵachotsa monga m'mene waoneramu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 8:6

Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuwona zimene Aisraele akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene akuchita kuno, zondichotsa ku Nyumba yanga yoyera? Ndipotu udzaona zonyansa zina zazikulu kuposa zimenezi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:10

Pambuyo pake mumabwera kudzaima pamaso panga m'Nyumba ino, Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa. Mumanena kuti, ‘Tapulumuka ife,’ koma mumapitirirabe kumangochita zonyansa zonsezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:12-15

Munthu wachabechabe, munthu woipa, amangoyendayenda nkumalankhula zabodza. Amatsinzinira masoŵa nkumakwekwesa pansi mapazi ake, amalozaloza ndi chala chake. Amalingalira zoipa ndi mtima wake wopotoka, amangokhalira kuvundula madzi pakati pa anthu. Nchifukwa chake tsoka lidzamgwera modzidzimutsa. Pa kamphindi kochepa adzaonongedwa, osapulumuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 17:4-5

Mkaziyo adaavala zovala zofiirira ndi zamlangali, ndipo adaadzikongoletsa ndi golide, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu. M'manja mwake anali ndi chikho chagolide chodzaza ndi zonyansa, ndi zoipa za ntchito zake zadama. Pamphumi pake padaalembedwa dzina lachinsinsi lakuti, “Babiloni wotchuka uja, manthu wa achiwerewere onse, ndi a zonyansa zonse za dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:29

“Musaipitse mwana wanu wamkazi pakumsandutsa mkazi wachiwerewere kuti dziko lingasanduke la anthu adama ndi loipa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:24

Inuyo sindinu kanthu konse, ndipo zochita zanu nzopandapake. Amene amakupembedzaniyo amandinyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:9

Zochita za anthu oipa zimamnyansa Chauta, koma wochita zachilungamo Chauta amamkonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:26-30

Koma inuyo mutsate malamulo anga ndi kuchita zimene ndikukulamulani. Musachite chilichonse mwa zonyansazi, ngakhale inu mbadwanu kapena mlendo wokhala pakati panu. Pajatu anthu am'dzikomo amene adaalipo inu musanafike, ankachita zonyansa zonsezi, kotero kuti dziko lidaipitsidwa. Musachite zimenezi kuti dziko lingakusanzeni mukaliipitsa, monga momwe lidasanzira mtundu wa anthu umene udaalipo m'dzikomo, inu musanafike. Pakuti aliyense amene adzachita zonyansa zimenezi, adzachotsedwa pakati pa anthu anzake. Musamachita zimene amachita anthu a ku Ejipito kumene munkakhala kuja, ndiponso musadzachite zimene amachita anthu a ku Kanani kumene ndikukufikitsaniko. Musatsate miyambo yao. Tsono mverani malamulo anga oletsa kutsata zonyansa zimene anthu ankazichita, inu musanafike. Musadziipitse nazo konse. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 5:11

“Pali Ine ndemwe Mulungu wamoyo, ndidzakuwonongani mopanda chifundo, chifukwa choti mwaipitsa Nyumba yanga ndi mafano anu oipa ndi miyambo yanu yonyansa. Tsono Ine sindidzakulekererani, sindidzakuchitirani chisoni mpang'ono pomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:9

Wina akamakana kumvera malamulo, ngakhale mapemphero ake amanyansira Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 44:4

Komabe ine ndidakhala ndikutuma atumiki anga aneneri kuti adzakuuzeni kuti, ‘Musamachita zoipa zimene Ine ndimadana nazo.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 23:13

Pambuyo pake mfumuyo idaononganso akachisi opembedzerapo mafano amene anali kuvuma kwa Yerusalemu, kumwera kwa phiri lotchedwa Chiwonongeko. Maguwawo Solomoni, mfumu ya ku Israele, adaaŵamangira fano lonyansa la Asidoni lotchedwa Asitoreti, ndi la Amowabu lotchedwa Kemosi, ndiponso la Aamoni lotchedwa Milikomu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 28:3

Adafukiza lubani ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza, potsata miyambo yonyansa ya anthu a mitundu ina imene Chauta adaaipirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:23

Ndipo usagone ndi nyama ndi kudziipitsa nayo, ngakhalenso mkazi aliyense asadzipereke kwa nyama kuti agone nayo, pakuti chimenecho ndi chisokonezo choopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:19

