Ana inu, ana ndi dalitso lochokera kwa Mulungu. Tiyenera kuwaphunzitsa mawu a Mulungu kuyambira ali aang'ono, kuwaphunzitsa kumuopa Iye. Akakumana ndi mavuto m'moyo wawo, adzakumbukira zimene anaphunzira ndipo adzafuna Mulungu.
Ambuye Yesu amakonda ana, ndipo amatiuza ife akuluakulu kuti tikhale ngati iwo kuti tilowe mu ufumu wakumwamba. Monga mmene Baibulo limatiuza, “Yesu anati: Lolani ana aang’ono abwere kwa Ine, musawaletse; pakuti ufumu wakumwamba uli wa otere.” (Mateyu 19:14)
Mtima woyera wa mwana, kudzichepetsa kwawo, ndi mmene amamvekelera msanga kukhululukira ena, ndi makhalidwe abwino amene ana ali nawo, ndipo Mulungu amawakonda chifukwa cha zimenezi. Tiyenera kusamalira makhalidwe amenewa mwa kuwaphunzitsa mawu a Mulungu usana ndi usiku. “Unikire mwana njira yoyenera iye; angakhale wokalamba sadzachoka m’menemo.” (Miyambo 22:6)
Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.
ndipo adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mukapanda kusintha ndi kusanduka ngati ana, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.
nafunsa Yesu kuti, “Kodi mukumva zimene akunenazi?” Yesu adaŵayankha kuti, “Inde. Kani simudaŵerenge konse mau a Mulungu aja akuti, ‘Mudaphunzitsa ana ndi makanda omwe kukutamandani kotheratu?’ ”
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
Nawonso ana ndi makanda omwe amauimbira. Mwamanga linga chifukwa cha adani anu, kuti mugonjetse onse okuukirani.
Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.”
Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.”
Nchifukwa chake munthu wodzichepetsa ngati mwana uyu, ameneyo ndiye wamkulu mu Ufumu wakumwamba.
Iye ndi a m'banja mwake atabatizidwa, iyeyo adatipempha kuti, “Ngati mwandiwonadi kuti ndine munthu wokhulupirira Ambuye, dzaloŵeni m'nyumba mwanga, mudzakhale nafe.” Mwakuti adatikakamiza ndithu, ife nkukaloŵadi.
Nthaŵi yomweyo, ngakhale unali usiku, iye adaŵatenga nakaŵatsuka mabala ao. Ndipo pompo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake adabatizidwa.
Krispo, mkulu wa nyumba yamapempheroyo pamodzi ndi onse a pa banja lake adakhulupirira Ambuye. Ndipo anthu ambiri a ku Korinto atamva mau a Paulo, adakhulupirira nabatizidwa.
Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.
Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.
Pamene mudabatizidwa, mudachita ngati kuikidwa m'manda pamodzi ndi Khristu. Ndipo ndi ubatizowo mudaukitsidwanso pamodzi naye, pakukhulupirira mphamvu za Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.
Anthu ena ankabwera ndi ana omwe kwa Yesu kuti aŵakhudze. Ophunzira ake poona zimenezi, ankaŵazazira. Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere. Ndithu ndikunenetsa kuti amene salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzaloŵamo.”
Yesu ataona zimenezi, adakalipa naŵauza kuti, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.
Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao.
“Anthu aŵa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angaŵaletse kubatizidwa ndi madzi?” Motero adalamula kuti abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Ndipo anthuwo adampempha kuti akhale nawo masiku angapo.
Iyeyo adzakuuza mau amene iwe udzapulumuka nawo, ndiponso onse a m'banja mwako.’
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.
Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu. Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.
Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye. M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse. Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu. Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika. Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano. Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye. Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, kuti angataye mtima. Inu antchito, muziŵamvera pa zonse ambuye anu apansipano. Musamangochitatu zimenezi pamene muli pamaso pao kuti akuyamikireni, koma muziŵamvera ndi mtima wonse, chifukwa choopa Ambuye. Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu. Koma munthu amene amachita zosalungama, zidzamubwerera, chifukwa Mulungu amaweruza mosakondera. Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.
Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Kubatizidwa kumeneku si kuchotsedwa litsiro la m'thupi, koma kudzipereka kwa Mulungu ndi mtima woona, kudzera mwa Yesu Khristu
Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa.
Tsiku lina anthu onse aja atabatizidwa, Yesu nayenso adabatizidwa. Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka,
Koma pamene Filipo ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, ndiponso za dzina la Yesu Khristu, anthu adakhulupirira, ndipo adabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.
Pompo m'maso mwake mudachoka zinthu zonga mamba a nsomba, ndipo adayambanso kupenya. Adaimirira nabatizidwa,
Nanga tsono ukuchedweranji? Dzuka ndi kutama dzina lake mopemba, ubatizidwe ndi kusambitsidwa kuti machimo ako achoke.’ ”
Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano.
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwa m'madzi ndi mwa Mzimu Woyera, sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu.
Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi ndi mwa magazi. Sadabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi mwa magazi omwe. Ndipo Mzimu Woyera ndiye amene amachitirapo umboni, pakuti Mzimuyo ndiye choona.
Ine sindinkamudziŵa, koma Mulungu amene adandituma kudzabatiza ndi madzi, ndiye adaandiwuza kuti, ‘Amene udzaone Mzimu Woyera akutsika ndi kukhazikika pa Iye, ndi Iyeyo wobatiza mwa Mzimu Woyera.’
Koma Afarisi ndi akatswiri a Malamulo, pakukana kubatizidwa ndi iye, adakana okha zimene Mulungu adafuna kuŵachitira.
Kodi inu simukudziŵa kuti tonse amene tidasanduka amodzi ndi Khristu Yesu pakubatizidwa, ndi ubatizo womwewo tidasandukanso amodzi ndi Iye mu imfa yake?
ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Ndakhala ndikudalira Inu chibadwire changa, Inu mwakhala Mulungu wanga kuyambira pamene mai wanga adandibala.
Ndidzathira madzi pa dziko louma, ndidzayendetsa mitsinje m'chipululu. Ndidzatumizira ana anu Mzimu wanga, ndidzatsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
Chauta akuyankha kuti, “Ndithudi, ankhondo adzaŵalanda akaidi ao, ndipo mfumu yankhalwe adzailanda zofunkha zake. Ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu, ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
Ndidzakuwazani madzi angwiro, ndipo mudzayera, zonse zokuipitsani zidzachoka. Ndiponso ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse.
Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.
Paja Khristu adandituma, osati kuti ndizibatiza ai, koma kuti ndizilalika Uthenga Wabwino. Ndipo ndiyenera kumaulalika mosagwiritsa ntchito luso lake la ulaliki, kuwopa kuti mtanda wa Khristu ungatheretu mphamvu.
Kuumbalidwa si kanthu, kusaumbalidwa si kanthunso, chachikulu nchakuti Mulungu apatse munthu moyo watsopano.
Motero mumtambomo ndi m'nyanjamo onsewo adachita ngati kubatizidwa ndi kukhala amodzi ndi Mose.
Iye sadzachita makani, kapena kufuula. Palibe munthu wodzamva mau ake m'miseu ya m'mizinda.
Inu anyamata pamodzi ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe! Onsewo atamande dzina la Chauta, pakuti dzina lake lokha nlolemekezeka, ulemerero wake ndi woposa, pansi pano nkumwamba komwe.
Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani, Inu Chauta, ndinu amene ndimakudalirani kuyambira ubwana wanga.
Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.