Palibe wolingalira, palibe wanzeru kapena womvetsa woti anganene kuti, “Chigawo china cha mtengo ndidatentha pa moto, pa makala ake ndidaphikapo buledi, ndidaotchapo nyama ndipo ndidadya. Tsopano chigawo chotsalachi ndipangira chinthu chonyansa! Monga ine ndizipembedza mtengo?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:27

Nsembe ya anthu oipa imamnyansa Chauta, nanji tsono akaipereka ndi cholinga choipa!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 7:20

“Kale ankanyada chifukwa cha zodzikongoletsera zao zamakaka. Koma ankazigwiritsa ntchito popanga mafano onyansa. Nchifukwa chake zodzikongoletsera zaozo ndidzazisandutsa zoŵanyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 3:2

Mumadana ndi zabwino, mumakonda zoipa. Anthu anga mumaŵasenda amoyo, ndi kukangadzula mnofu wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 6:15

Kodi akamachita zonyansa, amachita manyazi ngati? Iyai, sachita manyazi mpang'ono pomwe. Sadziŵa nkugwetsa nkhope komwe. Nchifukwa chake adzagwera pakati pa anzao amene adagwa kale. Adzagweratu pa tsiku limene ndidzaŵalanga!” Akutero Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 8:12

Kodi akamachita zonyansa, amachita manyazi ngati? Iyai, sankachita manyazi mpang'ono pomwe. Sadziŵa nkugwetsa nkhope komwe. Nchifukwa chake adzagwera pakati pa anzao amene adagwa kale. Adzagweratu pa tsiku limene ndidzaŵalanga,” akutero Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:20

Tsoka kwa amene zoipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoipa, amene mdima amauyesa kuŵala, ndipo kuŵala amakuyesa mdima, amene zoŵaŵa amaziyesa zozuna, ndipo zozuna amaziyesa zoŵaŵa!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 9:10

Chauta akuti, “Israele ndidampeza ngati mphesa zam'thengo. Makolo ake aja ndidaŵakondwerera ngati nkhuyu zoyamba kupsa. Koma iwowo adapita kwa Baala-Peori, ndipo kumeneko adadzipereka kwa Baala. Motero adasanduka chinthu chonyansa ngati fano laolo, limene ankalikonda lija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:15

Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:3-4

Senderani kuno, inu anthu ochita zoipa, pakuti muli ngati zidzukulu zam'chigololo, zochokera m'zadama. Kodi inu mukuseŵera ndi yani? Kodi mukunena yani? Mukunyoza yani? Kodi ochimwa sindinu? Onyenga sindinu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 8:13

Chauta adandiwuzanso kuti, “Udzaŵaonanso akuchita zonyansa zina zazikulu kupambana zimenezi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 2:7

Ndidakufikitsani ku dziko lachonde kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina. Koma mutangoloŵa m'dzikolo, mudaliipitsa, dziko limene ndidakupatsani mudalisandutsa lonyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 13:27

Ndaona zonyansa zanu, zigololo zanu, kutchetcherera kwanu, ndi ziwerewere zanu zochitika pa mapiri, kuthengo. Tsoka kwa inu a ku Yerusalemu! Mudzakhala osayeretsedwabe pa zachipembedzo mpaka liti?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:2

“Iwe mwana wa munthu, umuwonetse Yerusalemu makhalidwe ake onyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zefaniya 1:17

Chauta akuti, “Chifukwa anthuwo adandichimwira, ndidzaŵasautsa koopsa, kotero kuti azidzayenda ngati akhungu. Magazi ao adzachita kuti mwaa ngati fumbi, matupi adzangoti vuu, nkumaola ngati ndoŵe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 6:10

Pakati pa Aisraele ndaonapo zinthu zonyansa. Aefuremu adachita zadama, Aisraele adadziipitsa pakupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 22:11

Ena amachita chigololo ndi akazi a anzao, ena amachita zoipa ndi apongozi ao. Enanso amaipitsa alongo ao, ana a atate ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 14:1

Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 5:30-31

M'dziko muno mwachitika chinthu chododometsa ndi choopsa. Aneneri akulosa zabodza, ndipo ansembe akuvomerezana nawo. Komabe anthu anga akukondanso zomwezo. Kodi mudzatani potsiriza?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 33:29

Ndikadzalanga anthu chifukwa cha zonyansa zimene adachita, ndi kusandutsa dzikolo kuti likhale tsala ndiponso chipululu, pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 16:18

Ndidzaŵalanga moŵirikiza, chifukwa cha kuipa kwao ndi machimo ao. Ndidzatero chifukwa chakuti aipitsa dziko langa ndi mafano ao amene ali ngati mitembo, ndipo dziko limene lili choloŵa changa adalidzaza ndi mafano ao onyansa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:9

Kukonzekera zopusa nkuchimwa, munthu wonyoza amanyansa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:21

Usatenge mwana wako aliyense kuti umpereke ngati nsembe yamoto kwa Moleki, kuti ungaipitse dzina la Mulungu wako. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:16

Adamchititsa nsanje ndi mafano ao achilendo, ndipo zonyansa zimene adachita zidamkwiyitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 44:22

Nchifukwa chake Chauta sadathenso kupirira ntchito zanu zoipa ndi zonyansa zimene munkachita. Choncho dziko lanu lidasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa, dziko lopanda anthu, monga liliri leromu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:1-5

Chauta adauza Mose kuti, “Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo onsewo aphedwe. Munthu wogona ndi mkazi wa bambo wake, wavula bambo wake, ndipo onsewo ayenera kuphedwa. Magazi ao akhale pa iwowo. Munthu akagona ndi mkazi wa mwana wake, onsewo ayenera kuphedwa. Iwowo achita chigololo pachibale, ndipo magazi ao akhale pa iwowo. Munthu akagona ndi munthu wamwamuna mnzake ngati mkazi, onsewo achita chinthu chonyansa, ndipo ayenera kuphedwa. Magazi ao akhale pa iwowo. Munthu akakwatira mkazi, nakwatiranso mai wake wa mkaziyo, kuteroko nkuchita chinthu choipa kwambiri. Onsewo ayenera kuŵatentha pa moto, mwamunayo pamodzi ndi akazi omwewo, kuti chinthu choipa kwambiri chotere chisapezeke pakati panu. Mwamuna akagona ndi nyama, ayenera kuphedwa, ndipo nyamayo muiphenso. Mkazi akagona ndi nyama, aphedwe pamodzi ndi nyamayo. Aphedwe ndipo magazi ao akhale pa mkaziyo ndi nyamayo. “Munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, onse aŵiriwo achita chinthu chochititsa manyazi, ndipo onsewo aphedwe pakhamu pa anthu a mtundu wao. Chifukwa aphwanya malamulo motero, alipire choipa chake. Munthu akagona ndi mkazi wosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, nayenso mkaziyo wadzivula. Onse aŵiriwo achotsedwe pakati pa anthu anzao. Musavule mbale wa mai wanu kapena mlongo wa bambo wanu, poti kuteroko nkuvula wa pa chibale chanu. Onse aŵiriwo adzalipira machimo ao. “Uza Aisraele kuti: Mwisraele aliyense, kapena mlendo wokhala nao m'dziko mwanu, akapereka ana ake kwa Moleki, aphedwe: anthu am'dzikomo amponye miyala. Munthu akagona ndi mkazi wa mbale wa bambo wake, wavula mbale wa bambo wake. Onse aŵiriwo adzasenza machimo ao ndipo adzafa opanda ana. Munthu akakwatira mkazi wa mbale wake, ndiye kuti wachita chinthu chonyansa. Wavula mbale wake, ndipo onse aŵiriwo adzakhala opanda ana. “Nchifukwa chake muzisunga malamulo anga, ndipo muzichita zonse zimene ndimakulamulani ndi kuzitsata, kuti dziko limene mukupita kuti mukakhalemolo lingakudeni. Musatsanzire miyambo ya mtundu wa anthu amene ndikuupirikitsa inu mukufika. Iwo ankachita zimenezi, nchifukwa chake ndidanyansidwa nawo kwambiri. Koma inuyo ndakuuzani kuti: Mudzalandira dziko lao, ndipo ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale lanu, dziko lake lamwanaalirenji. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu. Nchifukwa chake muzisiyanitsa pakati pa nyama zoipitsidwa ndi zosaipitsidwa, pakati pa mbalame zosaipitsidwa ndi zoipitsidwa. Musadziipitse pakudya nyama kapena mbalame, kapenanso zinthu zilizonse zimene zadzaza pansi pano, zomwe ndazipatula kuti inu muzidziŵe kuti nzoipitsidwa. Muzikhala oyera pamaso panga, pakuti Ine Chauta ndine woyera, ndipo ndakupatulani pakati pa anthu onse kuti mukhale anthu anga. “Mwamuna kapena mkazi wolankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena munthu wanyanga, ayenera kuphedwa. Aŵaponye miyala, ndipo magazi ao akhale pa iwowo.” Munthu ameneyo ndidzamfulatira, ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anzake, chifukwa wapereka ana ake kwa Moleki ndi kuipitsa malo anga oyera, ndiponso waipitsa dzina langa loyera. Anthu am'dzikomo akachita ngati sakumuwona munthuyo, pamene akupereka mmodzi mwa ana ake kwa Moleki, namleka osamupha, Ineyo ndidzamfulatira munthu ameneyo ndi banja lake lonse. Ndidzaŵachotsa pakati pa anthu anzao, pamodzi ndi onse amene amaŵatsanzira nadziipitsa pakupembedza Moleki.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 19:4-5

Anthu andikana Ine, ndipo aipitsa malo ano. Akhala akufukiza lubani kwa milungu yachilendo imene iwowo, makolo ao ndiponso mafumu a ku Yuda sadaidziŵe. Ndipo pa malo ano adakhetserapo magazi a anthu osachimwa. Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala, pamene amaperekapo ana ao kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala. Zimenezo sindidalamule konse, sindidazilankhule, ngakhale kuziganiza komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 8:17

Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziwona zimenezi? Ayuda sakukhutira nazo zonyansa akuchita panozi. Koma akufalitsanso zandeu m'dziko lonse. Motero akuutsa ukali wanga, akundipsetsa mtima ndi zochita zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:5

Anthu onyada sangathe kuwonekera pamaso panu. Inu mumadana ndi anthu onse ochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 5:21-24

Chauta akuti, “Masiku anu achikondwerero ndimadana nawo ndipo ndimaŵanyoza. Misonkhano yanu yachipembedzo siindikondwetsa konse. Ngakhale mudzapereke nsembe zanu zopsereza ndiponso zaufa, Ine sindidzazivomera. Nsembe zanu zachiyanjano zophera ng'ombe zonenepa sindidzaziyang'ana nkomwe. Musandisokose nazo nyimbo zanu zachipembedzo, sindingathe kupirira kulira kwa azeze anu. Koma kuweruza kwanu kwangwiro kuziyenda kosalekeza ngati madzi, kulungama kwanu kukhale ngati mtsinje wosaphwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:24-27

Nchifukwa chake Mulungu adaŵasiya kuti azingochita zonyansa zimene mitima yao inkalakalaka, mpaka kunyazitsa matupi ao. Adasiya zoona za Mulungu namatsata zabodza. Adayamba kupembedza ndi kutumikira zolengedwa m'malo mwa kupembedza ndi kutumikira Mlengi mwini, amene ali woyenera kumlemekeza mpaka muyaya. Amen. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adaŵasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe adaleka machitidwe achibadwa pa zachikwati, namatsata machitidwe ena otsutsana ndi achibadwawo. Chimodzimodzinso amuna, adaleka machitidwe achibadwa osirira akazi, nkumakhumbana amuna okhaokha. Ankachitana zamanyazi, motero adadziitanira chilango choyenera molingana ndi zochita zao zopotokazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:27

Anthu osoŵa chilungamo amanyansa anthu ochita chilungamo, monga momwe anthu abwino amanyansira anthu oipa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:24

Tsono musagwadire milungu yao kapena kuipembedza. Musamachita nao zimene amachita anthu amenewo. Mukaonongeretu milungu yao, ndiponso mukaphwanye miyala yao yopembedzerapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 21:26

Iyeyo adachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga m'mene ankachitira Aamori aja, amene Chauta adaŵachotsa pamene Aisraele ankafika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 19:13

Nyumba za ku Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti, chifukwa ndizo nyumba zimene pa madenga ao ankaotcherapo nsembe kwa milungu ya mumlengalenga, namapereka nsembe yazakumwa kwa milungu ina.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:20-21

Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana. Simungathe kumwera m'chikho cha Ambuye nkumweranso m'chikho cha Satana. Simungathe kudyera pa tebulo la Ambuye nkudyeranso pa tebulo la Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:30

Chauta ataiwononga mitunduyo inu mukuwona, mukachenjere kuti musakatsate zipembedzo zao. Musadzayese kufunsafunsa za milungu yao kuti, “Kodi mitundu ya anthu iyi imapembedza bwanji milungu yao, kuti ifenso tichite chimodzimodzi?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 15:23

Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:9

Mukadzaloŵa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musakatsate machitidwe onyansa a mitundu ya anthu akumeneko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:30

Chauta akuti, “Anthu a ku Yuda achita zoipa Ine ndikuwona. Aimika mafano ao onyansa m'Nyumba ino imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo aiipitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:58

Motero iwe uyenera kulangidwa chifukwa cha zigololo zako ndi makhalidwe ako onyansa. Ndikutero Ine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 15:8

Tsono Asa atamva mau ameneŵa, mau aulosi a Azariya mwana wa Odedi, adalimba mtima. Adachotsa mafano onyansa ku dziko lonse la Yuda ndi la Benjamini. Adachotsanso mafano ku mizinda imene adailanda ku dziko lamapiri la Efuremu. Ndipo adakonza guwa la Chauta limene linali patsogolo pa khonde la Nyumba ya Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 16:22

Ndipo musadzaimiritse miyala yachipembedzo, popeza kuti Chauta, Mulungu wanu, amadana nazo zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:43

Iwe udaiŵala masiku a ubwana wako, ndipo udandikwiyitsa ndi zinthu zonse zimene udachita. Nchifukwa chake Ine ndidzakubwezera pamutu pako chilango cha zimene udachitazo. Pajatu udaonjezera zigololo pa zonyansa zako zina zonse. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:33

Asadzakhale m'dziko mwanu, kuwopa kuti angadzakuchimwitseni. Mukamapembedza milungu yao, ndithu mudzakodwa mu msampha.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:10

Amene amasokeza anthu olungama kuti azitsata njira yoipa, adzagwa m'dzenje lake lomwe. Koma anthu amene alibe cholakwa adzalandira choloŵa chabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:24

“Musadziipitse ndi zinthu zimenezi, chifukwa mitundu ina ya anthu amene ndikuipirikitsa inu mukubwera, idadziipitsa ndi zoipa zoterezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 6:30

Iwo ali ngati siliva wotaya, pakuti Chauta waŵakana.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 3:8-9

Zoonadi Yerusalemu akusakazika ndipo Yuda akugwa, chifukwa zokamba ndiponso ntchito za anthu am'menemo nzonyoza Chauta. Salabadako za ulemerero wa Mulungu. Maonekedwe a nkhope zao amaŵatsutsa. Amachimwa poyera ngati m'mene ankachitira anthu a mu Sodomu, sabisa konse. Tsoka kwa iwowo, achita kudziputira okha mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 22:2

“Iwe mwana wa munthu, kodi ukufuna kudzaweruza Yerusalemu? Kudzaweruza mzinda wodzaza ndi anthu opha anzaoŵa? Tsono uudzudzule chifukwa cha machitidwe ake onse onyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:27

Onse amene ali kutali ndi Inu adzaonongeka, Inu mumaŵaononga amene ali osakhulupirika kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 5:23

Koma anthu ameneŵa ndi okanika ndiponso a mtima waupandu. Adapatuka ndipo adapitiratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Wamphamvuzonse, wodalitsidwa ndi ulemerero wonse, dzina lanu Mulungu ndi lokwezeka nthawi zonse. Ndinu wapamwamba, wosaoneka, ndi woopsa, ndipo ndikukupatsani ulemu wanga wonse lero Ambuye wanga. Ndinu Woyera, ndikukulemekezani chifukwa cha zimene muli, ndikukulemekezani chifukwa cha zonse zomwe mwandithandiza, chifukwa cha chikondi chanu chosatha ndi chifundo chanu. Ambuye, ndikudziwa kuti pali zambiri zomwe ndiyenera kusintha, koma ndikuulula kuti sindingathe ndi mphamvu zanga. Ndikufuna thandizo lanu kuti ndizitsatira chifuniro chanu osati zilakolako za thupi langa. Mundilengere mtima woyera Ambuye, ndi kundikonzanso mzimu wolungama mkati mwanga. Mundipatse chiyero chanu, kuti moyo wanga wonse ukhale woyera kuti ndisachite chilichonse chomwe chingakukhumudwitseni. Mundipatse mantha ndi ulemu pamaso panu, kuti ndizikulemekezani ndi moyo wanga ndi maganizo anga. Mundisinthe kukhala munthu watsopano amene amakhala kokha kuti akukondweretseni ndi kukweza dzina lanu. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa